Yehova Wandipatsa Nyonga
MONGA MOMWE YASIMBIDWIRA NDI EKUMBA OKOKA
NDINABADWIRA m’banja “Lachikristu” m’dziko Lapakati pa Afirika, ndipo ndinakula wokonda Mulungu. Bambo wanga adali mlaliki wamba wachangu, ndipo kaŵirikaŵiri ndinkapita nawo pamene ankaphunzitsa m’tchalitchi kapena nthaŵi zopemphera m’nyumba za anthu. Popeza kuti ndinawoneka kukhala mnyamata wopembedza, alaliki wamba ena anandisankha kumatumikira ndi wansembe pa Misa. Iwo anandiuza kuti tsiku lina ndidzaphunzira kukhala wansembe inemwini.
Komabe, usiku ndinali woimba ndi wovina wotsogolera m’gulu la oimba lakomweko, lotchedwa Matumba-Ngomo. Paudindo umenewo, ndinaphatikana ndi amuna ndi akazi achichepere a m’boma lathu m’mitundu yonse ya chisembwere. Komabe ndinkayembekezera kukhala ndi mkazi mmodzi yekha ndipo potsirizira pake kupita kumwamba kukakhala ndi “oyera mtima.” Sindinawone chifukwa choyeretsera moyo wanga chifukwa chakuti, mogwirizana ndi chiphunzitso cha Katolika, machimo anga onse anakhululukidwa madzulo a Loŵeruka lirilonse pambuyo powaulula.
Mavuto Ayambika
Mu 1969, pamene ndinkaphunzira pakoleji, ndinayamba kumva kupweteka m’mfundo za mafupa anga. Sindinadziŵe chochititsa, koma pamiyezi imene inatsatirapo, zinaipirapo. Makolo anga, mosasamala kanthu zakukhala Akatolika otchuka, anasankha kundipereka kwa amatsenga osiyanasiyana, amene ananena kuti winawake anandilodza, koma chifukwa cha mapemphero awo ndi mankhwala, ndikachira. Komabe, ndinayamba kutsimphina, ndipo pofika 1970, sindinkatha kuyenda nkomwe, ngakhale nditayedzamira pandodo. Panthaŵiyo, ndinalingalira kuti masiku anga a kuyenda adzaiwalidwa posachedwapa.
Mu February 1972 bambo wanga analingalira zondipereka kuchipatala ku Wembo Nyama. Ndinakhala m’chipatalamo kwa nthaŵi yaitali kwabasi kwakuti anayamba kunditcha mwini wake! Anthu ankabwera kuchipatalako, kuchira, kutulutsidwa, kenaka nkubweranso ndi matenda ena, ndipo ine ndinali ndidakali kumeneko! Bambo wanga anafunikira kubwerera kumudzi kukadula mpunga, koma panthaŵiyi nkuti ndiri wokwatira, ndi ana aŵiri, ndipo mkazi wanga wokondedwa, ngakhale kuti anali ndi zaka 21 zokha, anandisamalira napeza ntchito kotero kuti adzisamalira zosoŵa zathu.
Komabe, ndinali wopsinjika ndi mkhalidwe wonsewo. Pamsinkhu wa zaka 24, ndinkadwalirirabe, pamene mabwenzi anga ankachita bwino, ambiri a iwo tsopano anali ndi ntchito zokhazikika. Chinawoneka kwa ine kuti chingakhale bwino kwa onse nditadzipha. Chotero, ndinagaŵira ana anga ndi abale anga zonse zimene ndinali nazo, osawauza zimene ndinkaganiza. Ndinatsala ndi malaya apamtima panga okha omwe ndinafuna kuikidwa nawo.
Kuyambika kwa Moyo Watsopano
Kenaka mmodzi wa Mboni za Yehova anapatsidwa kama woyandikana ndi wanga. Ngakhale kuti diso limodzi linali lakhungu ndipo linalo linali pafupi kuleka kuwona, iye mwamsanga anayamba kuchitira umboni kwa ine kuchokera m’Baibulo ponena za Yehova ndi Ufumuwo. Pambuyo pa masiku ochepa, iye anachoka m’chipatalamo, koma anandisiya m’chisamaliro cha Mboni zomwe zinabwera kudzamchezera. Pambuyo pa kukambitsirana kungapo, awanso anafunikira kuchoka, koma mmodzi wa iwo anapitiriza kuphunzira nane mwakulemberana makalata. Iye anandipatsanso mabuku ophunzirira Baibulo osiyanasiyana, amene ndinawaŵerenga mosangalala.
Mwanjirayi ndinalandira chakudya chauzimu, ndipo kupsinjika kwanga mwapang’onopang’ono kunasintha kukhala chimwemwe. Zinawoneka ngati kuti tchalitchi changa chinkandimwetsa “asidi,” koma tsopano ndinkalandira kwaulere madzi amoyo. Ndinayamika Yehova mumtima mwanga chifukwa chondimasula kuzikhulupiriro zamalaulo, monga ngati Utatu, kusakhoza kufa kwa moyo, kuopa akufa, ndikulambira makolo.
Panthaŵiyi ndinafuna kutuluka m’chipatalamo. Komano ndinamva kuti mabanja aŵiri a aminisitala anthaŵi zonse akagaŵiridwa kubwera ku Wembo Nyama, choncho ndinasankhapo kukhalabe kufikira atafika. Ndinasangalala chotani nanga pamene pomalizira pake anabwera nandipeza pakama wanga wa m’chipatala! Tsopano ndinali wokhoza kupitiriza phunziro langa la Baibulo ndi munthu weniweni mmalo mwakulemba makalata.
Patapita masiku oŵerengeka, ndinawafunsa ngati amachitira misonkhano m’Nyumba Yaufumu, monga mmene ndinaŵerengera m’magazini. Mwachifundo anandiuza kuti amachitira misonkhano yawo m’nyumba yaing’ono ya mmodzi wa iwo. Iwo ananenanso kuti adzakhala osangalala kunditengera kumeneko panjinga! Mosasamala kanthu za kupweteka kwakukulu kumsana ndi m’mfundo zonse za mafupa anga, mosangalala ndinapezekapo pa misonkhano yonse. Pamene ndinafikitsa ziyeneretso, ndinakhozadi kupereka lipoti mwezi uliwonse monga wofalitsa wosabatizidwa, kuyambira mu April 1974.
Miyezi itatu pambuyo pake, ndinachitira chinthuzi kudzipereka kwanga kwa Yehova mwakumizidwa m’madzi. Ndinachitira umboni kwa ogwira ntchito pachipatalapo, odwala, ndi amishonale Achiprotestanti omwe anabwera kudzacheza, ndi ziŵalo za banja langa—mosasamala kanthu za chitsutso chotsimikiza mtima cha banjalo. Panthaŵiyi, ndinkachitira umboni ndiri gone pakama kapena ndikuyenda pampando wamagudumu umene chipatalacho chinandibwereka podikirira kuti ndidzagule wanga.
Chipiriro Chinabweretsa Mapindu
Mosasamala kanthu za chitsutso cha banja langa, ndinapitirizabe kuyenda m’njira ya Yehova ndipo ndinadalitsidwa molemera. Mkazi wanga anachirimika m’chowonadi ndipo anabatizidwa mu 1975. Tinalingalira zokakhala ku Katako-Kombe, kumene kudali mpingo wokhazikitsidwa kale. Makolo anga ankadera nkhaŵa za ife chifukwa chakuti winawake adawauza kuti Mboni zonse zikaphedwa mu 1975. Pamene tinakana kuleka mayanjano athu, iwo analeka kutitumizira chakudya, ndipo tinaloŵa m’vuto lalikulu la kusoŵa zinthu zakuthupi. Ndimakumbukira kuti mwana wanga wamwamuna wam’ng’ono anakomoka ndi njala pambuyo pakukhala osadya kwa tsiku limodzi ndi theka. Komano abale athu Achikristu anatibweretsera nsomba ndi ufa. Pambuyo pake, makolo anga anayamba kutithandizanso, koma abale athu sanaleke konse kutithandiza mwakuthupi.
Mu February 1975 mkono wanga wakulamanja unachita manjenje ndipo unayamba kupuwala. Koma ndinasungabe chikhulupiriro ndipo ndinatsimikiza mtima kupitiriza kutumikira Yehova mosangalala. Ndine wachimwemwe kunena kuti mkono wangawo pambuyo pake unakhalanso wamphamvu, ndipo lerolino ndingathebe kuugwiritsira ntchito, ndiwo umanditheketsa kutsegula Baibulo langa ndikugwiritsira ntchito mabuku a Sosaite.
Kulimba Mtima Pamaso pa Olamulira
Mu 1977 bwanamkubwa wakumaloko anandipatsa mlandu pamaso pa bungwe lachigawo, lomwe linangogwira kumene mpainiya wapadera mumpingo wapafupipo. Tsiku lina msilikali anabwera kwa ine ndi zisamani. Ndinapemphera limodzi ndi banja langa, kulimbikitsa mpingo, ndipo kenaka ndinanka naye. Ndiyamikira mzimu wa Yehova, kuti ndinali wokhoza kupereka yankho lolimba mtima ku zinenezozo, ndipo pambuyo pa kukambitsirana kwakutali ndi akuluakulu a boma ndi ankhondo, ndinamasulidwa limodzi ndi mpainiya wapaderayo.
Miyezi ingapo pambuyo pake, ndinaitamidwa ndi bwanamkubwa wina, ndipo kachiŵirinso, ndi thandizo la Yehova, ndinali wokhoza kuchinjiriza mbiri yabwino mwachisangalalo ndi molimba mtima. Tinakambitsirana kwa nthaŵi yaitali ndi munthuyu, ndipo pamapeto pake, iye anandimasula ndipo iyemwini anandikankhira mpando wanga wamagudumu potuluka mu ofesi yake. Kenaka ananena mwakachetechete kuti: “Madzulo ano ubwere kunyumba kwanga.” Pambuyo pa maulendo angapo, ndinatha kuyamba phunziro Labaibulo ndi iye. Pomalizira pake, ndinali ndi maphunziro Abaibulo asanu ndi aŵiri ndi anthu osiyanasiyana olamulira. Ambiri a iwo anapezekapo pamisonkhano yampingo yolinganizidwa kumaloko.
Utumiki Wapadera
Ndinampempha Yehova kundithandiza, mosasamala kanthu za matenda anga, kukwaniritsa chiwindo changa cha kumtumikira ndi nyonga yanga yonse. Popanda kulembetsa mwalamulo, ndinayesa kukwaniritsa ziyeneretso za mpainiya wothandiza. Yehova anandithandiza kupambana, choncho ndinapereka chofunsirapo utumiki umenewu kaamba ka miyezi ya June mpaka October. Kenaka Sosaite inavomereza pempho langa lakukhala mpainiya wokhazikika, ndipo ndinayamba utumiki umenewu mu November 1976. Mu September 1977 chimwemwe changa chinakwanira pamene ndinalandira gawo monga mpainiya wapadera mu mpingo wa Katako-Kombe.
Kodi ndinakhoza bwanji kukwaniritsa chimenechi? Ndinakwaniritsa gawolo pampando wanga wamagudumu ndi thandizo la mkazi wanga wokondedwa ndi abale mumpingo. Nthaŵi zina ndinkapita ndekha ndindodo. Ndinagwa kamodzi kapena kaŵiri. Pamenepo ndinkadikirira, osasuntha, kufikira wodutsa atandithandiza kuima ndikundipatsira ndodo zangazo. Nthaŵi zonse ndinkakumbukira kutsimikiza mtima kwa atumwi ndi ophunzira a Yesu. (Machitidwe 14:21, 22; Ahebri 10:35-39) Nthaŵi iriyonse pamene ndinagwa, ndinapemphera kwa Yehova kuti asandilole kulefulidwa, koma mmalo mwake, andipatse nyonga yopitirizira kumtumikira. Nthaŵi zonse ndinakumbukira lonjezo losangalatsa lolembedwa mu ulosi wa Yesaya, lakuti “wopunduka adzatumpha ngati nswala.”—Yesaya 35:6.
Pamene ndinawonjezera utumiki wanga, ndipamenenso ndinakhoza kulaka kupunduka kwanga kwakuthupi mowonjezereka. Mu 1978 ndinali ndi mwaŵi wakupezeka pa Sukulu ya Utumiki Waufumu ku Lubumbashi, imene inaloŵetsamo kuyenda mtunda wa makilomita 2,000 pagalimoto, bwato, ndi sitima. Zowonadi, paulendo umenewu Yehova anandiwonjezeradi mphamvu. (Yesaya 12:2; 40:29) Tsopano ndingathe kuyenda—movutikira kwenikweni—mtunda wa mamita 100 popanda thandizo la ndodo zoyendera. Ndine wokhutira kuti Yehova anamva pemphero langa kalelo mu 1973 lakundipatsa nyonga yakumtumikira motsimikiza mtima.
Gawo Latsopano
Mu 1984, pambuyo pa zaka zisanu ndi ziŵiri mu mpingo ku Katako-Kombe, ndinalandira gawo latsopano kugwira ntchito ndi mpingo wa Lodja-Centre. Chaka chimodzi pambuyo pake tinayambitsa gulu la phunziro labukhu latsopano pa mtunda wa makilomita 12, ndipo posakhalitsanso tinayambitsa lina pamtunda wa makilomita 30 kuchokera pa linalo. Gulu lomalizirali linayamikiridwa mwamsanga monga gulu lakutali ndipo mu 1988 linavomerezedwa monga mpingo, kumene tsopano ndikutumikira monga mkulu.
Upainiya wakhala wothandiza kwa ine, ponse paŵiri kuuzimu ndi kuthupi. Pamene ndinatulukira mu utumiki ndi ndodo zanga zoyendera, ndinakhoza kuchita zolimbitsa thupi zimene adokotala anandilangiza. Ndine wamphamvu kwambiri tsopano kuposa pamene ndinayamba kuchita upainiya, ndipo chikhumbo changa ndicho kupirira m’ntchitoyi kufikira mapeto. Ndikulakalaka kudzawona mmene Yehova adzandithandizira ‘kutumpha ngati nswala’ panthaŵi imene sindidzafunikiranso kupirira kupweteka kwa matendawa.
Ndimtima wanga wonse, ndikuyamika Atate wathu wakumwamba, amene wandipatsa nyonga, kulimba mtima, ndi utumiki wanthaŵi zonse. Tsopano ndiri ndi zaka 36 zakubadwa, ndipo pambuyo pa zaka 11 za ntchito yaupainiya, ndikuyembekeza kupitirizabe, mosasamala kanthu za zimene ziri kutsogolo. Ndine wotsimikiza mtima kugwiritsira ntchito nyonga zanga zonse m’kulemekeza ndikutamanda Mulungu wamkulu, Yehova.