Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w90 7/15 tsamba 7
  • Nkhondo ya Yeriko—Nthano Kapena Yeniyeni?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Nkhondo ya Yeriko—Nthano Kapena Yeniyeni?
  • Nsanja ya Olonda​—1990
  • Nkhani Yofanana
  • Mafunso Ochokera kwa Owerenga
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Kodi “Chipangano Chakale” Nchokhulupirika Motani?
    Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu?
  • Mfundo Zazikulu za M’buku la Yoswa
    Nsanja ya Olonda—2004
  • Tizikhulupirira Khristu Yemwe Ndi Mtsogoleri Wathu
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2018
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda​—1990
w90 7/15 tsamba 7

Nkhondo ya Yeriko​—Nthano Kapena Yeniyeni?

KWA zaka makumi angapo, akatswiri ofukula m’mabwinja ayesa kupereka chikaikiro pa cholembedwa cha Baibulo cha Yoswa ndi nkhondo ya Yeriko. Mogwirizana ndi Baibulo, Yoswa ndi gulu lankhondo la Israyeli anaguba mozungulira Yeriko kwa masiku asanu ndi aŵiri, kufikira Mulungu anachititsa malinga olimba am’zindawo kugwa. Izi zinatheketsa Aisrayeli kuloŵa ndi ‘kutentha mzindawo ndi moto ndi chirichonse chokhalamo.’​—Yoswa 6:1-24.

Koma akatswiri ambiri ofukula m’mabwinja, osokeretsedwa ndi buku lotchuka kwambiri la Kathleen Kenyon m’ma 1950, anakhutiritsidwa kuti Yeriko sanakhaleko nkomwe mkati mwa nthaŵi ya kuukira kwa Aisrayeli. Eya, iwo ananena kuti mzindawo unali utawonongedwa kale zaka zana limodzi pasadakhale! Motero, cholembedwa Chabaibulo cha Yoswa ndi Aisrayeli chinakanidwa ndi ambiri. Komabe, posachedwapa, Dr. Bryant G. Wood, katswiri wofukula m’mabwinja wa ku Yunivesite ya Toronto, Canada, wakhala ndi lingaliro latsopano paumboni wochokera ku Yeriko. Mogwirizana ndi The New York Times, iye wapeza kuti Dr. Kenyon “anali kufunafuna zoumba zadongo zolakwika, ndipo m’malo olakwika,” ndikuti umboniwo uli kwenikweni “wogwirizana kotheratu” ndi Baibulo.

Dr. Wood akusonyeza muyalo wochindikala 1 mitala waphulusa losanganizana ndi zibenthu zadongo za woumba, zidutswa zanjerwa zochokera ku linga lakugwa, ndi matabwa, zonse ziri zakuda ngati kuti zinadetsedwa ndi moto woŵaula mzinda wonse. Zidutswa zadongozo zaikidwa deti (mwanjira zokhalapo zovomerezedwa kukhala zosatsimikizirika) la 1410 Nyengo Yathu ino isanakhale, kuwonjeza kapena kuchotsa zaka 40​—pafupi kwambiri ndi 1473 B.C.E., chaka cha nkhondo ya Yeriko yotchulidwa m’Baibulo.

Ofukula m’mabwinja apeza kuti nyumba mu Yeriko wakale zinali ndi nkhokwe zambiri za dzinthu. Izi nzokondweretsa, popeza kuti Baibulo limasonyeza kuti Yeriko anagwa nthaŵi yochepa pambuyo pa kukolola kwa m’ngululu ndipo palibe njala yochititsidwa ndi msasa wozinga mzindawo. (Yoswa 3:14-16) Zonse ziŵiri nzifukwa zabwino chifukwa chake nyumba za Yeriko ziyenera kukhala zinali ndi dzinthu zambiri pamene mzindawo unawonongedwa.

Asayansi amazengereza kuvomereza pa mfundo ya kulondola kwa Baibulo. Motero, Times ikugwira mawu katswiri wina wotchuka kukhala akunena molabadira ku zimene Wood anapeza: “Palibe chikaikiro kuti unyinji wa chidziŵitso chopezedwa m’Baibulo uli ndi chowonadi mkati mwake.” Komabe, pamene zolembedwa Zamalemba zowonjezerekawonjezereka zikuchirikizidwa ndi zopezedwa zamakono zasayansi ndi za ofukula m’mabwinja, kuli komvekera bwino kwa olama maganizo kuti Baibulo siliri konse chiungwe cha zinyengo zophatikizidwa ndi chowonadi cha apa ndi apo. Monga momwe Baibulo lenilenilo likunenera kuti: “Mulungu akhale wowona, ndimo anthu onse akhale onama.”​—Aroma 3:4.

Pamene kuli kwakuti mamasuliridwe atsopano a zofukulidwa m’mabwinja a ku Yeriko ali osangalatsa, Akristu owona ‘akuyenda mwachikhulupiriro, simwakuwona ayi.’ (2 Akorinto 5:7) Chikhulupiriro chawo sichimadalira pa ofukula m’mabwinja. Kaya akhale ndi umboni wa zofukulidwa m’mabwinja kapena ayi, Baibulo mobwerezabwereza limatsimikizira kukhala magwero odalirika a chidziŵitso chonena za nthaŵi yakale, yatsopano, ndi yamtsogolo.​—Salmo 119:105; 2 Petro 1:19-21.

[Chithunzi patsamba 7]

Mabwinja a Yeriko, kumene Yehova anapatsa Aisrayeli chilakiko

[Mawu a Chithunzi]

Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena