Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w90 9/1 tsamba 10-14
  • Kukhulupirira Yehova Kumadzetsa Chimwemwe

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kukhulupirira Yehova Kumadzetsa Chimwemwe
  • Nsanja ya Olonda​—1990
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kupeza Chifuno m’Moyo mu Indiya
  • Kubwereranso ku Mangalande
  • Uminisitala Wofutukulidwa m’Canada
  • Zaka za Kuletsedwa
  • Moyo Wanga Monga Woyang’anira Woyendayenda
  • Mwaŵi Wowonjezereka wa Kutumikira
  • Moyo Wanga m’Gulu Lotsogozedwa ndi Mzimu la Yehova
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Yehova Amachita Mokhulupirika
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Moyo Waulemerero Potumikira Yehova
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Yehova Wandidalitsa Kwambiri Chifukwa cha Zimene Ndinasankha
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2018
Nsanja ya Olonda​—1990
w90 9/1 tsamba 10-14

Kukhulupirira Yehova Kumadzetsa Chimwemwe

MONGA MOMWE YASIMBIDWIRA NDI JACK HALLIDAY NATHAN

Mwinamwake munamvapo kanenedwe kakuti, “kubadwa wolemera.” Eya, pamene ndinabadwa kalelo mu 1897, zimenezo zinali zowona pafupifupi m’lingaliro lenileni kwa ine.

CHINALI chaka chachi 60 cha kulamulira kwa Mfumukazi Victoria, kusangalalira kwake zaka makumi asanu ndi limodzi. Ana obadwa chaka chimenecho mu Mangalande anapatsidwa chuma. Ulamuliro wa Britain unali muulemerero wake, ukumapindula ndi chuma chochuluka cha m’maindasitale m’dzikomo ndi kuchokera ku malonda ake olemera aku maiko omwe ankalamulira.

Agogo ŵanga ŵamuna adali Myuda, ndipo bambo wanga anafikira kukhala katswiri Wachihebri, wodziŵa bwino Malemba Achihebri. Koma agogo ŵanga ŵakazi anali mwana wamkazi wa bishopu wa Angilikani, ndipo chifukwa cha chisonkhezero cha agogo, abambo ŵanga analandira Yesu Kristu monga Mesiya. Mabuku a Charles Taze Russell anasonkhezera makolo anga aŵiriwo, chotero sitinakhulupirire konse Utatu kapena chiphunzitso cha moto wa helo.

M’nthaŵi yaubwana wanga, akavalo adaali chikhalirebe choyendera chachikulu mu Mangalande, ndipo panali magareta oŵerengeka osakokedwa ndi akavalo, kapena kuti magalimoto. Mu 1913, chifukwa chakukonda kwanga akavalo, ndinagwirizana ndi gulu lamtengatenga wapa akavalo la asirikali a m’dzikomo (militia). Pamene Nkhondo Yadziko I itaulika, ndinatsamutsidwira kugulu lomenya nkhondo ndikuperekedwa kubwalo lankhondo la Girisi, kumene ndinakadwala malungo. Pambuyo pake, ndinatumizidwa kubwalo lankhondo lakumadzulo m’Faransa monga wogwiritsira ntchito mfuti yachiwaya ndipo pomalizira pake ndinatengedwa wandende mu 1917 ndi Ajeremani.

Kupeza Chifuno m’Moyo mu Indiya

Nkhondo itatha mu 1918, sindinathe kupeza ntchito mu Mangalande, chotero ndinagwirizananso ndi gulu lankhondo ndikupita ku Indiya monga m’modzi wa gulu lankhondo lopereka chitetezo. M’May 1920 malungo anayambiranso, ndipo ndinatumizidwa kumapiri kuti ndikapeze bwino. Kumeneko ndinaŵerenga mabuku onse omwe ndinatha kupeza, kuphatikizapo Baibulo. Kuŵerenga Malemba kunakulitsa chikondwerero changa m’kubweranso kwa Ambuye.

Miyezi ingapo pambuyo pake, ndiri m’Kanpur, ndinayambitsa kagulu ka ophunzira Baibulo, nchiyembekezo chakuphunzira zochuluka ponena za kubweranso kwa Ambuye. Ndinakumana ndi Fredrick James kumeneko, amene kale anali msirikali Wachibritishi amene tsopano anali Wophunzira Baibulo wachangu. Iye anandifotokozera kuti Yesu anali atakhalapo chiyambire 1914, wosawoneka kwa anthu. Iyi inali mbiri yosangalatsa koposa kwa ine imene sindinamvepo ndikale lonse. Chinthu choyamba chimene ndinafuna kuchita ndicho kuchoka m’gulu lankhondo. Mwazi wokhetsedwa ndi imfa za nkhondo ya ku Ulaya zinandinyansa. Ndinafuna kukhala mishonale wamtendere ndi kulalikira mbiri yabwino imeneyi yonena za kukhalapo kwa Kristu.

Komabe, gulu lankhondo sirinalole kundimasula. M’malo mwake, ananditumiza kumadzulo kwa Indiya, tsopano Pakistan. Ndiri komweko, ndinaŵerenga Studies in the Scriptures, lolembedwa ndi Charles Taze Russell, ndipo ndinakhutiritsidwa koposa ndikale lonse kuti ndiyenera kuyankha kuchiitano chakulalikira. Ndinayamba kukhala ndi atulo oipa amene anandichititsa tondovi. Mosoŵa chochita ndinalembera kalata Mbale James, amene anandiitanira kunyumba kwake ku Kanpur. Tsiku limene ndinafika linali tsiku la Chikumbutso cha imfa ya Ambuye. Tsikulo linali ndi chisonkhezero chachikulu pamoyo wanga​—ndinatsimikiza ponse paŵiri kukhala mbeta ndi kupanga uminisitala wanthaŵi zonse kukhala chonulirapo changa m’moyo.

Kubwereranso ku Mangalande

Kumapeto kwa 1921, ndinabwezeredwanso ku Mangalande, ndipo m’ngululu ya 1922, ndinasiya kugwira ntchito m’gulu lankhondo. Chirimwe chimenecho J. F. Rutherford, pulezindenti wachiŵiri wa Watch Tower Society, anabwera ku Mangalande, ndipo ndinapita ndi makolo anga kukamvetsera nkhani yake ku Royal Albert Hall, London. Pambuyo pake, ndinasonkhezeredwa kutumikira pa Beteli, monga momwe maofesi anthambi a Watch Tower Society amatchedwera, komabe ndinalimbikitsidwa mokoma mtima kuchita ntchito yaukopotala (kulalikira kwanthaŵi zonse) choyamba. Chotero ndinaleka ntchito yanga ndikulandira gawo kummwera kwa Mangalande. Ndiri wosazoloŵera, ndi ndalama zisanu (50 cents, U.S.) m’thumba langa, ndi kukhulupirira Yehova, ndinayamba ntchito yanga monga minisitala wanthaŵi zonse. Pafupifupi March 1924, ndinaitanidwa ku Beteli.

Komabe, chaka chotsatira, ndinapemphedwa kuchoka pa Beteli, ndipo ndinasweka maganizo, ndikumalingalira kuti ndinali kulangidwa kaamba ka chinthu chimene sindinachite. M’nthaŵi yochepa imeneyo, Beteli inali itafikira kukhala malo a moyo wonse. Koma mwakuika vutolo m’manja mwa Yehova m’pemphero ndikukhulupirira kuti chifuniro chake chidzachitika, ndinatha kupitiriza mwachisangalalo m’gawo langa laupainiya limene ndinapatsidwa. M’May 1926, ndinaitanidwanso ku Beteli, kumene ndinakhala zaka 11 zotsatira.

Mbale Rutherford anachezeranso Mangalande mu 1936 ndipo anandipempha kupita ku Canada kukakhala ndi phande m’ntchito Yaufumu kumeneko. Komabe, chifukwa chakusamvetsetsa bwino, ndinachititsa Mbale Rutherford kusandivomereza kupita chifukwa chakuti ndinavumbula mawu ena achinsinsi. Ndikukumbukirabe mawu ake enieniwo: “Jack, sindingathe kukudalira. Ng’amba matikiti ako!” Chinali chokumana nacho choziziritsa m’maondo chotani nanga! Koma icho chinali chilango chofunikiradi kwa ine, ndipo pambuyo pake, limodzi ndi mbale wina, ndinagaŵiridwa monga mpainiya kwa miyezi isanu ndi itatu yotsatira. Mwaŵi wautumiki umenewu unanditsitsimula, ndipo ndinaphunzira kuchokera ku chilangocho.

Uminisitala Wofutukulidwa m’Canada

Mkati mwa kucheza kwake kotsatira ku Mangalande pafupifupi chaka chimodzi pambuyo pake, Mbale Rutherford anabweretsanso nkhani ya Canada. Ndinali wofunitsitsa mwaŵi umenewo ndipo mosazengereza ndinalandira gawo limenelo. Pambuyo pakutumikira kwa miyezi yoŵerengeka pa Beteli ya Canada, ndinagaŵiridwa monga woimira Saisaite woyendayenda kummwera chakumadzulo kwa Ontario. Mipingo yambiri kumeneko inali yaing’ono ndipo inafunikira chilimbikitso champhamvu. Koma zaka zoyambirira zinali zosangalatsa chotani nanga, mosasamala kanthu za mavuto akuthupi a mphepo yoipa ndi kuvuta kwa zoyendera!

Sindidzaiŵala konse chikondi ndi chiyamikiro chauzimu cha mpingo wina waung’ono wa Amwenye amomwemo pafupi ndi Brantford. Inali nthaŵi yachisanu, ndipo chipale chofeŵa chinali chochuluka, kupangitsa vuta ku galimoto langa la Model T Ford kudutsa. Palibe amene anali kundiyembekezera, ndipo pamene ndinafika, ndinapeza kuti abalewo adapita m’nkhalango kukatola nkhuni. Chotero ndinakawafunafuna, chipale chofeŵa chikufika m’chuuno. Pamene ndinawapeza pomalizira pake, anadabwa, komabe anali achimwemwe kundiwona. Anasiya zonse zimene ankachita, nabwerera kunyumba, ndikulinganiza msonkhano madzulo amenewo.

Pa Beamsville wapafupi, abale okhulupirika ndi ine tinalimbana kwa miyezi yambiri ndi akulu osankhidwa mwakuchita masankho ndiponso ndi ampatuko. Unali mwaŵi wotani nanga kuwona mmene mzimu wa Yehova unagwirira ntchito kuwongolera mkhalidwewo! Kukhulupirira Yehova ndi kukhulupirika ku gulu lake kunatulukira m’madalitso ambiri ku mipingoyo mkati mwa zaka zoyambirirazo. Ana ambiri a mipingo imeneyo anakula ndikutenga mathayo aupainiya, kupita ku Beteli, kusangalala ndi magawo aumishonale, ndikukhala oyang’anira oyendayenda. Sindinaiŵale chisangalalo chakukhala pamodzi ndi mabanja Achikristu okhulupirika amene anatulutsa ana abwino chotero. Mabanja ameneŵa anakhala banja langa, ndi ana awo anakhala ana anga.

Zaka za Kuletsedwa

Mkati mwa chipwirikiti chankhondo mu 1940, ntchito ya Mboni za Yehova inaletsedwa. Zinali zoziziritsa m’maondo chotani nanga! Zilengezo zaboma zoulutsidwa pawailesi zinatiuza kuti tipereke mabuku athu kupolisi, zolembapo zathu zampingo, ndi makiyi athu a Nyumba Yaufumu. Pozindikira kufulumira kwa chochitikacho, ndinazungulira m’mipingo ndikuwalangiza kubisa mabuku awo ndi zolembapo. Abale analimbikitsidwa kumakumana m’nyumba wamba, panyumba yosiyana mlungu uliwonse. M’kupita kwanthaŵi mipingoyo inayambiranso uminisitala wakukhomo ndi khomo, akumagwiritsira ntchito Baibulo lokha. Izi zinatsimikizira kukhala dalitso, popeza kuti tonsefe tinaphunzira kugwiritsira ntchito Mabaibulo bwinopo.

Pambuyo pake m’chaka chimenecho tinalandira mtokoma waukulu wa kabuku ka End of Nazism kuchokera ku United States. Kuloŵetsa mabuku oletsedwa ameneŵa m’Canada kunafunikira kuchenjera kwakukulu. Abale ena ananyamula asirikali opempha matola m’njira, amene anakhala pamabokosiwo, mosadziŵa akumaphimba kabuku koletsedwako. Ndiyeno mmaŵa ena m’November, pakati pa 3 ndi 6 koloko, dziko lonse linakutidwa ndi Mboni zimene zinasiya kope la kabuku kameneka pamakomo a nyumba zambiri m’Canada.

Mkati mwa zaka zakuletsedwa zimenezo, ndinapitiriza muuminisitala waupainiya kudera lakumadzulo kwa Canada la British Columbia. Kuletsedwa kusanayambe, abalewo anagwiritsira ntchito bwato kufikira anthu m’midzi yakutali m’mphepete mwanyanja kuchokera ku Vancouver mpaka ku Alaska. Pamene chiletso chinayamba, mabuku ambiri anatengedwa pabwato, kotero kuti Mbonizo zinawasiya kwa anthu okondwerera paulendo wopita kudoko kumene bwatolo linayenera kusungidwako. Pambuyo pake, ndinatenga bwato losodzera kukafuna mabuku ameneŵa, kenaka, m’nyengo yosodza nsomba za salmon, ndinachita makonzedwe oti akatengedwe ndi abale kuchokera kwa anthu okondwerera ameneŵa. M’kupita kwanthaŵi mabukuwo anabweretsedwa ku Vancouver kaamba ka kugaŵiridwa kwakukulu, ali obisidwa m’mabwato ambiri osodzera.

Chakumapeto kwa 1943, tinalandira uthenga wakuti kuletsedwa kwa Mboni za Yehova kwatha. Komabe, sikunathe pa Watch Tower Society. Chotero tinapitiriza monga kale, kugwiritsira ntchito Baibulo lokha muuminisitala wathu wakunyumba ndi nyumba. Koma tsopano tinakhoza kudzidziŵikitsa poyera monga Mboni za Yehova. Pamene kuletsedwa kunayamba, tinali pafupifupi Mboni zokwanira 6,700; pamene kunatha, tinawonjezereka kukhala okwanira 11,000!

Moyo Wanga Monga Woyang’anira Woyendayenda

Monga woimira wa Sosaite woyendayenda, ndinafola mamailo ambirimbiri mkati mwa zaka zochepekera zotsatira, kugwira ntchito ndi mipingo ndikuilimbikitsa. M’nyengo yachisanu, ndinatsagana ndi abale m’choyendera chapadera chotchedwa caboose. Limeneri linali gareta lopanda magudumu lokokedwa ndi akavalo, lophimbidwa kouse konse, ndilokhala ndi chitofu chankhuni m’kati mwake ndi chumuni. Kaŵirikaŵiri, tinkalaŵira m’mbandakucha titakweramo okwanira asanu ndi mmodzi, tinkayenda kudutsa m’chipale chofeŵa chokhuthala mamailo 20 kapena kuposerapo, tikumafikira mafama m’njiramo. Woyendetsa anayenera kukhala maso chifukwa chakuti chipale chomayenda chikakhoza kugubuduza caboose ameneyo, ndikukhuthula okweramo limodzi ndi makala otentha apachitofu chankhunicho.

Mu 1947, ndinaikidwa kuyang’anira chigawo choyamba m’dzikomo, chimene chinaphatikizapo dziko lonselo. Ndinatumikira pamsonkhano wadera pafupifupi mlungu uliwonse. Misonkhano inachitidwira m’mabwalo amaseŵera achipale chofeŵa, mabwalo ampira, mabwalo a maseŵera othamanga, maholo achitaganya, ndi maholo a anthu onse. Makonzedwe a misonkhano imeneyi anafunikira chisamaliro chachikulu programu isanayambe. Mu 1950, Frank Franske anaikidwa kukhala woyang’anira chigawo wachiŵiri m’Canada, ndipo pambuyo pake ena asanu a oyang’anira oyendayenda amenewa anawonjezeredwa.

M’zaka zonsezo, ndayenda pandege zazing’ono, pamabwato osodzera, pazombo zazikulu zoyenda pachipale chofeŵa ndi pazoyendera zina zapachipale zotchedwa bombardier, ndi ndege zapachipale chofeŵa (zoyendera zokhala ndi injini kumbuyo ndi chowongolera kutsogolo kwake), ndi pazoyendera zina zozoloŵereka kwambiri​—tireni, basi, ndi magalimoto. Nthaŵi zina, tinalikuuluka m’dege pamwamba pansonga za Phiri lalikulu la Rocky, ndiyeno kuzolikira m’zigwa zakuya ndi zobisika kuti tifikire timagulu takutali ta abale.

Ndazungulira m’Canada yonse nthaŵi zambiri. Ndinakhalapo m’zinyumba zopangidwa ndi zikuni zozizira kwambiri kotero kuti ndinakhoza kuwona mpweya wathu mmamaŵa ndiponso m’nyumba zam’mafama zopanda ziŵiya zamakono. Komabe, m’zonsezi, ndinali ndi maganizo akukhutira kwakukulu, podziŵa kuti ndinalikuchita ntchito ya Yehova, kulimbikitsa anthu a Yehova.

Mwaŵi Wowonjezereka wa Kutumikira

Kwazaka 33 zapitazo, ndakhala ndi mwaŵi wakukhala chiŵalo cha banja la Beteli la Canada, limodzinso ndikutumikira monga wokamba nkhani pamsonkhano ku Mangalande, Ulaya, Afirika, Australia, New Zealand, ndi ku Far East. Ku Australia, ndinakumana ndi mwana wamkazi wa Mbale James, amene anandilimbikitsa kwambiri ku Indiya. Mbale James sanakhalepo mishonale, komabe anapitirizira choloŵa chauzimu kwa banja lake.

Lerolino ndiri wozingidwa ndi mazana ambiri a amuna ndi akazi achichepere pa Beteli ya Canada. Kumalimbikitsa ndi kusonkhezera kuwona njira imene amagwiritsirira ntchito nyonga yawo yaunyamata muutumiki wa Yehova. Maso anga akuwona mwachimbuuzi, koma achicheperewa amandiŵerengera. Miyendo yanga yafooka, koma amanditenga kupita nawo muuminisitala wakumunda. Ena amafunsa mmene ndimachitira ndi mavuto anga athanzi ochititsidwa ndi ukalamba. Eya, mfundo njakuti, ndimaphunzira Mawu a Mulungu tsiku lirilonse. Izi zimasunga maganizo anga ndi mtima ziri zosumikidwa pazinthu zauzimu.

Zowonadi, wakhala mwaŵi waukulu kuyenda ndi kulankhula ndi Atate wanga wakumwamba, Yehova, kwazaka 69 za moyo wodzipereka, 67 za izo ndazithera muutumiki wanthaŵi zonse. Nthaŵi zonse ndapeza kuti Yehova ali Mulungu wachikondi, ndi wachifundo, wokhululukira zofooka za anthu ndikupereka mphamvu ndi nyonga kwa omkhulupirira. Chiyembekezo changa ndicho kusunga umphumphu wanga ndi kukhulupirika kwa Yehova ndi gulu lake kufikira mapeto, kukhulupirira lonjezo lakuti panthaŵi yake ndidzagwirizana ndi Ambuye wanga wokondedwa, Yesu Kristu, limodzinso ndi abale ndi alongo anga ambiri okhulupirika muulemerero wakumwamba.​—Salmo 84:12.

[Chithunzi patsamba 12]

Ndege zapachipale chofeŵa zinayenda modutsa dzikolo pamaliŵiro ofika 80 makilomita pa ora

[Chithunzi patsamba 13]

M’nyengo yachisanu, camboose wokokedwa ndi akavalo anagwiritsiridwa ntchito pochitira umboni m’mafama a ku Canada

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena