Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w90 4/15 tsamba 29
  • Kodi Mumakumbukira?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mumakumbukira?
  • Nsanja ya Olonda​—1990
  • Nkhani Yofanana
  • Tsatirani Chitsanzo cha Yesu cha Kudzipereka Kwaumulungu
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Londolani Kudzipereka Kwaumulungu Monga Akristu Obatizidwa
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Onjezerani Kudzipereka kwa Mulungu pa Chipiriro Chanu
    Nsanja ya Olonda—2002
  • Wonjezerani Pachipiriro Chanu Kudzipereka Kwaumulungu
    Nsanja ya Olonda—1993
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda​—1990
w90 4/15 tsamba 29

Kodi Mumakumbukira?

Kodi mwapeza makope aposachedwapa a Nsanja ya Olonda kukhala a phindu logwira ntchito kwa inu? Pamenepa bwanji osayesa chikumbukiro chanu ndi zotsatirazi?

◻ Kodi tiyenera kuchita chiyani ngati titi tizindikire chigwirizano ndi mtendere kaamba ka anthu a mitindu yonse zowonedwa m’masomphenya pa Yesaya 2:4?

Choyamba, tiyenera kuzindikira kuti Mlengi wathu, Yehova, ali ndi kuyenerera kwa kutilangiza “m’mayendedwe ake.” Ndipo chachiŵiri, tiyenera kukhala ndi chikhumbo chofunitsitsa cha kumamatira ku malamulo a Mulungu mwakunena kuti: “Tidzayenda m’mayendedwe ake.” (Yesaya 2:2, 3)​—12/15, masamba 5, 6.

◻ Kodi nchifukwa ninji Mboni za Yehova sidzimalefulidwa ndi kukhwethemulidwa ndi udani wadziko lonse ndi chitsutso?

Yesu ananeneratu kuti chitsutso choterocho ndi udani zikakhala chizindikiro chodziŵitsa cha alambiri enieni. (Yohane 15:20, 21; 2 Timoteo 3:12) Chotero alengezi a mbiri yabwino akutsimikiziridwanso kuti ali ndi chivomerezo cha Mulungu. Kuwonjezerapo, Mboni za Yehova zimadziŵa kuti ziri ndi chirikizo la Mulungu Wam’mwambamwamba, Yehova.​—1/1, tsamba 12.

◻ Kodi ndi ziyeneretso zazikulu zina ziti zimene tiyenera kuzifikira ngati mapemphero athu ati ayankhidwe?

Tiyenera kukhulupirira mowona mtima kuti Mulungu aliko. Tiyenera ‘kumfunafuna mwamphamphu,’ tiri ndi chidaliro kuti adzapereka mphotho kwa aja amene atero. (Ahebri 11:6, NW) Ndiponso, tiyenera kumfikira Yehova kupyolera mwa Yesu Kristu ndipo iye yekha. (Yohane 14:6, 14)​—1/15, masamba 4, 6.

◻ Kodi “kudzipereka kwaumulungu” nchiyani? (1 Timoteo 3:16, NW)

Kudzipereka kwaumulungu kuli ulemu, kulambira, ndi utumiki kwa Mulungu, limodzi ndi chikhulupiriro ku ulamuliro wake wa chilengedwe chaponseponse.​—1/15, tsamba 11.

◻ Kodi ndani amene ali “munthu wosayeruzika” wolankhulidwa ndi Paulo pa 2 Atesalonika 2:3?

Paulo sakulankhula za munthu mmodzi, popeza kuti iye akuti “munthu” ameneyu anali wowoneka m’tsiku la Paulo ndipo akapitirizabe kukhalapo kufikira Yehova atamuwononga kumapeto kwa dongosolo lino. Chotero, “munthu wosayeruzika” liri liwu lophiphiritsira. Umboni ukusonyeza kuti iye ali bungwe la atsogoleri achipembedzo onyada, odzikuza a Dziko Lachikristu, amene kwa zaka mazanamazana adzikweza okha kukhala lamulo mwa iwo eni.​—2/1, tsamba 11.

◻ Kodi umbombo ungachotsedwe motani?

Umbombo pakati pa anthu ungachotsedwe kupyolera mwa maphunziro abwino ndi kuphunzitsidwa, ndi kutsatiridwa kwa zitsogozo zosamalitsa, kapena malamulo a mayendedwe. Maphunziro oterowo ayenera kuchokera ku magwero opanda umbombo iwo eni. Ali Mulungu wakumwamba yekha amene angapereke maphunziro a mtundu wotero, ndipo akupezeka m’bukhu lake lophunzirira, Baibulo Loyera.​—2/15, tsamba 5.

◻ Ngati phunziro la Baibulo laumwini liti likulitse kudzipereka kwaumulungu, kodi phunzirolo liyenera kuphatikizapo chiyani?

Cholinga cha phunziro laumwini sichingangokhala kumaliza masamba a nkhani ndipo mwakutero kudzaza maganizo ndi chidziŵitso. M’malo mwake, pamene mbali ya Mawu a Mulungu iŵerengedwa, nthaŵi iyenera kutengedwa kulingalira pa nkhaniyo mofuna kudziŵa chimene ikuphunzitsa ponena za makhalidwe ndi njira za Yehova kotero kuti wophunzirayo angakhale wofanana ndi Yehova m’mbali zimenezi.​—3/1, tsamba 13.

◻ Kodi nchifukwa ninji phunziro la Baibulo laumwini liyenera kuphatikizapo kuŵerenga kokhazikika kwa Uthenga Wabwino wa Yesu?

Chitsanzo cha Yesu chimatithandiza kukulitsa kudzipereka kwaumulungu. Yesu anadziŵa Atate wake bwino lomwe kuposa wina aliyense, chotero anakhoza kutsanzira njira za Yehova ndi mikhalidwe yake mosamalitsa. Motero, iye anakhala kwa ife monga chitsanzo changwiro cha kudzipereka kwaumulungu. (Yohane 1:18; 14:9; Aroma 13:14)​—3/1, tsamba 19.

◻ M’fanizo la Yesu la matalente, kodi kugwiritsira ntchito matalente kunatanthauzanji? (Mateyu 25:19-23)

Kugwiritsira ntchito matalente kunatanthauza kuchita mokhulupirika monga oimira a Mulungu, kupanga ophunzira, ndi kugaŵira zowonadi zauzimu kwa nyumba ya Mulungu. (Mateyu 24:45; 28:19, 20; 2 Akorinto 5:20)​—3/15, tsamba 13.

◻ Kodi Baibulo liri lapadera m’mbali zitatu ziti poliyerekeza ndi magwero ena a uphungu?

Choyamba, uphungu wake nthaŵi zonse umakhala wopindulitsa. (Salmo 93:5) Chachiŵiri, Baibulo lapirira chiyeso cha nthaŵi. (Yesaya 40:8; 1 Petro 1:25) Chachitatu, kuchuluka kwa uphungu wa Baibulo kuli kosayerekezereka. Mosasamala kanthu za vuto kapena chosankha chimene tingayang’anizane nacho, Baibulo liri ndi nzeru imene ingatithandize.​—4/1, tsamba 13.

◻ Kodi ndi maumboni aŵiri ati amene amasonyeza kuti Baibulo liri Mawu a Mulungu, osati a munthu?

Nzeru yosayerekezereka ya Baibulo ndi mphamvu yake ya kusintha anthu. (Miyambo 2:1, 5, 6; Ahebri 4:12)​—4/1, tsamba 21.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena