Dalitsani Dzina Loyera la Yehova!
‘Pakamwa panga padzanena [chitamando, “NW”] cha Yehova; ndi zinthu zonse [zidalitse, “NW”] dzina lake loyera ku nthaŵi za nthaŵi.’—SALMO 145:21.
1, 2. (a) Kodi Satana watokosa ufumu wa Mulungu mwanjira yotani? (b) Kodi ndimafunso otani amene amadzutsidwa ponena za Salmo 145:11-21?
MOSAKAIKIRA Yehova ndi Mfumu Yachilengedwe Chonse. Koma Satana watokosa chilungamo ndi kulondola kwake kwa ufumu wa Mulungu. (Genesis 2:16, 17; 3:1-5) Mdyerekezi wakaikiranso umphumphu wa atumiki onse a Mulungu m’mwamba ndi padziko lapansi. (Yobu 1:6-11; 2:1-5; Luka 22:31) Chotero Yehova walola nthaŵi kaamba ka zolengedwa zonse zaluntha kuti ziwone zipatso zoipa za kupandukira ufumu wake ndikusonyeza kumene akuima pankhanizi.
2 Salmo 145 limatithandiza kutenga kaimidwe kolimba nji kuufumu wa Mulungu. Motani? Kodi Davide akunenanji ponena za ufumu wa Yehova? Ndipo kodi Mulungu amazisamalira motani nzika zake? Mayankho othandiza akupezeka pa Salmo 145:11-21.
Kunena za Ufumu wa Yehova
3. Ngati ufumu wa Yehova ngwapamtima pathu, kodi tidzachitanji?
3 Ufumu wa Yehova unali cholingalira chachikulu cha Davide, amene anati: ‘Adzanenera ulemerero wa ufumu wanu, adzalankhulira mphamvu yanu; kudziŵitsa ana a anthu zamphamvu zake, ndi ulemerero waukulu wa ufumu wake.’ (Salmo 145:11, 12) Anthu amanena ponena za zinthu zowakondweretsa. Chotero mwamuna amalankhula za banja lake, nyumba yake, dzinthu zake. ‘Munthu wabwino atulutsa zabwino m’chuma chokoma cha mtima wake,’ anatero Yesu. (Luka 6:45) Ngati ufumu wa Mulungu ngwapamtima pathu, pamenepo tidzapempherera Ufumu wake kuti ubwere, ndipo tidzafotokozera ena za chilungamo, mtendere, ndi chilunjiko zimene zidzafalikira pansi pa kulamulira kwake. Tidzatamanda Yehova “Mfumu ya nthawi zosatha,” ndipo tidzalankhula za mawu a kulamulira kwake kupyolera mu Ufumu Waumesiya wokhala m’manja mwa Mwana wake wokondeka, Yesu Kristu. (Chibvumbulutso 15:3; Yesaya 9:6, 7) Ndi mwaŵi wotani nanga kulankhula za ulemerero wakumwamba wa ufumu wa Yehova, umene posachedwapa udzasonyezedwa m’paradaiso wokongola wa padziko lapansi wodzala ndi zolengedwa zangwiro zosangalala!—Luka 23:43.
4. Kodi ndiliti pamene timakhala ndi nthaŵi ya kulankhula za ‘mphamvu’ za Yehova, ndipo kodi timachilikizidwa motani m’ntchito yoteroyo?
4 Chiyamikiro chidzatisonkhezeranso kulankhula za “mphamvu” za Yehova. Chinkana kuti “ndiye wa mphamvu yoposa,” iye samaigwiritsirapo ntchito molakwa. (Yobu 37:23) Iye anagwiritsira ntchito mphamvu yake kulenga dziko lapansi ndi anthu ndipo adzasonyezabe kuwonongera oipa. Tiri ndi nthaŵi ya kulankhula za mphamvu za Mulungu pamene tikulengeza mbiri yabwino. Ndipo kodi sindife oyamikira kuti Magwero otheratu awa a nyonga amatilimbitsa kuichita ntchitoyi? (Yesaya 40:29-31) Inde, monga Mboni za Yehova, timachilikizidwa muutumiki wopatulika ndi nyonga ndi mzimu wa Mulungu. Ndimwanjira yokhayi mmene uthenga Waufumu ukulengezedwera ndi chipambano chodabwitsa padziko lonse.—Salmo 28:7, 8; Zekariya 4:6.
5. Popeza kuti khamu la anthu ambiri samadziŵa za ‘ntchito zamphamvu’ za Yehova, kodi tiyenera kuchitanji?
5 Pali kufunikira kuti ife tidziŵitse ana a anthu ‘ntchito zamphamvu’ za Yehova, mongadi mmene Aisrayeli anafotokozera ana awo za njira imene Mulungu anawapulumutsira kutuluka muukapolo wa Igupto. (Eksodo 13:14-16) Anthu amaumbira zikumbukiro anthu amene zochita zawo amazilingalira kukhala zotchuka, koma kodi ndi anthu angati amene amadziŵa za ntchito zamphamvu za Mulungu? Katswiri wina anafotokoza ichi motere: “Iwo amazokota mawu antchito za ngwazi zawo pamkuwa, koma ntchito zachisomo za Yehova zimalembedwa pamchenga, ndipo kupita kwanthaŵi kumazichotsa osakumbukiridwa lerolino.” Ntchito zimenezo sizimachotsedwadi, chinkana kuti nzosadziŵidwa ndi makamu aanthu. Chotero m’ntchito yathu ya kunyumba ndi nyumba, pamene tikutsogoza maphunziro Abaibulo apanyumba, ndi panthaŵi zina, tiyeni tilankhule mwachangu ntchito zamphamvu za Mulungu.
6. (a) Kodi ndipachochitika chiti zaka zambiri zapitazo pamene mzimu wachangu umene timanyamulira nawo uminisitala wathu unafotokozedwa bwino? (b) Mwapang’ono, kodi nchiyani chimene chinanenedwa mu 1922 ponena za kulengeza Ufumu?
6 Tiyeneranso kudziŵitsa mwachangu ulemerero wa ufumu wa Mulungu. Changu cha utumiki wa Ufumu woterowo chinatsimikiziridwadi mu 1922, pamene J. F. Rutherford, amene panthaŵiyo anali prezidenti wa Watch Tower Society, anapereka nkhani kunthumwi zopezeka pamsonkhano wachigawo pa Cedar Point, Ohio, ndikuti: “Chiyambire 1914 Mfumu yaulemerero yayamba kulamulira . . . Ufumu wakumwamba wayandikira; Mfumu ikulamulira; ufumu wa Satana ukugwa; mamiliyoni ambiri omwe tsopano ali ndi moyo sadzafa konse. Kodi mukuchikhulupirira? . . . Pamenepo bwererani m’munda ana inu a Mulungu wamwambamwamba! Valani zida zanu zankhondo! Khalani olama maganizo, khalani atcheru, khalani okangalika, khalani olimba mtima. Khalani mboni zokhulupirika ndi zowona za Ambuye. Pitirizanibe kumenya nkhondo kufikira chotsala chirichonse cha Babulo chitakhala bwinja. Bukitsani uthenga kutali ndi padziko lonse. Dziko lifunikira kudziŵa kuti Yehova ndiye Mulungu ndikuti Yesu Kristu ndiye Mfumu ya mafumu ndi Mbuye wa ambuye. Ili nditsiku la masiku onse. Tawonani, Mfumu ikulamulira! Inu ndinu nthumwi zake zolengezera. Chotero ilengezeni, ilengezeni, ilengezeni, Mfumuyo ndi ufumu wake.”
7. Kodi tiyenera kulingalira motani ponena za ntchito yathu monga alengezi Aufumu?
7 Nkosangalatsa chotani nanga ‘kulingalira padzina la Mulungu,’ kufotokozera ena za ufumu wake, ndi kulengeza Ufumu Waumesiya wa Mwana wake wokondeka! (Malaki 3:16) Monga alengezi ndi achilikizi Aufumu, timauwona kukhala wamtengo wapatali mwaŵi wathu wa kulengeza mbiri yabwino ndi kutembenuzira mitima ya ena kwa Mulungu, Kristu, ndi Ufumu. Mwa ife, muyenera kukhala chikhumbo chonga moto wotentha cha kufotokozera ena za ulemerero waukulu wa ufumu wa Yehova.—Yerekezerani ndi Yeremiya 20:9.
8. (a) Kodi ufumu wa Yehova umaimiridwa nchiyani lerolino? (b) Kodi nchifukwa ninji kunganenedwe kuti Mulungu akulamulira “mibadwo yonse yonse”?
8 Tiyenera kufulumizidwa kulengeza Ufumu wa Mulungu ndi changu champhamvu, pakuti Davide chotsatira anati: “Ufumu wanu ndiwo ufumu womka muyaya, ndi kuweruza kwanu kufikira mibadwo yonse yonse.” (Salmo 145:13) Pamene kusinkhasinkha kwa wamasalmo pa ufumu wa Yehova kunapitirizabe, iye anasinthasintha amloŵa mmalo adzina kuyambira ndi “chake” kunka ku “wanu,” akumafotokoza mawu ake apemphero mwachindunji kwa Mulungu. Ndithudi, ufumu wa Yehova monga momwe waimiridwa ndi Ufumu Waumesiya sumaulowa mmalo ufumu wa ku nthaŵi zosatha wa Mulungu. Kwenikweni, pamene anthu omvera abweretsedwa kuungwiro, Kristu adzapereka Ufumuwo kwa Atate wake. (1 Akorinto 15:24-28) Chotero Mulungu adakali ndi ufumu “kufikira mibadwo yonse yonse.” Yehova ndiye anali Mfumu pamene Adamu analengedwa ndipo adzakhala ndi ufumu pa anthu angwiro ku nthaŵi za nthaŵi.
9. Mu Salmo 145, kodi nchiyani chinganenedwe ponena za vesi loyambira ndi chilembo cha Chihebri chakuti nun?
9 M’salmo ya ndakatulo ili, malemba a Masorete amasiya vesi loyambira ndi chilembo cha Chihebri chakuti nun. Koma mogwirizana ndi Septuagint Yachigiriki, Peshitta Yachisuriya, ndi Vulgate Yachilatini, malembo owerenga ena Achihebri amaŵerengedwa motere: “Yehova ngokhulupirika m’mawu ake onse, ndipo ngwokoma mtima mwachikondi [kapena kuti, “mokhulupirika”] m’ntchito zake zonse.” (New World Translation of the Holy Scriptures—With References, mawu amtsinde) Mulungu amakwaniritsa malonjezo ake onse ndipo ngwokhulupirika, wachikondi, ndi wokoma mtima kwa anthu onse amene amayamikira ubwino wake.—Yoswa 23:14.
Chilikizo la Yehova Silimalephera
10. Kodi Mulungu ‘amatichilikiza’ motani?
10 Mfumu Yosatha simanyalanyazapo tsoka la atumiki ake. Chotero, Davide anatha kunena motere: ‘Yehova [achilikiza] onse akugwa, naongoletsa onse owerama.’ (Salmo 145:14) Chiyambire m’masiku a Abele, Yehova wakhala akuchilikiza alambiri Ake. Akadangosiira zinthu m’manja mwathu, tikadagwa nazo zolemetsa zathu nthaŵi zambiri. Ife timasowa nyonga yokwanira ya kupirira nawo masoka athu onse ndi zizunzo zimene zimatigwera monga anthu a Mulungu, koma Yehova amatichilikiza. Mtundu wa mneni Wachihebri wogwiritsiridwa ntchito panopa umasonyeza kuti Mulungu amapitirizabe ‘kutichilikiza.’ Kungazindikiridwe kuti Yohane Mbatizi ndi Mwana wake wa Mulungu anathandizira kuwongoletsa makhalidwe akugwa a anthu ochimwa. Pamene anthuwa analapa ndikukhala atumiki a Yehova, iwo anasangalala ndi madalitso odabwitsa a chilikizo laumulungu.—Mateyu 21:28-32; Marko 2:15-17.
11. Kodi Yehova ‘amaongoletsa onse owerama’ motani?
11 Nkodzetsa chitonthozo kudziŵa kuti ‘Yehova akuongolera onse oweramitsidwa’ ndi ziyeso zosiyanasiyana. Iye amasangalatsa anthu otaikiridwa chiyembekezo pakati pathu, amatonthoza achisoni athu, ndikutithandiza kulankhula mawu ake molimba mtima titazunzidwa. (Machitidwe 4:29-31) Iye samalola konse zotilemetsa zathu kutigwetseratu titalivomerezadi thandizo lake. (Salmo 55:22) Chotero, mofanana ndi ‘mwana wamkazi wa Abrahamu’ amene anali “wopeteka” koma anachiritsidwa mwakuthupi ndi Yesu, ifenso tiyenera ‘kulemekeza Mulungu’ pamene ationgolera mwachikondi mwauzimu. (Luka 13:10-17) Odzozedwa oweramira muukapolo wa mu Babulo anasangalala pamene Mulungu anawaongolera mu 1919, ndipo wakhala akuongolera “nkhosa zina” zoyamikira chiyambire 1935.—Yohane 10:16.
12. Kodi ndimotani mmene ‘maso a onse amayang’ana moyembekezera’ Mulungu?
12 Yehova samakhumudwitsa konse kwa anthu ake, monga mmene Davide chotsatira anachimveketsera mwakuti: ‘Maso a onse ayembekeza Inu; ndipo muwapatsa chakudya chawo m’nyengo zawo. Muolowetsa dzanja lanu, nimukwanirirtsa zamoyo zonse chokhumba chawo.’ (Salmo 145:15, 16) Zikumveka ngati maso a zolengedwa zamoyo zonse atembenutsidwa kuyembekezera Mfumu ya Chilengedwe Chonse. Angelo amayang’ana kwa Mulungu kaamba ka moyo wopitirizabe. Ndipo monga mmene mwana amayang’anira kwa kholo kaamba ka zinthu zomwe zikumsowa, ifenso timayang’ana kwa Atate wathu wakumwamba. Kwenikweni, nkwa iye kumene anthu ndi nyama onsewo amalandirako zakudya. Palibe munthu wina aliyense amene angakhutiritse zosowa zawo. Mulungu amawapatsa ‘chakudya m’nyengo yake,’ ndiko kuti, pamene chafunidwa.
13. Kodi ndimwanjira yotani mmene Yehova ‘amaolowetsera dzanja lake ndi kukwaniritsa cha moyo chonse zokhumba zawo’?
13 Mulungu ‘amaolowetsa dzanja lake nakwaniritsa chamoyo chonse chokhumba chake.’ (Salmo 104:10-28) Zowonadi, nyama zina zimafa kaamba ka kusowa zakudya. Anthu ambiri amafa ndi njala monga minkhole yadyera, kutsendereza, ndi kugwiritsira molakwa chuma. Ndiponso, Yesu ananeneratu kuti “kuperewera kwa zakudya” kukakhala mbali ya ‘chizindikiro’ cha kukhalapo kwake m’masiku otsiriza ano. (Mateyu 24:3, 7) Koma apa palibetu chirichonse cha zinthuzi chomwe chimachitika chifukwa chakuti Yehova ngwaliuma kapena wosatha kugaŵira. Taganizani zolengedwa mamiliyoni zikwi zambiri zomwe zimadyetsedwa! Ndiponso, salmo ili likupereka chitsimikiziro chakuti pansi pa kulamulira kwa Ufumu, pamene ‘munthu sadzapweteka mnzake pomulamulira,’ Mulungu adzakwaniritsa zokhumba zathu zakuthupi ndi zauzimu. (Mlaliki 8:9; Yesaya 25:6) Ngakhale makonoli, nkukhaliranji ndi njala ya chakudya chauzimu, pakuti Mulungu amachipereka kwamwana alirenji m’nyengo yake kupyolera mwa ‘gulu la kapolo wokhulupirika ndi wochenjera.’ (Mateyu 24:45-47; 1 Petro 2:2) Mwauzimu, Mboni za Yehova ziri anthu odyetsedwa bwino zedi kuposa onse padziko lapansili. Kodi inuyo mumasonyeza chiyamikiro chakuya kaamba ka kuchulukaku?
Yehova Amasunga Omukonda
14. Kodi nchifukwa ninji Davide anati ‘Yehova ngwolungama m’njira zake zonse ndi wokhulupirika m’ntchito zake zonse’?
14 Kupusa kwathu ‘kungakhotetse njira yathu’ ndikutibweretsera zovuta, koma tisaimbe mlandu Mulungu kaamba ka mavutowa. (Miyambo 19:3) Davide akusonyeza chifukwa chosachitira tero pamene akuti: ‘Yehova ali wolungama m’njira zake zonse, ndi [wokhulupirika, “NW”] m’ntchito zake zonse.’ (Salmo 145:17) Mulungu nthaŵi zonse amachita m’njira yolunjika, yachilungamo, ndi yachifundo. Chifundochi chimawonekera makamaka m’makonzedwe ake a chipulumutso chopyolera m’nsembe ya dipo ya Yesu. (Machitidwe 2:21; 4:8-12) Yehova ‘ngwokhulupirikanso m’ntchito zake zonse,’ wokhulupirika, wachikondi, ndi wopanda tsankho, nthaŵi zonse. Pamenepo, monga “akutsanza a Mulungu,” tiyeni tikhale oongoka, olungama, achifundo, opanda tsankho, ndi okhulupirika.—Aefeso 5:1, 2; Deuteronomo 32:4; Salmo 7:10; 25:8; Yesaya 49:7; Machitidwe 10:34, 35.
15. Kodi ife ‘taitanira motani padzina la Mulungu m’chowonadi,’ ndipo kodi chatulukapo nchiyani pakuchita kwathu tero?
15 Popeza kuti Mulungu ngwachilungamo ndi wokhulupirika, ife timayandikitsidwa kwa iye. Ndiponso, Davide akutitsimikizira motere: ‘Yehova ali pafupi ndi onse akuitanira kwa Iye, onse akuitanira kwa Iye m’chowonadi.’ (Salmo 145:18) Pamene tinabatizidwa monga akhulupiriri odzipereka, tinaitanira pa dzina la Yehova. (Machitidwe 8:12; 18:8; Aroma 10:10-15) Chotero popeza kuti tinayandikira pafupi ndi Mulungu, iye amayandikira pafupi nafe. (Yakobo 4:8) Ife ‘timaitanira kwa iye m’chowonadi’ chifukwa chakuti uku timakuchita m’njira ya chowonadi, kupyolera mwa Yesu Kristu. Ndipo Yehova adzakhalabe pafupi ngati timlambira ‘mumzimu ndi m’chowonadi,’ mwa kusonyeza ‘chikhulupiriro chopanda chinyengo,’ ndi ‘kupirirabe molimbika, monga ngati tikuwona Wosaonekayo.’ (Yohane 4:23, 24; 1 Timoteo 1:5; Ahebri 11:27) Titatero sitidzapempherapo kwachabe kapena kuyang’anizana ndi dziko la Satana tiri tokha, koma tidzapitirizabe kusangalala ndi thandizo ndi chitsogozo chaumulungu. (Salmo 65:2; 1 Yohane 5:19) Ha ichi chikutanthauza chisungiko chotani nanga!
16. Kodi nchifukwa ninji ndipo ndimotani mmene Yehova ‘amachitira chikhumbo cha omuwopa iye’?
16 Tirinso ndi chisungiko chenicheni, chifukwa cha zinthu zina zimene Yehova amatichitira. Davide anati: ‘Adzachita chokhumba iwo akumuopa; nadzamva kufuula kwawo, nadzawapulumutsa.’ (Salmo 145:19) Yehova ‘amachita zokhumba zathu’ chifukwa chakuti timamuwopa Mulungu kuchokera kumtima ndipo tiri ndi mantha akuya a kusamkondweretsa. (Miyambo 1:7) Mitima yathu yachimvero yatisonkhezera kupanga kudzipereka kwa Yehova, ndipo mkhalidwe wathu wamaganizo ngwakuti, ‘Kufuna kwanu kuchitidwe.’ Popeza kuti n’chifuniro chake chimene timalalikira uthenga Waufumu, iye amakwaniritsa chokhumba chathu cha kuchita ntchito imeneyo. (Mateyu 6:10; Marko 13:10) Mulungu ‘amachitanso zokhumba zathu’ chifukwa chakuti sitimapemphera mwadyera koma timapempha zinthu zogwirizana ndi chifuniro chake. Iye amapatsa zinthu zomvana ndi chifuniro chake ndi zaubwino kwa ife.—1 Yohane 3:21, 22; 5:14, 15; yerekezerani ndi Mateyu 26:36-44.
17. Kodi nchifukwa ninji tingakhale otsimikizira kuti ‘kufuulira’ thandizo kwathu kudzamvedwa ndi Mulungu?
17 Monga Mboni zokhulupirika za Yehova, tingakhalenso otsimikizira kuti ‘kufuulira kwathu’ thandizo sikudzaloŵa konse m’makutu ogontha. Mulungu anapulumutsa Davide m’tsoka ndipo anapulumutsa Yesu, namuukitsadi kwa akufa. Titaukiridwa ndi adani, makamaka pakuukira kwa Gogi, tingatsimikizire kuti Yehova adzatipulumutsa. (Ezekieli 38:1–39:16) Kwenikweni, panthaŵi iriyonse ya mavuto, mofanana ndi Davide tingapemphere mwachidaliro kuti: ‘Mundichitire chifundo, Yehova, pakuti ndasautsika ine. . . . Pakuti ndamva ugogodi wa ambiri, mantha andizinga: Pondipangira chiwembu, anatsimikiza mtima kulanda moyo wanga. Koma ine ndakhulupirira inu, Yehova: Ndinati, Inu ndinu Mulungu wanga.’—Salmo 31:9-14.
18. Kodi timapindula motani mwakudziŵa kuti Yehova ‘amasunga onse akukondana naye’ koma ‘adzawononga oipa’?
18 Yehova Mulungu nthaŵi zonse ngwokonzekera kutithandiza. Monga mmene Davide ananenera kuti: “Yehova asunga onse akukondana naye; koma oipa onse adzawaononga.” (Salmo 145:20) Inde, ngati timukonda Mulungu, iye adzatidalitsa ndi kutisunga. (Numeri 6:24-26) Iye ‘amapatsa mphoto yoipa kwa odzitukumula’ koma amasunga atumiki ake odzichepetsa, osalola chirichonse kuchita chowavulaza iwo kosatha. Popeza kuti Yehova ali nafe, tiyeni tikhale olimba mtima. (Salmo 31:20-24, NW; Machitidwe 11:19-21) ‘Palibe chida chosulidwira ife chimene chidzapambana.’ (Yesaya 54:17; Salmo 9:17; 11:4-7) Ichi nchokumana nacho cha anthu omwe adzatsimikizira chikondi chawo kwa Mulungu monga atumiki ake odzipereka okhulupirika. Monga gulu, Mboni za Yehova zidzapyola mwachisungiko pa ‘chisautso chachikulu’ chobweretsedwa pa oipa. (Chibvumbulutso 7:14) Ndipo kuthetsa nkhani yaikulu ya ufumu wa chilengedwe cha ponseponse wa Yehova kudzakhala dalitso chotani nanga kwa “onse akukondana naye”!
Pitirizani Kudalitsa Dzina Loyera la Yehova
19. Kodi nchifukwa ninji milomo yathu imalankhula ‘chitamando cha Yehova’?
19 Davide akumaliza salmo lochititsa chidwili ndi mawu awa: ‘Pakamwa panga padzanena [chitamando, “NW”] cha Yehova; ndi zinthu zonse [zidalitse] dzina lake loyera ku nthaŵi za nthaŵi.’ (Salmo 145:21) Monga Mboni za Yehova, timayamikira ukulu, ubwino, ukoma wa ufumu wa Mulungu, chilikizo losalephera, ndi chisamaliro chosatopa. Chotero, mofanana ndi Davide, milomo yathu imalankhula chitamando cha Mulungu. Timasonkhezeredwa kumpatsa kudzipereka kotheratu, kumuyamikira kaamba ka madalitso ake ambiri, ndi kutamanda ‘dzina lake lokoma.’—1 Mbiri 29:10-13; Eksodo 20:4-6.
20. Ndi lingaliro la kunthaŵi zosatha, kodi nchiyani chimene chiyenera kukhala chitsimikiziro chathu tsopano?
20 Popeza kuti Yehova amatidalitsa tsiku lirilonse, tiyeni timudalitse mokhazikika, kapena kumthokoza. Tiyeni tilalikire mbiri yabwino mwachangu kutamanda Mulungu, kufotokozera ena kuti posachedwapa ‘zamoyo zonse zidzadalitsa dzina lake loyera.’ Kudzakhala kokoma chotani nanga kukhala ndi moyo pamene nzika zonse za dziko lapansi—indetu, zolengedwa zonse zaluntha m’chilengedwe chonse—zidzaimbira chitamando Atate wathu wakumwamba! (Salmo 148:1-13) Adalitsike Yehova kaamba ka kutivumbulira dzina lake ndi kutipatsa mwaŵi wa kukhala Mboni zake. (Salmo 83:18; Yesaya 43:10-12) Tiyeni tiyende m’njira yoyenerera anthu onyamula dzinalo mopatulika ndi kupempherera kupatulikitsidwa kwake. (Luka 11:2) Tiyeni titumikire Mulungu mokhulupirika, kotero kuti m’dongosolo lake latsopano, liwu lathu likamvedwe pakuimba kwa anthu odalitsa dzina loyera la Yehova ku nthaŵi za nthaŵi.
Kodi Ndemanga Zanu Nzotani?
◻ Kodi tidzachitanji ngati ufumu wa Yehova ngwapamtima pathu?
◻ Kodi ufumu wa Mulungu ukuimiridwa nchiyani lerolino?
◻ Kodi ndimotani mmene Yehova ‘amaongolera onse owerama’?
◻ Kodi Mulungu ‘amaolowetsa dzanja lake ndi kukwaniritsa chamoyo chonse zokhumba zawo’ m’njira yotani?
◻ Kodi dzina loyera la Yehova tingalidalitse motani?
[Chithunzi patsamba 17]
Mu 1922, mawu akuti ‘ilengezeni Mfumuyo ndi Ufumu wake’ anasonkhezera achilikizi a ufumu wa Yehova kuchita ntchito yaikulu