Kuwona Mtima Kuli Lamulo Labwino Koposa
KUWONA mtima kumayamikiridwa mokwezeka m’Baibulo ndipo kuli chiyeneretso kwa Akristu owona. (Mateyu 22:39; 2 Akorinto 8:21) Ndiponso, kuwona mtima kulidi lamulo labwino koposa, monga likusonyezedwa m’miyoyo ya ambiri lerolino amene maganizo ndi mitima yawo yasandulizidwa ndi chidziŵitso cholongosoka cha m’Baibulo. Chitsanzo cha zimenezi chikuchokera ku Liberia.
Pambuyo pa kulingalira kwakukulu kochitidwa mwapemphero, mkulu Wachikristu ndi mkazi wake anatseka shopu yawo yautelala. Nchifukwa ninji? Chifukwa chakuti iyo inadya nthaŵi yawo yopambanitsa ndi kubweza kumbuyo ntchito zawo zautumiki ndi phunziro laumwini. Iwo anavomerezana kukhala okhutiritsidwa ndi ndalama zachikatikati zopezedwa mwa kugulitsa dye ya nsalu. Komabe, mwamsanga pamene anatenga sitepe limeneli, mitengo ya dye inagwa pa msika wakumaloko. Tsopano ndalama zawo sizikakhoza kuchirikiza banja lawo. Kodi iwo akachita chiyani?
Iwo anapempha kampani yogulitsa dyeyo kutsitsa mitengo yawo, kotero kuti alole mlingo wabwino wa phindu. Ichi chinakanidwa. Komabe, kampaniyo inavomera kutumiza mainvoisi aŵiri, imodzi yosonyeza mtengo weniweni ndipo inayo mtengo wotsitsidwa umene akasonyeza ku Customs kotero kuti alipire msonkho wochepa. Zimenezi zikalola mkuluyo kusangalala ndi phindu losakhala lalamulo la $2,000 pa oda iriyonse.
Mbaleyo anakana kukhala mbali ya kachitidwe kosawona mtima ndi kamene kakabera boma. Akulu antchito apa kampaniyo anadabwa. Iwo analemba kuti: “Tikulemekeza chikumbumtima chako,” ndipo anaika mkuluyo kukhala wowagulitsira zopanga zawo yekha mu Liberia. Pokhala tsopano okhoza kusamalira mokwanira zosoŵa zakuthupi za banjalo, mkuluyo ndi mkazi wake akhala okhoza kuchita upainiya wothandizira, akugwirira limodzi ndi abale kulimbitsa mpingo. Zowonadi, kuwona mtima kwawo kunatsimikizira kukhala dalitso kwa iwo.
Alfonso, mu Spain, nayenso anapeza kuti kuwona mtima kuli lamulo labwino koposa. Mnyamata ameneyu anachoka panyumba ali ndi msinkhu wa zaka 12, ndipo pasanapite nthaŵi yaitali anayamba kugulitsa mankhwala ogodomalitsa, limodzinso ndi kuba m’magalimoto, m’nyumba, ndi m’mashopu. Nthaŵi zina ankaba m’masitolo ofika pa khumi tsiku limodzi. Pa msinkhu wa 21, anayi a mabwenzi ake adampanda mowopsya, kuba mankhwala ake ogodomalitsa onse, ndi kuwopsyeza kumupha ngati akanawanenera kwa apolisi. Popeza kuti anali wodziŵika bwino lomwe kwa apolisi, iye anachitadi mantha kupita ku chipatala kukalandira thandizo.
Pamene zironda zake zinkapola pang’onopang’ono, Alfonso analingalira mosamalitsa pa njira ya moyo wake. Anakumbukira zinthu ponena za Baibulo ndi malamulo amakhalidwe abwino Achikristu amene amake adamuwuza pamene adali mwana. Kenaka, iye ananyalanyaza mawu awo, koma tsopano anapempha phunziro la Baibulo ndi Mboni za Yehova. M’miyezi isanu ndi umodzi iye anasintha kotheratu mkhalidwe wake ndi umunthu ndipo anayeneretsedwa kaamba ka ubatizo.
Komabe, patsiku lotsatira ubatizo wake, analandira chisamoni kukawonekera m’khoti kaamba ka mlandu wakuba ali ndi mfuti. Unali upandu umene anachita panthaŵi inayake kale. Ngakhale kuli tero, Alfonso mwapoyera anavomereza kulakwa kwake ndipo anaponyedwa m’ndende moyembekezera kuzengedwa mlandu. Loya wake womuimira anamsonkhezera kukana kuti sanabe chirichonse ndi kuti sananyamule mfuti. Koma Alfonso anaumirira pa kunena zowonadi. Chifukwa cha mlandu wake ndi cholembedwa chake choipa kwa apolisi, wozenga mlanduyo analamula chilango cha zaka 13. Koma powona mkhalidwe wake wabwino ndi kuwona mtima kwake, anapatsidwa miyezi isanu ndi umodzi, imene anali atatumikira kale poyembekezera kuzengedwa mlandu.
Tsopano Alfonso ndi mkazi wake akutumikira Yehova mokhulupirika, ali achimwemwe pokhala atapeza chifuno chenicheni cha moyo ndi kutsimikizira mwa chokumana nacho cha iwo eni kuti kuwona mtima kuli lamulo labwino koposa.