Ripoti la Olengeza Ufumu
Yehova Amadalitsa Kuwumirira
MBONI ZA YEHOVA zimamva chikondi chozama kaamba ka Yehova Mulungu ndi thayo kwa anthu anzawo, kuwasonkhezera iwo kuyesera kupereka mwaŵi kwa aliyense wa kumva mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu. (Mateyu 24:14) Chimenecho ndicho chifukwa chake mlongo anagamulapo kulalikira kwa asilikali ankhondo ndi mabanja awo m’mudzi wa asilikali ankhondo m’gawo lake.
Nthaŵi iriyonse imene anayesera, iye anakanizidwa kulowa ndi kaputeni wolamulira. Iye akusimba kuti: “Chotero ndinagamulapo kuwona nduna yolamulira, kaputeni wamkulu. Pamene ndinatumira foni mlembi wake, iye anakana kundigwirizanitsa ine ndi kaputeni wamkuluyo. Ndinakonza kumuyendera kaputeni wamkuluyo kunyumba kwake, popeza ankakhala kutali ndi malo a asilikali ankhondowo. Pamene ndinatero, iye anandifunsa ine kumene ndinachokera. Mwamwaŵi, ndinabadwira pa chisumbu cha maziko chaching’ono mu Fiji. Chifukwa cha ulemu, iye anamvetsera ku pempho langa ndipo ananena kuti anamvapo za Mboni za Yehova koma anali asanakhalepo ndi ntchito yathu italongosoledwa kwa iye. Chinandipatsa ine mwaŵi wabwino wa kuchitira umboni kwa iye, ndipo analandira zothandiza phunziro za Baibulo zitatu kuchoka kwa ine. Iye anandiuza ine kukhala pa ofesi yake m’malo a asilikali a nkhondowo pa 9:00 a.m. Lachiŵiri lotsatira. Pamene mlongo wina ndi ine tinafika, alondawo anali atawuzidwa kale ponena za kuchezera kwathu ndipo anatiuza ife kuti chilolezo chinaperekedwa kaamba ka ife kulalikira m’mudzimo. Mlonda wolamulira ananena kuti: ‘Ndikudziŵitsa nduna zonse tsopano kuti pa Lachisanu zitseko zonse zidzayenera kukhala zotseguka kwa inu, ndipo ngakhale kuti tonsefe tiri ndi zipembedzo zosiyana, chanu chingakhale chopereka chenjezo la Ufumu wa kumwamba ndi mapeto a dziko.’
“Pamene tinafika pa Lachisanu,” iye akupitiriza tero, “galimoto yankhondo yokweza mawu inadutsa mu msasawo ikumalengeza kuti: ‘Akazi achikulire aŵiri adzakhala mu msasawo kulengeza chenjezo kwa inu, chotero chonde tsegulani zitseko zanu ndi kumvetsera kwa iwo. Musakangane nawo kapena kuyambitsa udani.’ Tinagwirira ntchito mu msasawo kuyambira 8:30 a.m. mpaka 5:00 p.m., kugawira mabukhu 100 ndi magazini 200. Ndipo chotulukapo? Maulendo obwereza ambiri anapangidwa ndipo maphunziro a Baibulo ambiri anayambitsidwa.”
Kuchokera ku chisumbu china mu South Pacific chomwe posachedwapa chinatsegulidwa ku ntchito yolalikira ndi apainiya apadera kukuchokera chokumana nacho chosangalatsa. Apainiya apadera amenewa amatsutsidwa ndi atsogoleri a United Church. Mkati mwa ulendo wa woyang’anira wadera, iwo anali ndi vuto la kupanga ulendo wobwereza, popeza kuti mfumu ya m’mudziwo, mosonkhezeredwa ndi atsogoleri a chipembedzo, inakana kulola Mboni za Yehova m’mudzimo. Pamene anafika, mfumuyo sinaliko, chotero anthu okondwerera anaitanidwa ndipo umboni wabwino unaperekedwa. Pamene iwo anachoka, ngalawa yaikulu inawonedwa ikubwera, ndipo mwachidziŵikire iyo inali ndi vuto la injini, popeza anthuwo anali kupalasa. Inde, inali mfumu ya mudziwo ikufika mochedwa kudzaletsa ulendo wobwereza. Pobwerera kunyumba, apainiyawo anauza woyang’anira waderayo m’chipidgin: “Me fella thinkim might angel now breakim engine belong him.”
Chotero Yehova anadalitsa kuwumirira kwa abale amenewa m’kumvera lamulo lake la kulalikira “mbiri imeneyi yabwino ya ufumu.”