Nkuti Kumene Mumapita Kaamba ka Chitsogozo?
KODI winawake anayamba wakupatsani ndalama zonyenga? Mwinamwake ayi, koma ndimotani mmene mukachitira ngati winawake anakuwuzani kuti ndalama zabodza zinali kuzungulira? Kodi mungakwiye? Ndithudi ayi! Inu mwachidziŵikire kwenikweni mungakhale woyamikira kuti mwagalamutsidwa ndi kutenga chisamaliro kusapereka ndalama zanu zopezedwa movutikira, zowona kaamba ka zabodza.
Ambiri a ife timalandira chitsogozo kapena machenjezo ku nthaŵi ndi nthaŵi. Zowona, machenjezo ena ali ofunika kwenikweni kuposa ena. Koma ngakhale ngati sitiwona phindu laumwini la chitsogozo china kapena uphungu, kodi chimenecho chiri chifukwa chirichonse cha kukwiyira chifukwa chakuti chaperekedwa?
Chowonadi chiri chakuti, aliyense amafunikira thandizo ndi chitsogozo ku nthaŵi ndi nthaŵi. Palibe aliyense amene ali ndi mayankho onse. Pokhala ndi kusatsimikizika kwa zachuma ndi ndale kotizinga, aliyense amafunikira chiyembekezo cholimba kaamba ka mtsogolo. M’dziko limene chifupifupi theka la maukwati amathera m’kusudzulana, kumene kukhala ndi pakati kwa a zaka za pakati pa 13 ndi 19 kuli kokulira, ndi kumene matenda opatsirana mwa kugonana ali ofalikira, pali chifuno chofulumira kaamba ka chitsogozo chodekha, ndi chogwira ntchito. Makolo afunikira thandizo m’kugamulapo njira yabwino koposa ya kulerera ana awo m’dongosolo la kachitidwe ka zinthu losokonezeka iri. A zaka za pakati pa 13 ndi 19 amafunikira thandizo m’kusanthula malingaliro awo owombana ndi zididikizo zomwe zingawoneke kukhala zokhwethemula. Aliyense amafunikira thandizo m’kugwirira ntchito pa makhalidwe abwino othandiza m’dziko limene kusawona mtima, chisembwere, ndi chiwawa zikukhala zolandiridwa mowonjezerekawonjezereka.
Nkuti kumene thandizo loterolo lingapezeke? Magwero abwino koposa a chitsogozo cha kakhalidwe ali Baibulo, Mawu owuziridwa a Mulungu. Wamasalmo wakale analemba kuti: “Mawu anu ndiwo nyali ya kumapazi anga.” (Salmo 119:105) Awo omwe amaŵerenga ndi kugwiritsira ntchito Mawu a Mulungu amapeŵa misampha yambiri imene iripo lerolino. Chimenecho ndicho chifukwa chimodzi chimene Mboni za Yehova zimathera maora mazana a mamiliyoni chaka chirichonse kuchezera anansi awo ndi kukambitsirana nawo Baibulo. Komabe, anthu ambiri samvetsera, ndipo ena amakhoza ngakhale kukwiya. Nchifukwa ninji izi ziri tere?
Maganizo Otsekeka—Chifukwa Ninji?
Chabwino, anthu ambiri amakwiyitsidwa kwenikweni ponena za kulandira chitsogozo, makamaka pa nkhani ya chipembedzo. Ngakhale ziŵalo za tchalitchi nthaŵi zambiri sizimafuna kumvetsera ku uphungu umene alaliki awo amapereka. Mtsogoleri wa chipembedzo mmodzi wa ku Britain anachitira chisoni kuti: “Aliyense ali ndi malingaliro akeake ndipo amalingaliridwa kukhala abwino mofanana ndi a mlalikiyo.” Chotero, nchosadabwitsa kuti anthu samafuna kumvetsera kwa mlendo pakhomo pawo.
M’kuwonjezerapo, ngakhale kuti tikukhala mu mbadwo wokaikira, ambiri adakali ndi kugwirizana kolimba, kwa maganizo ku tchalitchi chawo. Monga mmene bukhu la nazonse lina linadziŵitsira kuti, “chipembedzo chimakhudza malingaliro ozama kwambiri a anthu osaŵerengeka.” Anthu oterowo sangawone kufunika kwa kulankhula kwa winawake wa chipembedzo china ponena za Baibulo, ngakhale pamene kukambitsiranako kukuchita ndi kupeza mayankho ku mavuto awo.
Ena samafuna kukambitsirana Baibulo chifukwa chakuti awona chinyengo chochulukira ndi kuipitsidwa m’chipembedzo. Iwo amakwiyitsidwa kuti atsogoleri ena a chipembedzo amalekerera chisembwere, kapena iwo anyansidwa ndi umbombo wopanda nawo manyazi wa ambiri a alengezi a pa wailesi ya kanema. Mwinamwake amakhumudwitsidwa pamene mtsogoleri wachipembedzo agwiritsira ntchito ulamuliro wake kuchirikiza mbali imodzi molimbana ndi ina mu nkhondo ya ndale zadziko. Kwa iwo, chipembedzo chimawoneka kukhala chopangitsa mavuto ambiri kuposa mmene chimathetsera iwo.
Mavuto amene oterowo amadandaula nawo ali enieni. Kulankhula mwachipembedzo, pali “ndalama zonyenga” zambiri zomwe zikuzungulira. Koma ndithudi, kukana kulandira thandizo laphindu kuchokera m’Baibulo kaamba ka chifukwa chimenechi kuli kopanda nzeru mofanana ndi kukana kulandira ndalama zenizeni chifukwa chakuti ndalama za ku banki zonyenga zikuzungulira!
Ndipo monga momwe zatchulidwira kale, tonsefe timafunikira uphungu m’dziko iri la zosankha zovuta ndi mikhalidwe yowopsya. Kodi pali njira ina iriyonse ya kukhalira wolangizidwa mwanzeru m’nkhani ya kulandira chitsogozo? Kodi chiri chosayenerera kapena ngakhale cholakwika kulankhula kwa winawake wa chipembedzo chosiyana ponena za Baibulo? Kodi nchotheka kukhala wotseguka maganizo mokwanira kulandira uphungu wabwino ndipo komabe kusanyengedwa ndi chitsogozo chonyenga? Nchiyani chimene Baibulo limanena ponena za ichi?