Ripoti la Olengeza Ufumu
Yehova Amachirikiza Atumiki Ake Okhulupirika
YESU ananena kuti: “Kapolo samakhala wokulirapo koposa mbuye wake. Ngati iwo andizunza, iwo adzakuzunzaninso.” (Yohane 15:20, NW) Koma atumiki okhulupirika a Yehova ali otsimikiziridwa kuti iye adzawachirikiza iwo. (Salmo 18:2; Nahumu 1:7) M’dziko lina la ku Africa kumene ntchito ya mtendere ya Mboni za Yehova iri yoletsedwa mowopsya, Yehova anachirikiza atumiki ake pamene anayang’anizana ndi kumenyedwa ndi kumangidwa, monga mmene ripoti lotsatirali likusonyezera:
“Woyang’anira wadera ndi abale anayi a kumaloko anamangidwa monyenga ndi kuponyedwa m’kachipinda kakang’ono komwe nthaŵi zonse kanasundidwa kaamba ka agalu osochera,” likutero ripotilo. “Iwo anasungidwa mmenemo kwa masiku 123 ndi zovala zawo zamkati ndipo sanaloledwe nkomwe kutuluka kunja kupita ku chimbudzi.” Ciwalo cha Nyumba ya Malamulo chinamva za mikhalidwe ya nkhalweyo ndipo anayamba kutsutsa, ndipo potsirizira pake, patapita masiku 123, abalewo anatulutsidwa. Yehova anachirikiza abale okhulupirika amenewa ndi mzimu wake.
Chokumana nacho china kuchokera m’dziko limodzimodzili chimasonyeza ziyambukiro zopindulitsa za ntchito yathu yolalikira. Ripotilo likusimba kuti: “M’mudzi wina, anthu anali otchuka kaamba ka chiwawa ndi kuwukira. Ngakhale kuli tero, pambuyo pa kulalikira kwa Mboni za Yehova kumeneko, ambiri anayamba kulemekeza maulamuliro a kumaloko ndipo anayamba kugawanamo mu ntchito ya m’mudzi ya mlungu ndi mlungu pa misewu.” Mfumu imodzi ya kumaloko inafuna kudziŵa chifukwa kaamba ka kusintha kumeneku mu mkhalidwe wa anthuwo ndipo inawuzidwa kuti: “Chinali chifukwa cha kuphunzitsa kwa ‘pasitala’ wa Mboni za Yehova.” “Tsiku lina mfumu imeneyi inandiitana ine kunyumba yake,” ikutero Mboniyo, “ndipo inandilimbikitsa ine kupitiriza ndi ntchito yabwino imeneyi. Iye anadipatsa mphatso ya nkhuku yaikulu kukadya ndi banja langa.” Pa nthaŵi ina, nduna yaikulu ya mzinda ya kumaloko inadza kudzachezera mbale, ndipo mbaleyo anamuitanira iye mkati ndi kuchitira umboni kwa iye. Nduna yaikulu ya mzindayo “inafunsira magazini ena ndi kunena kuti, ‘Sitimaganizira kuti mumachita choipa chirichonse. Pitirizani kuchita apilu. Tiribe malamulo a kukumangani inu. Ndiganiza kuti posachedwapa Boma lidzasamalira vuto lanu.’”
Mpainiya wapadera akulemba kuti: “Kutsatira zinenezo zochokera kwa mlembi wa chipani cha ndale zadziko, mfumu ya kumaloko inalamulira kumangidwa kwanga ndi kuikidwa m’ndende m’chipinda chonyansa choipitsidwa ndi mkodzo wa nyama ndi ndowe. Ndinasungidwa mu mdima umenewu kwa masiku asanu. Panjira ndikupita kumeneko, ndinapemphera kwa Yehova ndi kukumbukira Salmo 50:15. Alonda kumeneko anandimvera chifundo ndipo sanatsekeretu chitsekocho kotero kuti ndinkapumako mpweya wabwino. Pambuyo pa masiku asanu m’ndendeyi, ndinaikidwa ku chiyeso pamene anandipatsa ine mbuzi yokapereka kwa mfumu ya kumaloko, popanda wondiperekeza. Popeza sindinathaŵe, ndinapatsidwa ufulu tsiku lirilonse kuchokera pa 3:00 p.m. kufika ku 7:00 p.m. Ndinkakumana ndi abale, ndipo tinakhoza kulalikira pamodzi. Ngakhale kuti ndinadwala mkati mwa nthaŵe yovutitsa imeneyi ndipo adani anga anayembekezera kuti ndingafe, Yehova sanandisiye ine. Chokumana nacho chimenechi chandibweretsa ine chapafupi ndi Yehova, ndipo ndiri wotsimikiza kuti chizunzo sichidzandilekanitsa ine nkomwe kuchoka kwa anthu a Yehova.”—Yerekezani ndi Aroma 8:35-39.
Mboni za Yehova zimayamikira mmene Mulungu amawachirikizira iwo m’nthaŵi zovuta. Iwo amayamikiranso aja omwe amasonyeza kukoma mtima kwa iwo pamene akupitiriza ndi ntchito iyi yofunika kwambiri yopulumutsa moyo ya kulalikira mbiri yabwino. Yehova sadzaiwala kukoma mtima koteroko.—Mateyu 25:40.