Mphamvu Yosintha ya Chowonadi
“Mbala yothyola nyumba ina yomwe inamasulidwa mwamsanga, inaba mwakuthyola nyumba nthaŵi 500 m’miyezi isanu ndi iŵiri. Wogwirira chigololo amene anamasulidwa zaka zinayi chilango chake cha zaka khumi chisanathe, anaukira mwakugonana ndi kupha mwambanda mkazi wina. Wakupha womasulidwa ndi chikole anathyola nyumba ziŵiri napha anthu atatu.”—Reader ’s Digest, November 1990.
“Pafupifupi 63 peresenti ya akaidi otulutsidwa m’ndende zazikulu anagwidwanso chifukwa chochita upandu wowopsa m’zaka zitatu, inanena motero Dipatimenti ya Chiweruzo m’kupenda kotulutsidwa lero.”—The New York Times, April 3, 1989.
“Lingaliro lakuti ndende ndimalo osinthira apandu siliri lowona. Ndende ndi ‘malo osungira’ ndi ‘ophunzitsira upandu.’”—Sunday Star ya Toronto, March 20, 1988.
Wolonda akaidi wa ku Rikers Island, ndende ya ku New York City akunena kuti: “Mwana amabwera kuno ali ndi zaka khumi mphambu zisanu ndi zinayi zakubadwa, ndiye amene anali kufunidwa chifukwa chakuba. Pamene atuluka kuno, iye sadzakhala munthu wofunidwa. Nthaŵi yotsatira, adzakhala mbala yonyamula mfuti.”—Magazini a New York, April 23, 1990.
“Zipata za ndende zakhala ngati zitseko zozungulirazungulira: pafupifupi aŵiri mwa atatu a akaidi onse amagwidwanso m’zaka zitatu za kumasulidwa kwawo.”—Magazini a Time, May 29, 1989.
PALIBE chirichonse cha zapamwambazo chomwe chiri chatsopano kwa ife. Ndinkhani yakale: Ndende sizimasintha anthu. Chowonadi chimasintha. Nkhaniyo ndi ya: Ron Pryor.
Ron amayamba tsiku lirilonse mwakuŵerenga lemba m’Baibulo ndi banja lake. Ukwati wake uli wamtendere ndi wachikondi. Nyumbayo ili yolongosoka ndi yaukhondo. Ana awo amuna aŵiri anali ophunzira abwino—samagwiritsira ntchito mankhwala ogodomalitsa, samamwa zoledzeretsa, alibe vuto lirilonse. Panthaŵi ino amakhala okha ndipo amakhala ndi phande m’ntchito Yachikristu. Ron ndi mkazi wake, Arlynn, ali otanganitsidwa m’mudzi mwawo kuchita ntchito yodzifunira monga Akristu. Miyoyo yothandiza kutumikira ena.
Komabe, mu 1970, Ron Pryor anali m’ndende kudikirira kuzengedwa mlandu chifukwa cha mbanda. Iye anapezeka waliŵongo, anaweruzidwa, nayamba kutumikira m’ndende yokhaulitsira. Ameneŵa anali mapeto a ntchito yaupandu ya nyengo yaitali yomwe inamloŵetsa m’ndende mobwerezabwereza. Koma muloleni Ron asimbe nkhani yake.
“Ndikukumbukira kuti ‘kuponyedwa m’ndende’ koyamba kunali kumangiriridwa ku chingwe choyanikapo zovala. Pamene ndinali ndi zaka zakubadwa zitatu kapena zinayi, ndinawonekera ngati kuti ndinali ndi dongosolo loyendayenda lokhazikitsidwiratu mwa ine. Ndinkachoka panyumba, kutaika, kutoledwa ndi apolisi ndikubwezedwa kunyumba. Potsirizira pake, amayi anandiuza kuti ngati sindidzaleka, adzatumiza lamya kwa osunga ana amasiye kuti abwere kudzanditenga ndikunditsekera. Ndinakhala pabwalo ndikumalira, kuwadikirira kuti abwere. Iwo sanabwere. M’malomwake, amayi anandimangilira ku chingwe choyanikapo zovala.
“Pamene ndinali kukula, ndinkaloŵa m’vuto mosalekeza, ndipo chiwawa chinakhala yankho langa ku vuto lirilonse. Ndinadzimva kukhala wosokonezeka, wokwiitsidwa, ndi wokanidwa. Sindinali kudziŵa chabwino ndi choipa. Ndinalola malingaliro anga, osati chikumbumtima, kunditsogolera. Kusukulu ndinachotsedwa m’giredi lina kupita mu lina chifukwa chakuti aphunzitsi anali osangalala kundithamangitsa. Ndinaleka sukulu m’giredi lachisanu ndi chiŵiri ndipo ndinathaŵa panyumba. Ndinaloŵa m’mayanjano oipa, ndipo motsimikiziradi chenjezo Lamalemba, anandiloŵetsa m’mavuto aakulu.—1 Akorinto 15:33.
“Sukulu zosintha zinaloŵa m’malo kumangiriridwa ku chingwe choyanikapo zovala. Izo sizinandisinthe. Ndinkathaŵa ndikugwidwanso. Ndikuthaŵa kusukulu ina ku Virginia, ndinaba galimoto lalikulu ndipo ndinagwidwa. Ndikumawonekera pamaso pa woweruza wotchedwa Jenkins pamilandu yakuba galimoto, ndinapeza kuti galimoto lalikulu lomwe ndinabalo linali la Woweruza Jenkins! Ndinali ndi zaka 16 zokha, koma ndinalengezedwa kukhala wosasinthika ndipo ndinazengedwa mlandu monga munthu wachikulire. Ndinaponyedwa m’ndende kwa zaka ziŵiri.
“Pambuyo pakutuluka m’ndende ndipo ndiri m’zaka zanga za m’ma 20, ndinagula njinga yamoto. Ndinasangalatsidwa ndi lingaliro la mphamvu lomwe inandipatsa, koma zimenezo sizinali zokwanira. Ndinaphatikana ndi anthu otchedwa Pagans—gulu lokhala ndi njinga zamoto lomwe nthaŵi zonse linkakhala m’mavuto, nthaŵi zonse kukhala ndi chikhumbo choyambitsa ndewu. Ndinayenerana nawo bwino lomwe.
“Pambuyo pake, ndinali woyendetsa galimoto lalikulu kumapereka zakudya kuchoka ku Florida. Sindinalinso wokangalika ndi anthu otchedwa Pagans, koma pamene ndinafika ku Virginia panthaŵi imeneyi, mu 1969, ndinakumana ndi mabwenzi anga akale otchedwa Pagans. Tinayamba kusangalala—kumwa vinyo, ndikuledzera ndi mankhwala ogodomalitsa. Panabuka mkangano, unakula, ndipo pamene ndewu yomenyana ndi manja inayambika mosonkhezeredwa ndi zakumwa zoledzeretsa ndi mankhwala ogodomalitsa, ndinaombera mfuti ndikupha munthu. Zipatso zowonjezereka kuchokera ku mayanjano oipa! Pambuyo pake, atifitifi aŵiri anandifunsa, ndipo ndinavomera mbandayo. Umu munali mu 1970.
“Ndinali m’ndende kudikirira kuzengedwa mlandu komabe mpandu wovutitsa. Mwachitsanzo, m’maŵa wina mkaidi wokhala ndi thayo anabwera ndi khofi. Nthaŵi zambiri ankatipatsa kapu yowonjezereka yodzamwa pambuyo pake. M’maŵa umenewo, ndinachinjiriza kapu yanga pansi pa mphika wakhofi, koma iye anati, ‘Palibe wowonjezereka.’ Ine ndinagamulapo kuti anasankha kukapatsa munthu wina. Chotero ndinati, ‘Ndiye kuti ulibe khofi wokwanira lero ati?’ Iye anati, ‘Inde.’ ‘Chabwino, tengatu wangayu.’ Ndinamtaira kumaso. Ndinabindikiritsidwa.
“Choncho ndikuyendayenda m’lumande lopanda mazenera la utali wa [mamita aŵiri ndi theka ndi mamita atatu] m’bwambi. Kwanthaŵi yoyamba m’moyo wanga, ndinayambadi kuganizira. Mafunso anadzaza m’mutu mwanga. ‘Kodi nchifukwa ninji moyo wanga nthaŵi zonse umakhala m’vuto chotero? Kodi nchifukwa ninji ndiri kabwerebwere m’ndende? Kodi nchifukwa ninji ndiri m’lumande lino? Kodi nchifukwa ninji ndiri ndi moyo? Chifukwa ninji? Chifukwa ninji? Chifukwa ninji?’ Mafunsowo anapitirizabe kudza koma panalibe mayankho. Ndiyeno ndinadziuza kuti: ‘Ndafika pamapeto. Kulibe malo opitako. Kusiyapo kokha ngati—kusiyapo kokha ngati kuli Mulungu—Mulungu amene amandiwona, amadziŵa kuti ndiripo, amandimvetsetsa—zomwe sindikudziŵadi! Mulungu, ngati muliko, ngati mukudziŵa kuti ndiripo, ngati pali chinachake chimene ndingachite—tangondiuzani chinachake, chirichonse!’
“Mkatimo munali Baibulo. Ndinaganiza kuti, ‘Apa ndipo poyambira.’ Ndinayamba kuliŵerenga. Koma sindikumbukira zimene ndinaŵerenga. Ndingokumbuka kuti ndinaliŵerenga, osamvetsetsa kalikonse. Mkati mwa mlungu umodzi wokha ndinabwereranso ku lumande. Lumande limodzi linali lotsegula, makama ake onse aŵiri anali opanda anthu. Anandiika mmenemo, ndipo masiku aŵiri pambuyo pake anaikamo mkaidi wina woti adzikhala nane. Panthaŵiyo ndinkaŵerenga Baibulo, kuyesayesa kulimvetsetsa. Iye anandiwona ndikuŵerenga nafunsa kuti: ‘Kodi ungakonde kumvetsetsa Baibulo?’ ‘Inde!’ ‘Ndidzakupezera bukhu lomwe lidzakuthandiza.’ Iye analembera kalata mmodzi wa Mboni za Yehova—panthaŵi ina iwo anaphunzira naye—ndipo posakhalitsa anandipatsa bukhu lokhala ndi mutu wakuti Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya. Mmenemo munali mu July 1970.
“Ndinayamba kuliŵerenga, ndipo ndinaliŵerenga kuchokera kuchikuto mpaka kuchikuto. Sindinamvetsetse zonse, koma zinamveka zanzeru. Pamene Mboni za Yehova zinabwera ndikuphunzira nane, mafunso onse omwe ndinkafunsa pamene ndinali m’chipinda chobindikiritsira anayamba kuyankhidwa. Kwa nthaŵi yoyamba m’moyo wanga, ndinazindikira chimene chinali chabwino ndi chimene chinali choipa. Pamene ndinadya chakudya chauzimu chimenechi chochuluka, ndinayandikira kwenikweni kukhala ngati awo ‘amene mwa kuchita nazo anazoloŵeretsa zizindikiritso zawo kusiyanitsa chabwino ndi choipa.’ (Ahebri 5:14) Chikumbumtima changa chinayamba kugwira ntchito, chinakhala ndimoyo!
“Kupeza chowonadi Chabaibulo kwamwadzidzidziku kunapangitsa kusintha kwenikweni mkhalidwe wanga wamaganizo. Ndinaŵerenga bukhulo m’maola 24. Usiku umodzi wokha ndinachoka kumkhalidwe woipitsitsa kufika ku mkhalidwe wabwino koposa. Ndinatsimikiza mtima kudziŵitsa akaidi anzanga chowonadi chomwe ndinali kuphunzira. Ndinaganiza kuti aliyense adzasangalatsidwa nacho monga mmene ndinaliri. Iwo sanasangalatsidwe. Kalelo ndinali wovutitsa kwa akaidi enawo; tsopano ndinawakwiitsa kwenikweni—kwakuti palibe aliyense anaganiza kuti zinali zotheka! Koma pamene Mbonizo zinapitiriza kubwera kundendeko kudzaphunzira nane, ndinakhala wochenjera kwenikweni m’kulalikira kwanga.
“Ndinapanga masinthidwe ambiri, ndipo m’miyezi iŵiri ndinakhala kaidi wokhala ndi thayo. Anandilola ngakhale kupita kunja, chomwe chinali chosayembekezereka polingalira za cholembedwa changa chakale ndi chifukwa chomwe ndinaliri kumeneko. Malamulo amakhalidwe abwino amene ndinali kuphunzira m’Baibulo anali kukhala ndi chiyambukiro. Madzi a chowonadi ochokera m’Mawu a Mulungu anali kuchita ntchito yake yoyeretsa, monga momwe anachitira nthaŵi za atumwi. Mphamvu yake yosintha ikusonyezedwa pa 1 Akorinto 6:9-11, motere:
“‘Kapena simudziŵa kuti osalungama sadzalandira ufumu wa Mulungu? Musasocheretsedwe; adama, kapena opembedza mafano, kapena achigololo, kapena olobodoka ndi zoipa, kapena akudziipsa ndi amuna, kapena mbala, kapena osirira, kapena oledzera, kapena olalatira, kapena olanda, sadzalowa ufumu wa Mulungu. Ndipo ena a inu munali otere; koma munasambitsidwa, koma munayeretsedwa.’
“Potsirizira pake ndinapita kumilandu. Anandiweruza zaka 20 chifukwa cha mbanda. Mu 1971, ndinatumizidwa kundende ya akaidi amilandu yaikulu. Kunali kumeneko kumene phunziro langa Labaibulo ndi Mboni linayambanso. Mkhalidwe wanga unasintha modabwitsa. Posakhalitsa anandipanga kukhala mkaidi wokhala ndi thayo m’ndende yatsopanoyi, ndipo anayamba kundipatsa chilolezo chakuchokapo. Panthaŵi ina, ndinafunsa Mboni yomwe ndinkakhala nayo kuti: ‘Kodi nchiyani chindiletsa kubatizidwa?’ Iye anafufuza ku mpingo wakumaloko ndipo yankho linabwera lakuti: ‘Palibe.’ Mu 1973, m’madzulo, ndinabatizidwa m’dziŵe lomwera ng’ombe pafamu yapafupi. Ndinapemphera pamene ndinkaloŵa m’madzimo, popeza kuti zimenezo ndizimene Yesu anachita pamene anamizidwa m’Mtsinje wa Yordano ndi Yohane Mbatizi.
“Pambuyo pake, kupita patsogolo kwanga kwauzimu kunali kofulumira. Ndinaloŵa m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki yochititsidwa mumpingo wakumaloko—ndithudi, sindinali kupezekapo mwaumwini. Ndinalandira magawo m’sukulu ndipo ndinajambula nkhani zanga patepi, ndipo anaziseŵera ku mpingo. Phungu wasukuluyo anabweza uphungu woti undithandize kuwongokera. Tinali kuchititsa msonkhano mlungu ndi mlungu m’ndendemo kumene akaidi ena anali olandiridwa kufika.
“Panthaŵi yonseyi ndinkawonjezera malemba ambiri ku chidziŵitso changa cha Baibulo. Iwo anali ngati miyala yopondapo yonditsogoza kutuluka m’makhalidwe osokonezeka omwe ndinakhalamo kwa mbali yaikulu ya moyo wanga, kufikira ndinamvetsetsa kusandulizika kumene mtumwi Paulo ananena pa Akolose 3:9, 10 (NW) kuti: ‘Vulani umunthu wakale ndi zochita zake, ndi kudziveka umunthu watsopano, umene mwa chidziŵitso cholongosoka ulinkupangidwa kukhala watsopano mogwirizana ndi chifanefane cha Uyo amene anaulenga.’
“Mu 1978 kuzengedwa mlandu kwachitatu kochitidwa pamaso pa bungwe lolumbiritsa kunali pafupi. Ndinabwezedwa nthaŵi ziŵiri chifukwa cha kuwopsa kwa maupandu anga. Nthaŵi ino bungwelo linalandira makalata 300 kuchokera kwa Mboni ndi anthu ena kutsimikizira za masinthidwe amene ndinawapanga.
“Pokhala kuti mwaŵi wanga wakutulutsidwa unawonekera bwino, ndinalingalira za kukwatira. Arlynn, mkazi wamasiye wokhala ndi ana aŵiri, anali Mboni yomwe inandilembera makalata pamene ndinali m’ndende. Anandichezera ndi ana ake aamuna aŵiri. Tinakondana. Ndinamasulidwa pa February 1, 1978. Tinakwatirana pa February 25, 1978. Tsopano, zaka 13 pambuyo pake, tidakali okwatirana achimwemwe. Mmodzi wa ana athu ngokwatira ndipo ali wokangalika monga mmodzi wa Mboni za Yehova. Mwana winayo amagwira ntchito yanthaŵi zonse pamalikulu a padziko lonse a Mboni za Yehova m’Brooklyn, New York.
“Mapemphero anga ayankhidwa. Ndine woyamikira kwa abale ndi alongo omwe andithandiza kwambiri. Ndiri ndichimwemwe chifukwa cha Mulungu wathu wachimwemwe, Yehova.—1 Timoteo 1:11, NW.
“Komabe, ndimanyansidwa ndi machimo anga akale. Ndimaipidwa kwambiri ndi mayendedwe anga akale oluluzika. Ndapemphera nthaŵi zambiri kwa Yehova kuti andikhululukire, ndipo ndimalingalira kuti wandikhululukira. Ndikhulupiriranso kuti anthu amene ndinawachimwira kalelo angakhoze kundikhululukira. Makamaka ndimakhulupirira kuti Yehova adzaukitsa munthu amene ndinamupha ndikuti adzapatsidwa mwaŵi wakukhala ndi moyo kosatha m’dziko lapansi Laparadaiso la Mulungu. Chimenecho chidzakwaniritsa chimwemwe changa!”
Zimene ndende ndi kubindikiritsidwa sizikanachita, chowonadi cha Baibulo chinazichita. Chinamutheketsa Ron Pryor kuvula umunthu wakale waupandu ndikudziveka umunthu watsopano Wachikristu. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti “mawu a Mulungu ali amoyo ndipo amapereka mphamvu,” kuphatikizapo mphamvu yakusintha.—Ahebri 4:12, NW.
[Mawu Otsindika patsamba 12]
Linali galimoto lalikulu la Woweruza Jenkins limene ndinaba!
[Mawu Otsindika patsamba 13]
M’chipinda chobindikiritsiramo munali Baibulo. Ndinayamba kuliŵerenga
[Mawu Otsindika patsamba 13]
Anandiweruza zaka 20 chifukwa cha mbanda
[Chithunzi patsamba 14]
Ron Pryor ndi mkazi wake, Arlynn, lerolino