Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w95 11/1 tsamba 22-25
  • ‘Wogwetsedwa, Koma Wosawonongeka’

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • ‘Wogwetsedwa, Koma Wosawonongeka’
  • Nsanja ya Olonda—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kubwevuka Kwakukulu
  • Banja Lachimwemwe
  • Kugonjetsa Kupuŵala Kwauzimu
  • Kulimbana ndi Kubwevuka Kwina
  • Kuchita Zimene Ndingathe
  • Yehova Wandipatsa Nyonga
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Kuyamikira Chichilikizo CHosalekeza cha Yehova
    Nsanja ya Olonda—1993
  • ‘Ndidzadumpha Ngati Nswala’
    Galamukani!—2006
  • Mavuto Anga Andithandiza Kulimbitsa Ubwenzi Wanga ndi Yehova
    Nsanja ya Olonda—2014
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1995
w95 11/1 tsamba 22-25

‘Wogwetsedwa, Koma Wosawonongeka’

YOSIMBIDWA NDI ULF HELGESSON

Mu July 1983, madokotala ataŵeramira pa ine anadzuma kuti: “Ha, ali moyo!” Chotupa chotalika masentimita 12 chinali chitachotsedwa kumsana kwanga pa opaleshoni yovuta ya maola 15. Ndinakhala wopuŵala kotheratu.

PATAPITA masiku angapo, ndinasamutsidwira ku chipatala china pamtunda wa makilomita pafupifupi 60 kuchokera kutauni ya kwathu ya Hälsingborg, kummwera kwa Sweden. Kumeneko ndinaloŵa programu yondiphunzitsa kuyenda. Mlangizi wa kumeneko anati ndinafunikira kulimba kwenikweni, komabe ndinali wofunitsitsa kuyamba. Ndinafunadi kuyendanso. Mwa kutsatira mwakhama zochitachita zolimbitsa thupi kwa maola asanu patsiku, ndinapita patsogolo mofulumira.

Pambuyo pa mwezi umodzi pamene woyang’anira woyendayenda anachezera mpingo wathu, iye ndi akulu ena Achikristu anayenda ulendo wautali kudzachitira msonkhano wa akulu wampingo m’chipinda changa cha m’chipatala. Ha, mtima wanga unasangalala chotani nanga poona chikondi chaubale chimenechi! Manesi mu wadi mmenemo anaperekera tiyi ndi buledi kwa gulu lonselo pambuyo pa msonkhanowo.

Poyamba madokotalawo anadabwa ndi kupita patsogolo kwanga. Pambuyo pa miyezi itatu ndinakhoza kukhala tsonga mu mpando wanga wamagudumu ndipo ngakhale kuimirira kwa mphindi zoŵerengeka. Ndinali wokondwera ndi wofunitsitsa kuyendanso. Banja langa ndi Akristu anzanga anandilimbikitsa kwambiri pamene ankandichezera. Ndipo ndinakhoza ngakhale kupita kunyumba panyengo zazifupi.

Kubwevuka Kwakukulu

Komabe, pambuyo pa zimenezo, sindinapitenso patsogolo. Posapita nthaŵi mlangizi ananditulira uthenga wopweteka mtima: “Sudzakhala bwino kuposa apa!” Cholinga tsopano chinali kundilimbikitsa kumayendayenda ndekha pa mpando wamagudumu. Ndinada nkhaŵa ndi zimene zidzandichitikira. Kuti mkazi wanga adzakhoza motani? Iyenso anachitidwapo opaleshoni yaikulu ndipo ndinali kumthandiza. Kodi ndidzafunikira kukakhaliratu kunyumba ya boma yosamalira ovutika?

Ndinapsinjika mtima kwambiri. Nyonga yanga, kulimbika mtima kwanga, ndi mphamvu zanga zonse zinaphwa. Masiku anapita, ndipo sindinathe kuyenda. Sindinapuŵale kuthupi kokha komanso ndinatha mphamvu mwamaganizo ndi mwauzimu. Ndinali ‘wogwetsedwa.’ Zimenezi zisanachitike, nthaŵi zonse ndinamva kukhala wolimba mwauzimu. Ndinali ndi chikhulupiriro cholimba chozikidwa pa Ufumu wa Mulungu. (Danieli 2:44; Mateyu 6:10) Ndinali wotsimikiza za lonjezo la Baibulo lakuti matenda onse ndi kupunduka zidzathetsedwa m’dziko latsopano lolungama la Mulungu ndi kuti anthu onse adzapezanso moyo wangwiro. (Yesaya 25:8; 33:24; 2 Petro 3:13) Tsopano ndinazizira m’mawondo kuthupi ndi kuuzimu komwe. Ndinamva kukhala ‘wowonongeka.’​—2 Akorinto 4:9.

Ndisanafike patali, lekani ndikusimbireni pang’ono za mbiri yanga.

Banja Lachimwemwe

Ndinabadwa mu 1934, ndipo thanzi langa linali labwino nthaŵi zonse. Kuchiyambi kwa ma 1950, ndinakumana ndi Ingrid, ndipo tinakwatirana mu 1958 ndi kukakhala mu tauni ya Östersund, m’chigawo chapakati cha Sweden. Nthaŵi yosinthirapo zinthu m’moyo wathu inafika mu 1963 pamene tinayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Panthaŵiyo tinali ndi ana atatu aang’ono​—Ewa, Björn, ndi Lena. Posapita nthaŵi banja lathu lonse linayamba kuphunzira ndi kupita patsogolo bwino lomwe m’choonadi cha Baibulo.

Posapita nthaŵi titayamba kuphunzira, tinasamukira ku Hälsingborg. Kumeneko, ine ndi mkazi wanga tinadzipatulira kwa Yehova ndi kubatizidwa mu 1964. Chimwemwe chathu chinawonjezeka pamene mwana wathu wamkulu wamkazi, Ewa, anabatizidwa mu 1968. Pambuyo pa zaka zisanu ndi ziŵiri, mu 1975, Björn ndi Lena anabatizidwa nawonso, ndipo chaka chotsatira ndinaikidwa kukhala mkulu mumpingo Wachikristu.

Ntchito yanga yakuthupi inandikhozetsa kusamalira banja langa mwakuthupi. Ndipo tinakhala achimwemwe kwambiri pamene Björn ndi Lena anayamba utumiki wanthaŵi yonse. Posapita nthaŵi Björn anaitanidwa kukatumikira pa ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova mu Arboga. Moyo unatiyanja ndithu, nditero kunena kwake. Ndiyeno mu 1980, ndinayamba kumva kupweteka kwa chotupa chimene potsirizira pake chinadzachotsedwa pa opaleshoni yaikuluyo mu 1983.

Kugonjetsa Kupuŵala Kwauzimu

Pamene ndinauzidwa kuti sindidzayendanso, ndinamva ngati kuti amenewo anali mapeto a moyo wanga. Kodi ndinaipezanso motani nyonga yauzimu? Zinali zosavuta kuposa mmene ndinaganizira. Ndinangotenga Baibulo langa ndi kuyamba kuliŵerenga. Pamene ndinaŵerenga kwambiri, mpamenenso ndinapeza nyonga yowonjezereka. Mpamene ndinamvetsetsa kwambiri Ulaliki wa pa Phiri wa Yesu. Ndinauŵerenga mobwerezabwereza ndi kuusinkhasinkha.

Ndinayambanso kukondwera ndi moyo. Mwa kuŵerenga ndi kusinkhasinkha, ndinayamba kuona mipata ya mwaŵi m’malo mwa zopinga. Ndinapezanso chikhumbo changa cha kugaŵana choonadi cha Baibulo ndi ena, ndipo ndinakhutiritsa chikhumbo chimenechi mwa kuchitira umboni kwa antchito a m’chipatala ndi ena omwe ndinakumana nawo. Banja langa linandichirikiza kwambiri ndipo anaphunzira mmene angandisamalirire. Potsirizira pake ndinatuluka m’chipatala.

Tsopano ndinali kunyumba. Linali tsiku losangalatsa chotani nanga kwa ife! Banja langa linalinganiza ndandanda imene inaphatikizapo kundisamalira. Mwana wanga wamwamuna, Björn, analeka ntchito pa ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova, ndipo anabwera kudzathandiza kundisamalira. Kunali konditonthoza kwambiri kuona chikondi chachikulu ndi chisamaliro zimene banja langa linandisonyeza.

Kulimbana ndi Kubwevuka Kwina

Komabe, m’kupita kwa nthaŵi, matenda anga anakulirakulira, ndipo kuyenda kunali kondivuta. Potsirizira pake, mosasamala kanthu za khama la banja langa, iwo sanathenso kundisamalira panyumba. Choncho ndinaona kuti ndi bwino kukakhala kunyumba ya boma yosamalira ovutika. Zimenezi zinafunanso masinthidwe ndi kachitidwe ka zinthu katsopano. Koma sindinalole zimenezi kundibwevutsa mwauzimu.

Sindinaleke kuŵerenga Baibulo ndi kufufuza. Ndinapitiriza kulingalira pa zimene ndingachite, osati zimene sindingachite. Ndinasinkhasinkha pa madalitso auzimu onse amene Mboni za Yehova zili nawo. Ndinakhala pafupi ndi Yehova mwa pemphero ndipo ndinagwiritsira ntchito mpata uliwonse kulalikira kwa ena.

Tsopano ndimakhala kunyumba yosamalira ovutika usiku wonse ndi mmaŵa. Masana ndi madzulo ndimakhala kunyumba kapena kumisonkhano yathu Yachikristu. A boma amapereka galimoto nthaŵi zonse yondipereka ndi kukanditenga kumisonkhano ndi kunyumba kwanga. Banja langa lodziperekalo, abale a mumpingo, ndi antchito a panyumba yosamalira ovutika amandisamalira bwino kwambiri.

Kuchita Zimene Ndingathe

Sindimadziona kukhala wotha ntchito, ndipo banja langa silimandiyesa wotero, ngakhalenso abale anga Achikristu. Amandisamalira mwachikondi, akumandikhozetsa kutumikira bwino lomwe monga mkulu. Ndimachititsa Phunziro Labuku Lampingo mlungu ndi mlungu, limodzinso ndi phunziro la Nsanja ya Olonda la mlungu ndi mlungu pa Nyumba ya Ufumu. Kusanthula masamba a Baibulo kumandivuta, choncho munthu wina amapemphedwa kundichitira zimenezo pamisonkhono. Ndimachititsa misonkhano ndi kupereka nkhani zapoyera ndili pa mpando wanga wamagudumu.

Motero ndikhozabe kuchita zinthu zambiri zimene ndinakonda kwambiri kuchita kale, kuphatikizapo kupanga maulendo akuŵeta. (1 Petro 5:2) Ndimachita zimenezi pamene abale ndi alongo afika kwa ine kudzapempha chithandizo kapena uphungu. Ndimagwiritsiranso ntchito telefoni, ndikumaimbira foni ena. Chotulukapo nchakuti tonse timalimbikitsidwa. (Aroma 1:11, 12) Posachedwapa bwenzi lina linati: “Pamene ndingoyamba kupsinjika mtima, umandiimbira telefoni ndi kundilimbikitsa.” Koma inenso ndimalimbikitsidwa, podziŵa kuti Yehova akudalitsa zoyesayesa zanga.

Misonkhano isanayambe ndi pambuyo pake, ndimakhala ndi mayanjano abwino ndi ana mumpingo. Pokhala kuti ndimakhala mu mpando wanga wamagudumu, timakambitsirana bwino chifukwa timalingana msinkhu. Ndimayamikira kwambiri kuona mtima kwawo ndi kulankhula mosabisa kanthu. Tsiku lina kamnyamata kena kanati kwa ine: “Ndinu wotha ntchito wabwino koposa!”

Mwa kusinkhasinkha zimene ndingachite m’malo mwa kudera nkhaŵa ndi zimene sinditha kuchita, ndakhala wosangalala ndi utumiki wa Yehova. Zimene zandichitikira zandiphunzitsa zambiri. Ndazindikira kuti mayesero amene timapyolamo amatiphunzitsa ndi kutilimbitsa.​—1 Petro 5:10.

Ndaona kuti anthu ambiri athanzi labwino amalephera kuzindikira kuti nkhani ya kulambira Atate wathu wakumwamba tiyenera kuitenga mwamphamvu. Ngati sititero, ndandanda yathu ya phunziro laumwini, misonkhano, ndi utumiki wakumunda zidzangokhala chizoloŵezi wamba. Ndimaona makonzedwe ameneŵa kukhala ofunika kwambiri ngati nditi ndikapulumuke mapeto a dzikoli ndi kuloŵa m’Paradaiso wa Mulungu wa pa dziko lapansi wolonjezedwayo.​—Salmo 37:9-11, 29; 1 Yohane 2:17.

Tiyenera nthaŵi zonse kukumbukira za chiyembekezo cha moyo m’dziko latsopano la Mulungu likudzalo. (1 Atesalonika 5:8) Ndaphunziranso kuti sindiyenera kuleka nkhondo yolimbana ndi chizoloŵezi chilichonse chofuna kundilefula. Ndaphunzira kuona Yehova monga Atate ndi gulu lake monga Amayi. Ndazindikira kuti ngati tiyesayesa, Yehova angagwiritsire ntchito aliyense wa ife kukhala mtumiki wake wachangu.

Ngakhale kuti nthaŵi zina ndadzimva monga “[w]ogwetsedwa,” ‘sindinawonongeke.’ Yehova ndi gulu lake sanandisiyepo, ngakhalenso banja langa ndi abale anga Achikristu. Chifukwa cha kutenga kwanga Baibulo ndi kuliŵerenga, ndinapezanso nyonga yauzimu. Ndikuyamikira Yehova Mulungu, amene amatipatsa “mphamvu yoposa yachibadwa” pamene tidalira iye.​—2 Akorinto 4:7, NW.

Pokhala ndi chidaliro chonse ndi kukhulupirira Yehova ndi mtima wonse, ndikuyang’ana kutsogolo mwachidwi. Ndili ndi chidaliro chakuti posachedwapa Yehova Mulungu adzakwaniritsa lonjezo lake la kubwezeretsa paradaiso pano pa dziko lapansi limodzi ndi madalitso onse odabwitsa amene adzakhalapo.​—Chivumbulutso 21:3, 4.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena