Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w90 7/15 tsamba 24-26
  • Kuchereza kwa Melita Kudzetsa Madalitso

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuchereza kwa Melita Kudzetsa Madalitso
  • Nsanja ya Olonda​—1990
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Alendo Abweretsa Mbiri Yabwino
  • Chitonthozo cha Malemba
  • Chirimbikitso cha Kukhala Wachangu
  • Chilangizo Chothandiza Chidzetsa Madalitso
  • Kusinthana Chirimbikitso
  • “Mwina Nyimbo Ndi Imene Ingathandize”
    Galamukani!—2010
  • Chuma Chosayerekezereka Chogaŵana ndi Ena
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Kondwerani M’chiyembekezo
    Galamukani!—2006
  • Umphawi Komanso Vuto Losowa Pokhala Zidzatha
    Galamukani!—2015
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda​—1990
w90 7/15 tsamba 24-26

Kuchereza kwa Melita Kudzetsa Madalitso

MELITA anali malo abwino oterapo kwa mtumwi Paulo pamene ngalaŵa yawo inasweka m’zaka za zana loyamba C.E. Nzika za pachisumbupo zinamlandira iye ndi amalinyero anzake ndi ‘manja aŵiri.’ Kunena zowona, nzika za Melita zinachitira alendowo, “zokoma zosachitika pena ponse.”​—Machitidwe 28:1, 2.

Pambuyo pake, mkulu wapachisumbupo, Publiyo, analandira Paulo ndi anzakewo mochereza ‘nawasamalira kwa masiku atatu.’ Pamene mbiri inafalikira yakuti Paulo anachiritsa atate wa Publiyo malungo ndi m’mimba mwakamwazi, “enanso a m’chisumbu, okhala nazo nthenda, anadza, nachiritsidwa.” (Machitidwe 28:7-9) Koma Paulo anachita zowonjezereka. Iye anafesa mbewu za chowonadi m’mitima ya anthuwo, ndipo izi zinatulukira m’madalitso ambiri kwa apachisumbu ochereza ameneŵa. Lerolino, zofananazo zikuchitika pachisumbu cha Melita. Idzani mudzawone mmene ziriri choncho.

Alendo Abweretsa Mbiri Yabwino

Mutayang’ana kuchokera m’ndege, Melita wounikiridwa ndi dzuŵa amanyezimira ngati juweli yoikidwa panyanja yabulu ya Mediterranean. Poyandikira Bwalo Landege la Luqa, mlendo amawona mtunda woŵaulidwa ndi dzuŵa ndi zomera zowonekera kukhala zochepa. Pamene atera pamtunda, iye amawona kuti chisumbu cha makilomita 11 muutali ndi 16 muufupi ichi chiri ndi anthu pafupifupi 347,000. Akachisi amasindwi obulungika ndi osongoka ambirimbiri a Melita amavumbula mbiri yake yachipembedzo. Koma m’zaka za zana la 20 lino, kodi nzika za Melita zapindula motani ndi kucheza kwa Mboni za Yehova?

Woyang’anira woyendayenda wina wotchedwa David anafika panyumba pa Juliana napeza kulabadira kwachiyanjo kuuthenga wa Ufumu. “Ndinakhwethemulidwa maganizo ndi kudziloŵetsa m’ndale zadziko kwa tchalitchi,” akutero Juliana, “chotero ndinayesa kufunafuna chowonadi chonena za boma la Mulungu m’Baibulo. Koma pamene ndinaliŵerenga, ndinapeza kuti panali zinthu zovuta kumvetsetsa. Tangolingalirani chidwi chomwe ndinali nacho pamene wofika panyumba panga anafunsa ngati ndinadziŵa Ufumu wa Mulungu! Mwamsanga, ndinampempha kundisonyeza yankho m’Baibulo langa Lachikatolika. Iye anatero. Tsiku lomwero ndinadziŵa kuti ndinapeza chowonadi.”

Mboni yakumaloko inapanga makonzedwe a kuphunzira Baibulo ndi Juliana. Pamene David anabwerera ku Melita miyezi isanu ndi umodzi pambuyo pake, zinali zodabwitsa mokondweretsa chotani nanga kuwona Juliana akumlonjera kuloŵa m’Nyumba Yaufumu! Iye mwamsanga anali atakonzekera kukhala wofalitsa wa mbiri yabwino ya Ufumu.

Mwamuna wa Juliana, Francis, nayenso anali atasokonezeka maganizo ndi ziphunzitso zatchalitchi. Pamene ankachezera mkazi wake pamene anali m’chipatala, anampeza akumvetsera kunkhani Zabaibulo zojambulidwa patepi zokambidwira pa Nyumba Yaufumu. Atamvetsera nkhani yonena za banja, Francis anawona mmene uphungu wa Baibulo unaliri wabwino, ndipo monga chotulukapo, anasankha kuyamba kufika pamisonkhano Yachikristu. Mosataya nthaŵi anazindikira vuto loyenera kuthetsedwa. Kodi linali chiyani?

Kwazaka 20, Francis ankagwira ntchito monga wosonkhanitsa ndalama pamalo otchovera juga. Tsopano anazindikira kuti ntchito yoloŵetsamo kutchova juga inali yosagwirizana ndi malamulo a makhalidwe abwino Achikristu amene amatsutsa umbombo ndi chisiriro. (Aroma 13:9, 10; 1 Akorinto 6:9, 10) “Ngakhale kuti poyamba ndinalibe chikhulupiriro chondikhozetsa kusintha ntchito yanga,” akuvomereza Francis, “ndinapempherera thandizo la Yehova. Pomalizira, ndinapeza ntchito ina imene ikundikhozetsa kusamalira mkazi wanga ndi mwana wamwamuna, Sandro.” Lerolino, Francis akutumikira monga mkulu mumpingo wakwawo wa Mboni za Yehova.

Chitonthozo cha Malemba

Rose ndi George anali okwatirana achimwemwe kwazaka zisanu ndi chimodzi pamene George mwatsoka anafa m’ngozi. Rose sanapeze chitonthozo konse m’zitsimikiziro za wansembe zakunena kuti Mulungu anatenga George chifukwa chakuti anachitira nsanje chikondi cha mkaziyo kwa mwamuna wake. Rose anachita tondovi kwambiri kotero kuti analingalira za kupha ana ake atatu ndiyeno nkudzipha.

Koma ndikusintha kotani nanga kunachitika kwa Rose pamene Mboni yoyandikana nayo yotchedwa Helen inayamba kuchita naye phunziro Labaibulo! Pasanapite nthaŵi Rose anatonthozedwa ndi chiphunzitso Chamalemba cha chiukiriro. (Yohane 5:28, 29) Panthaŵi imodzimodziyo, chirimbikitso chinachokera kwa Peter, woyang’anira wina wocheza. Iye anapindula kwakukulu ndi nkhani zake zonena za chiukiriro. Posonkhezeredwa ndi chiyembekezo chimenechi, Rose anatsagana ndi Helen kukachitira umboni wapoyera, ndipo tsopano aŵiriwo akutumikira monga apainiya okhazikika, kapena alaliki a Ufumu anthaŵi zonse.

Chirimbikitso cha Kukhala Wachangu

Joe akuchokera m’banja lalikulu, popeza ali ndi abale ndi alongo 12. Atalimbikitsidwa ndi woyang’anira woyendayenda, anachitira umboni mwachangu kwa achibale ake ambiri. “Poyamba,” iye akutero, “banja langa linadziŵa kuti zimene ndinkawalongosolera kuchokera m’Baibulo zinali zanzeru. Koma pamene anawona kuti chifuno changa cha kukhala Mboni chinakula, anasintha maganizo awo, ndipo onsewo anatsutsana nane​—makamaka Atate.” Kodi mkhalidwe wawo unazimitsa changu cha Joe?

Kutalitali! Mwachitsanzo, pamene khanda la mmodzi wa alongo ake linadwala pafupi kufa, Joe anachitira umboni kwa iye, kulankhula naye ponena za chiyembekezo cha chiukiriro. Tsopano mlongoyu ali Mboni yobatizidwa ya Yehova. Chotsatira, mmodzi wa abale aakulu a Joe ndi banja lake anasonyeza chikondwerero m’chowonadi. Kenaka mbale wawo wamkulu koposa ndi banja lake anatenga kaimidwe koyanja Ufumu wa Mulungu. Panthaŵiyo, atate wa Joe anakwiya mowonjezereka. Pamene mlongo wa Joe wamng’ono koposa nayenso anayamba kuphunzira Baibulo, atatewo anathamangitsa Joe panyumba. Mosabwerera m’mbuyo, Joe anagwiritsira ntchito mwaŵi uliwonse kukacheza ndi achibale ake ndi kulankhula nawo ponena za uthenga wa Baibulo. Komabe, atate wake analabadira mwaukali kuti: “Kodi nchifukwa ninji suulankhula kwa wansembe? Iye amalidziŵa Baibulo koposa!” Joe anayankha kuti akachita zimenezo mokondwa ngati atate wake akatsagana naye. Kodi kuchezera kwawo kunatembenuka motani?

“Tinalinganiza tsiku ndi nthaŵi,” Joe akukumbukira, “koma wansembeyo anafuna kudziŵa nkhaniyo kuti akaikonzekere, akumafotokoza kuti popeza kuti panapita zaka zisanu chichokere kuseminale, tsopano anafunikira kusanthula. . . . Koma pambuyo pa mlungu umodzi, mwezi, ndipo ngakhale miyezi iŵiri, wansembeyo sanasunge pangano lirilonse. Pamene atate anawona izi, anasintha maganizo awo ponena za tchalitchi ndipo pang’onopang’ono anazindikira kuti chomwe ndinaphunzira m’Baibulo chinali chowonadi.” Pomalizira pake atate wa Joe anavomereza chowonadi, akufikitsa 29 chiŵerengero cha ziŵalo za banja lake zophatikizidwa muutumiki wa Yehova.

Chilangizo Chothandiza Chidzetsa Madalitso

Polankhula motenthedwa maganizo ponena za woyang’anira wina wodzacheza, minisitala wokwatira wokhala mpainiya wotchedwa Ignatio akulongosola kuti: “Paul ndi mkazi wake anabwera kudzakhala nafe. Iwo anatithandiza aŵirife muunansi wathu waukwati limodzinso ndi muuminisitala wakumunda. Iye nthaŵi zonse anagogomezera kufunika kwa kulalikira.”

Ignatio akukumbukira chimene chinachitika pamene Paul anakumana ndi akulu ampingo ndi atumiki otumikira m’kuchezetsa kwake kotsirizira. “Pamene ndinati ndinafunikira kapatula nthaŵi kuchokera kuntchito ya kulalikira mmaŵa amenewo kuti ndikonzekere nkhani yanga paprogramu ya msonkhano,” akutero Ignatio, “Paul anati akapita muutumiki wakumunda monga momwe kunalinganizidwira ngakhale kuti sindikatsagana naye. Nditamva zimenezo, ndinasankhanso kupita. Yehova anadalitsa chosankha changa motani nanga! Mmaŵa amenewo ndinayambitsa phunziro Labaibulo, ndipo kuchokera m’phunzirolo, tsopano pali anthu asanu ndi mmodzi oloŵa m’chowonadi.”​—Yerekezerani ndi 3 Yohane 4.

Kusinthana Chirimbikitso

Nthaŵi zonse pamene mkulu woyendayenda achezetsa Mboni zinzake ku Melita, amamlandira ndi manja aŵiri ndipo amakhala ofunitsitsa kupindula ndi chirimbikitso ndi chirangizo chake. (Yerekezerani ndi 3 Yohane 5-8.) Monga chotulukapo, anthu a ku Melita owonjezereka akutenga kaimidwe kolimba kumbali ya Yehova Mulungu ndi Ufumu wake. Podzafika kumapeto kwa chaka chautumiki cha 1989, okwanira 389 mwa anthu a pachisumbu ochereza ameneŵa anatero. Tsopano olinganizidwa kukhala mipingo isanu yokangalika (inayi pa Melita ndi umodzi pafupi ndi chisumbu cha Gozo), amalengeza mbiri yabwino molimba mtima.

Oyang’anira oyendayenda onse ogaŵiridwa kuchezera Melita m’zaka zaposachedwapa amva monga anachitira mtumwi Paulo, yemwe anauza Akristu Achiroma kuti: “Ndilakalaka kuwonana nanu, kuti ndikagaŵire kwa inu mtulo wina wauzimu, kuti inu mukhazikike.” Kuchezetsa kwawo mowonadi kwatulukira ‘m’kusinthana chirimbikitso’ kotsitsimula. (Aroma 1:11, 12) Ndiponso, ntchito za Mboni za Yehova za kulalikira Ufumu zikudzetsa madalitso auzimu olemeretsa kwa anthu owoloŵa manja a Melita.

[Mapu/​Zithunzi pamasamba 24, 25]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

GOZO

COMINO

MELITA

Valleta

Nyanja ya Mediterranean

8 km

5 mi

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena