Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w93 3/1 tsamba 26-29
  • Yehova Anandichirikiza M’ndende ya M’chipululu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yehova Anandichirikiza M’ndende ya M’chipululu
  • Nsanja ya Olonda—1993
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kumangidwa
  • Pamene Tinali Omangidwa
  • Ndende ya M’chipululu
  • Moyo wa m’Ndende
  • Kukhala Olimba Mwauzimu
  • Kulankhulirana ndi Mabwenzi Athu
  • Kenako Kumasulidwa!
  • Ndinali Wandale Tsopano Ndinasanduka Mkristu Wosakhudzidwa N’zandale
    Galamukani!—2002
  • Zaka Zoposa 50 za ‘Kuwolokerako’
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Mmene Chowonadi Chinandisinthira Kuchokera ku Mpandu Kukhala Mkristu
    Galamukani!—1989
  • Kumapeza Chomchitira Yehova Nthaŵi Zonse
    Nsanja ya Olonda—1989
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1993
w93 3/1 tsamba 26-29

Yehova Anandichirikiza M’ndende ya M’chipululu

MONGA MOMWE YASIMBIDWIRA NDI ISAIAH MNWE

Panalibe kuzengedwa mlandu, ndipo sindinachite upandu uliwonse. Komabe, ndinaŵeruzidwira ku ukaidi wa ntchito yakalavulagaga m’ndende yokhaulitsira chapakati pa Chipululu choŵaula cha Sahara cha mu Afirika. Chimene chinachititsa mkhalidwewo kuyipirapo, nchakuti palibe mmodzi wamabwenzi anga anadziŵa kumene ndinali. Izi zinachitika zoposa zaka zisanu ndi zitatu zapitazo, m’chirimwe cha 1984. Tandilolani ndifotokoze mmene ndinafikira mu mkhalidwe womvetsa chisoni umenewu.

MU 1958, pamene ndinali kokha wazaka 12 zakubadwa, mchimwene wanga wamkulu anakhala mmodzi wa Mboni za Yehova. Komabe, atate ndi amayi anapitirizabe kulambira milungu yafuko la Chigawo cha Abia, Nigeria, kumene tinali kukhala.

Mu 1968, ndinaloŵa m’gulu lankhondo la ku Biafra. Pamene ndinali kubwalo lankhondo, ndinalingalira zamkhalidwe wauchete wa Mboni za Yehova, ndipo ndinapemphera kwa Mulungu kundithandiza. Ndinalonjeza kuti ngati anandilola kupulumuka nkhondoyo, ndikakhala mmodzi wa Mboni zake.

Pambuyo pankhondoyo ndinachita mofulumira kukwaniritsa lonjezo langa. Ndinabatizidwa mu July 1970 ndipo mwamsanga ndinayamba uminisitala wanthaŵi yonse monga mpainiya. M’kupita kwanthaŵi ndinaikidwa kukhala mkulu wa mpingo Wachikristu. Mwamsanga ndinalandira chiitano kuchokera ku ofesi yanthambi ya Nigeria kukayamba gawo laumishonale m’dziko lapafupi kumene ntchito ya Mboni za Yehova inali yosavomerezedwa mwalamulo. Ndinavomera, ndipo podzafika January 1975, ndinali paulendo ndiri ndi pasipoti yanga.

Kumangidwa

Mu 1978 ndinalandira gawo la kukachezera Mboni m’dziko lonselo. Popeza kuti zinali zochepekera, ndinayenda mitunda yaitali, ndikumachezera mizinda yonse mmene munali mipingo, kuphatikizapo madera amene anali ndi anthu okondwerera. Kaŵirikaŵiri ndinkafunsidwa ndi apolisi pamalo osechera. Kaŵiri, m’masiku anayi nthaŵi iriyonse, ndinali kumangidwa ndi kufunsidwa za ntchito yathu.

Ndiyeno, mu June 1984, pamene tinali kukonzekera kupita muutumiki wakumunda pa Sande lina, mkulu waboma wina waubwenzi anatiuza kuti apolisi anali kufunafuna kumanga Mboni za Yehova. Mlungu umodzi pambuyo pake Djagli Koffivi, wa ku Togo, ndi ine tinamangidwa. Tinapititsidwa ku malikulu apolisi ndi kulamulidwa kupereka maina a Mboni za Yehova zonse mu mzindawo. “Kusiyapo ngati mutipatsa maina,” iwo anatero, “sitidzakumasulani.”

“Inu ndinu apolisi,” ndinayankha. “Ndintchito yanu kukapeza anthu amene mufuna. Ine sindine woimira wanu.” Tinakangana kwa pafupifupi mphindi 30, ndipo apolisi anatiopseza kuti akatimenya. Komabe, sitinawapatse maina a abale athu Achikristu. Pamenepo iwo anasankha kulanda mabukhu anga ambirimbiri ofotokoza Baibulo.

Pamene Tinali Omangidwa

Titabwerera kupolisi ndi mabukhu, Djagli ndi ine tinawatsitsa. Pamene tinali kutero, pepala lina linasololoka kuchokera mu Baibulo langa lazilembo zazikulu. Inali programu ya msonkhano wachigawo pomwe panasindikizidwa maina a akulu onse a Chikristu m’dzikolo. Mwamsanga ndinalitola ndi kulipanikizira mthumba. Komabe, mmodzi wa apolisi anandiwona ndipo anandiwuza kuti ndimpatse pepalalo. Ndithudi, ndinavutika maganizo.

Pepalalo linaikidwa pagome m’chipinda chimene Djagli ndi ine tinali kukatula mabukhu. Pamene ndinaloŵamo ndi mtokoma wanga wotsatira, ndinapita kugomeko, ndinatola pepalalo, ndi kulikanikizira mthumba. Ndiyeno ndinanena kuti ndinafuna kupita kuchimbuzi. Wapolisi anandiperekeza kuchimbuziko. Nditaloŵa ndi kutseka chitseko, ndinang’amba pepalalo kukhala tizidutswa ndi kuliponya m’chimbuzi ndipo linakokoleredwa ndi madzi am’chimbuzi.

Pamene apolisi anadziŵa zimene zinali zitachitika, anakwiya. Koma anachita mantha kuchita chirichonse, popeza kuti akuluakulu awo akanawaimba mlandu wakunyalanyaza pondilola ine kukhala ndi mpata wakuwononga pepala limenelo. Atatisunga muukaidi kwa masiku 17, woyang’anira wapolisi anatiuza kusonkhanitsa zinthu zathu chifukwa chakuti tinali kudzasamutsidwira kumalo ena. Tinaika zovala zathu m’thumba laplasitiki, ndipo pansi pake ndinaikapo Baibulo laling’ono limene wodzacheza wina analizembetsera kwa ife.

Tinali okhoza kuuza Mboni zina kuti ife tinali kusamutsidwa koma kuti sitinali kudziŵa kumene tinali kupita. M’mamaŵa patsiku lotsatira, July 4, 1984, woyang’anira wapolisi anatidzutsa. Anatisecha, akumandipempha kuchotsa zovala m’chola ndi kuzikoloŵeka pamikono yanga. Koma pamene ndinafika pashati yomalizira, iye anati ndingabwezere zovalazo m’cholacho, chotero Baibulo silinatulukiridwe.

Ndende ya M’chipululu

Apolisi anatiyendetsa pagalimoto kumka kubwalo landege, kumene tinakwera ndege ya asilikali ankhondo. Maola angapo pambuyo pake tinafika kutawuni ina yokhala ndi anthu pafupifupi 2,000, limene liri ndi ndende pafupi pake. Iri pafupifupi makilomita 650 kuyenda pagalimoto kumka kutawuni yapafupi koposa. Tinatengedwa kuchokera m’ndege kumka nafe kundende ndi kuperekedwa kwa woyang’anira ndende. Palibe aliyense wamabanja athu kapena mabwenzi amene anadziŵa kumene tinapititsidwa.

Tawuni imene tinapititsidwako iri ngati kasupe wamadzi m’chipululu cha Sahara. Muli zitsamba, mitengo yochepekera, ndi nyumba za makoma adothi. Madzi angapezedwe mwakukumba pafupifupi mita imodzi kapena mita imodzi ndi theka. Komabe, nzika yakumalowo ya zaka 31 zakubadwa inatiuza kuti inawona mvula iri kuvumba nthaŵi imodzi yokha m’nthaŵi yonse yamoyo wake! Ndipo malowo anali otentha kwadzawoneni. Kaidi wina ananena kuti makina oyezera kutentha ndi kuzizira m’nyumba za akaidi tsiku lina anafika pa 60 digiri Celsius! Chimphepo champhamvu chinawomba mosalekeza, chikumaulutsa mchenga umene unalasa khungu ndi kupweteka m’maso.

Munthu aliyense wofika kumalowo ankazindikira kuti anali kumalo oipitsitsa operekera chilango chokhaulitsa. Ndendeyo inali yozunguliridwa ndi makoma otalika amene anatumikira monga chitetezo kumphepo ndi dzuŵa. Komabe, makomawo sanali ofunika kutetezera kuzemba, popeza kuti kunalibe kulikonse kopitako. Kunja kwa malo achondewo m’chipululucho, kunalibe mtengo ngakhale umodzi, kunalibiretu, woti nkupereka mthunzi kwa aliyense amene akanafuna kuzemba.

Tisanaloŵe, woyang’anira ndendeyo anatisecha. Anatiuza kuti titulutse kanthu kalikonse m’chola chathu. Ndinayamba kutulutsa mashati athu limodzi ndi limodzi. Pamene chokha chimene chinatsala chinali shati imodzi yophimba Baibulo, ndinagwira cholacho kumsonyeza shati m’katimo ndi kuti: “Izi ndizo zokha zimene anatilola kunyamula.” Atakhutira, anati tipite kukaloŵa m’bwalo landende. Baibulo linali bukhu lokha lomwe tinali nalo.

Moyo wa m’Ndende

Onse pamodzi, munali pafupifupi akaidi 34. Anali apandu owopsa ndi aupandu koposa m’dzikolo. Ambiri anali akupha anthu olingaliridwa kuti sakakhoza kukonzeka. Tonsefe tinagona m’zipinda zandende ziŵiri zolekanitsidwa ndi malo osatchingidwa achimbuzi. M’malo achimbudziwo munali chitini chosatsekedwa chimene chinagwiritsidwa ntchito monga chimbuzi. Ngakhale kuti chitinicho chinakhutulidwamo matubzi m’mmaŵa aliwonse ndi andende, kunawonekera kuti ntchentche zonse m’chipululucho zinadza kudzasangalala ndi kuzizirira ndi uve wa chitini chimenecho!

Chakudya chokha chimene tinali nacho chinali mapira. Anagayidwa ndi mkaidi, kuŵiritsidwa, ndi kuwomolera m’mbale, zimene pambuyo pake zinali kuperekedwa, imodzi pamkeka wogonapo mkaidi aliyense. Chakudyacho sichinavundikiridwe. Podzafika nthaŵi imene tinabwerera kuchokera kuntchito, panali ntchentche miyandamiyanda zodzala pambale yachakudya cha mapira chimenecho. Pamene tinanyamula mbale zathu, ntchentchezo zinkauluka ng’waa. Kwamasiku aŵiri oyamba sitinadye kalikonse. Potsirizira pake, patsiku lachitatu, titatha kuingitsa ntchentche ndi kuchotsa nkhoko pamwamba, tinayamba kudya nsima yamapira. Tinapempherera kuti Yehova akatetezere thanzi lathu.

Tinagwira ntchito m’dzuwa lotentha, tikumagumula makoma amabwalo andende yakale ndi kumanga makoma atsopano. Inali ntchito yakalavulagaga mopambanitsa. Tinagwira ntchito mosapuma kuyambira 6:00 a.m. kufikira dzuŵa litafika pamutu, tinali kupatsidwa chakudya, ndiyeno nkugwirabe ntchito kufikira 6:00 p.m. Panalibe masiku akupuma. Sikokha kuti tinavutika ndi chitungu komanso m’nthaŵi yachisanu tinavutika ndi kuzizira. Ndipo tinavutikanso ndi alonda ankhalwe.

Kukhala Olimba Mwauzimu

Djagli ndi ine tinaŵerenga Baibulo mobisa, ndipo tinakambitsirana zimene tidaphunzira. Sitikanaŵerengera poyera chifukwa chakuti Baibulolo likanatengedwa ndipo tikanalangidwa. Mkaidi wina amene ndinayamba kuchita naye phunziro la Baibulo anali ndi nyali yaparafini imene anandibwereka. Kaŵirikaŵiri ndinadzuka pa 1 koloko kapena 2 koloko mbandakucha ndi kuŵerenga kufikira 5 koloko. Mwanjirayo ndinali wokhoza kuŵerenga Baibulo lonse lathunthu.

Tinalalikira kwa akaidi enawo, ndipo mmodzi wa iwo anauza mkulu wosunga ndende za ife. Mosayembekezereka, wosunga ndendeyo anapatsa mkaidi wina magazini a Galamukani! amene iye anali nawo, ndipo wandendeyo anawapitirizira kwa ife. Ndinawaŵerenga mobwerezabwereza. Kuŵerenga kwathu ndi kulalikira kunathandizira kukhalabe tiri olimba mwauzimu.

Kulankhulirana ndi Mabwenzi Athu

Sitinali kuloledwa kulemba kapena kutumiza makalata. Komabe, munthu wina amene anali waubwenzi kwa ife ananena kuti akandithandiza. Pa August 20, pafupifupi masabata asanu ndi limodzi titafika, ndinalemba makalata aŵiri mobisa, imodzi yopita kunyumba yaukazembe ya Nigeria m’dzikolo ndipo ina yopita kwa mabwenzi Mboni. Ndinawakwirira mu mchenga ndi kuika chizindikiro pamalowo mwa kuikapo mwala waukulu. Pambuyo pake bwenzi langalo linadza nalifukula makalatawo.

Masabata anapita, ndipo sindinamve chirichonse. Potsirizira pake ndinataya chiyembekezo chakuti makalatawo anatumizidwa. Koma iwo anali atatumizidwa, ndipo Mboni zinzathu zinayamba kumenyera nkhondo kuti timasulidwe. Ndiponso unduna Wankhani Zakunja m’Nigeria nawonso unali ndi chikondwerero m’nkhaniyo ndipo unafunsa boma la m’dziko limene ndinamangidwira chifukwa chake bomalo linandiponya m’ndende yotero.

Panthaŵiyi, m’maŵa wa tsiku la November 15, 1984, tinatengedwa kukachita ntchito yokolopa. Alondawo anapita nane kuchimbudzi cha kusukulu ya sekondale chimene anthu anali kugwiritsira ntchito kwa masabata angapo mosasamala kuti chinali chitatsekeka. Chinali chodzala ndi tubzi. Ntchito yanga, anatero alondawo inali kuchitsegula. Zipangizo zokha zimene ndinali nazo zinali manja anga. Pamene ndinali chidabwire mmene ndikachitira ntchito yochititsa nseruyo, mkulu wa alonda anafika nanena kuti ofisala waboma m’chigawocho anafuna kundiwona.

Pamene ndinafika ofisala waboma ananena kuti osati kale kwambiri iye anali atalankhula ndi pulezidenti wadzikolo, amene anali atamva zakuvutika kwanga. Pulezidenti anafotokoza kuti ngati ndingapereke maina a Mboni za Yehova m’dzikolo, ndikamasulidwa nthaŵi yomweyo ndipo ndikanapita ndi ndege yotsatira. Kachiŵirinso ndinanena kuti ngati iwo anafuna Mboni za Yehova, inali ntchito ya apolisi kukawapeza. Ofisala waboma anandiuza kuti ndifunikira kupenda mosamalitsa kwambiri zimene analonjeza. Anati akandipatsa masiku anayi kapena asanu kuti ndikaganize. Pamenepo anandiuza kuti ndichoke, ndipo alonda anandiperekeza kubwerera kundende ndipo mwamwaŵi, osati kubwereranso kuchimbudzi chija!

Pambuyo pamasiku asanu ofisala waboma anandiitanitsa nandifunsa zimene ndinasankha. Ndinanena kuti chifukwa chokha chimene ine ndinaikidwira m’ndende yawo chinali chakuti ndinachitira umboni Mulungu wowona ndi kuti sindinachite cholakwa chirichonse. Ndinafotokoza kuti ndinali ndi pasipoti yololedwa ndi lamulo ndi chilolezo chakukhala m’dzikolo. Zikalata zanga zonse zinalibe chifukwa, ndipo paliponse pamene ndinapita ku mzinda uliwonse, nthaŵi zonse ndinawonana ndi apolisi kutsimikizira kuti zinthu zonse zinali bwino. Popeza kuti sindinachite upandu uliwonse, ndinafunsa kuti: “Kodi ndikulangidwira chiyani? Ngati sindinali wofunika m’dzikoli, kodi nchifukwa ninji sindinathamangitsidwe? Kodi nchifukwa ninji ndinaŵeruzidwa kudza malo ano?”

Ndinalankhula kwa pafupifupi mphindi 15. Pamene ndinamaliza, ndinapemphedwa kulemba zimene ndinali nditanena kumene, ndipo ndinauzidwa kuti mawu anga akaperekedwa kwa pulezidenti. Ndinapatsidwa pepala, ndipo ndinalemba masamba anayi.

Kenako Kumasulidwa!

Sindinamve chirichonse chokhudza nkhaniyo kufikira January 1985, pafupifupi miyezi isanu ndi iŵiri nditaikidwa m’ndende. Panthaŵiyo, mkulu wa alonda anadza nandifunsa ngati ndinalemba kalata yopita kunyumba yaukazembe ya Nigeria. Ndinayankha kuti, “Inde.”

“Kodi unachitiranji? Kodi nchifukwa ninji sunandiuze?” Iye anafunsa.

“Ndinamuuza kuti iye analibe chochita ndi nkhaniyo. Koma ndinamtsimikizira kuti sindinalembe chirichonse chotsutsana naye, popeza kuti iye analibe thayo lirilonse lokhudza kuponyedwa kwanga m’ndende. “Ngakhale amayi sadziŵa kumene ine ndiri,” ndinatero. Pamenepo anafuna kudziŵa mmene ndinatumizira kalatayo, koma ndinakana kumuuza.

Tsiku lotsatira alonda anakonzekeretsa Land-Rover nandiuza kuti Djagli ndi ine tinali kusamutsidwa. Tinatulutsidwa, kuvulidwa, ndi kusechedwa. Pasadakhale ndinali nditapatsa Baibulo langa mkaidi wina amene ndinaphunzira naye chifukwa chakuti ndinadziŵa kuti alonda akalifunkha ngati anandipeza nalo. Mwamunayu anatiuza kuti pamene akamasulidwa, akakhala mmodzi wa Mboni za Yehova. Pemphero lathu nlakuti iye akatero.

Mwamsanga pambuyo pake, ndinathamangitsidwira ku Nigeria, ndipo February 1985, ndinayambiranso uminisitala wanga monga woyang’anira woyendayenda m’dziko limenelo. Kuyambira 1990, ndakhala ndikutumikira monga woyang’anira chigawo m’Nigeria. Djagli tsopano akutumikira monga Mboni yokhulupirika mu Côte d’Ivoire.

Kuchokera ku chokumana nacho chimenechi, ndinaphunzira mwachindunji kuti Yehova Mulungu angathe kutichirikiza ngakhale titapanikizika kwadzawoneni. Mobwerezabwereza tinawona dzanja lake lotetezera m’ndendemo. Kumasulidwa kwathu kunakhomereza m’maganizo mwanga kuti sikokha kuti Yehova amadziŵa kumene atumiki ake ali ndi kuti akuvutikiranji komanso amadziŵa mmene angawalanditsire kuchiyeso.​—2 Petro 2:9.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena