Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 9/10 tsamba 19
  • “Mwina Nyimbo Ndi Imene Ingathandize”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Mwina Nyimbo Ndi Imene Ingathandize”
  • Galamukani!—2010
  • Nkhani Yofanana
  • Musamatengere Maganizo a M’dzikoli Mukamakonzekera Ukwati
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2019
  • Kuchereza kwa Melita Kudzetsa Madalitso
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Kodi Ndingatani Ngati Ndikudwala Matenda Aakulu?—Gawo 2
    Zimene Achinyamata Amafunsa
  • Gwirizanani Nawo m’Nyimbo Yaufumu!
    Imbirani Yehova Zitamando
Onani Zambiri
Galamukani!—2010
g 9/10 tsamba 19

“Mwina Nyimbo Ndi Imene Ingathandize”

● Juliana anali Mkhristu wachikulire wa ku Philippines amene anthu ankamukonda kwambiri. Koma iye anali ndi matenda enaake a mu ubongo amene amachititsa kuti munthu aziiwala kwambiri, ndipo anafika poti sankazindikira ngakhale ana ake. Ngakhale zinali choncho, nthawi zonse ndikakhala m’dera lakufupi ndi kwawo, ndinkapita kukamuona.

Juliana ankangokhala chigonere ndipo nthawi zambiri ankangosuzumira pawindo. Zinkandimvetsa chisoni kwambiri ndikakhala naye chifukwa sankandikumbukiranso. Ngakhale kuti ankandiyang’anitsitsa, ankaoneka kuti sakundizindikira ngakhale pang’ono. Tsiku lina ndinamufunsa kuti: “Kodi mumaganizirabe za Yehova?” Ndinamuuza nkhani inayake imene inandichitikira n’kumufunsa mafunso ena, koma ankaoneka kuti palibe chimene akumva. Ndiyeno ndinayamba kumuimbira nyimbo. Kenako zimene zinachitika zinandikhudza kwambiri.

Juliana anatembenuka n’kumandiyang’anitsitsa, ndipo nayenso anayamba kuimba. Kenako ndinasiya kuimba nyimboyo chifukwa sindinkaidziwa yonse m’chilankhulo chachitagalogi. Koma Juliana anapitirizabe kuimba. Anakumbukira mawu a ndime zonse zitatu za nyimboyo. Kenako, ndinapempha munthu amene ndinali naye kuti athamange akabwereke buku la nyimbo kwa munthu winawake wa Mboni amene ankakhala chapafupi. Iye anakabwerekadi n’kubwera nalo mwamsanga. Sindinkadziwa nambala ya nyimboyo, koma zinangochitika kuti nditatsegula bukulo, ndinangofikira pa nyimbo yomwe ndimafunayo. Ndiyeno tinaimbira limodzi nyimbo yonseyo. Kenako ndinamufunsa Juliana ngati ankakumbukiranso nyimbo zina, ndipo iye anayamba kuimba nyimbo inayake yachikondi yakale kwambiri ya ku Philippines.

Ndinamuuza Juliana kuti: “Sindikutanthauza nyimbo ya pawailesi, koma nyimbo imene timaimba ku Nyumba ya Ufumu.”a Kenako ndinayamba kuimba nyimbo ina ya m’bukulo, ndipo Juliana anayambanso kuimba nawo. Nkhope yake yonse inayamba kuwala. Sankaonekanso ngati mmene ndinamupezera poyamba, koma anayamba kumwetulira mosangalala kwambiri.

Pa nthawiyi n’kuti anthu ena oyandikana nawo nyumba atabwera kudzaona kuti nyimbozi zikuchokera kuti. Iwo anaima panja, pawindo, n’kumasuzumira uku akumvetsera nyimbozo. Zinali zosangalatsa kwambiri kuona mmene nyimbozo zinamukhudzira Juliana, ndipo iye anatha kukumbukira mawu a nyimbozo.

Zimenezi zinandiphunzitsa kuti nthawi zina simungadziwe zimene zingakhudze mtima wa munthu amene sakuthanso kulankhula kapena kudziwa bwinobwino zimene zikuchitika. Mwina nyimbo ndi imene ingathandize.

Patangopita nthawi yochepa zimenezi zitachitika, Juliana anamwalira. Ndinakumbukira nkhani ya Juliana pamene ndinkamvetsera nyimbo zatsopano zokhudza mtima kwambiri zimene Mboni za Yehova zinatulutsa mu 2009. Ngati mutafuna nyimbo zotsitsimulazi, mukhoza kufunsa Mboni za Yehova zakwanuko kuti zikuuzeni mmene mungazipezere.

[Mawu a M’munsi]

a Nyumba ya Ufumu ndi malo amene Mboni za Yehova zimachitirako misonkhano mlungu uliwonse.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena