Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w87 12/1 tsamba 21
  • Achichepere mu Italy Apanga Mwaŵi wa Kuchitira Umboni

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Achichepere mu Italy Apanga Mwaŵi wa Kuchitira Umboni
  • Nsanja ya Olonda—1987
  • Nkhani Yofanana
  • Lalikirani Uthenga Wabwino Paliponse
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Sukulu Yopambana Yapadziko Lonse
    Galamukani!—1996
  • Ripoti la Olengeza Ufumu
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Gwiritsirani Ntchito Magazini Athu m’Njira Yabwino Koposa
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1987
w87 12/1 tsamba 21

Ripoti la Olengeza Ufumu

Achichepere mu Italy Apanga Mwaŵi wa Kuchitira Umboni

AWO amene amayamikira zifuno zabwino kwambiri za Mulungu amakhala osangalatsidwa kuthandiza ena kuphunzira ponena za chiyembekezo chozizwitsa cha Ufumu. Ichi kaŵirikaŵiri chimaphatikizapo kutenga mwaŵi womwe umabuka, monga mmene ripoti lotsatirali lochokera ku Sardinia likusonyezera.

◻ “Wofalitsa wa zaka zakubadwa 12 anali kubwerera kuchokera mu utumiki wa m’munda pa basi. Mu basimo munalinso anyamata aŵiri achichepere ndi mtsikana, onse achifupifupi zaka zakubadwa 18. Wofalitsa wachichepereyo anakhala pafupi ndi mtsikanayu ndi kuyamba kuŵerenga magazini ya Galamukani! akuyembekezera kudzutsa chidwi cha mtsikanayo. Iye anawona magaziniyo ndi kufunsa chimene mnyamatayo anali kuŵerenga. Iye analongosola kuti anali kuŵerenga nkhani yochita ndi yankho ku mavuto amene anthu achichepere amakumanizana nawo. Iye ananena kuti iye wapindula mokulira kuchokera ku nkhani zimenezi, ndipo kuti ingathandizenso mtsikanayo. Iye mwachimwemwe analandira magaziniyo.

“Kukhala atamvetsera ku kukambitsanaku, achichepere aŵiri enawo anafunsanso kaamba ka magaziniyo. Pamene anali kutenga zopereka, woyendetsa basi anawauza iwo kusawononga ndalama zawo pa zinthu zopanda pake zoterozo. Achicheperewo anayankha kuti iwo anali anzeru ndipo kuti magaziniwo anali osangalatsa. Pa ichi woyendetsa basiyo anapita m’mphepete mwa msewu, ndi kuimitsa basi, ndi kufuna kuwona chimene chinali chosangalatsa m’magaziniwo. Iyenso analandira makope.

“Mboni yachichepere yomwe inapereka chokumana nacho chimenechi inanena kuti: ‘Ndiridi wachimwemwe kwenikweni kuti ndinayamba kuchitira umboni pa basi.’”

◻ Mboni ina yachichepere inatenga mwaŵi wa mkhalidwe ku sukulu. Wachichepere ameneyu akulongosola kuti: “Mphunzitsi wathu wa pa sukulu anatiphunzitsa ife njira yophunzirira imene inali yosiyana ndi ija ya mwambo. Pambuyo pa kulingalira nkhaniyo, tinafunsidwa kupanga autilaini kuphatikizapo mfundo zazikulu ndi mfundo zothandizira ndipo kenaka kupereka nkhani yosakonzekera pa nkhaniyo.

“‘Ndiri wozoloŵerana kwambiri ndi njirayi,’ inatero Mboniyo. ‘Iri imodzi yolingaliridwa ndi Bukhu Lolangiza la Sukulu ya Utumiki wa Teokratiki.’ Mphunzitsiyo mwamsanga anazindikira kuti ndinali mmodzi yekha amene anali wopambana kugwiritsira ntchito njirayi. Iye anandifunsa ine chifukwa chake panali kusiyana koteroko pakati pa ntchito yanga ndi ija ya ena. Ndinalongosola kuti ndinaphunzira njirayi mu Sukulu ya Utumiki wa Teokratiki. Iye anasangalatsidwa kwambiri ndi kundiitana ine kukachitira chitsanzo kwa kalasi, mwa kugwiritsira ntchito Bukhu Lolangiza la Sukulu ya Utumiki wa Teokratiki. Ichi ndinachichitadi.

“Pamene ndinapita kunyumba, ndinaliuza banja langa chimene chinachitika. Atate anga, amene sali Mboni, nthaŵi zonse anali kunena kuti kukhala mmodzi wa Mboni za Yehova kunali monga chopundula ku sukulu, koma pambuyo pa kumvetsera ku chokumana nacho changa, iwo anakakamizidwa kusintha malingaliro awo.”

Ndi mwaŵi wokulira chotani nanga umene inu achichepere, limodzinso ndi inu achikulire, muli nawo wa kusungilira ndi kudziŵikitsa dzina la Yehova!​—Masalmo 148:12, 13.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena