Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w89 12/1 tsamba 3
  • Kodi Ubwino wa Mulungu Umakukokani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ubwino wa Mulungu Umakukokani?
  • Nsanja ya Olonda—1989
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mikhalidwe Yaikulu ya Mulungu
  • Mbali Yodabwitsa ya Ubwino wa Mulungu
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Ubwino Waukulu wa Yehova
    Nsanja ya Olonda—1991
  • “Ubwino Wake Ndi Waukulu Kwambiri!”
    Yandikirani Yehova
  • Yehova Ndiye Chitsanzo Chachikulu Pankhani Yosonyeza Ubwino
    Nsanja ya Olonda—2002
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1989
w89 12/1 tsamba 3

Kodi Ubwino wa Mulungu Umakukokani?

KODI muli ndi bwenzi la pamtima? Ngati nditero, kodi munalingalirapo za chimene chinakukokerani kwa munthuyo? Kodi chinali mawonekedwe ake? Kodi chinali chifukwa chakuti munali okondweretsedwa m’zinthu zofanana? Kapena kodi inali mikhalidwe yakuya, yonga ngati kukoma mtima kapena nzeru? Ngati mkhalidwe umene unalimbitsa ubwenzi wanu unali ubwino, pamenepo mulidi ndi unansi wolemera. Ubwino weniweni sumapezeka kaŵirikaŵiri lerolino pamene, kwakukulukulu, anthu ali “osakonda abwino.”​—2 Timoteo 3:3.

Kwa Mkristu, unansi wofunika koposa m’moyo suli wa munthu mnzake koma wa Mulungu. Chotero pamene muganiza za unansi umenewu, kodi munalingalirapo kuti: ‘Kodi ndi uti wa mikhalidwe ya Mulungu umene umandikokeradi kwa Mulungu?’

Mikhalidwe Yaikulu ya Mulungu

Kwenikwenidi, Baibulo limalongosola mikhalidwe yaikulu yambiri ya Mulungu. Inayi yogogomezeredwa kaŵirikaŵiri ndiyo chikondi chake, chilungamo chake, nzeru zake, ndi mphamvu yake yosayerekezeka. (Deuteronomo 32:4; Yobu 12:13; Salmo 147:5; 1 Yohane 4:8) Ngati tinati tisankhe pakati pa mikhalidwe inayi yaikulu imeneyi, mwinamwake tinganene kuti chikondi cha Mulungu ndicho chinatikoka koposa. Komabe, chogwirizana kwenikweni ndi chikondi chake ndiwo ubwino wake wopambana. Alembi a Baibulo analemba momvekera bwino ponena za chimenechi, ndipo ubwino woterowo ungakokere anthu mu unansi wabwino, wosangalatsa ndi Mlengi wawo.

Mwachitsanzo, cha kumapeto kwa zaka za zana lachisanu ndi chimodzi B.C.E., mneneri Zekariya anafuula za Yehova kuti: “Pakuti ukoma wake ndi waukulu ndithu, ndi kukongola kwake nkwakukulu ndithu!” (Zekariya 9:17) Zaka zambiri Zekariya asadakhale, Yesaya anatamanda Mulungu mofananamo pamene analemba kuti: “Ndidzatchula za chifundo chake cha Yehova, . . . ndi ubwino wake waukulu kwa banja la Israyeli, umene iye wapereka kwa iwo.”​—Yesaya 63:7.

Zaka mazana atatu pasadakhale, Mfumu Davide adalemba mogwiradi mtima ponena za ubwino wa Mulungu. Davide analemba kuchokera ku zokumana nazo, pokhala atasangalala ndi ubwino umenewo kwa moyo wake wonse. Mulungu anali wabwino koposa kwa Davide, makamaka pambuyo pa machimo ake owopsya omwe anachita ndi Bateseba ndi mwamuna wake Uriya, pamene Mulungu anamchitira chifundo. (2 Samueli 12:9, 13) Pa Salmo 31:19, Davide analengeza moyamikira kuti: “Ha! kukoma kwanu ndiko kwakukulu nanga, kumene munasungira iwo akuopa inu!”

Kodi mumatenga ubwino wa Mulungu kukhala wamtengo kwenikweni mongadi mmene alambiri akale amenewo anachitira? Ngati ndi tero, mudzakhala ndi “mtendere [weniweni] wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse,” ndi kukhalanso wosonkhezeredwa mozama kuchita chifuniro cha Mulungu nthaŵi zonse. (Afilipi 4:7) Tsopano tiyeni tilingalire kwa mphindi zoŵerengeka zimene ubwino wa Mulungu umaphatikizapo ndi kuzizwitsa kwa ukulu wake. Mosakaikira zimenezi zidzazamitsa chiyamikiro chathu kwa Atate wathu wakumwamba wachikondi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena