Chigamulo
Chiŵerengero cha opezekapo pa Misonkhano ya “Chilungamo Chaumulungu” mosakaikira chidzakhala chitapambana chija cha chaka chatha, pamene 6,443,597 anasonkhana pa malo 1,098 dziko lonse, okhala ndi 93,822 akubatizidwa. Nkhani yakuti, “ ‘Mkazi Wachigololo’ wa Mbiri Yoipa” yoperekedwa pa Misonkhano yonse ya “Chilungamo Chaumulungu,” inatsatiridwa ndi kutulutsidwa, m’zinenero zoposa 20, kwa bukhu lalikulu lochitiridwa chitsanzo mokongola la masamba 320 Revelation—Its Grand Climax at Hand! Mlankhuli anauza omvetsera ake kuti: “Gwiritsirani ntchito bukhuli bwino m’maphunziro anu aumwini ndi a mpingo. Ligwiritsireni ntchito, kachiŵirinso, m’kulengeza ku dziko kuti Babulo Wamkulu waukiridwa, kuti itundu tsopano ikuyang’anizana ndi Armagedo, ndipo kuti chimake chachikulu chidzafikiridwa mu ulamuliro wa Ufumu waukulu wa Yehova mwa Kristu ndi mkwatibwi wake. Mudzakhala achimwemwe kumva ndi kuwona zinthu izi, ‘popeza nthaŵi yoikidwiratu iri pafupi’!”—Chibvumbulutso 1:3, “NW.”
Ife, amene chiyambire 1914 takhala tikukhala ndi moyo “m’tsiku la Ambuye” ndipo pa nthaŵi ino ya chiweruzo chaumulungu, tikusangalala mokulira m’thayo lokulira kuposa onse, lija la kutumikira Mfumu Ambuye Yehova pansi pa Mfumu yake ya mafumu, Yesu Kristu. (Chibvumbulutso 1:10) Monga MBONI ZA YEHOVA, tichitira umboni kuti:
(1) TIMADA chitonzo chimene Babulo Wamkulu, ndipo makamaka Chikristu cha Dziko, chapereka pa dzina la Mulungu yekha wowona ndi wamoyo, Yehova. Kaamba ka mbali yathu, TIVOMEREZA ndi mtima wonse, m’mawu a Chibvumbulutso 4:11: “Muyenera inu, [Yehova, NW], Mulungu wathu, kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphamvu.”
(2) TIMADA kumamatira kwa Chikristu cha Dziko ku ziphunzitso za Chibabulo, zodziŵika zija za mulungu wa utatu, kusafa kwa moyo wamunthu, kuzunzidwa kosatha m’moto wa helo, purigatoriyo wa moto, ndi kulambira kwa mafano—konga kuja kwa Madonna ndi mtanda. M’chigwirizano ndi Chibvumbulutso 22:18, 19, TIMAMAMATIRA MOLIMBA ku Mawu olembedwa a Mulungu ndi zonse zimene zirimo.
(3) TIMADA nthanthi ndi machitachita okana Mulungu, zofala kwambiri m’Chikristu cha Dziko, zonga ngati chisinthiko, kuthiridwa mwazi, kuchotsa mimba, kunama, umbombo, ndi kusawona mtima. M’kulambira kwathu ndi njira yathu ya moyo, TIDZALEMEKEZA Mlengi wathu, Yehova Mulungu, Wamphamvuyonse, yemwe njira zake zalongosoledwa pa Chibvumbulutso 15:3 monga “zolungama ndi zowona.”
(4) TIMADA kulephera kwa Chikristu cha Dziko kulabadira mauthenga a Yesu ku mipingo isanu ndi iŵiri pa Chibvumbulutso mitu 2 ndi 3 m’nkhani zoterezi zonga mpatuko, mafano, dama, chisonkhezero cha Yezebeli, kufunda, ndi kusowa kudziyang’anira. Ku mbali yathu, TIDZAMVETSERA NDI KUMVERA chimene “mzimu unena ku mipingo.”
(5) TIMADA chisembwere ndi kuloleza kokhala mu Chikristu cha Dziko ndi pakati pa atsogoleri ake a chipembedzo, ndipo timalandira chiweruzo chabwino cha Yehova chosonyezedwa pa Chibvumbulutso 21:8 kuti aja omwe apitiriza m’kuipa kwawo—adama, abodza, ndi otero—adzawonongedwa kotheratu. IFE MWA MTIMA WONSE TICHIRIKIZA miyezo ya Baibulo pa kugonana, ukwati, ndi moyo wa banja.
(6) TIMADA chigololo chauzimu cha utali wa mazana cha atsogoleri a chipembedzo cha Babulo Wamkulu mu ubwenzi wake ndi atsogoleri a dziko kupeza mphamvu, chuma, ndi ulamuliro wopondereza pa anthu wamba. TIRI OGAMULAPO kuthandiza anthu owona mtima kulabadira kuitana kwa mngelo pa Chibvumbulutso 18:4: “Tulukani mmenemo, anthu anga.”
(7) TIMADA liwongo la mwazi lalikulu lotulukapo kuchokera ku 100 miliyoni ya miyoyo yoperekedwa mu nkhondo m’zana lino lokha, kwakukulukulu yochititsidwa ndi dama la mkazi wachigololo wamkulu ndi mphamvu za ndale zadziko. TIMASANGALALA kuti nthaŵi yoikidwiratu iri pafupi kaamba ka Mulungu kupereka chiweruzo cha chilango pa Babulo Wamkulu, monga kwasonyezedwera bwino lomwe pa Chibvumbulutso 18:21-24.
Monga Mboni za Yehova, TIMACHIPENDA ICHO KUKHALA CHISANGALALO NDI MWAŴI kulengeza ku dziko kuti mu 1914 “ufumu wa dziko lapansi wayamba kukhala wa Ambuye wathu [Yehova], ndi Kristu wake.” (Chibvumbulutso 11:15) TIRI OGAMULAPO kupita patsogolo mopanda mantha kudziŵitsa ziweruzo za Yehova zolengezedwa pa Babulo Wamkulu ndi m’kuchenjeza nkhondo ya Mulungu ya Armagedo irinkudza. TIRI OGAMULAPO kumveketsa, m’mawu ofuula “kwa mtundu uliwonse ndi fuko ndi manenedwe ndi anthu,” nkhani zosangalatsa kuti “m’mwamba mwatsopano ndi dziko latsopano” ziri pafupi kaamba ka kudalitsa mtundu wa anthu omvera. (Chibvumbulutso 14:6; 21:1) TIMASANGALALA kuti monga chotulukapo cha kulengeza kumeneku, khamu lalikulu la anthu oposa mamiliyoni atatu kuchokera ku mitundu yonse liri tsopano logwirizana limodzi nafe kuzungulira dziko lonse. Limodzi ndi mngelo wowuluka m’mwamba, tonsefe timalingeza kuti: “Opani Mulungu, mpatseni ulemerero; pakuti yafika nthaŵi ya chiweruziro chake; ndipo mlambireni Iye amene analenga m’mwamba ndi mtunda ndi nyanja ndi akasupe a madzi.”—“Chibvumbulutso 14:7.
[Mafunso]
1. Ndi m’chiyani mmene Mboni za Yehova tsopano zikusangalala?
2. Pa iriyonse ya nsonga zisanu ndi ziŵiri za Chigamulocho, longosolani (a) chimene Mboni za Yehova zimada ndi (b) kutsimikizira kowona kumene Mboni zimapanga.
3. (a) Ndi chisangalalo chotani ndi thayo zimene Mboni za Yehova ziri nazo? (b) Nchiyani chomwe chiri chigamulo cha Mboni? (c) Nchiyani chimenenso tiri ogamulapo kuchita? (d) Ndi m’kusangalala kotani ndi kulengeza kumene Mboni za Yehova zimagawanamo?