Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w89 2/15 tsamba 3-4
  • Chilungamo Kaamba ka Onse—Kodi Icho Chidzabwera Nkomwe?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chilungamo Kaamba ka Onse—Kodi Icho Chidzabwera Nkomwe?
  • Nsanja ya Olonda—1989
  • Nkhani Yofanana
  • “Njira Zake Zonse Ndi Zolungama”
    Yandikirani Yehova
  • Yehova Amakonda Chilungamo
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Kodi Zinthu Zopanda Chilungamo Zidzatha Padzikoli?
    Nkhani Zina
  • Kodi Mulungu Adzachitapodi Kanthu Ponena za Chisalungamo?
    Nsanja ya Olonda—1989
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1989
w89 2/15 tsamba 3-4

Chilungamo Kaamba ka Onse​—Kodi Icho Chidzabwera Nkomwe?

ALENDO ku malo otchuka m’mbiri yakale a Old Bailey ku London, pa chimango cha Central Criminal Court, amawona chapamwamba chithunzi chowumba cha mkazi yemwe amaimira chilungamo. M’dzanja limodzi, mkaziyo akugwira muyeso, kusonyeza kuti umboni udzayesedwa mosamalitsa. Dzanja lake lina likugwira lupanga, lochinjirizira opanda liwongo ndi kulanga a liwongo. M’malo ena ambiri, mungawone zojambulidwa za choimirakochi, nthaŵi zina ndi “Chilungamo” zotsekedwa maso kuimira kupanda tsankho kwake.a

Inu mungafunse, ngakhale ndi tero kuti: ‘Kodi chimene mkaziyo akuimira, chilungamo kaamba ka onse, mowonadi chiriko m’dziko lirilonse?’ M’dziko lirilonse, ndithudi, muli malamulo, limodzinso ndi awo omwe amachirikiza iwo. Ndipo kenaka muli oweruza ndi mabwalo amilandu. Motsimikizirika, amuna a lamulo ambiri ayesera kusungirira zoyenerera za munthu ndi kuwona kuti pali chilungamo cholingana kaamba ka onse. Chikhalirechobe, nchachidziŵikire kuti zoyesayesa zawo zambiri zalephera. Chifupifupi tsiku lirilonse, timawona, kumva, kapena kuŵerenga za kudyerana masuku pamutu, kupanda chilongosoko, ndi chisalungamo.

Lingalirani chitsanzo cha mkazi wina amene anabweretsedwa ku bwalo lamilandu. Kukhala kwake wa liwongo kapena wopanda liwongo kusanatsimikiziridwe, woweruza anamudziŵitsa iye kuti “akasamalira” za mlandu wotsutsa mkaziyo ngati akakumana naye ku motelo, mwachiwonekere kaamba ka unansi woipa. Inde, awo olingaliridwa kuchirikiza chilungamo kaŵirikaŵiri atsimikizira kukhala odyerana masuku pamutu kapena operewera mu ntchito yawo. Magazini ya Time inanena za boma lina mu United States kumene magawo atatu mwa asanu a oweruza a bwalo lalikulu lamilandu anazengedwa mlandu wa mkhalidwe wosavomerezedwa ndi lamulo lokhazikitsidwa wa kuthandiza woweruza mnzawo.

M’kuwonjezerapo, anthu aphunzira za anthu omaswa lamulo omwe amapitirizabe kupulumuka chilango, ambiri amakhala opanda chikhulupiriro ndi kuchipeza kukhala chosavuta kuswa lamulolo iwo eni. (Mlaliki 8:11) Ponena za Netherlands timaŵerenga kuti: “Ambiri a anthu a chiDutch amapatsa mlandu a ndale zadziko kaamba ka kulimbikitsa kulekerera komwe kumayambitsa upandu. Ena amapatsa mlandu mabwalo amilandu, makamaka oweruza . . . omwe amapitiriza kupereka, zilango zazing’ono, nthaŵi zina zolekerera mosalingalira.” Koma kusowa kwathu chochita m’kufuna chilungamo kumaphatikizapo zoposa kuwongolera madongosolo opereka lamulo kapena achiweruzo.

Inu mukudziŵa kuti m’maiko ambiri olemera ochepera apitirizabe kulemera, pamene osauka ambiri amayang’anizana ndi kupanda chilungamo kwa za ndalama. Kupanda chilungamo koteroko kumakhalapo pamene anthu, chifukwa cha mtundu wa khungu lawo, chiyambi cha ufuko, chinenero, umuna kapena ukazi, kapena chipembedzo, amakhala ndi mwaŵi wochepera wa kuwongolera mkhalidwe wawo, ngakhale kudzisunga iwo eni. Chotulukapo chimakhala chakuti mamiliyoni amakanthidwa ndi umphaŵi, njala, ndi matenda. Pamene kuli kwakuti anthu ambiri m’maiko olemera amapindula kuchokera ku njira zopita patsogolo za kuchiritsa, mamiliyoni osaneneka amavutika ndi kufa chifukwa chakuti sangakhoze kupeza mankhwala ofunikira kapena madzi audongo. Lankhulani kwa iwo ponena za chilungamo! Kwawo kuli kupanda chilungamo kuchokera ku ukhanda kufikira ku manda.​—Mlaliki 8:9.

Ndipo bwanji ponena za kupanda chilungamo kowonekera komwe kuli kosachititsidwa ndi munthu? Lingalirani za makanda obadwa ndi kupunduka kobadwa nako​—khungu, kusakula, kapena kulemala? Kodi mkazi akakhala ndi lingaliro la chilungamo ngati khanda lake linabadwa lopuwala kapena lakufa, pamene akazi ena chapafupi akufungatira tiana ta thanzi? Monga momwe kukambitsirana kotsatira kudzasonyezera, kupanda chilungamo koteroko kudzawongoleredwa.

Ngakhale kuli tero, pa malo ano a nthaŵi, kodi simukuvomerezana ndi ndemanga ya pa Mlaliki 1:15? Pamenepo mfumu yanzeru ndi yozoloŵera inavomereza, kuchokera ku lingaliro la umunthu: “Chokhotakhota sichingawongokenso, ndipo choperewera sichingaŵerengeredwe.”

Munthu wotchuka kwambiri anali Yesu Kristu. Pa Luka 18:1-5 timaŵerenga fanizo lake la woweruza amene “sanawopa Mulungu ndi wosasamala anthu.” Chabwino, mkazi wamasiye anachondererabe kwa woweruzayo kaamba ka chilungamo chimene lamulo linamuyeneretsa mkaziyo. Koma Yesu ananena kuti woweruza woipayo anathandiza mkaziyo kokha chifukwa chakuti kuchonderera kwa mkaziyo kunakhala kovutitsa. Chotero Yesu, mungadziŵe kuti, anali kudziŵa kuti kupanda chilungamo kunachuluka. M’chenicheni, iye mwiniyo pambuyo pake anazunzidwa ndi kuphedwa pa mlandu wonyenga, kusoweka kwina koipa kwa chilungamo!

Ambiri amakhulupirira kuti pali Mulungu amene ali wodera nkhaŵa ponena za kupanda chilungamo. Mkati mwa Misa m’dziko lina la Central America, Papa John Paul II ananena kuti: “Pamene umenya munthu, pamene uwukira kuyenera kwake kwa lamulo, pamene uchita kupanda chilungamo koipitsitsa motsutsana naye, pamene umuzunza, kuthyola m’nyumba yake ndi kumuba kapena kuwukira kuyenerera kwake ku moyo, ukuchita upandu ndi mlandu waukulu motsutsana ndi Mulungu.” Mawu abwino. Komabe, kupanda chilungamo kumapitirizabe. Nthenda ya kaliwondewonde m’dziko limenelo ikukantha 8 pa 10 a ana a msinkhu wa zaka zochepera pa zisanu. Maperesenti aŵiri a anthu ali ndi 80 peresenti ya nthaka yoti ingalimidwe.

Chotero kodi palidi Mulungu amene kwenikweni amasamala ponena za kupanda chilungamo koipitsitsa koteroko, Mulungu amene angadere nkhaŵa ngakhale ponena za kupanda chilungamo komwe kumakuyambukirani? Kodi iye adzawona nkomwe kuti chilungamo chabwera?

[Mawu a M’munsi]

a Chithunzi chathu cha pa chikuto nchochokera ku Justitia Fountain mu Frankfurt am Main, Germany. Chifano chowumba cha pa tsamba lino chiri pa municipal building mu Brooklyn, New York, U.S.A.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena