Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w89 6/15 tsamba 29
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
  • Nsanja ya Olonda—1989
  • Nkhani Yofanana
  • Kulinganiza Banja—Lingaliro Lachikristu
    Galamukani!—1993
  • Kodi Ndani Ayenera Kusankha za Ukulu wa Banja?
    Galamukani!—1996
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—2002
  • Kodi Moyo wa Munthu Umayamba Liti?
    Galamukani!—2009
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1989
w89 6/15 tsamba 29

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

◼ Kodi chiri chogwirizana ndi maprinsipulo a Baibulo kaamba ka Akristu aŵiri okwatirana kugwiritsira ntchito mibulu yoletsa kubala?

Malemba samanena mowonekera kuti aŵiri okwatirana Achikristu akulamulidwa kukhala ndi ana kapena, ngati iwo atero, ndi angati. Aŵiri okwatirana aliwonse ayenera mwamseri ndi mwathayo kugamulapo kaya kuyesera kulamulira ukulu wa banja lawo. Ngati iwo avomerezana kuchita kachitidwe koletsa kubala, chosankha chawo cha njira zoletsera kubala chirinso nkhani yaumwini. Ngakhale kuli tero, iwo afunikira kulingalira​—m’chigwirizano ndi kumvetsetsa kwawo kwa Baibulo ndi chikumbumtima chawo​—kaya ngati kugwiritsira ntchito njira inayake kukasonyeza ulemu kaamba ka kupatulika kwa moyo.

Baibulo limasonyeza kuti moyo wa munthu umayamba pa kukhala ndi pakati; Mpatsi wa Moyo amawona moyo womwe wangoyambika m’mimba, “ngakhale mluza” womwe pambuyo pake udzakula m’chibaliro. (Salmo 139:16, NW; Eksodo 21:22, 23a; Yeremiya 1:5) Chotero, palibe kuyesayesa komwe kuyenera kupangidwa kuthetsa moyo woyambitsidwawo. Kuchita tero kukakhala kuchotsa mimba.

Mibulu yoletsa kubala imagwiritsidwa ntchito mofala kuzungulira dziko. Ndimotani mmene imaletsera kubadwa kwa mwana? Pali mitundu yaikulu iŵiri ya mibulu​—combination pill ndi progestin-only pill (m’bulu waung’ono). Kufufuza kwamveketsa kugwira ntchito kwawo koyambirira kaamba ka kuletsa kubala.

Combination pill iri ndi estrogen (zinthu zodzetsa mwamkazi nyengo yofuna kugonana) ndi progestin (zoletsa mimba) Mogwirizana ndi U.S. Food and Drug Administration, “kugwira ntchito koyambirira” kwa combination pill kuli “kuletsa kutulutsidwa kwa dzira.” Chikuwoneka kuti utatengedwa mosalekeza, mtundu umenewu wa m’bulu chifupifupi nthaŵi zonse umaletsa kutulutsidwa kwa dzira kuchoka mu ovary (chiŵalo cha mkazi chotulutsa mazira). Pamene palibe dzira lirilonse kapena magwero otulutsidwa, kukhala ndi pakati sikungachitike mu Fallopian tubes (machubu otsogoza dzira ku chibaliro). Pamene kuli kwakuti mtundu umenewu wa m’bulu ungapangitse masinthidwe mu “endometrium [khungu lopyapyala la mkati mwa chibaliro] (yomwe imachepetsa kuthekera kwa kuzikidwa),” uku kukulingaliridwa kukhala kugwira ntchito kwachiŵiri.

Ndi cholinga chofuna kuchepetsa ziyambukiro za pambali, macombination pill okhala ndi mphamvu yochepera ya estrogen apangidwa. Mwachiwonekere, macombination pill okhala ndi mphamvu yochepera amenewa amalola zochitika zowonjezereka m’maovary. Dr. Gabriel Bialy, mkulu wa Contraceptive Development Branch of the National Institutes of Health, akunena kuti: “Kuwona kwapasadakhale kwa umboni wa sayansi kumasonyeza kuti ngakhale ndi m’bulu wokhala ndi mlingo waung’ono wa estrogen, kutulutsidwa kwa dzira kumaletsedwa, osati 100 peresenti, koma mwachidziŵikire kwenikweni chifupifupi 95 peresenti. Koma nsonga yakuti kutulutsidwa kwa dzira kumachitika siimafikira kutanthauza kuti kupangidwa kwa dzira la umoyo kwachitika.”

Ngati mkazi aphonya kumwa combination pill mogwirizana ndi ndandanda yake yolinganizidwa, pali kuthekera kowonjezereka kwakuti kugwira ntchito kwachiŵiri kudzachita mbali yake m’kuletsa kubala. Phunziro la akazi omwe anaphonya iŵiri ya mibulu yochepa mphamvu yomwedwa linapeza kuti 36 peresenti anali ndi kutulutsidwa kwa dzira “kolumphalumpha.” Magazini yakuti Contraception ikusimba kuti m’nkhani zoterozo “ziyambukiro za mibulu pa endometrium ndipo madzi a kotulukira kwa chibaliro angapitirizebe kupereka . . . chitetezero choletsa kukhala ndi pakati.”

Bwanji ponena za mtundu wina wa m’bulu​—progestin-only pill (m’bulu waung’ono)? Drug Evaluations (1986) ikusimba kuti: “Kuletsa kutulutsidwa kwa dzira sikuli mbali yokulira ya kuletsa kukhala ndi pakati ya mibulu yaing’ono ya progestin-only. Zinthu zimenezi zimapangitsa kupangidwa kwa madzi olimba a kotulukira kwa chibaliro omwe mwapang’ono ali osakhoza kuloŵereredwa ndi ubwamuna; iwo angawonjezere nthaŵi ya kayendetsedwe ka mkatimo ndiponso amapangitsa kuchepera kwa madzi a m’chibaliro [komwe kukaletsa kukula kwa dzira lamoyo lopangidwa lirilonse].”

Ofufuza ena adzinenera kuti ndi progestin-only pill, “kutulutsidwa kwa dzira kwachibadwa kumachitika mwa oposa 40% a ogwiritsira ntchito.” Chotero m’bulu umenewu mobwerezabwereza umalola kutulutsidwa kwa dzira. Madzi olimba a potulukira pa chibaliro angaletse kuloŵerera kwa ubwamuna ndipo mwakutero kusalola kukhala ndi pakati; ngati sitero, malo amkati ankhalwe omwe m’buluwo umapanga m’chibaliro amaletsa dzira laumoyo kuzikika ndi kukula kukhala mwana.

Chingayamikiridwe, kenaka, kuti itagwiritsidwa ntchito mokhazikika kaamba ka kuletsa kubala, mitundu yaikulu yonse iŵiri ya mibulu imawonekera kuletsa kukhala ndi pakati kuchitika mu nkhani zambiri ndipo chotero siziri kuchotsa mimba. Ngakhale kuli tero, popeza kuti progestin-only pill (m’bulu waung’ono) kaŵirikaŵiri umalola kutulutsidwa kwa dzira kowonjezereka, pali kuthekera kwakukulu kwakuti iko nthaŵi zina kumaletsa kubala mwa kusokoneza kuzikika m’chibaliro kwa moyo wopangidwa womwe wangoyambika. Maphunziro a sayansi amasonyeza kuti mwachibadwa (mimba yosayambukiridwa ndi mibulu yoletsa kubala) “mazira aumoyo maperesenti makumi asanu ndi imodzi . . . amawonongedwa kusamba kophonyedwa koyambirira kusanachitike.” Kunena kuti ichi chimachitika, ngakhale ndi tero, kuli kosiyana kwenikweni ndi kusankha kugwiritsira ntchito njira ya kuletsa kubala yomwe mwachiwonekere kwenikweni imaletsa kuzikika kwa dzira laumoyo.

Chotero, pali mbali zenizeni za makhalidwe zofunika kuzilingalira ngati aŵiri okwatirana akambitsirana ndi sing’anga nkhani yogwiritsira ntchito mibulu yoletsa kubala. Akristu ayenera kugamulapo ngakhale mafunso amseri ndi aumwini kotero kuti asungilire “chikumbumtima choyera” pamaso pa Mulungu wathu ndi Mpatsi wa Moyo.​—Machitidwe 23:1; Agalatiya 6:5.

[Mawu a M’munsi]

a Onani Nsanja ya Olonda ya August 1, 1977, masamba 478-80 m’Chingelezi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena