Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
◼ Kodi mtumwi Paulo anali kusonyeza kunyada kwaufuko mu kuvomerezana ndi kusuliza kophimba kwa anthu aku Krete?
Ayi, Paulo sanagonjere ku kachitidwe ka kupanga manenedwe osuliza ponena za anthu a fuko lina kapena chiyambi cha mtundu.
Funso iri limabwera kuchokera ku ndemanga ya mu kalata ya Paulo kwa wophunzira Tito. Paulo anali atamusiya iye pa chisumbu chachikulu cha Mediterranean cha Krete kuti “alongosole zosowa, naike akulu m’midzi yonse.” Paulo anandandalitsa ziyeneretso zina kaamba ka akulu a mpingo koma analangiza Tito kuti: “Pakuti alipo ambiri osamvera mawu, olankhula zopanda pake, ndi onyenga, makamaka iwo a kumdulidwe, amene ayenera kutsekedwa pakamwa; ndiwo amene apasula mabanja [onse, NW].”—Tito 1:5, 10, 11.
Paulo anapitiriza mu vesi 12 kuti: “Wina wa mwa iwo, ndiye mneneri wa iwo okha, anati, Akrete ndiwo amabodza masiku onse, zirombo zoipa, aumbombo, aulesi.” Mu vesi 13, iye anawonjezera kuti: “Umboni uwu uli wowona. Mwa ichi uwadzudzule mokalipa, kuti akakhale olama m’chikhulupiriro.”
Otembenuza ambiri a Baibulo analola ndemanga ya Paulo yakuti “umboni uwu uli wowona” kupitiriza pambuyo pa mawu amene iye anagwira kuchokera kwa mneneri wa ku Krete. Ena amayamba ndime yatsopano ndi vesi 13.a Mu nkhani iriyonse, ndi ku chiyani kumene Paulo anali kulongosola kuvomereza?
Iye motsimikizirika sanali kuvomerezana ndi kalankhulidwe kodzala ndi ufuko kapena utundu motsutsana ndi Akrete. Tingakhale otsimikiza za chimenecho, popeza kuti Paulo anadziŵa kuti ku Krete kunali Akristu abwino omwe Mulungu anavomereza ndi kuwadzoza ndi mzimu Wake woyera. (Machitidwe 2:5, 11, 33) Panali Akristu odzipereka okwanira kupanga mipingo “m’midzi yonse.” Pamene kuli kwakuti Akristu oterowo sanali anthu angwiro, tingakhale otsimikiza kuti sanali abodza ndi aumbombo aulesi; kupanda apo iwo sakanapitiriza kukhala ndi chivomerezo cha Yehova. (Afilipi 3:18, 19; Chibvumbulutso 21:8) Ndipo monga mmene ife lerolino tikupezera m’mitundu yonse, mwachiwonekere analipo mu Krete anthu a mitima yowona omwe anaipidwa ndi miyezo yotsika ya makhalidwe oipa yowazungulira ndipo anali okonzekera kuvomereza ku uthenga Wachikristu.—Ezekieli 9:4; yerekezani ndi Machitidwe 13:48.
Kumbali ina, panalinso anthu mu Krete omwe analibe miyezo yapamwamba ya makhalidwe abwino. Paulo anachipeza icho kukhala choyenera kugwira mawu omwe mwachiwonekere anayambitsidwa ndi Epimenides, wolemba ndakatulo wa ku Krete (mneneri kapena wolankhulira) m’zana lachisanu ndi chimodzi B.C.E. Koma Paulo anali kuvomerezana ndi kalongosoledwe kameneko monga kogwira ntchito ku mbali ina yapadera ya chiŵerengero cha anthu a ku Krete.
Awa anali ‘olankhula zopanda pake ndi onyenga’ omwe anali ogwirizana ndi Akristu okhulupirika ndipo anali kuyesera ‘kupasula mabanja [onse, NW].’ Onyenga opasula oterowo mowonadi amayenera kalongosoledwe kakuti “abodza, zirombo zoipa,” chimene chinali chowona mokwanira kwa anthu onga amenewo kulikonse. (2 Timoteo 3:6, 13) Kuwonjezerepo, aliyense amene anali kale m’mipingo yemwe ananyengedwa kutenga njira zimenezo anafunikira ‘kudzudzulidwa mokalipa.’ Awo opindula kuchokera ku kudzudzulidwa mwakutero angathandizidwe kukhala a chitsanzo chabwino ponena za ntchito zabwino ndi a “mawu olama osatsutsika.”—Tito 2:6-8.
Tiyenera kupeza chenjezo mu ichi kaamba ka ife tonse. Kunyada kwaufuko kapena kwa mtundu kungatigwere. (Yerekezani ndi Yohane 7:47-52.) Ife mwachidziŵikire timamva anansi, anzathu a kusukulu, kapena ogwira nawo ntchito akumapanga ndemanga zosankhana ponena za anthu ena, zonga ngati, ‘Eya, akumpoto aja onse ali achete ndi osadzimva’; ‘Chabwino, mumadziŵa mmene akum’mwera aja aliri onyada’; kapena, ‘Kuli kuika moyo pachiswe kukhulupirira anthu aja akutsidya kwa malire.’
Tiyenera kukalamira kupeŵa kugonjera ku katchulidwe kofala komwe mwinamwake kali kopanda maziko kapena kusinjirira mokulira. Ena angakhale omasuka kwenikweni ndi olankhulalankhula, ena angakhale achete kwenikweni kapena ochedwa kusangalatsa alendo. Komabe, tiyenera kukumbukira kuti ena a abale athu Achikristu mosakaikira angapezeke pakati pa anthu a gulu limenelo la fuko kapena mtundu, limodzinso ndi ena ambiri amene sanakhale Akristu owona koma omwe ali ndi zikhoterero zokhumbirika ndi omwe ali ndi njala kaamba ka chilungamo.
Mtumwi Petro anagogomezera chenicheni chakuti “Mulungu alibe tsankhu; koma m’mitundu yonse, wakumuwopa lye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.” (Machitidwe 10:34, 35) Tingakhale otsimikizira kotheratu kuti Paulo anavomerezana ndi chimenecho, akumawunikira kawonedwe kamodzimodziko m’zolembera zake ndi zolankhula. Nafenso tiyenera kutero.
[Mawu a M’munsi]
a Onani The New Berkeley Version limodzinso ndi matembenuzidwe olembedwa ndi R. F. Weymouth, F. A. Spencer, K. S. Wuest, ndi Abner Kneeland.