Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w90 3/15 tsamba 10-14
  • ‘Kapolo Wokhulupirika’ ndi Bungwe Lake Lolamulira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • ‘Kapolo Wokhulupirika’ ndi Bungwe Lake Lolamulira
  • Nsanja ya Olonda​—1990
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Manijala wa Nyumba wa m’Zaka za Zana Loyamba
  • Bungwe Lolamulira la Nyumbayo
  • Nthaŵi Yoŵerengera Manijala wa Nyumba
  • “Kapolo” ndi Bungwe Lake Lolamulira Pamene Nthaŵi Yamapeto Ikuyandikira
  • Khalani Okhulupirika kwa Khristu ndi kwa Kapolo Wake
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Mdindo Wokhulupirika ndi Bungwe Lake Lolamulira
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Kugwirizana ndi Bungwe Lolamulira Lerolino
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Kodi “Kapolo Wokhulupirika Ndi Wanzeru” Ndi Ndani, Nanga Amachita Zotani?
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda​—1990
w90 3/15 tsamba 10-14

‘Kapolo Wokhulupirika’ ndi Bungwe Lake Lolamulira

Ndani kodi ali kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, amene mbuye wake anamkhazika woyang’anira banja lake, kuwapatsa zakudya pa nthaŵi yake?”​—Mateyu 24:45.

1. Kodi nchifukwa ninji Yehova ali wofunitsitsa kupatsa ena ulamuliro, ndipo kodi nkwandani poyambirira kumene wachita tero?

Yehova ali Mulungu wadongosolo. Alinso Magwero a ulamuliro woyenerera. Pokhala ndi chidaliro m’kukhulupirika kwa zolengedwa zake zokhulupirika, Yehova ngwofunitsitsa kupatsa ena ulamuliro. Amene iye wampatsa ulamuliro waukulu ali Mwana wake, Yesu Kristu. Ndithudi, Mulungu “anakonza zonse pansi pa mapazi ake, nampatsa Iye akhale mutu pamtu pa zonse, kwa Eklesia.”​—Aefeso 1:22, 23.

2. Kodi Paulo akutcha mpingo Wachikristu kukhala chiyani, ndipo kodi nkwandani kumene Kristu wapereka ulamuliro?

2 Mtumwi Paulo akutcha mpingo Wachikristu kukhala “nyumba ya Mulungu” ndipo akunena kuti Mwana wokhulupirika wa Yehova, Yesu Kristu, anaikidwa woyang’anira wa nyumba imeneyi. (1 Timoteo 3:15; Ahebri 3:6) Kristu nayenso amapereka ulamuliro kwa ziŵalo za nyumba ya Mulungu. Tingawone zimenezi kuchokera ku mawu a Yesu olembedwa pa Mateyu 24:45-47. Iye anati: “Ndani kodi ali kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, amene mbuye wake anamkhazika woyang’anira banja lake, kuwapatsa zakudya pa nthaŵi yake? Wodala kapolo amene mbuye wake, pakufika, adzampeza iye alikuchita chotero. Indetu, ndinena kwa inu, kuti adzamkhazika iye woyang’anira zinthu zake zonse.”

Manijala wa Nyumba wa m’Zaka za Zana Loyamba

3. Kodi ndani amene akupanga “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” ndipo kodi ndi liwu lotani limene limalozera kwa iwo aliyense payekha?

3 Kuchokera ku kuphunzira kwathu kosamalitsa kwa Malemba, tikudziŵa kuti ziŵalo zodzozedwa ndi mzimu za nyumba ya Mulungu pa nthaŵi iriyonse yopatsidwa onse pamodzi amapanga “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” “mdindo,” kapena “manijala wa nyumba.” Aliyense payekha, ziŵalo za nyumba ya Yehova zimatchedwa “banja” kapena “bungwe la akalinde.”​—Mateyu 24:45; Luka 12:42; Reference Bible, mawu am’munsi.

4. Mwamsanga imfa yake isanafike, kodi ndi funso lotani limene Yesu anadzutsa, ndipo kodi anadzifanizitsa ndi yani?

4 Miyezi ina isanafike imfa yake, Yesu anadzutsa funso, lolembedwa pa Luka 12:42: “Ndani tsono ali mdindo wokhulupirika ndi wanzeru, amene mbuye wake adzamuika kapitao wa pa banja lake, kuwapatsa iwo phoso lawo pa nthaŵi yake” Kenaka, masiku oŵerengeka asanafe, Yesu anadzifanizitsa iyemwini ndi munthu amene anali pafupi kupita kutali, yemwe anaitana akapolo ake ndi kuwapatsa chuma chake.​—Mateyu 25:14.

5. (a) Kodi ndiliti pamene Yesu anagaŵira ena kuyang’anira chuma chake? (b) Kodi ndi ntchito yowonjezereka yotani imene Kristu anagaŵira awo amene anakhala mbali yaikulu ya manijala wa nyumba yake?

5 Kodi ndiliti pamene Yesu anagawira ena kuti asamalire chuma chake? Zimenezi zinachitika pambuyo pa chiukiriro chake. M’mawu ake ozoloŵereka pa Mateyu 28:19, 20, choyamba Kristu anapatsa awo amene akakhala mbali ya manijala wake wanyumba wa mbali zambiri ntchito yowonjezeka ya kuphunzitsa ndi kupanga ophunzira. Ngati akalindewo aliyense payekha akachitira umboni “kufikira malekezero ake a dziko,” iwo akafutukula munda waumishonale umene Yesu anayamba kuulima mkati mwa uminisitala wake wapadziko lapansi. (Machitidwe 1:8) Zimenezi zinaloŵetsamo kuchita kwawo monga “atumiki m’malo mwa Kristu.” Monga “adindo a zinsinsi za Mulungu,” iwo akapanga ophunzira ndipo akawapatsa chakudya chauzimu.​—2 Akorinto 5:20; 1 Akorinto 4:1, 2.

Bungwe Lolamulira la Nyumbayo

6. Kodi kagulu ka mdindo ka zaka za zana loyamba kanauziridwa mwaumulungu kupereka chiyani?

6 Onse pamodzi, Akristu odzozedwa ndi mzimu anayenera kukhala mdindo wa mbuyeyo, kapena manijala wa nyumba, wogaŵiridwa kupereka chakudya chauzimu cha pa nthaŵi yake kwa chiŵalo chirichonse cha nyumba ya Mulungu. Pakati pa zaka za 41 C.E. ndi 98 C.E., ziŵalo za kagulu ka mdindo za zaka za zana loyamba zinauziridwa mwaumulungu kulemba zochitika zam’mbiri 5, makalata 21, ndi bukhu la Chibvumbulutso kaamba pa phindu la abale awo. Zolembedwa zouziridwa zimenezi ziri ndi chakudya chabwino chauzimu cha ambanjawo, uku ndiko kuti, wodzozedwa aliyense wa nyumba ya Mululngu.

7. Kodi ndi chifuno chanji chimene Kristu anasankhira chiŵerengero chochepa cha amuna kuchokera ku kagulu kakapolo?

7 Pamene kuli kwakuti Akristu odzozedwa onse pamodzi amapanga nyumba ya Mulungu, pali umboni wochuluka wakuti Kristu anasankha chiŵerengero chochepa cha amuna a kagulu kakapolo kutumikira monga bungwe lolamulira lowoneka ndi maso. Mbiri yakale ya mpingo imasonyeza kuti atumwi 12, kuphatikizapo Matiya, anali maziko a bungwe lolamulira la zaka za zana loyamba. Machitidwe 1:20-26 amatipatsa chisonyezero cha chimenechi. M’chigwirizano ndi kuloŵedwa m’malo kwa Yudasi Isikariote, chilozero chikupangidwa pano ku “uyang’aniro wake” ndi ku “utumiki uwu ndi utumwi.”

8. Kodi mathayo a bungwe lolamulira la zaka za zana loyamba anaphatikizapo chiyani?

8 Uyang’aniro umenewo unaphatikizapo thayo la atumwi la kuika amuna oyeneretsedwa m’malo a utumiki ndi kulinganiza uminisitala. Koma zinatanthauza zoposapo. Zinaloŵetsamonso kuphunzitsa ndi kumveketsa nsonga zachipunzitso. Pokwaniritsa lonjezo la Yesu lolembedwa pa Yohane 16:13, “mzimu wa chowonadi” unayenera kutsogoza mpingo Wachikristu mopitirizabe ku chowonadi chonse. Kuyambira pachiyambi, awo amene anagwira mawu ndi kubatizidwa, Akristu odzozedwa anapitirizabe kudzipereka iwo eni ku “chiphunzitso cha atumwi.” Kwenikwenidi, chifukwa chimene amuna asanu ndi aŵiri oyamikiridwa anaikidwa ku mathayo ofunika a kugaŵira chakudya chakuthupi chinali chakuti “khumi ndi aŵiriwo” akhale omasuka ku ‘kulimbika m’kupemphera ndi kutumikira mawu.’​—Machitidwe 2:42; 6:1-6.

9. Kodi ndimotani mmene chiŵerengero cha bungwe lolamulira la zaka za zana loyamba chinachepetsedwa kufika pa 11, koma kodi nchifukwa ninji chiŵerengerocho sichinabwezeretsedwe ku 12 mwamsanga?

9 Zikuwoneka kuti poyamba bungwe lolamulira linapangidwa ndi atumwi a Yesu okha okha. Koma kodi zikakhalabe tero? Chifupifupi chaka cha 44 C.E., mtumwi Yakobo, mbale wa Yohane, anaphedwa ndi Herode Agripa 1. (Machitidwe 12:1, 2) Mwachiwonekere palipe kuyesayesa kumene kunapangidwa kumuloŵa m’malo monga mtumwi, monga mmene zinachitidwira ndi Yudasi. Nchifukwa ninji ayi? Mosakaikira chinali chifukwa chakuti Yakobo anamwalira ali wokhulupirika, woyamba kumwalira wa atumwi 12 amenewo. Ku mbali ina, Yudasi anali wonyenga woipa ndipo anayenera kuloŵedwa m’malo kuti chiŵerengero cha miyala yamaziko ya Israyeli wauzimu chibwerere pa 12.​—Aefeso 2:20; Chibvumbulutso 21:14.

10. Kodi ndiliti ndipo ndimotani mmene bungwe lolamulira la zaka za zana loyamba linafutukulidwa, ndipo kodi ndimotani mmene Kristu analigwiritsira kutosgoza nyumba ya Mulungu?

10 Ziŵalo zoyambirira za bungwe lolamulira la zaka za zana loyamba zinali atumwi, amuna amene anayenda ndi Yesu ndipo anali mboni za imfa yake ndi chiukiriro. (Machitidwe 1:21, 22) Koma mkhalidwe umenewu unayenera kusintha. Pamene zaka zinapita, amuna ena Achikristu anafikira uchikulire wauzimu ndipo anaikidwa monga akulu mu mpingo wa ku Yerusalemu. Pofika chaka cha 49 C.E., bungwe lolamulira linali litafutukulidwa kuphatikizapo osati kokha atumwi otsalira komanso unyinji wa amuna ena achikulire mu Yerusalemu. (Machitidwe 15:2) Chotero kapangidwe ka bungwe lolamulira sikanali kokhazikitsidwa mosasintha, koma Mulungu mwachiwonekere anatsogoza zinthu kotero kuti linasintha kuyenerera mikhalidwe ya anthu ake. Kristu, Mutu wokangalika wa mpingo, anagwiritsira ntchito bungwe lolamulira lofutukulidwa limeneli kuthetsa nkhani yofunika yachiphunzitso yakudulidwa kwa Akristu osakhala Achiyuda ndi kugonjera ku Chilamulo cha Mose. Bungwe lilamulira linalemba kalata yolongosola chosankha chake ndi kupereka malamulo ofunika kusungidwa.​—Machitidwe 15:23-29.

Nthaŵi Yoŵerengera Manijala wa Nyumba

11. Kodi chitsogozo champhamvu chochitidwa ndi bungwe lolamulira chinayamikiridwa ndi abalewo, ndipo kodi nchiyani chimene chikusonyeza kuti Yehova anadalitsa kakonzedwe kameneka?

11 Aliyense payekha ndiponso mongo mipingo, Akristu oyambirira anayamikira chitsogozo chaphamvu chimenechi chiperekedwa ndi bungwe lolamulira. Pambuyo pakuti mpingo mu Antiokeya wa Syria unaŵerenga kalata yochokera ku bungwe lolamulira, anakondwera ndi chilimbikitsocho. Pamene mipingo ina inalandira chidziŵitsocho ndi kusunga malamulowo, iyo “inalimbikitsidwa m’chikhulupiriro, nachuluka m’chiŵerengero chawo tsiku ndi tsiku.“ (Machitidwe 16:5) Mowonekera, Mulungu anadalitsa kakonzedwe kameneka.​—Machitidwe 15:30, 31.

12, 13. Kodi ndizochitika zotani zimene Yesu ananeneratu m’mafanizo ake a ndalama ndi matalente?

12 Koma tiyeni tiyang’ane ku mbali ina ya nkhani yofunikayi. M’fanizo lake la ndalama, Yesu anadzifanizitsa iyemwini ndi munthu wa fuko lomveka amene anapita ku dziko lakutali kukadzilandirira yekha ufumu ndipo kenaka anabwerera. (Luka 19:11, 12) Monga chotulukapo cha kuukitsidwa kwake mu 33 C.E., Yesu Kristu anakwezedwa kudzanja lamanja la Mulungu, kumene anayenera kukhala kufikira adani ake akaikidwa monga chopondapo mapazi ake.​—Machitidwe 2:33-35.

13 M’fanizo lofanana nalo, fanizo la matalente, Yesu analongosola kuti patapita nthaŵi yaitali, mbuyeyo anadza kudzaŵerengera ndi akapolo ake. Kwa akapolo amene anakhala okhulupirika, mbuyeyo anati: “Unali wokhulupirika pa zinthu zazing’ono, ndidzakhazika iwe pa zinthu zambiri; lowa iwe m’chikondwero cha mbuye wako.“ Koma ponena za kapolo wosakhulupirika, iye analengeza kuti: “Kudzachotsedwa, chingakhale chimene anali nacho. Ndipo ponyani kapoloyo wopanda pake ku mdima wakunja.”​—Mateyo 25:21-23, 29, 30.

14. Kodi Yesu anayembekezera chiyani kwa akapolo ake odzozedwa ndi mzimu?

14 Patapita nthaŵi yaitali​—chifupifupi zaka manzana 19​—Kristu anavekedwa ulamuliro waufumu mu 1914, pamapeto pa “nthaŵi zawo za anthu akunja.” (Luka 21:24) Mwamsanga pambuyo pake, iye “anabwera . . . naŵerengera nawo pamodzi” akapolo ake, Akristu odzozedwa ndi mzimu. (Mateyu 25:19) Kodi Yesu anayembekezanji kwa iwo aliyense payekha ndi onse pamodzi? Ntchito ya mdindoyo inapitiriza monga mmene inaliri chiyambire zaka za zana loyamba. Kristu anaikiza matalente kwa munthu payekha​—“kwa iwo onse monga mwa nzeru zawo.” Chotero, Yesu anayembekezera zotulukapo zosiyanasiyana. (Mateyu 25:15) Lamulo la pa 1 Akorinto 4:2 likugwira ntchito pano, limene limati: “Komatu pano pafunika za adindo, kuti munthu akhale wokhulupirika.” Kugwiritsira ntchito matalentewo kunatanthauza kuchita mokhulupirika monga atumiki a Mulungu, kupanga ophunzira ndi kuwapatsa chowonadi chauzimu.​—2 Akorinto 5:20.

“Kapolo” ndi Bungwe Lake Lolamulira Pamene Nthaŵi Yamapeto Ikuyandikira

15. (a) Kodi Kristu anayembekezanji kwa manijala wake wanyumba? (b) Kodi nchiyani chimene chikusonyeza kuti Kristu anayembekezera kagulu ka kapolo kumachita zimenezi kudza kwake kudzayendera nyumba kusanafike?

15 Yesu anayembekezera Akristu odzozedwa onse pamodzi kukhala akuchita monga mdindo wokhulupirika, kupatsa bungwe lake la akalinde “phoso lawo pa nthaŵi yake.” (Luka 12:42) Mogwirizana ndi Luka 12:43, Kristu anati: “Wodala kapoloyo amene mbuye wake pakufika, adzampeza alikuchita chotero.” Zimenezi zikusonyeza kuti kwa nthaŵi ina Kristu asanafike kudzaŵerengera ndi akapolo ake odzozedwa ndi mzimu, iwo akakhala akugaŵira chakudya chauzimu kwa ziŵalo za mpingo Wachikristu, nyumba ya Mulungu. Kodi ndani amene Kristu anampeza akuchita chotero pamene anafika mu ulamuliro waufumu mu 1914 ndi kupitirizabe kuyendera nyumba ya Mulungu mpaka mu 1918?​—Malaki 3:1-4; Luka 19:12; 1 Petro 4:17.

16. Pamene Kristu anafika kudzayendera nyumba ya Mulungu mu 1918, kodi nchifukwa ninji sanapeze matchalitchi a Dziko Lachikristu akupereka chakudya chauzimu pa nthaŵi yake?

16 Pamene nyengo yaitali ya kudikira kwa Yesu kudzanja lamanja la Yehova inakafika kumapeto, chinakhala chodziŵikiratu amene ankapereka chakudya chauzimu ku banja la Kristu isanafike 1914. Kodi mukuganiza kuti anali matchalitchi a Dziko Lachikristu? Ndithudi ayi, popeza kuti anali odziloŵetsa kotheratu m’ndale zadziko. Iwo anali zida zodzifunira zofutukulira ulamuliro ndi kuyesera kupikisana kuti atsimikizire kukonda kwawo dziko lawo, mwakutero kulimbikitsa utundu. Posakhalitsa zimenezi zinabweretsa liŵongo la mwazi pa iwo, uku ndiko kuti, pamene anapereka chirikizo lawo ku maboma andale zadziko oloŵetsedwa mu nkhondo yoyamba ya dziko. Mwauzimu, chikhulupiriro chawo chinafooketsedwa ndi Umakono. Vuto lauzimu lilnadza chifukwa atsogoleri achipembedzo ambiri anakhala minkhole yosavuta ya kuphunzira zolembedwa zabaibulo kosuliza ndi chisinthiko. Palibe chakudya chodzetsa thanzi chauzimu chimene chikanayembekezeredwa kuchokera kwa atsogoleri a Dziko Lachikristu!

17. Kodi nchifukwa ninji Kristu anakana Akristu odzozedwa ena, ndipo ndi zotulukapo zotani kwa iwo?

17 Mofananamo, palilbe chakudya chodzetsa thanzi chauzimu chimene chinkabwera kuchokera kwa Akristu odzozedwa amene anali odera nkhaŵa za chipulumutso chawo chaumwini m’malo mogwiritsira ntchito talente ya Mbuyeyo. Iyo anasanduka kukhala “waulezi,” osayenerera kusamalira zinthu za Mbuyeyo. Chotero, iwo anatayidwa “ku mdima wakunja,” kumene matchalitchi a Dziko Lachikristu adakali.​—Mateyo 25:24-30.

18. Kodi ndani amene Mbuyeyo anapeza akupereka chakudya chauzimu kwa bungwe lake la akilinde pa nthaŵi yake, ndipo nchiyani chimene chikutsimikizira zimenezi?

18 Pamene anafika kudzayendera akapolo ake mu 1918, kodi ndi ndani amene Mbuyeyo, Yesu Kristu, anapeza akupereka kwa bungwe la akalinde ake phoso lawo pa nthaŵi yake? Zowonadi, pa nthaŵi imeneyo, kodi ndani amene anapatsa ofuna chowonadi enieni kumvetsetsa kwabwino kwa nsembe ya dipo, dzina la Mulungu, kusawoneka ndi maso kwa kukhalapo kwa Kristu, ndi kufunika kwa 1914? Kodi ndani amene anavumbula chinyengo cha Utatu, kusafa kwa moyo wa munthu, ndi moto wa helo? Ndipo kodi ndani amene anachenjeza za kuwopsya kwa chisinthiko ndi kukhulupirira mizimu? Nsonga zikusonyeza kuti linali gulu la Akristu odzozedwa oyanjanitsidwa ndi afalitsi a magazini a Zion’s Watch Tower and Herald of Christ’s Presence, tsopano yotchedwa Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova.

19. Kodi ndimotani mmene kagulu ka kapolo wokhulupirika kanadziwonetsera kokha isanafike 1918, kodi kanalikugwiritsira chiyani kupereka chakudya chauzimucho, ndipo chiyambire liti?

19 M’kope lake la November 1, 1944, The Watchtower inalongosola kuti: “Mu 1878, zaka makumi anayi kubwera kwa Ambuye kukachisi mu 1918 kusadakhale, panali kagulu ka Akristu opatulikitsidwa owona mtima kamene kanapatuka ku udindo ndi magulu a atsogoleri achipembedzo ndi kamene kanafuna kuchita Chikristu . . . Chaka chotsatira, mu July, 1879, kuti zowonadi zimene Mulungu anapereka kupyolera mwa Kristu monga ‘zakudya m’nyengo yake’ zingaperekedwe mokhazikika kwa am’nyumba yake onse a ana opatulikitsidwa, magazine ameneŵa, The Watchtower, anayamba kufalitsidwa.”

20. (a) Kodi ndimotani mmene Bungwe Lolamulira lamakono linafikira kukhalako? (b) Kodi ziŵalo za Bungwe Lolamulira zinali kuchita chiyani, ndipo pansi pa chitsogozo cha yani?

20 Popereka chidziŵitso cha chiyambi cha Bungwe Lolamulira lamakono, kope la May 15, 1972, la Nsanja ya Olonda linalongosola kuti: “Zaka zisanu pambuyo pake [mu 1884] Zion’s Watch Tower Tract Society inapangidwa mwalamulo ndipo inatumikira monga ‘chiwiya’ chopereka chakudya chauzimu kwa anthu owona mtima zikwizikwi ofunafuna kudziŵa Mulungu ndi kumvetsetsa Mawu ake . . . Akristu odzipatulira, obatizidwa, odzozedwa anakhala oyanjana ndi Sosaite imeneyo pa malikulu mu Pennsylvania. Kaya anali mu Bungwe la Otsogolera kapena ayi, iwo anadzipereka okha kaamba ka ntchito yapadera ya kagulu ka ‘kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.’ Iwo anathandizira m’kudyetsa ndi kutsogolera kwa kagulu ka kapolo, ndipo chotero bungwe lolamulira linawonekera. Ichi chinali mwachiwonekere pansi pa chitsogozo champhamvu yogwira ntchito yosawoneka kapena mzimu woyera wa Yehova. Ndiponso, pansi pa chitsogozo cha Mutu wa mpingo Wachikristu, Yesu Kristu.”

21. (a) Kodi Kristu anapeza yani akugaŵira chakudya chauzimu, ndipo ndimotani mmene anawafupira iwo? (b) Kodi nchiyani chimene chinayembekezera kapolo wokhulupirika ndi Bungwe lake Lolamulira?

21 Mu 1918, pamene Yesu Kristu anayendera awo odzinenera kukhala akapolo ake, iye anapeza gulu la mitundu yonse la Akristu likufalitsa zowonadi za Baibulo zogwiritsidwa ntchito ponse paŵiri mkati ndi kunja kwa mpingo mu ntchito yolalikira. Mu 1919 zinachitikadi monga mmene Kristu aneneneratu: “Wodala kapolo amene mbuye wake, pakufika, adzampeza iye alikuchita chotero. Indetu, ndinena kwa inu, kuti adzamkhazika iye woyang’anira zinthu zake zonse.” (Mateyo 24:46, 47) Akristu owona ameneŵa analoŵa m’chikondwero cha Mbuye wawo. Pokhala atasonyeza kukhala ‘okhulupirika pa zinthu zazing’ono,’ anaikidwa ndi Mbuyeyo “pa zinthu zambiri.” (Mateyu 25:21) Kapolo wokhulupiririka ndi Bugwe lake Lolamulira anali m’malo mwake, wokonzekera kaamba ka ntchito yowonjezereka. Tiyenera kukhala achimwemwe chotani nanga kuti mmenemu ndi mmene zinaliri, popeza kuti Akristu okhulupirika akupindula molemera ndi ntchito yodzipereka ya kapolo wokhulupiririka ndi Bungwe lake Lolamulira!

Nsonga Zazikulu Zofunika Kukumbukira

◻ Kodi ndani amene ali Mutu wa nyumba ya Mulungu, ndipo kodi Ameneyu wapereka ulamuliro kwa yani?

◻ Kodi ndi ntchito yoloŵetsamo zambiri yotani imene Kristu anapereka kwa kagulu ka kapolo?

◻ Kodi ndi bungwe lina liti limene linakhalapo mkati mwa kagulu ka kapolo, ndipo kodi mathayo ake enieni anali otani?

◻ Pamene Kristu anafika kudzayendera nyumba ya Mulungu, kodi ndani amene ankapereka chakudya chauzimu kwa ziŵalo zake?

◻ Kodi ndimotani mmene Bungwe Lolamulira lamakono linakhalirako?

[Chithunzi patsamba 10]

“Kapolo” wa zaka za zana loyamba anali ndi bungwe lolamulira lopangidwa ndi atumwi ndi akulu a mpingo wa Yerusalemu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena