Yehova Amachita Mokhulupirika
YOSIMBIDWA NDI PETER PALLISER
Munali mu December 1985. Tinasangalala kwambiri pamene ndege inayamba kutsika kuti itere pa bwalo lalikulu la ndege mu Nairobi, Kenya. Tili m’galimoto kuloŵa mu mzindawo, tinakumbukira zakale pamene tinaona zinthu zomwe tinakumbukira ndiponso kumva phokoso lozoloŵereka.
TINABWERA ku Kenya kudzakhala nawo pa Msonkhano Wachigawo wa Mboni za Yehova wa “Asungiliri a Umphumphu.” Zaka khumi ndi ziŵiri kumbuyoko, ine ndi mkazi wanga tinakakamizidwa kuchoka m’Kenya, chifukwa ntchito yathu yolalikira inaletsedwa. Tinkakhala kumeneko pa Beteli, dzina la nyumba za nthambi za Mboni za Yehova. Tinapeza zodabwitsa zosangalatsa chotani nanga pamene tinapitakonso kukacheza!
Yemwe anali kuthandiza kukonza chakudya cha masana pa Beteli anali Mboni yachitsikana yemwe tinamudziŵa kuyambira ali ndi zaka ziŵiri. Pafupifupi mamembala asanu ndi mmodzi a banja la Beteli anali anthu omwe tinawadziŵa adakali ana. Chinali chosangalatsa chotani kuwaona tsopano ali akuluakulu, pamodzi ndi mabanja awo, onse adakali olimbikira mu utumiki! Mulungu wathu, Yehova, anawasamalira mogwirizana ndi lonjezo la Baibulo: “Ndi achifundo inu mudzadzionetsa wachifundo.” (2 Samueli 22:26) Ndinaona kusiyana kotani nanga pakati pa moyo wanga wapaunyamata ndi moyo wopatsa mphotho womwe achinyamatawa anali nawo!
Moyo Wapaunyamata Wopanda Cholinga
Ndinabadwira mu Scarborough, England, pa August 14, 1918. Zaka ziŵiri pambuyo pake amayi anga ndi mlongo wanga wopeza anapita ku Canada, choncho ndinatha zaka zitatu zotsatira ndikukhala ndi atate anga, amayi wawo, ndi alongo awo. Pamene ndinali ndi zaka zisanu, Amayi anandiba napita nane ku Montreal, Canada. Patatha zaka zinayi ananditumizanso ku England kuti ndikakhale ndi Bambo ndi kuyamba sukulu.
Amayi ndi mlongo wanga wopeza amandilembera makalata pafupifupi miyezi isanu ndi umodzi iliyonse. Pa mapeto pa makalata awo, amalemba zofuna zawo kuti ndidzakhale nzika yabwino, yomvera Mfumu ndiponso dziko. Mwinamwake mayankho anga amaŵakhumudwitsa chifukwa ndimalemba kuti ndimakhulupirira kuti kukonda dziko lako ndiponso nkhondo nzoipa. Komabe, chifukwa chopanda chitsogozo cholongosoka, mzaka zanga zapaunyamata, ndinkangotsatira zilizonse.
Ndiye mu July 1939, milungu isanu ndi umodzi Nkhondo ya Dziko II isanayambe, ndinalembedwa usilikali m’gulu la nkhondo la Britain. Ndinali ndi zaka 20 zokha. Mwamsanga gulu lathu linatumizidwa kumpoto kwa France. Pamene ndege za nkhondo za Germany zimafika, ang’onoang’onofe timatenga mfuti zathu nkumaziombera. Timakhala mwa mantha. Tinathaŵa asilikali a ku German amenewo, ndipo ndinali mmodzi wa omwe anasamutsidwa kuchokera pa Dunkirk mlungu woyamba wa June 1940. Ndimachitabe mantha ndikakumbukira kuona mitembo ya gulu lonse la asilikali ili ngundangunda pa gombe la nyanja. Ndinapulumuka ngozi imeneyo ndipo ndinafika pa Harwich kummawa kwa England pa sitima yaing’ono yonyamula katundu.
Chaka chotsatira, mu March 1941, ndinatumizidwa ku India. Kumeneko ndinaphunzitsidwa umakanika. Nditatha nthaŵi ndili m’chipatala chifukwa cha matenda, ndinatumizidwa ku kampu ya asilikali ku Delhi, likulu la dziko la India. Ndinayamba kuganiza za mtsogolo ndili kuno, kutali ndi kwathu ndiponso ndidakali wosapezabe bwino. Makamaka ndimadabwa za chimene chimatichitikira tikafa.
Mtundu Watsopano Wakumvera
Mngelezi mzanga, Bert Gale, ndiye amene ndimagona naye chipinda chimodzi ku Delhi. Tsiku lina anati “zipembedzo ndi za Mdyerekezi,” ndemanga yomwe inadzutsa chidwi mwa ine. Mkazi wake anali atakhala Mboni ya Yehova, ndipo nthaŵi ndi nthaŵi amamtumizira mabuku ofotokoza za m’Baibulo. Limodzi la iwo, kabuku kotchedwa Hope, kanandisangalatsa. Nkhani yake yonena za chiyembekezo cha chiukiriro inanditonthoza.
Nthaŵi ina kumayambiriro kwa 1943, Bert analankhula ndi munthu wina wosakhala msilikali, mkaladi wobadwa kwa mzungu ndi mwenye, Teddy Grubert, yemwe tinkagwira naye ntchito limodzi pa kampu ya asilikali. Tinadabwa kumva kuti Teddy anali Mboni. Ngakhale kuti mu 1941 analetsa zofalitsa za Mboni za Yehova, anatitengera ku misonkhano ya Mboni mu Delhi. Mu mpingo waung’ono umenewo, ndinapeza mabwenzi enieni kwa nthaŵi yoyamba m’moyo wanga. Basil Tsatos, mbale wachikristu wachikulire wa ku Greece, anandikonda kwambiri ndipo anayankha mafunso amene ndinali nawo. Anapereka mayankho omveka bwino ochokera m’Baibulo pa mafunso monga akuti nchifukwa ninji timakalamba ndi kufa, chiukiriro, ndiponso dziko latsopano lachilungamo limene Mulungu analonjeza.—Machitidwe 24:15; Aroma 5:12; 2 Petro 3:13; Chivumbulutso 21:3, 4.
Kabuku kotchedwa Peace—Can It Last?, kofalitsidwa mu 1942, ndiko kanandigwira mtima kwambiri. Kanasonyeza kuti League of Nations ndiye “chirombo chofiiritsa.” (Chivumbulutso 17:3) Pogwira mawu chaputala 17, vesi 11, m’Chivumbulutso, kabukuko kanati: “Tsopano kunganenedwe kuti League ‘inalipo, ndipo kulibe.’” Popitiriza, kanati: “Chigwirizano cha maiko chimenechi chidzabukanso.” Mu 1945, pambuyo pa zaka zoposa zitatu, ndizo zenizeni zimene zinachitika, pamene bungwe la United Nations linapangidwa!
Pa nthaŵi ya chiletso cha mabuku a Mboni, ndinatha kuthandiza mabwenzi anga omwe ndinali nditawapeza kumenewo. Katoni ya mabuku a Peace—Can It Last? ikabwera, mpingo umandipatsa ine kuti ndisunge. Ndani akanalingalira zodzafufuza za mabuku oletsedwawo pa kampu ya asilikali? Nthaŵi iliyonse ndikamapita ku msonkhano, ndimatengako timabuku tingapo kuti abale azipezako. Ndinkabisa ngakhale mabuku ofotokoza za m’Baibulo awoawo akakhala ndi nkhaŵa kuti mwina adzawasecha m’nyumba zawo. Potsiriza, pa December 11, 1944, chiletso chinachotsedwa.
Kumvera kwanga chiphunzitso chachikristu kunaikidwa pa chiyeso pa chikondwerero cha Krisimasi mu 1943 chomwe chinakonzedwa chifukwa chakuti gulu lathu linali kutumizidwa kwina. Ndinakana kusangalala nawo, chifukwa ndinali nditaphunzira kuti Yesu sanabadwe mu nthaŵi yozizira mu December ndi kutinso Akristu oyambirira sankakondwerera Krisimasi.—Luka 2:8-12.
Pamene msonkhano wakuti “Alengezi Ogwirizana” unachitika mu Jubbulpore (Jubalpur) kuyambira pa December 27 mpaka 31, 1944, ndinali pakati pa 150 omwe anapezekapo. Ambiri mwa omwe anapita ku msonkhanowo anayenda pasitima za pamtunda kuchokera ku Delhi, mtunda wa makilomita 600. Sindidzaiŵala malo amene aja, pamene ndinaona gulu la Yehova likugwira ntchito.
Nthumwi za pamsonkhano zinapatsidwa malo ogona pa sukulu, mmene tinayimba nyimbo za Ufumu ndi kusangalala ndi mayanjano achikristu. Pa msonkhano umenewo ndinayamba kulalikira nawo, ntchito yomwe ndaikonda kwambiri kuyambira panthaŵiyo.
Utumiki wa Nthaŵi Zonse mu England
Ndinabwerera ku England mu 1946 ndipo posakhalitsa ndinayamba kusonkhana nawo mumpingo wa Wolverton. Ngakhale kuti tinali ndi ofalitsa Ufumu pafupifupi khumi okha, ameneŵa anandipangitsa kudzimva wolandiridwa, ndipo ndinapeza chisangalalo monga chomwe ndinali nacho pakati pa abale anga a ku India. Vera Clifton anaoneka kukhala munthu wokoma mtima kwambiri mu mpingomo. Pamene ndinazindikira kuti anali ndi cholinga chofanana ndi changa chokhala mpainiya, dzina la atumiki a nthaŵi zonse, tinakwatirana pa May 24, 1947. Ndinakonza nyumba yokoka (caravan) ndipo chaka chotsatira tinalandira gawo lathu loyamba lochitirako upainiya, tauni yakumidzi ya Huntingdon.
M’masiku amenewo tinkanyamuka mmamaŵa panjinga ulendo ku gawo la kumidzi. Timapumulako pang’ono masana kuti tidye masangweji basi. Kaya kukhale chimphepo kapena chimvula chotani, timabwerera kunyumba tili okondwa ndi okhutira chifukwa cha ntchito ya Ambuye.
M’kupita kwa nthaŵi tinafuna kuwonjezera utumiki wathu mwa kukalalikira “uthenga . . . wabwino” kwa anthu a m’maiko ena. (Mateyu 24:14) Choncho tinafunsira mwaŵi wokaloŵa nawo sukulu ya amishonale ya Gileadi ku South Lansing, New York, U.S.A. Potsirizira, tinaitanidwa m’kalasi ya 26 ya Gileadi yomwe inatsiriza maphunziro mu February 1956.
Kuwonjezera Utumiki Wathu mu Afirika
Gawo lathu la umishonale linali Northern Rhodesia (tsopano lotchedwa Zambia) mu Afirika. Titangofika, tinaitanidwa kukatumikira pa Beteli m’dzikomo. Monga mbali ya ntchito yanga pa Beteli, ndimayankha makalata a ku East Africa. Mu 1956, m’Kenya—limodzi la maiko a ku East Africa,—munali Mboni zinayi zokha, pamene mu Northern Rhodesia munali Mboni zoposa 24,000. Ine ndi Vera tinayamba kuganiza za mmene kukanakhalira bwino kukatumikira kumene kunali kusoŵa kokulira.
Ndiye, mosayembekezera, ndinaitanidwanso ku Sukulu ya Gileadi, nthaŵi ino kukachita kosi ya miyezi khumi ya oyang’anira. Ndinamusiya Vera ku Northern Rhodesia, ndipo ndinapita ku New York City, kumene Sukulu ya Gileadi inali panthaŵiyo. Nditatsiriza maphunziro mu November 1962, ndinatumizidwa ku Kenya kukakhazikitsa ofesi ya nthambi kumeneko. Panthaŵi ino Kenya anali ndi Mboni zoposa zana limodzi.
Pa ulendo wanga wobwerera ku Northern Rhodesia kukamutenga Vera, ndinayenera kuima mwachidule ku Nairobi, Kenya. Koma nditangofika, Bill Nisbet, womaliza sukulu ya Gileadi m’kalasi ya 25, anandiuza kuti panali mwaŵi wopeza chilolezo cha boma chokhalira m’Kenya pa nthaŵi yomweyo. Tinafikira ku imigireshoni, ndipo m’mphindi zochepa chabe, ndinapeza chilolezo chogwira ntchito zaka zisanu m’Kenya. Motero sindinabwererenso ku Northern Rhodesia; mmalo mwake, Vera ananditsatira ku Nairobi.
Titaphunzira Chiswahili pang’ono, tinayamba kulalikira ndi mpingo waung’ono wa mu Nairobi. Nthaŵi zina tikaŵerenga ulaliki wathu womwe tinalemba m’Chiswahili, mwini nyumba amanena kuti, “Sindimva Chingelezi!” Mosasamala kanthu za zimenezo, tinapirira ndipo pang’ono ndi pang’ono tinalaka vuto la chilankhulo.
Gawo lathu linaphatikizapo nyumba za nsanjika za maina a m’Baibulo monga akuti Yerusalemu ndi Yeriko. Anthu amasangalatsidwa, ndipo m’madera ameneŵa munachokera ofalitsa Ufumu atsopano ambiri. Ndi kukhudzidwa mtima ndi choonadi cha Baibulo kotani kumene anthu ameneŵa anali nako! Kukhulupirika ku Ufumu kunabweretsa mtendere pakati pa anthu a Yehova ndipo maganizo akuti fuko lathu ndi lapamwamba anazimiririka. Ngakhale maukwati pakati pa amafuko osiyana ankachitika, chinthu chomwe sichingachitike wamba pakati pa omwe sali Mboni.
Olengeza Ufumu atsopano amavomereza choonadi ndi mtima wonse. Mwachitsanzo, Samson, anali wofunitsitsa kuti choonadi cha Baibulo chiloŵerere m’dera la kwawo mwakuti ankapempha kuti apainiya atumizidweko. Anafika mpaka powonjezera nyumba yake m’chigawo cha Ukambani kuti apainiyawo azidzakhalamo. Posapita nthaŵi mpingo wa alengezi a Ufumu unakhazikitsidwa kumeneko.
Ndinakachezera abale m’dziko la ku East Africa la Ethiopia nthaŵi zambiri. Iwo anali kuchita avareji ya maola 20 pamwezi mu utumiki, mosasamala kanthu za kumangidwa, kumenyedwa, ndi kufufuzidwa kosalekeza. Nthaŵi ina mabasi aŵiri odzaza ndi abale ndi alongo a ku Ethiopia anayenda mlungu wonse, kudutsa njira ya m’mapiri yoopsa, kuti akapezeke pamsonkhano wachigawo ku Kenya. Khama lawo pofuna kuti mabuku a Ufumu azipezeka kwawoko linali loyamikirika. Ife ku Kenya tinali osangalala kuthandiza kuti aziwalandira.
Boma linaletsa ntchito yathu mu Kenya mu 1973, ndipo amishonale anakakamizidwa kuchoka. Panthaŵiyo tinali ndi Mboni 1,200 mu Kenya, ndipo ambiri a ameneŵa analipo pa bwalo la ndege kudzalaŵirana nafe. Kubwera kwawo kunapangitsa wapaulendo wina kufuna kudziŵa ngati tinali apadera mwanjira ina yake. Ine ndi Vera tinabwerera ku England ndipo tinapatsidwa gawo kumeneko, koma tinkalakalaka kubwerera ku Afirika.
Kubwerera ku Afirika
Choncho, miyezi pang’ono pambuyo pake, tinalandira gawo lathu latsopano, kupita pa Beteli ku Accra, likulu la Ghana dziko la kumadzulo kwa Afirika. Kuno imodzi mwa ntchito zimene ndinagaŵiridwa inandipangitsa kudzionera mavuto amene abale athu amakumana nawo kumeneko. Pamene ndinali wogula zakudya ndi zipangizo zina zofunika pa banja la Beteli, ndinadabwa ndi kukwera mitengo kwa zakudya. Kaŵirikaŵiri zinali zoti munthu sangathe kugula zomwe afuna. Kusoŵa kwa petulo ndi zitsulo za m’galimoto kumabweretsa mavuto ena apadera.
Ndinafika poyamba kuzindikira ubwino wa kuleza mtima, khalidwe limene abale athu a ku Ghana anali atakulitsa. Zinali zolimbikitsa kuona chimwemwe chimene anali nacho pamene ankapewa chiyeso chopeza zosoŵa za moyo wawo mwa kupereka ziphuphu. Zotsatira zake, anthu a Yehova ku Ghana anafika podziŵika bwino kwambiri chifukwa cha kuona mtima kwawo ndipo anali ndi mbiri yabwino pamaso pa akuluakulu a Boma ambiri.
Komabe, mosasamala kanthu za kusoŵeka kwa zinthu zina, zauzimu zinali kupita patsogolo. Paliponse m’dzikomo, mabuku athu ofotokoza za m’Baibulo anali kupezeka pafupifupi nyumba iliyonse. Ndipo tinaona ofalitsa Ufumu mu Ghana akuwonjezeka kuchokera pa 17,156 mu 1973 pamene tinafika kufika pa oposa 23,000 mu 1981. M’chaka chimenecho matenda anga a kansa ya khungu anayambika, mosakayika chifukwa chokhalitsa m’malo a dzuŵa ku India ndi ku Afirika, anatikakamiza kuchoka ku Ghana ndi kubwerera ku England kukapeza chithandizo cha mankhwala chanthaŵi zonse.
Mikhalidwe Yatsopano mu England
Kwa ine kubwerera kunatanthauza kusintha kwakukulu mu utumiki wanga. Ndinali nditazoloŵera kulankhula mwaufulu ndi anthu omwe amalemekeza Mulungu ndi Baibulo. Koma mu London, anthu otero anapezeka mwa kamodzikamodzi chabe. Ndimasirira kupirira kwa abale a ku Britain. Zimenezi zandipangitsa kuona kufunika kwa kukulitsa chifundo changa pa anthu “okambululudwa ndi omwazikana” mwauzimu.—Mateyu 9:36.
Titabwera kuchokera ku Afirika, Ine ndi Vera tinatumikira limodzi pa Beteli mu London mpaka pa nthaŵi ya imfa yake mu September 1991 pa usinkhu wa zaka 73. Zinandiŵaŵa kwambiri kusiyana ndi mnzanga wokhulupirika amene takhalira limodzi mu utumiki kwa zaka zambiri. Ndimamlakalaka kwambiri. Komabe, ndine wokondwa chifukwa cha chilimbikitso chomwe ndimalandira kuchokera ku banja lathu la Beteli lokhala ndi mamembala 250.
Ndithu ine ndimauona kuti ndi mwaŵi kuona gulu la Yehova likupita patsogolo ndiponso kuona ambiri akupanga utumiki wa nthaŵi zonse kukhala ntchito ya moyo wawo wonse. Kunena zoona, palibe njira ina yamoyo yoposa imeneyi, chifukwa “Yehova . . . sataya okondedwa.”—Salmo 37:28.
[Chithunzi patsamba 23]
Tinachita upainiya mu England kuyambira 1947 mpaka 1955
[Chithunzi patsamba 23]
Nthaŵi yoyamba mu utumiki pa nthaŵi ya msonkhano wachigawo ku India
[Chithunzi patsamba 23]
Pamene tinali amishonale ku Northern Rhodesia
[Chithunzi patsamba 23]
Mu 1985, ndili ndi anzanga omwe sindinawaone kwa zaka 12