Mmene Chowonadi Chinandisinthira Kuchokera ku Mpandu Kukhala Mkristu
NDINAKULIRA mu tauni yaing’ono mu Maine. Nthaŵi zonse ndinali kuwoneka kugwera mu mkhalidwe wa kusamvera kochepera. Pamene atate wanga anandigwira m’zolakwa zoterozo, ndinkapatsidwa chilango chowopsya. Nthaŵi zina ndinkadzimva wosungulumwa, makamaka pambuyo pa imfa ya atate wanga—iwo anafa pa tsiku limene ndinakwanitsa zaka 11 zakubadwa.
Pamene ndinasamukira ku tauni yaikulu, ndinadziloŵetsa mu zolakwa zoposa zazing’onozo, zinthu zowopsya kwenikweni monga kuba m’sitolo limodzinso ndi kuphwanya ndi kuloŵamo. Ndinkaphwanya sitolo yogulitsa ziŵiya kokha kuti ndiwone ngati ndingatero. Sindinali kutenga zambiri nthaŵi zambiri. Chinakulamo chinali chisangalatso kuposa china chirichonse. Popeza tsono ndikuyang’ana m’mbuyo, ndiganiza kuti chochititsa chachikulu chinali kupenyerera TV kochulukira—ndinakokedwera kwambiri ku ziwonetsero zachiwawa.
Maupandu anga anapitiriza kuipirako. Kuchuluka kwa kupulumuka komwe ndinapeza, kunakhalanso kuchuluka kwa kulakalaka komwe ndinakhala nako. Kenaka ndinagwidwa. Ndinali ndi zaka 15 kapena 16 zakubadwa, “kugula” m’sitolo yaikulu pa ola lachiŵiri m’mawa—sinali nthaŵi yabwino konse kaamba ka chimenecho. Pokhala wam’ng’ono, ndinapatsidwa chilango cha kuphunzitsidwa kwa miyezi isanu ndi umodzi. Sindinaphunzire chirichonse m’chokumana nacho chimenechi; kuba kwanga kwakung’onoko kunapitirizabe.
Pa nthaŵi imene ndinali ndi zaka 21, iko sikunalinso kwakung’ono. Usiku wina ntchito yanga yaupandu inathera m’kupha munthu. Pambuyo pa kuba m’sitolo yogulitsa ziŵiya ndi zakudya, ndinalonga katundu wanga kumbuyo kwa imodzi ya magalimoto awo aakulu, kuvundumuka nayo, ndi kuthaŵa. Pamene ndinali kuthaŵa, ndinalingalira kuti chinali chinthu chachikulu chotani nanga chomwe ndinachita. Sitolo imeneyo inali itaberedwa kwa nthaŵi zambiri, ndipo mwiniwake anali atangopanga chochinjiriza. Palibe wina aliyense akaloŵanso m’malo amenewo. Koma ndinatero! Ndinalidi winawake!
Koma osati kwa nthaŵi yaitali. Galimotoyo inatitimira, chotero ndinaisiya ndi kupita ku nyumba ina kukafuna choyendera china. Mwamuna wa m’nyumbayo anandiwona ndi kuwunguzawunguza ndipo anawopsyeza kuti adzaitana apolisi. Sindinafune konse kuwalola iwo kubwera, popeza ndinali nditangoba kumene m’sitolo. Ndinachita mantha, ndikusolola mfuti yanga, ndi kumuwombera iye. Kukanganako kunatha pamene iye anafa ndipo ine ndinapitiriza kuthaŵa.
Madontho a thukuta anatuluka. Ndinachita mantha. Ndinanjenjemera. Poyamba ndinapita ku Augusta, ndinataya galimoto yobedwayo, ndi kuyamba kuyenda kuwoloka ulalo. Ndinayang’ana m’madzi pansipo. ‘Kodi ndilumphiremo?’ ndinaganiza choncho. Lingaliro la kudzipha linabwera m’maganizo anga nthaŵi zambiri mkati mwa masiku otsatira, koma sindinadzilole inemwini kutero. Chotero ndinapitirizabe kuthaŵa kwa zaka ziŵiri.
Potsirizira pake ndinakwera basi kupita ku Boston. Panthaŵiyo apolisi anali ataleka kundifunafuna, komabe ndinali ndidakali ndi mantha. Pamene ndinali m’basimo, anthu ovala yunifomu anali kuloŵa, ndipo ndinkachita mantha. Panthaŵiyo ndinali ndinataya mfutiyo. Pambuyo pa kupha mwamuna uja, sindinafune kuchita nayo chirichonse. Pamene ndinafika ku Boston, ndinali kuyendayenda masana ndipo usiku ndinkagona m’malo otayira zinyalala kapena pa malo amene anali kumanga nyumba. Ndalama zochepa zomwe ndinali nazo mofulumira zinathera pachakudya. Ndinatembenukira ku kuba m’masitolo kamodzi kapena kaŵiri, koma sindinafunenso zowonjezereka za chimenecho tsopano. Mzimu wa kudzigangira, chisangalatso, chitokoso cha kuba ndi kuthaŵa—unali utatha tsopano.
Ndinapeza ntchito, kupeza chipinda cha mtengo wotsika, kugwiritsira ntchito dzina labodza, ndipo ndinali wamantha nthaŵi iriyonse pamene ndinawona wapolisi. Nditawona wina akubwera, ndinkapita njira ina. Nthaŵi zonse ndinali wosamala, sindinali kudutsa konse makwalala mosasamala, kuwopera kugwidwa. Mmenemo ndi mmene zinaliri ndi ine, mbala yomwe pa nthaŵi imodzi inali yofunafuna chisangalalo, tsopano wothaŵathaŵa wokhala ndi liwongo.
Ndinali ndi bukhu laling’ono la miyambo, ndipo nthaŵi zina ndinali kuliŵerenga. Kenaka ndinakumbukira bukhu la Miyambo m’Baibulo. Ndinatenga Baibulo ndi kuyamba kuliŵerenga. Sindidziŵa chifukwa chake. Banja lathu silinali konse la chipembedzo. Pamene ndinali ndi zaka 13, mayi wanga anapita ku misonkhano ingapo ku Nyumba Yaufumu ya Mboni za Yehova. Sindinafune chirichonse chochita ndi chimenecho, ndiponso nawo sanapitirize kutero.
Ngakhale panthaŵiyo, pamene ndinkaŵerenga zinazake m’Baibulo, sindinali kulingalira za kukhala ndi chipembedzo. Koma ndinatopa ndi kuthaŵa, kukhala ndikuwunguzawunguza maso nthaŵi zonse, kudera nkhaŵa kuti mwina olamulira anali kundidikira mobisala kuti andigwire. Ndikhulupirira kuti m’kuganiza kwanga ndinali kufunafuna chinachake, ngakhale kuti sindinachidziŵe.
Ndinali kuŵerenga zinthu zomwe zinandipangitsa kukhala wolakalaka. Ndinafuna kumvetsetsa. Mafunso anali kudzaza m’maganizo mwanga, ndipo sindinadziŵe kumene ndikanapita kaamba ka mayankho. Ndikhulupirira kuti chifukwa chakuti mayi wanga anapitapo ku Nyumba Yaufumu ya Mboni za Yehova, ndinasankha kupita kumeneko. Ndinali wamantha ponena za icho. Sindinali wotsimikizira ponena za kulandiridwa komwe ndikalonjeredwa nako, komabe ndinapita. Kulandiridwako kunali kwabwino. Ambiri anandilandira; Mboni ina inayamba phunziro la Baibulo ndi ine.
M’miyezi yomwe inatsatira, chikumbumtima changa chinabwezeretsedwanso. Kuchulukira komwe ndinaphunzira, kunali kuchulukira komwe ndinalingalira kuti, ‘Sindingapitirize motere. Chinachake chiyenera kuchitika. Kaya ndileke kuphunzira Baibulo kapena ndikadzipereke.’ Mwamsanga ndinazindikira kuti sindikanaleka kuphunzira kwanga Baibulo, koma chosankha chinacho chinali chochititsa mantha. Sindinachifune. Sindinafune kupita ku ndende.
Chinali chosankha chovuta koposa chomwe sindinachichitepo ndi kale lonse, koma ndinatero. Pa msinkhu wa zaka 24, ndinapita kwa mmodzi wa akulu mu mpingo, Willard Stargell. Ndinamuwuza iye kuti ndinapha munthu ndipo ndinafuna kukadzipereka.
“Kodi uli wotsimikiza kuti nchimene ukufuna kuchita?” iye anandifunsa tero.
“Ndiri wotsimikizadi.”
“Ndidzathandiza m’njira iriyonse yomwe ndingakhoze. Kodi ungakonde kuti ndidzakuperekeze ku polisi?”
“Ndithudi ndingatero.”
“Chabwino, padzakhala msonkhano wadera wa Mboni za Yehova kothera kwa mlungu uno,” iye anandikumbutsa tero. “Tidzapita kukapezekako, ndipo kenaka tidzapita ku polisi Lolemba m’mawa.”
Ndinalikonda lingalirolo. Ndinafuna kupezeka pa msonkhano, komanso ndinawopa lingaliro la kupita ku polisi. Ndinakondwera ndi mwaŵi wa kuchedwetsako. Chotero ndinapita naye ku msonkhano ndipo ndinakondwera. Lolemba m’mawamwake tinapita ku polisi, ndipo ndinadzipereka.
Apolisi sanachikhulupirire. Siambiri omwe amadzipereka—chifukwa cha kupha! Iwo anatumiza foni ku polisi mu Bangor, Maine, kuti atsimikizire. Tsiku limodzi ndi theka pambuyo pake, ndinali m’jere ya bomalo mu Bangor. Tsiku lotsatira Mboni ya kumaloko inandichezera. Pamene mlandu wanga unazengedwa, Stargell anabwera ku Maine kudzawonekera monga mboni yanga. Kumeneko ndinavomereza za kuba ndi kupha; mutu waukulu wolengeza zotulukapozo unalankhula za ine monga “Wodzisonyeza monga Woweruza Aweruzidwira M’ndende kwa Moyo Wonse.” Mwezi umodzi pambuyo pake ndinali mu ndende yaikulu ya Maine, kutumikira kwa zaka 15 ndi kupitiriza m’moyo wanga wonse. Kumenekonso Mboni zinandichezera.
Kulandiridwa kwanga ndi akaidi kunali kosiyanasiyana. Iwo anandiseka chifukwa ‘chokhala wopusa podzipereka ndekha,’ makamaka popeza kuti apolisi anali ataleka kundifunafuna. Pamene anadziŵa kuti ndinachita tero chifukwa chophunzira Baibulo, anandinyodola, akumanditcha ‘nkhosa pakati pa mimbulu.’ Kuchitiridwa moipako nthaŵi zonse kunali kwapakamwa, sikunakhudzepo thupi. Kwa mbali yaikulu, ndinadzipatula kwa akaidiwo.
Chowonadi chinakhala chinjirizo kwa ine. M’kupita kwa nthaŵi iwo anazindikira kuti ‘jaha ameneyu ndi mmodzi wa Mboni za Yehova. Iye ali wauchete. Sadzadziloŵetsa mu iriyonse ya mikangano ya mkatiyi.’ Ndiponso, anadziŵa kuti sayenera kubwera kudzandigulitsa anam’goneka kapena kundipangitsa kuti ndikabe chinachake ndi kupatsa iwo. Akuluakulu oyang’anira anazindikiranso kuti sindikaphwanya malamulo. Icho chinapangitsa mbiri yanga kukhala yosadetsedwa ndi kundipatsa ufulu wowonjezereka.
Pa nthaŵi ina mkati mwa nyengo imeneyi, ndinapatuka pa kulondola kwanga chowonadi cha Baibulo. Sikuti ndinasankha mwadala kusapitiriza. Kunali kulephera kulabadira Ahebri 2:1, pamene tikuchenjezedwa kuti ‘tisatengeke.’ Komabe, ndinatero. Ngakhale m’ndende, kukondetsa zinthu zakuthupi kungakutchereni msampha! Mwaŵi unatseguka pamene ndinkapanga zinthu zina zatsopano kaamba ka chiwonetsero m’chipinda chowonetsera cha ndende. Alendo anali kugula zinthuzi, ndipo zochulukira za ndalamazo zinapita kwa andende omwe anazipanga. Chotero ndinadziloŵetsa m’kupanga ndalama, ndipo phunziro langa laumwini linayambukiridwa.
Kenaka ndinayamba kulingalira inemwini kuti: ‘Kodi nchifukwa ninji unadzipereka wekha? Kodi nchifukwa ninji ndinabwerera ndi kupita kundende? Ndipo tsopano kodi ndikulekadi maphunziro anga a Baibulo? Chimenechi sichikutanthauza kanthu! Chotero sukanadzipereka konse.’ Mbali ya vuto langa inali yakuti ndinali ndi vuto la kukhulupirira kuti Yehova anandikhululukiradi pa kupha munthu. Mmodzi wa alondawo anali Mboni, ndipo anawona kuti ndinali wopsyinjika ponena za chimenechi. Chotero anandisimbira zinthu zina zomwe iye anachita pamene anali kugwira ntchito mu Vietnam asanakhale Mboni.
“Kodi nchiyani chikukupanga kukhala wapadera?” iye anafunsa tero. “Yang’ana kwa miyoyo yonse ya anthu wamba yomwe ndiri nayo liwongo. Pamene gulu langa linawukira m’midzi ya Vietnam, tinalikhadi unyinji wa anthu, ambiri a iwo anali akazi ndi ana opanda liwongo. Kodi ukuganiza kuti chimenecho sichindivutitsa tsopano? Sindingachiiwale konse! Komabe ndimadzimva kuti Yehova, Mulungu wachikondi chopanda malire, wandikhululukira. Chimene unachita sichinali choipa mofanana ndi chomwe ndinachita. Iwe unapha munthu mmodzi; ine sinditha konse kudziŵa unyinji womwe ndinapha!”
Ndicho chimene ndinafuna. Chinandipangitsa ine kulingalira, kuwunikira pa chifundo ndi kukhululukira kwa Yehova awo amene amalapa mowona mtima. Chotero ndinaleka ntchito zanga za kukondetsa zinthu zakuthupi ndi kubwereranso pa ndandanda yanga ya phunziro la Baibulo. Ndipo ndi mmene zakhalira chiyambire pa nthaŵiyo.
M’kupita kwa nthaŵi, phunziro la Baibulo la mlungu ndi mlungu linali kutsogozedwa kwa ine, ndipo kamodzi pa mwezi ndinali kuloledwa kupita kunja ndi Mboni zina kaamba ka misonkhano ya kutali. Pa nthaŵi ina, angapo a andende ena ndi ine tinali kuphunzira Baibulo. Tinali okhulupiriridwa ndipo tinapatsidwa mwaŵi wokulira. Akuluakulu anadziŵa kuti sanafunikire kutiyang’anira ife. Nthaŵi ina tinaloledwa kupita ku lumande ndi lumande tikumagaŵira matrakiti, limodzi ndi chiitano cha kuchiwonetsero cha zithunzithunzi za Mboni za Yehova. Oposa 20 anapezekako.
Yehova, chakudya chauzimu kupyolera m’gulu lake, ndi thandizo lachikondi la abale okhulupirika linandisungirira ine. Pamene ndinali m’ndende ndinalandira makadi ndi makalata ambiri olimbikitsa kuchokera kwa Mboni, ndipo izi zinali thandizo lauzimu lomwe linadzutsa uzimu wanga. Zonsezi zinatsogolera ku ubatizo wanga mwa kumizidwa m’madzi mu 1983 kuchitira chithunzi kudzipereka kwanga kwa kuchita chifuniro cha Yehova—pambuyo pa zaka zisanu ndi ziŵiri m’ndende yokhaulitsira ya boma la Maine.
Zaka ziŵiri pambuyo pake, patapita zaka zisanu ndi zinayi m’ndende yokhaulitsira, ndinasamutsidwira ku ndende yaing’ono ya pafupipo. Chaka chimodzi ndi theka pambuyo pake, ndinasamutsidwira ku malo ogwira ntchito mwaufuluko mu Bangor. Kumeneko andende amatumizidwa pa maprojekiti kukagwira ntchito, akumabwerera pamapeto pa tsikulo kumalowo. Miyezi isanu ndi umodzi pambuyo pake ndinafika kaamba ka kupereka lumbiro langa loyamba. Palibe ndi mmodzi yemwe wa alondawo kapena akaidi anaganiza kuti ndingakhoze. “Palibe amene amakhoza nthaŵi yoyamba,” iwo anatero. “Osati ndi mmodzi yense!”
Koma ndinatero. Zowona, ochepa anakhoza kwa nthaŵi yoyamba. Akaidi a nthaŵi zonse amanama ndi kuyesera kunyenga bungwe lolumbiritsa, koma amakhala atazimvapo kale zimenezo. Iwo amawona zonsezo. Ndinangopita patsogolo pawo ndi kunena kuti, ‘Umu ndi mmene ndiliri, ichi ndicho chomwe ndachita, umu ndi mmene ndasinthira, ndipo ichi nchomwe ndikufuna kuchita.’ Ndinawauza iwo ponena za kuphunzira kwanga Baibulo, ponena za kusintha komwe kwapanga kwa ine, ndi ponena za kukhala kwanga mmodzi wa Mboni za Yehova. Iwo anawona masinthidwe amenewa.
Ndikhulupirira kuti nsonga yakuti ndinadzipereka ndekha, kuti ponse paŵiri mkhalidwe wanga ndi mbiri yanga ya pa ntchito zinali zabwino, ndipo kuti malamulo abwino a m’Baibulo amene ndinaphunzira anawonekera mu kawonedwe ndi mkhalidwe wanga—zonsezo zinandilankhulira. Kuwonjezera apo ndinapemphera kwa Yehova ndi kuyedzamira pa iye. Ndimakonda kulingalira kuti iye angakhale anathandizira ku icho, ndipo ndikhulupirira kuti uku sikudzitukumula kwanga. Pa mlingo uliwonse, bungwelo linapereka lumbiro langa. Mu February 1987, pambuyo pa zaka 12 m’ndende, ndinali womasuka kuchoka.
Pa April 30, 1988, ndinakwatira mmodzi wa Mboni za Yehova. Iye ali ndi ana atatu kuchokera ku ukwati wake wakale. Monga banja, timakhala ndi phunziro lathu la Baibulo la mlungu ndi mlungu. Timapezeka pa misonkhano yonse pa Nyumba Yaufumu. Timalalikira mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu ku nyumba ndi nyumba. Timapanga maulendo obwereza kwa onse omwe ali okondweretsedwa, ndipo timatsogoza maphunziro a Baibulo apanyumba ndi omwe amafuna. Pambuyo pa zaka zingapo za kulalikira kokhala ndi polekezera m’ndende ndi kusapezeka konse pa misonkhano, nchosangalatsa chotani nanga kugawanamo m’ntchito Zachikristu za Mboni za Yehova ‘ndi kumasuka kwakukulu kwa kulankhula’!—Machitidwe 28:31.
Zonsezi zinatheka chifukwa chakuti chidziŵitso cholongosoka cha Mawu a Mulungu chinanditheketsa kuchotsa umunthu wanga wakale waupandu ndi kuvala umunthu watsopano Wachikristu wolengedwa m’chifanefane ndi chifaniziro cha Yehova Mulungu.—Akolose 3:9, 10.
Ndithudi, m’nkhani yanga ‘mawu a Mulungu anali akuthwa ndipo anapereka mphamvu’ m’kundichotsa ine mu mkhalidwe wakale ndi kundikonzanso monga chiŵalo chosunga lamulo cha chitaganya ndi mlaliki wa mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu. (Ahebri 4:12, NW) Zonsezi ku chitamando cha Yehova, “Atate wachifundo ndi Mulungu wachitonthozo chonse.”—2 Akorinto 1:3.—Dzina lasiyidwa mwapempho.
[Mawu Otsindika patsamba 19]
Usiku wina ntchito yanga yaupandu inathera m’kupha munthu
[Mawu Otsindika patsamba 20]
Kaya ndileke kuphunzira Baibulo kapena ndidzipereke
[Mawu Otsindika patsamba 21]
Apolisi sanachikhulupirire. Siambiri omwe amadzipereka—chifukwa cha kupha!
[Mawu Otsindika patsamba 22]
Tinaloledwa kupita ku lumande ndi lumande tikumagaŵira matrakiti a Baibulo