Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w90 7/1 tsamba 7
  • Ripoti la Olengeza Ufumu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ripoti la Olengeza Ufumu
  • Nsanja ya Olonda​—1990
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mfupo ya Kuwona Mtima
  • Achichepere mu Italy Apanga Mwaŵi wa Kuchitira Umboni
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Kuwona Mtima Kumakometsera Uminisitala Wathu
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Thandizo kwa ‘Aludzu’ ku Russia
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Chitani Zinthu Zonse Moona Mtima
    Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’?
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda​—1990
w90 7/1 tsamba 7

Ripoti la Olengeza Ufumu

◻ ‘CHIZUNZO chachikulu’ motsutsana ndi mpingo woyambirira Wachikristu chinatumikira kubalalitsa ophunzira ambiri a Kristu. (Machitidwe 8:1) Komabe, chizunzo chimenechi chinalephera chifukwa chakuti omwe anabalalitsidwawo “anapitapita nalalikira mauwo.” (Machitidwe 8:4) Filipo anapitirizabe kulalikira, ndipo “makamuwo ndi mtima umodzi anasamalira zonenedwa.” (Machitidwe 8:6) Monga mmene chizunzocho chinalepherera m’zaka za zana loyamba, ndi mmenenso chinachitira m’mudzi wa kumpoto kwa Thailand.

Mpainiya wapadera wa Mboni za Yehova anayamba kulalikira m’mudziwu, koma poyamba nzika za m’mudziwo sizinkamvetsera. Komabe, pamene analankhula ndi mlaliki wa komweko, anthu anasonkhana kudzamvetsera. Ena anadzazindikira kuti Mboniyo inadziŵa Baibulo bwino kwambiri kuposa minisitala wawoyo, chotero anayamba kuphunzira Baibulo ndi mpainiyayo ngakhale kuti ena anawaukira. Abakha awo ena anaphedwa, moyo wa mpainiyayo unali pangozi, ndipo nyumba ya munthu wina wokondwerera inawotchedwa. Mwamunayo anati: “Iwo angawotche nyumba yanga, koma sangawotche mtima wanga.” Ophunzira ndi Mboniyo anatchova njinga paulendo wautali kukapezeka pamisonkhano ku Nyumba Yaufumu. Anayi a iwo anabatizidwa, ndipo asanu ndi mmodzi adakapezekabe pamisonkhano limodzi nawo.

Mfupo ya Kuwona Mtima

◻ Abale mu Zambia adzipangira dzina labwino la kukhala owona mtima, ndipo ichi chatulukapo madalitso kwa iwo, limodzinso ndi kuthandiza ena kuzindikira chowonadi. Mkulu wina, yemwe ndi mpainiya wokhazikika, anali paulendo wa pabasi ndipo anamva Mboni m’basimo ikulankhula ndi ena ponena za chiukiriro. Wapaulendo wina anafunsa mlongoyo kuti: “Kodi nchifukwa ninji inu Mboni mumanena kuti chipembedzo chanu ndicho chowona chokha?” Mbaleyo anagwirizana nawo m’kukambiranako nati kwa wapaulendoyo kuti Yehova adzafupa Mboni zake chifukwa chakuti zimaphunzitsa chowonadi chochokera m’Baibulo.

Patapita pakati pausiku ali paulendowu, basiyo inafika pa rodibuloko. Kunkagwa mvula yamphamvu. Msilikali analoŵa m’basimo ndikufunsa ngati munakwera Mboni za Yehova zirizonse mkatimo. Munali zitatu. Pamenepo anati: “Chabwino, Mboninu bakhalani mom’muno, otsalanu tulukani panja ndi zola zanu.” Ena onsewo anatulukira panja pamvulapo, ndipo pambuyo pa kufufuzidwa, anabwerera ndi katundu wawo ndi zovala zitanyowa.

Atabwerera m’basimo, msilikali uja anati: “Chifukwa chomwe ndasiira Mboni muno nchakuti iwo ndi anthu owona mtima. Takhala ndi zokumana nazo zambiri ndipo tapeza kuti ndi okhawo omwe ali owona mtima; titawafunsa kutiuza zomwe ziri m’zola zawo, iwo amatiuza zowonadi.” Pamene basi inanyamuka, mbaleyo anafunsa kuti: “Kodi chipembedzo chowona nchiti?” Munthu wina anayankha kuti: “Chomwe sichinavumbidwe ndi mvula.”

Inde, kuwona mtima kumathandiza kuzindikira chipembedzo chowona, ndipo kulidi ndi mfupo zake!

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena