Chipembedzo Chonyenga Chichita Mbali ya Mkazi Wachigololo
1. Ndimotani mmene chigololo chawonedwera ndi ambiri?
ENA amaitcha iyo ntchito ya kalekale—ija ya mkazi wa chigololo, mkazi waganyu, kapena mkazi wachitole. Monga momwe amagwiritsiridwa ntchito mofala, mawu onse amenewa ali ndi tanthauzo lofanana, kulozera ku mkazi wachisembwere yemwe amagulitsa kugwiritsira ntchito kwa thupi lake kwa amuna. Komabe, panali nthaŵi pamene ichi chinawonedwa kukhala kuitana kolemekezedwa!
2, 3. Ndimotani mmene mbali yochitidwa ndi ansembe achikazi mu Babulo wakale inasiyanirana ndi chilamulo cha Yehova kwa Israyeli ponena za kuchita chigololo kwa amuna ndi akazi?
2 Kulankhula za unsembe wa Babulo wakale, Profesa S. H. Hooke, wokhala ndi ulamuliro pa zofukulidwa za Baibulo, ananena kuti: “Unsembe sunalekezere kwa amuna, koma akazi anapanga mbali ya ziŵalo za makachisi okulira. Chinalingaliridwa kukhala ulemu kukhala ku lamulo la ansembe achikazi, ndipo timamva za mafumu osiyanasiyana omwe anapereka ana awo aakazi ku chiitano chaunsembe. . . . Kugwira ntchito kwawo kofunika koposa kunali kutumikira monga akazi aganyu opatulika pa mapwando aakulu a m’nyengo. . . . Kachisi ya Ishtar [mulungu wachikazi wa kubala ndi nkhondo], mwachibadwa, inali ndi ogwirapo ntchito ochulukira a akazi oterowo.”
3 Ichi chinali chosiyana kwenikweni ndi kulambira komwe kunafunikira kuperekedwa kwa Yehova Mulungu ndi mtundu wa Israyeli. Lamulo linanena momvekera kuti: “Pasakhale mkazi [waganyu, NW] pakati pa ana akazi a Israyeli, kapena [mwamuna waganyu, NW] pakati pa ana amuna a Israyeli [wochita kugonana kofanana ziŵalo]. Musamabwera nayo mphotho ya wachigololo, kapena mtengo wake wa galu kuloŵa nazo m’nyumba ya Yehova Mulungu wanu, chifukwa cha chowinda chirichonse; pakuti onse aŵiriwa Yehova Mulungu wanu anyansidwa nawo.” (Deuteronomo 23:17, 18) Chotero, malipiro a mkazi wachigololo sanali olandirika kukhala chopereka ku mabwalo a Mulungu. Ngakhale kuchita chigololo popanda kulongosoledwa kulikonse kwa chipembedzo kunali konyansa. Aisrayeli analamulidwa kuti: “Usamaipsya mwana wako wamkazi ndi kumchititsa chigololo; lingadzale ndi chigololo dzikoli.” Malamulo otsutsa chigololo ndi kugonana kwa ofanana ziŵalo, zomwe zikulongosoledwa kukhala “zochititsa manyazi,” anali chinjirizo kaamba ka mtunduwo, ponse paŵiri mwauzimu ndi kuthupi.—Levitiko 19:29; 20:13.
Chigololo Chauzimu Ngakhale Choipirako
4. Ndi uti umene uli mkhalidwe woipitsitsa wa chigololo?
4 Kuchokera ku kawonedwe ka Mulungu, ngakhale kuli tero, pali mkhalidwe woipirako wachigololo—chigololo chauzimu, kapena kudzinenera kulambira Mulungu wowona pamene m’chenicheni akupereka kulambira ndi chikondi kwa milungu ina. Yerusalemu wakale anatenga chigololo chake moposerapo pang’ono. Iye anapereka mphatso kwa mitundu imene inachita chigololo mwauzimu ndi iye, kuipitsa kulambira kowona.—Ezekieli 16:34.
5, 6. Ndani omwe akuchita chigololo chauzimu m’zana lino la 20, akumatsogolera ku mafunso otani?
5 Ngakhale m’zana lino la 20, chigololo chauzimu chiri chofala m’dongosolo la chipembedzo cha dziko. Chikristu cha Dziko chiri mbali yotchuka kwenikweni ya dongosolo limenelo—dongosolo limene Baibulo limatcha “Babulo Wamkulu, amayi wa achigololo ndi wa zonyansitsa za dziko.”—Chibvumbulutso 17:5.
6 Koma kodi nchiyani chimene chiri malekezero otsirizira a Babulo Wamkulu? Ndipo ndimotani mmene chotulukapo chotsirizira chimenecho chidzayambukirira inu ndi okondedwa anu? Ngati Mulungu anaweruza moipa achigololo mu Israyeli wakale, nchiyani chomwe iye adzachita ponena za kuchita chigololo kwauzimu kwamakono? Nkhani zotsatira zidzasanthula mafunso amenewo ndi olinganako.