Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w90 8/15 tsamba 3-4
  • Kodi Kukhulupirira Kuikidwiratu Kumalamulira Moyo Wanu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Kukhulupirira Kuikidwiratu Kumalamulira Moyo Wanu?
  • Nsanja ya Olonda​—1990
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mbali ya Chipembedzo
  • Kuzungulitsa Ndalama ndi Kupenda Nyenyezi
  • Kodi N’chikonzero cha Mulungu Kapena Zangochitika?
    Galamukani!—1999
  • Kodi Baibulo Limaphunzitsa za Kukhulupirira Choikidwiratu?
    Nsanja ya Olonda—1996
  • kodi Kuikidwiratu Kuyenera Kulamulira Moyo Wanu?
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Kufunafuna Tsogolo la Munthu
    Galamukani!—1999
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda​—1990
w90 8/15 tsamba 3-4

Kodi Kukhulupirira Kuikidwiratu Kumalamulira Moyo Wanu?

MU September 1988 tsoka linakantha. Madzi osalamulirika pa mathiriro aakulu a mitsinje ya Ganges ndi Brahmaputra anakwera kwa mamita 9 ndi kusefukira ku mbali zitatu mwa zinayi za Bangladesh. Anthu zikwi zambiri anamizidwa. Anthu ena 37,000,000 anasiyidwa opanda pokhala. Mtunda wokwanira makilomita 60,000 a misewu unazimiririka.

Popeza kuti zigumula zoterozo zakantha Bangladesh kwa nthaŵi ndi nthaŵi, nyuzipepala ina inatcha dzikolo kukhala “Mathiriro Atsoka.” Kunena koteroko kukusonyeza zimene anthu ambiri amalingalira kukhala zochititsa masoka oterowo: tsoka, kapena kuikidwiratu.

Ngakhale kuti ena angaganize kuti kuikidwiratu sikulamulira moyo, malingaliro a kuikidwiratu ngofala padziko lonse. Kodi nchifukwa ninji ambiri chotero amakhulupirira kuikidwiratu, ndipo kodi choikidwiratu ndicho chiyani?

Mbali ya Chipembedzo

Liwu lakuti “kuikidwiratu” limachokera ku liwu Lachilatini lakuti fatum, kutanthauza “chimene chalankhulidwa.”a Akatswiri a kuikidwiratu amakhulupirira kuti zochitika nzokhazikidwiratu pasadakhale ndikuti anthu ngosatha kusintha zinthu. Lingaliro limeneli lafalitsidwa ndi zipembedzo zosiyanasiyana ndipo laumba malingaliro a akhulupiriri mamiliyoni ambiri. Kuyang’ana pa zipembedzo zitatu zazikulu kwambiri za padziko kumasonyeza kuti kuikidwiratu kuli ndi mafotokozedwe osiyanasiyana​—osiyanasiyanadi mofanana ndi mpangidwe wa akachisi Achihindu, misikiti Yachisilamu, ndi matchalitchi a Chikristu Chadziko.

Mwachitsanzo, Asilamu okwanira 900 miliyoni a padziko, amachilikiza kuti kuikidwiratu (Kismet) kumakhazikitsidwa ndi chifuniro chaumulungu.b Qur’ān imalengeza kuti: “Palibe choipa chimene chimagwera dziko lapansi . . . , koma chimakhala cholembedweratu m’bukhu chisanachitike.” “Ndipo moyo sudzafa koma uli ndi nyengo yokhala ndi polekezera; yololedwa ndi Allah.”​—Surah 57:22; 3:145.

Karma ndi lamulo la chochititsa ndi chiyambukiro​—iyi ndi mbali ina ya kuikidwiratu​—imene imayambukira miyoyo ya Ahindu pafupifupi 700 miliyoni padziko. Kumalingaliridwa kuti zochitika zimene zimachitika m’moyo wa Mhindu pamene ali ndi moyo zimalamulidwa ndi zochita zake za kuvala thupi lanyama kwapapitapo. Garuda Purana, bukhu lakale Lachihindu, likuti: “Ziri ntchito za munthu ameneyu pa kukhalapo kwake kwapapitapo zimene zimagamula mtundu wa cholengedwa chake chotsatira, limodzinso ndi mtundu wa matenda, kaya akuthupi kapena amaganizo, amene adzakhala mnkhole wake . . . Munthu amapeza m’moyo zomwe zaikidwiratu kwa iye.”

Kodi bwanji ponena za pafupifupi ziŵalo 1,700 miliyoni za Chikristu Chadziko? Kunena zowona, ena m’Chikristu Chadziko amanena kuti aloŵa m’malo kuikidwiratu ndi Mulungu, ndipo choikidwiratu achilowa m’malo ndi kulinganizidwiratu. Koma Encyclopædia of Religion and Ethics ikuvomereza kuti: “Sizinganenedwe kuti Chikristu . . . nchowonjoledwa ku kukhulupirira Kuikidwiratu.” Zipembedzo zina zimatchukitsabe chikhulupiriro cha wokonzanso wa m’zaka za zana la 16 Martin Luther, amene pa nthaŵi ina ananena kuti munthu “ngwopanda ufulu mofanana ndi chidutswa cha mtengo, thanthwe, chigulumwa, kapena chulu cha mchere.”

Kuzungulitsa Ndalama ndi Kupenda Nyenyezi

Ngakhale kuti malingaliro osasinthika oterowo tsopano azimiririka m’zikhulupiriro za Chikristu Chadziko chenicheni, katswiri wa zaumulungu wina anavomereza kuti ziŵalo zake zambiri zimavomerezabe chikhulupiriro cha “mpangidwe wakunja.” Mu mpangidwe umenewo, kuikidwiratu kumalondoledwa mwakamodzikamodzi ndi kukhalitsidwa machitachita achikristu a apa ndi apo. Inu mwachidziŵikire mumadziŵa za anthu ambiri amene kwanthaŵi ndi nthaŵi amazungulitsa ndalama pochonderera mwaŵi, kapena kuikidwiratu. Ngakhale kuti angayese kunyalanyaza chimenechi kukhala mwambo chabe, iwo amapitirizabe kuchichita, ndipo, nthaŵi zina, zimawoneka kugwira ntchito kwa iwo. Mwachitsanzo, The New York Times posachedwapa inasimba kuti munthu wokhala mu United States anapeza kobiri imene chithunzi cha mutu chinali kumwamba pambuyo pogula matikiti a lotale. Iye anati: “Nthaŵi zonse zimene ndinapeza kobiri yokhala ndi mutu kumwamba, chinachake chabwino chinandichitikira.” Pa chochitikachi, iye amapata mphotho ya madola 25.7 miliyoni. Kodi mukuganiza kuti kukhulupirira kwake mwaŵi, kapena kuikidwiratu, kwachepa?

Anthu ena amatsutsa za kuzungulitsa ndalama. Komabe, iwo angakhulupirire kuti mtsogolo mwawo mwalinganizidwa ndi kayendedwe ka nyenyezi​—mbali ina ya kuikidwiratu. Kumpoto kwa Amereka kokha, manyuzipepala okwanira 1,200 amakhala ndi madanga a kupenda nyenyezi. Kufufuza kumodzi kunasonyeza kuti achichepere a ku United States okwanira 55 peresenti amakhulupirira kuti kupenda nyenyezi kumagwiradi ntchito.

Inde, kaya kumatchedwa Kismet, Karma, Mulungu, mwaŵi, kapena nyenyezi, kukhulupirira kuikidwiratu kwakhala kofala padziko lonse ndipo kwatero kwa zaka zambirimbiri. Mwachitsanzo, kodi munkadziŵa kuti mwa anthu a m’mbiri ondandalitsidwa panopawa, mmodzi yekha ndamene sanakhulupirire choikidwiratu? Kodi ndani amene sanatero? Ndipo kodi ndimotani mmene kalingaliridwe kake pa kuikidwiratu kangayambukirire kanu?

[Mawu a M’munsi]

a The Encyclopedia of Religion, Volyumu 5, tsamba 290, ikulongosola kuti: “KUIKIDWIRATU. Liwu lotengedwa ku Lachilatini lakuti fatum (chinachake cholankhulidwa, chilengezo chaulosi, choneneratu, chosankha chaumulungu).”

b “Kismet njosiyana ndi Kuikidwiratu kokha chifukwa chakuti imalozeredwa kukhala Chifuniro cha mphamvu zonse; kuchonderera kwa munthu konse motsutsana ndi chirichonse cha ziŵirizi nkosaphula kanthu.”​—The Encyclopædia of Religion and Ethics ya Hastings, Volyumu V, tsamba 774.

[Bokosi patsamba 4]

KODI NDANI ANAKHULUPIRIRA KUIKIDWIRATU?

Maskarīputra Gośāla Yesu Kristu

Wodzikana mwachipembedzo Muyambitsi wa Chikristu, wa m’zaka

Wachimwenye, wa m’zaka za zana loyamba C.E.

za zana la 6/5 B.C.E.

Zeno wa ku Citium Jahm, mwana wa Safwān

Wanthanthi Wachigiriki, wa Mphunzitsi Wachisilamu,

m’zaka za zana la 4/3 B.C.E. wa m’zaka za zana la 8 C.E.

Publius Vergilius Maro John Calvin

Wolemba ndakatulo Wachiroma, Katswiri wa zaumulungu ndi

wa m’zaka za zana wokonzanso Wachifalansa, wa

loyamba B.C.E. m’zaka za zana la 16 C.E.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena