Ndinakwera Phiri Labwino Koposa Kuposa Onse
NDINABADWA ndi kuleredwera m’tauni yaing’ono yokhala m’mapiri a Kum’mawa kwa Europe. Makolo anga anali Aroma Katolika, koma sankanditenga ku tchalitchi, ndipo panyumba sitinapemphere pamodzi kapena kulankhula za chipembedzo. Chotero, mofanana ndi achichepere ena ambiri, ndinathera nthaŵi ndi nyonga yanga m’maseŵera, maphunziro, ndi kuyenda.
M’tauni yathu, munali gulu lokangalika kwambiri la okwera mapiri lotsogozedwa ndi mwamuna wokoma mtima wozoloŵera, yemwe anadziŵa zambiri ponena za mapiri. Ndimamuyamikira, popeza ndinakhala katswiri weniweni wokwera mapiri. Ndinali ndi zaka 18 zakubadwa nthaŵiyo, ndipo mwamsanga ndinakondadi mawonekedwe okoma kuchokera pamwamba pa nsonga za mapiri, chisangalalo cha kuyang’anizana ndi kupulumuka mikhalidwe yangozi, ndi ubwenzi ndi ena okhala ndi phande m’ngozi zoterozo.
Ndimakumbukira nthaŵi ina nditakhala m’gululo kwa zaka zisanu. Ndinkakwera phiri losatsetsereka kwambiri, ndipo ndinaleka kupereka chisamaliro pa nthaŵi yomwe ndinkafikira nsonga yake. Pamene ndinayandikira pamwamba pa thanthwe lalikulu, ilo linayamba kugwedera. Zomwe ndinangoyenera kuchita ndizo kulumphira pambali ndi kufuula chenjezo kwa wokwera mnzangayo. Thanthwe lomagwalo linadula chingwe chimene chinatimanga pamodzi, ndipo ndinagwa. Mwamwaŵi, ndinagwera pa kamtunda kaudzu wambiri pa utali wa mamita anayi okha pansi. Komabe, zinthu nthaŵi zonse sizimakhala bwino tero m’maseŵera ameneŵa!
Pa msinkhu wa zaka 24 zakubadwa, ndinamaliza maphunziro a pa yunivesite ndi kulingalira za utsogoleri wa kagulu kakang’ono ka okwera mapiri m’tauni yakwathu. Pambuyo pa nthaŵi yochepa, tinasonkhanitsa ndalama kugula basi yaing’ono kotero kuti ife limodzi ndi ziŵiya zathu tingafikire mapiri akutali kwambiri. Koma galimotoyo siinali mu mkhalidwe wabwino, ndipo ndinatha miyezi itatu, usana ndi usiku, ndikuikonza. Pamene inakhala bwino, tonsefe tinafunafuna ntchito zangozi za malipiro abwino, zonga ngati ntchito yomanga m’mwamba, ndipo mwanjirayi m’kupita kwa nthaŵi tinasonkhanitsa ndalama zokwanira kupanga ulendo wopita ku Iran. Kumeneko, mu 1974, tinakwera phiri la volcano la utali wa mamita 5,800 lotchedwa Damavand. Pamene kuli kwakuti kukwerako kunayamba mosavuta, poyandikira nsonga yake tinafunikira kupirira ndi chipale chofeŵa, kupereŵera kwa mpweya chifukwa cha malo okwezeka, ndi utsi wa paizoni wotuluka m’ziboo za phiri la volcano.
Pobwerera kunyumba m’basi yaing’onoyo, tinakonzekera kukwera Phiri la Ararati koma tinachotsapo makonzedwewo chifukwa cha m’kangano wa ndale zadziko. Mu 1975 tinakatsetsereka pa mapiri otchedwa Austrian Alps, ndipo pa nthaŵi imodzimodziyo, tinayambitsa mpikisano wojambula zithunzithunzi wa mitunduyonse umene tinatcha “Men and Mountains” (Anthu ndi Mapiri). Mpikisano umenewu umachitidwabe chaka chirichonse. Tonsefe tinalingalira kuti miyoyo yathu inali yokwanira ndi yokhutiritsa.
Kugwiritsidwa Mwala
Komabe, pamene ndinafika zaka 30, ndinayamba kugwetsedwa ulesi ndi kukwera mapiri ndipo ndinalingalira kuti: ‘Kodi izi ndizo zokha zimene ziriko ku moyo?’ Ena anandiwuza kuti ndikwatire, koma ndinali ndi anzanga okwatira, ndipo sanawoneke kukhala achimwemwe kwenikweni. Ngakhale okwatirana amene unansi wawo unazama m’ngozi ndi chisangalalo cha kukwera mapiri anawoneka kukhala akutaikiridwa chimwemwe chawo cha moyo weniweni wa tsiku ndi tsiku. Sindinadziŵe chifukwa chimene maukwati awo sanaliri achimwemwe, koma zoposapo zomwe ndinafuna pamene ndinakhumba kukhala wokwatira inemwini, sindinafune kukhala wopanda chimwemwe mofanana nawo.
Kuwonjezerapo, ndinawona kusintha mwa achichepere omwe ankapita kukwera mapiri. Poyambapo, nthaŵi zonse panali mzimu wa kulangidwa, chigwirizano, ndi ubwenzi m’misasa ya kukwera mapiri a Alpine. Tsopano, anyamata achichepere ndi osazoloŵera anali osalangizidwa ndipo sanali okhutiritsidwa kupanga kupita patsogolo mwa pang’onopang’ono. Iwo anangofuna kuwonekera mwa kukwera malo ovuta kwenikweni ndi angozi kwa iwo. Pomadzimva wogwiritsidwa mwala mowonjezerekawonjezereka, ndinakambitsirana ndi Bonjo, bwenzi langa kwa nthaŵi yaitali ndipo mozama. Iye pomalizira analingalira kuti ndilankhule ndi wokwera mapiri mnzathu, Henry.
Henry anandibwereka bukhu, Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya, ndipo poliŵerenga ilo, ndinadabwa kuwona mmene linafotokozera mafunso amene ndinalingalirapo mu mtima mwanga. Kungodziŵa pambuyo pake kuti Henry anali kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, chotero ndinampempha ngati ndingagwirizane nawo. Iye anavomereza, ndipo kwa zaka ziŵiri ndinadziloŵetsa m’kuphunzira Baibulo kwakuya ndi mabukhu Abaibulo alionse omwe ndinapeza.
Phunziro la Baibulo
Pamene chidziŵitso changa chinkazama, chisangalalo chinawonjezereka. Ndinali woyanjana ndi chipembedzo cha Roma Katolika kokha mwachiphamaso, koma ndinadabwa kuwona kuti Chikristu cha Baibulo sichinadalire pa mapwando, miyambo, ndi malingaliro opanda mutu. M’malomwake, icho chinaloŵetsamo malamulo a makhalidwe abwino apamwamba amene anakhudza mbali iriyonse ya moyo wa Mkristu. Kuwonjezerapo, ndinadabwitsidwa kuwona kuti Baibulo likupanga nzeru kwenikweni ndipo silimatsutsa nthanthi za sayansi zotsimikizidwa mowonadi.
Mboni yotsogoza kukambitsiranako pakati pa Henry ndi ine sinatikakamize kusintha malingaliro athu ndi njira yathu ya moyo. Zomwe anangochita zinali kulongosola momvekera chimene Baibulo limanena. Chotero, ndinapitirizabe kukwera mapiri kwa zaka ziŵiri zoyambirirazo za kuphunzira. Koma pamene chidziŵitso changa chinazama, ndinadzazindikira kuti kwa ine kukwera mapiri kunali ngati kumwerekera. Chochitika chija cha thanthwe lomagwa chinandikumbutsanso za mawu a Yesu kwa Satana pamene Satana anamtokosa iye kuti adzigwetse kuchokera pamwamba pa kachisi akumati: “Usamuyese [Yehova, NW] Mulungu wako.” (Mateyu 4:5-7) Ndinazindikira kuti zochita zimenezi sizinasonyeze ulemu kaamba ka moyo umene Yehova anandipatsa.
Chotero ndinapatsa thayo la uyang’aniro wa gulu lathu la okwera mapiri kwa wokwera mapiri wina wozoloŵera ndi kupeza kuti sikunali kovuta kudutsa kuchokera ku kukwera mapiri kupita ku Chikristu. Pamene ndinapatsa kapena kugulitsa ziŵiya zanga zonse—zotsetserekera, zitsulo zokwerera, misomali yokoloŵekera, nyundo, misomali yokoledwa, ndi nkhwangwa yodulira madzi owundana—ndinganene mowona mtima, m’mawu a mtumwi Paulo kuti kwa ine zinali kokha “zapadzala.” (Afilipi 3:8) Malingaliro a kukhutiritsidwa kozama anabwera mwa ine pamene ndinakhala wokhoza kudziloŵetsa m’ntchito yaikulu ya kutamanda dzina la Mulungu poyera. Mu 1977 aŵirife Henry ndi ine tinazindikiritsa kudzipereka kwathu kwa Yehova mu ubatizo wa m’madzi.
Kuchitira Umboni kwa Ena
Pa nthaŵi imeneyo, panali chifupifupi ziŵalo 15 za gulu lokwera mapiri m’tauni yathu, ndipo mwapang’onopang’ono Henry ndi ine tinachitira umboni kwa onsewo. Chinali chisangalalo chotani nanga pamene mbale wanga, yemwe analinso chiŵalo, limodzi ndi mkazi wake, anayamba kuphunzira Baibulo ndipo anabatizidwa mu 1981. Nthaŵi ina pambuyo pake, Bonjo anagwirizana nafe, limodzinso ndi winawake, wachisanu mu kalabu la okwera mapiri. Ife sitinafunikirenso kukwera mapiri aatali. Chisangalalo chathu chachikulu koposa chinali kuchezera anthu m’chigwacho amene anayamikira chowonadi cha Baibulo. Kusintha kumeneku kunalandiridwanso mwachitonthozo ndi amayi wanga, omwe anali odera nkhaŵa kwenikweni za zochitika zokwera m’mwamba za mbale wanga ndi ine. M’kupita kwa nthaŵi, nawonso anagwirizana nafe m’kulambiridwa koyenera kwa Yehova.
Tsopano chikhumbo chokwatira chinaleka kundifulumiza. Ndiyamikira Mawu a Mulungu, popeza ndinadziŵa malamulo a makhalidwe abwino amene akandithandiza kupanga chipambano cha ukwati, koma tsopano ndinali wachimwemwe pokhala mbeta ndikumatumikira Yehova popanda chocheutsa. Solomo analengeza kuti: “Mkazi wanzeru achokera kwa Yehova.” (Miyambo 18:22; 19:14) Chotero, ndinasankhapo kuyembekeza moleza mtima kwa Yehova kundipatsa mphatso imeneyi, panthaŵiyo ndinkakhala m’njira yakuti ndikakhale mwamuna waphindu pamene chikachitika. Munali mu 1982 pamene Yehova anandipatsa dalitso lalikulu la mkazi wabwino.
Mkazi wanga ndi ine tikukhalabe m’mapiri, ndipo ndidakawakondabe. Koma nkhaŵa yathu yaikulu tsopano iri kuthandiza anthu kukwera phiri lina. Kodi ilo ndi phiri liti? Lotchulidwa mu ulosi wa Yesaya kuti: “Ndipo padzakhala masiku otsiriza, kuti phiri la nyumba ya Yehova lidzakhazikika pa nsonga ya mapiri, ndipo lidzakwezedwa pamwamba pa zitunda; mitundu yonse idzasonkhana kumeneko. Ndipo anthu ambiri adzanka, nati, tiyeni tikwere kunka ku phiri la Yehova, ku nyumba ya Mulungu wa Yakobo; Ndipo iye adzatiphunzitsa za njira zake, ndipo tidzayenda m’mayendedwe ake; chifukwa m’Ziyoni mudzatuluka chilamulo, ndi mawu a Yehova kuchokera m’Yerusalemu.” (Yesaya 2:2, 3) Nchisangalalo chotani nanga kukhala wokhoza kukwera phiri limeneli, labwino koposa kuposa onse!—Yoperekedwa.