Olengeza Ufumu Akusimba
Mulungu Alibe Tsankhu
ZAKA zoposa 1,900 zapitazo, mtumwi Petro anachitira umboni kwa kazembe wa gulu lankhondo Korneliyo, kuti: “Zoona ndizindikira kuti Mulungu alibe tsankhu; koma m’mitundu yonse, wakumuopa iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.” (Machitidwe 10:34, 35) Korneliyo anasonyeza kuopa Mulungu ndi chikondi cha chilungamo. Iye analandira umboni woperekedwa ndi Petro ndi kukhala Mkristu.
Lamulo la mkhalidwe limodzimodzilo limagwira ntchito lerolino—Mulungu alibe tsankhu. Tikuona zimenezi m’chochitika china cha ku Germany. Lipotilo likuti:
“Mu gawo la mpingo wathu, muli msasa waukulu wa gulu la ankhondo a Russia. Mu 1989, Berlin Wall itangogwetsedwa, akulu anafunsa ngati panali ofalitsa alionse amene anadziŵa chinenero cha Chirasha. Ena a ife tinkadziŵa, ndipo tinamka kukagwira ntchito m’gawo limeneli, limene lakhaladi losangalatsa. Nachi chimodzi cha zokumana nazo zina zambiri.
“Ndinali ndi wofalitsa wosabatizidwa (amene tsopano ali wobatizidwa) pamene tinalankhula ndi mkulu wina wankhondo. Mkulu wankhondoyo anamvetsera zimene tinali kunena ndiyeno anatipempha kuti tilankhule kwa asilikali ake. Iye anati iwo ayeneranso kumva za Mulungu ndi Baibulo, chotero tinalonjeza zodzabweranso.
“Tinapempha mlongo wina amene amalankhula Chirasha mosadodoma kumka nafe monga wokamasulira. M’chipinda chosonkhanira cha mu msasawo, tinaikamo thebulo la zofalitsa ndipo tinakhoza kulankhula kwa asilikali 68 ndi kuyankha mafunso awo. Pambuyo pake iwo analandira mokondwera mabuku 35 ndi magazini pafupifupi 100. Pamene tinali kuchoka m’chipinda chosonkhaniracho, tinaona timagulu tikukambitsirana zofalitsazo.
“Tinalonjeza zobwereranso pa July 4, 1992. Titafika pa 10:50 a.m., mlonda wokhala pakhomo la msasawo anatiuza kuti asilikaliwo anali kutiyembekezera. Mkulu wa nkhondo anamka nafe m’chipinda chosonkhanira, ndipo tinapeza kuti mkazi wina, amene anali atalandira zofalitsa kwa ife papitapo zoika m’laibulale, anali atalengeza za kubweranso kwathu mwa kuika zikwangani mu msasawo. Abale atatu anapereka nkhani zazifupi zonena za ntchito yathu ya padziko lonse ndi kuwasonyeza chifukwa chimene tingakhalire ndi chidaliro m’Baibulo. Ndiyeno tinakambitsirana ndi omvetsera pamafunso awo, tikumapereka mayankho ochokera m’Baibulo. Pakati pa mafunsowo panali lakuti, Kodi Mboni za Yehova zili ndi kaimidwe kotani pankhani ya utumiki wankhondo, ndipo kodi palibe aliyense wa iwo amene ali msilikali? Limeneli linapatsa mpata kwa wofalitsa wosabatizidwa uja amene anatsagana nane poyamba wa kufotokoza ntchito yake ya zaka 25 m’gulu lankhondo la ku East Germany, zaka zotsirizira monga mtsogoleri wa gulu lankhondo la mu mlengalenga. Iye anasimba mmene anafikira pa kudziŵa Mulungu ndi Baibulo ndipo tsopano anafuna kukhala mmodzi wa Mboni za Yehova. Asilikaliwo anachita chidwi ndi zimene anamva. Mkati mwa mphindi zisanu ndi ziŵiri zofalitsa zonse zimene tinali nazo zinatengedwa ndi asilikaliwo, ndipo ambiri anafuna Mabaibulo. Pa sitolo lina logulitsa mabuku tinakhoza kugula Mabaibulo Achirasha asanu ndi aŵiri, amene anawalandira moyamikira. Chinali chisangalalo chenicheni kupatsa anthu anjala yauzimu ameneŵa chidiziŵitso cha m’Baibulo, ndipo tikhulupirira kuti adzachitapo kanthu.”
Zoonadi, Mulungu alibe tsankhu. Kupyolera mwa Mawu ake iye akupempha anthu oona mtima alionse, kulikonse kumene ali. Iye akuwaitana kudzaphunzira za iye ndi Mwana wake, Yesu Kristu, ndipo ambiri ochokera kumikhalidwe yosiyanasiyana ya moyo akuchita zimenezo.—Yohane 17:3.