“Insight on the Scriptures”—Bukhu la Nazonse Latsopano la Baibulo
PA Misonkhano Yachigwo ya “Chilungamo Chaumulungu” ya Mboni za Yehova, chilengezo chinapangidwa cha kutulutsidwa kwa bukhu la nazonse latsopano la Baibulo lokhala ndi mutu wakuti Insight on the Scriptures. Ichi ndi chofalitsidwa cha mavolyumu aŵiri, chokhala ndi chiwonkhetso cha masamba 2,560, onsewo okhala mu mtundu wowonekera bwino, wowerengeka. Pakali pano iripo kokha m’Chingelezi, koma kutembenuza kwayamba kale kuchitidwa mu unyinji wa zinenero zina.
Insight on the Scriptures imaphatikizapo zambiri za zomwe poyambapo zinali m’bukhu la Aid to Bible Understanding ndi zina zochulukira. Ndi m’mbali ziti mmene iyo iriri yosiyana? Unyinji wa mbali wakonzedwanso ndi kupangidwa chatsopano. Palinso nkhani zambiri zatsopano limodzinso ndi mbali zowonjezereka mu Insight on the Scriptures.
Mabukhu a Baibulo
Bukhu lirilonse la Baibulo lapatsidwa chisamaliro chapadera. Nsonga za kumbuyo za phindu zaperekedwa. Pali maautilaini atsopano a mabukhu onse a Baibulo, iriyonse ikumakokera chisamaliro ku mbali zapadera za bukhulo. Izi zimapereka kawonedwe kachidule koma komvetsetseka ka zamkati mwa bukhulo m’njira yomwe iri yopepuka kumvetseta. Mwachitsanzo, pali Mauthenga Abwino anayi a zolembera za moyo wa yesu wa pa dziko lapansi ndi utumiki, uliwonse wokhala ndi cholinga chosiyana. Pamene iyambitsa Mauthenga Abwinowo, maautilaini olunjikitsidwa amaika zolinga zimenezo mwa njira iyi: ‘Cholembera cha mtumwi Mateyu cha moyo wa Yesu chinalembedwa choyambirira ndi Ayuda m’malingaliro. Uthenga Wabwino umenewu umasonyeza kuti yesu ali Mfumu ya Umesiya yonenedweratuyo.’ ‘Marko amakhazikitsa zolembera zachidule, zoyenda mofulumira za moyo wa Yesu, zikumamuwunika iye kukhala Mwana wa Mulungu wogwira ntchito mozizwitsa.’ ‘Cholembera cha Luka cha moyo wa Yesu chinalembedwa kutsimikizira kuwona kwa zochitika zozungulira moyo wa Kristu ndi m’njira imene ikasangalatsa anthu a mitundu yonse.’ ‘Cholembera cha mtumwi Yohane cha moyo wa Yesu chimawunikira mutu wakuti Yesu ali Kristu Mwana wa Mulungu, kupyolera mwa amene moyo wosatha uli wothekera.’ Pambuyo pa mawu otsegulira amenewa, maautilainiwo amapereka zamkati mwa mabukhuwo pansi pa chiŵerengero chokhala ndi polekezera cha mitu yaikulu. Ichi chingakuthandizeni inu kukumbukira lingaliro lenileni limene wolemba Baibuloyo anakulitsa.
Zoyenga
Kufufuza kosamalitsa kwa ndemanga m’chofalitsidwa chimenechi kwapangidwa m’chiwunikiro cha tanthauzo la mawu ogwiritsiridwa ntchito m’chinenero choyambirira cha Baibulo. Tsatanetsatane waphatikizidwanso kutheketsa muŵerengi kuyamikira mbali za Baibulo za tanthauzo la mawu a chinenero choyambirira. Kuwonjezerapo, matanthauzo a maina a m’Baibulo ayengedwa m’chiwunikiro cha njira mu imene mbali zokulira za mainawo zaikidwira kwenikweni mu New World Translation.
Kuyesayesa kwa khama kwapangidwanso kubweretsa nkhani m’chofalitsidwachi kukhala zoyenderana ndi zimene zafalitsidwa mu Nsanja ya Olonda m’zaka za posachedwapa. Mwachitsanzo, taphunzira zochulukira ponena za mtima, bukhu la moyo, kulengezedwa olunjika, ndi zinthu zina zambiri. Chidziŵitso chimenechi chaikidwa mu Insight on the Scriptures.
Tsatanetsatane wa mbiri ya kudziko wafufuzidwa m’chigwirizano ndi magwero oyambirira, kumene apezeka, m’malo mwa kungodalira pa zimene olemba ena anena ponena za zamkati mwa magwerowo; mazana angapo a zilozero zaphatikizidwanso kusonyeza kumene chidziŵitso choterocho chingapezedwe. Mbali za sayansi za nkhanizo zakonzedwanso chatsopano. Pakhala kukonzedwanso kwathunthu kwa mbali za malo otizungulira pa maziko a kufufuza kwa zofukulidwa pansi kochitidwa m’zaka za posachedwapa.
Atilasi ya Baibulo
Insight on the Scriptures imaphatikiza mamapu ena 70, osonyeza mazana angapo a malo otchulidwa m’Baibulo. Chotero, yophatikizidwa m’chofalitsidwachi iri atilasi ya Baibulo yomveketsedwa. M’mbali zambiri, mapu imodzi ndi imodzi imaloza kokha pa mbali zochepera za Baibulo kapena mbiri ya kudziko. Ndiponso, imakokera chisamaliro ku malo omwe ali ndi phindu lapadera m’mawu ozungulira amenewo. Mudzapeza mapu yosonyeza kuyenda kwa Abrahamu, ina yondandalitsa kupupulikapupulika kwa m’chipululu kwa Israyeli, ina yokuta kugonjetsa kwa Dziko Lolonjezedwa, ina ya moyo wa Davide monga wothaŵathaŵa ndi ina kaamba ka zochitika zogwirizana ndi kukhala kwake mfumu, mpambo wa mamapu ondandalitsa malo kumene Yesu anayenda mkati mwa utumiki wake wa pa dziko lapansi, ndi chiŵerengero cha mamapu chosonyeza tsatanetsatane wa Yerusalemu wa nyengo zosiyanasiyana za m’mbiri. Chilozero cha mapu chaperekedwa kukuthandizani kupeza mamapu achindunji omwe amapereka chidziŵitso chothandiza kwenikweni ponena za malo opatsidwa kapena mbali.
Ndi mamapu ochulukira, palinso ndandanda ya malo a maina, limodzi ndi malemba amene amasonyeza chifukwa chimene malowo aliri apadera m’mawu ozungulira achindunji a mbiri yakale omwe akulingaliriridwa. Polumikizanira masamba a bukhulo pali zithunzithunzi za mitundu mitundu za malo owonetsedwa pa mapu. Mbali zimenezi zingakuthandizeni kupindula mokwanira kuchokera ku zolembera za Baibulo, pamene mukuwona kugwirizana kwa malo amodzi ku anzake, ŵerengani tsatanetsatane ponena za chimene chinachitika kumeneko, ndi kuwona mmene malowo akuwonekera lerolino.
Mbali Zapadera mu Mitundu Mitundu
Pokonzekera chofalitsidwachi, malo osungirako zinthu zakale mu North America, Europe, ndi mu Middle East anafikiridwa ndi cholinga chofuna kupeza zinthu zaphindu zogwirizana ndi zolembera za Baibulo. Zithunzithunzi za zinthu zofunika koposa zinapezedwa. Kuwonjezerapo, zosonkhanitsidwa zingapo za zithunzithunzi za malo otchulidwa m’Baibulo zinabwereredwamonso, ndi cholinga chofuna kusankha zimene zikakhala zothandiza kwenikweni. Chotulukapo chaikidwa mu m’phatika zisanu ndi zitatu za masamba 16 zokhala ndi zithunzithunzi zamitundu mitundu zomwe ziri ndi phindu logwira ntchito. Izi ziri mfundo zazikulu zosangalatsa zomwe mudzasangalala nazo ndipo mudzakhala okhoza kuzigwiritsira ntchito m’njira zosiyanasiyana pamene mukuphunzitsa ena.
Mwachitsanzo, pali gawo lokhala ndi mutu wakuti “How We Got the Bible” (Mmene Tinapezera Baibulo). Molemba mapu, ilo limasonyeza mbali kupyolera m’zimene Baibulo latifikira ife—kuchokera ku zolembera zoyambirira kufika ku kutembenuza kwamakono. Iyo iri ndi zithunzithunzi za mbali ya mamanusikripiti akale ndi umboni wowonekera wotsimikizira ku chisamaliro chotengedwa ndi alembi oyambirira, ngakhale ku mlingo wa kuŵerenga zirembo m’mamanusikripiti omwe iwo anajambula.
Mbali ina iri yonena za “Flood of Noah’s Day” (Chigumula cha Tsiku la Nowa). Iyo imalingalira nkhani zonga ngati, “Could the ark have held all the animals?” (Kodi chingalawa chikanasunga nyama zonsezo?) ndi “Where did the floodwaters go?” (Ndikuti kumene madzi a pachigumula anapita?) Iyo imawonetsanso kufufuza kwa nthanthi za Chigumula kuchokera ku makontinenti asanu ndi imodzi ndi zisumbu za nyanja kusonyeza kuti zikumbukiro za tsiku la Chigumula cha Nowa zikupezeka pakati pa anthu a miyambo yopatuka kuzungulira dziko lonse lapansi.
Mbali zina zimachita ndi malo ozungulira Dziko Lolonjezedwa, maufumu akale omwe zochitachita zawo zinakhudza Israyeli, ndi chithunzi cha ulendo wa malo amene alendo angakhoze kuwona mkati ndi kuzungulira Yerusalemu lerolino. Zonse pamodzi, pali nkhani 50 zoterozo zokulitsidwa m’zithunzi za mitundu mitundu.
Chidziŵitso chonsechi chapangidwa kukhala chofikirika mopepuka mwa kugwiritsira ntchito zilozero zakuya m’mavolyumu amenewa. Zilozero zimenezi zimakulozerani inu ku kukambitsirana kosankhika kwa malemba oikidwamo ndi nkhani zondandalitsidwa.
Kutenga kayang’anidwe konse ka ntchitoyo, mawu oyamba awa amawonekera mu volyumu yoyambirira: “Cholinga cha chofalitsidwa chimenechi chiri kukuthandizani kupeza chidziŵitso pa Malemba. Kodi chimachitidwa motani? Mwa kubweretsa pamodzi kuchokera m’mbali zonse za Baibulo tsatanetsatane yemwe amagwirizana ndi nkhani yomwe ikukambitsiridwa. Mwa kukokera chisamaliro ku mawu a chinenero choyambirira ndi matanthauzo ake enieni. Mwa kulingalira chidziŵitso cholinganako kuchokera ku mbiri yakale ya kudziko, kufufuza kwa zofukulidwa, ndi minda ina ya sayansi ndi kulinganiza zimenezi m’chiwunikiro cha Baibulo. Mwa kupereka zithandiziro zowoneka. Mwa kukuthandizani inu kuzindikira phindu la kuchita m’chigwirizano ndi chimene Baibulo limanena.” Chotero mkati mwa masamba a Insight on the Scriptures muli chuma cha chidziŵitso cha phindu mowonadi chomwe inu mungagwiritsire ntchito kupindula inu eni ndi ena.