Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w93 5/15 tsamba 8-11
  • Kodi Nkutumikiriranji Yehova?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Nkutumikiriranji Yehova?
  • Nsanja ya Olonda—1993
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kufunika kwa Cholinga Chabwino
  • Kutumikira ndi Zolinga Zabwino
  • Thayo ndi Mwaŵi
  • Chiyamikiro Chimapereka Chisonkhezero
  • Tamandani Yehova ndi Ufumu Wake
  • Chimwemwe ndi Chikhutiro
  • Kodi Nchifukwa Ninji Mumatumikira Mulungu?
  • Dalitsani Dzina Loyera la Yehova!
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Sankhani Kutumikira Yehova Mudakali Achinyamata
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Tumikirani Yehova ndi Chimwemwe cha Mtima
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Yehova Amafunikira Chitamando Chosatha
    Nsanja ya Olonda​—1990
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1993
w93 5/15 tsamba 8-11

Kodi Nkutumikiriranji Yehova?

“TSIKU la Yehova layandikira! ‘Chisautso chachikulu’ chili pafupi, ndipo simudzapulumuka ngati simukutumikira Mulungu.” Ngati munthu wina anakuuzani zimenezo, kodi mukanachita motani?​—Zefaniya 2:2, 3; Mateyu 24:21.

Zowonadi, tiyenera kumakumbukira tsiku la Yehova, ndipo kupulumuka chisautso chachikulu chikuyandikiracho kumadaliradi pa utumiki wokhulupirika kwa Mulungu. Koma kodi nsonga zimenezi ziyenera kukhala zifukwa zazikulu zimene timaperekera utumiki wopatulika kwa Yehova Mulungu? Kodi nchifukwa ninji inuyo mumatumikira Yehova?

Kufunika kwa Cholinga Chabwino

Ngati munthu satumikira Mulungu ndi cholinga chabwino, iye angaleke ngati ziyembekezo zake sizikwaniritsidwa mkati mwa nyengo ya nthaŵi yakutiyakuti. Mwachitsanzo, anthu ena anayembekezera Yesu Kristu kubweranso mu 1843 kapena 1844, masiku omwe anapita popanda kukwaniritsa ziyembekezo zawo. Zosangalatsa pa nkhaniyi ndi zimene zinalembedwa ndi George Storrs, wofalitsa wa Bible Examiner amene pambuyo pake anakhala mnzake wa Charles Taze Russell, prezidenti woyamba wa Watch Tower Society. Bible Examiner ya September 1846, Storrs analemba kuti:

“Thayo lakutumikira Mulungu lili lalikulu kwambiri kuposa mfundo yakuti tsikulo layandikira kwenikweni. . . . Kachitidwe kamene kadzakhalapo ngati [1846 ndi 1847] ipita monga momwe zingachitikire, popanda umboni wa kubweranso kwake, kadzakhala kokhumudwitsa kwambiri. Zochitika zimatsimikizira zimenezi​—ndikutanthauza zochitika za [mu 1843 ndi 1844]. Kodi ali kuti ochuluka a awo amene, mongonamizira, ‘anasonkhezeredwa kutumikira Mulungu’ monga momwe anafunikira chifukwa cha kulengezedwa kwa nthaŵi ya kudza kwa Ambuye? Ndipo namalowe amati​—ALI KUTI!!! Kokha mmodzi mwa anthu khumi ndiamene akuyenda molemekeza chikhulupiriro chawo Chachikristu. Chifukwa ninji? Iwo anasonkhezeredwa ndi zolinga zolakwa. Chinthu chachikulu chimene chinakopedwa ndi kusonkhezeredwa chinali dyera lawo. Iwo anali ngati wochimwa amene amalingalira kuti ali pafupi kufa pakama wodwalira kapena m’mkuntho wa m’nyanja. Ngati adziŵa kuti adzafa, iye amakhala Mkristu. Ngati adziŵa kuti sali pangozi, amakhala wamphwayi monga mwamasiku onse.”

Kutumikira ndi Zolinga Zabwino

Dyera ndi kuwopa kuwonongedwa zingasonkhezere ena kumachita chifuniro cha Yehova mwamwambo. Ena angasangalatsidwe kwambiri ndi chiyembekezo cha moyo m’Paradaiso kotero kuti angatumikire Mulungu pachifukwa chimenecho chokha. Komabe, ngati anthu osonkhezeredwa ndi zolinga zimenezo salingalira kuti tsiku la Yehova ndi chisautso chachikulu zili pafupi kwambiri, iwo sangatumikire Mulungu mwachangu.

Ndithudi, kukondwera ndi malonjezo a Mulungu ndi madalitso onenedweratu sindiko dyera. Iye amafuna kuti tisangalale ndi ziyembekezo zoikidwa patsogolo pathu monga otsatira a Mwana wake, Yesu Kristu. “Kondwerani m’chiyembekezo,” anatero mtumwi Paulo, nawonjezera kuti: “Pirirani m’masautso; limbikani chilimbikire m’kupemphera.” (Aroma 12:12) Pamodzi ndi pemphero, “chimwemwe cha Yehova” chimatithandiza kupirira ziyeso ndi kuyembekezera moleza mtima kukwaniritsidwa kwa malonjezo a Mulungu. (Nehemiya 8:10) Pakali pano, tili ndi zifukwa zambiri zotumikira Yehova. Kodi zina za izo nzotani?

Thayo ndi Mwaŵi

Monga Mfumu Yachilengedwe, Yehova ayenera ndipo amafuna kudzipereka kotheratu. (Eksodo 20:4, 5) Chotero Mkristu aliyense ali ndi mlingo wofanana wa thayo kwa Mulungu kaya chisautso chachikulu chiyambe maŵa, chaka chamaŵa, kapena pambuyo pake. Iye ali ndi thayo lakutumikira Yehova mopanda dyera chifukwa chokonda Mulungu ndi mtima wake wonse, moyo, nzeru, ndi mphamvu. (Marko 12:30) Akristu ena oyambirira analingalira kuti tsiku la Yehova linali pafupi, koma chiyembekezo chawo sichinakwaniritsidwe, ndipo anafa osawona chochitikacho. (1 Atesalonika 5:1-5; 2 Atesalonika 2:1-5) Komabe, ngati anali okhulupirika kufikira imfa, otsatira Kristu odzozedwa amenewo pomalizira pake analandira mphotho ya chiukiriro cha moyo wakumwamba.​—Chivumbulutso 2:10.

Mboni zobatizidwa za Yehova ziyenera kumtumikira mokhulupirika chifukwa zinanyamula thayo lakuchita chifuniro chake modzifunira. Tangolingalirani! Mofanana ndi angelo oyera, tingachite chifuniro cha Mfumu Yachilengedwe. (Salmo 103:20, 21) Yesu anauwona mwaŵi umenewo kukhala wamtengo wapatali kotero kuti anati: “Chakudya changa ndicho kuti ndichite chifuniro cha iye amene anandituma ine, ndi kutsiriza ntchito yake.” (Yohane 4:34) Ngati tikhala ndi mzimu wofananawo, tidzalengeza zitamando za Yehova mwachangu ndi kuuza ena ponena za zifuno zake, monga zavumbulutsidwa m’Malemba. Mwanjira imeneyi, timakhalanso ndi mwaŵi wothandiza ena mwauzimu. Ndithudi, kuchita chifuniro cha Mulungu chifukwa cha kumkonda iye kuli mwaŵi wabwino koposa, mosasamala kanthu kuti tsiku la Yehova lidzayamba liti.

Chiyamikiro Chimapereka Chisonkhezero

Chiyamikiro kaamba ka chikondi cha Mulungu popereka nsembe yadipo ya Mwana wake chiyeneranso kutisonkhezera kutumikira Yehova. Panthaŵi ina tinali otalikirana ndi Yehova Mulungu chifukwa cha uchimo. Komabe, Yesu anati: “Mulungu anakonda dziko lapansi [la mtundu wa anthu] kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Yehova ndiye anayamba kuchitapo kanthu pankhaniyi, monga momwe Paulo analembera kuti: “Mulungu atsimikiza kwa ife chikondi chake cha mwini yekha mmenemo, kuti pokhala ife chikhalire ochimwa, Kristu adatifera ife.” (Aroma 5:8) Chiyamikiro kaamba ka kusonyeza chikondi kwa Mulungu kumeneku chiyenera kutisonkhezera kumtumikira ndi mtima wonse.

Chiyamikiro kaamba ka zogaŵira zauzimu ndi zakuthupi za Yehova chimatipatsa chifukwa chowonjezereka chomtumikirira iye mokhulupirika. Mawu a Mulungu ali chitsogozo chotsimikizirika​—kuunika kwa panjira yathu. Zofalitsa zoperekedwa kupyolera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” zimatithandiza kugwirizanitsa miyoyo yathu ndi chifuniro chaumulungu. (Mateyu 24:45-47; Salmo 119:105) Ndipo chifukwa timafuna Ufumu choyamba, Yehova amatigaŵiranso zinthu zakuthupi. (Mateyu 6:25-34) Kodi mukusonyeza chiyamikiro chanu kaamba ka zinthu zimenezi?

Chiyamikiro kaamba ka ufulu wopatsidwa ndi Mulungu kuchoka ku chipembedzo chonyenga chimatipatsa chifukwa china chotumikirira Yehova mokhulupirika. Mkazi wachigololo wachipembedzo Babulo Wamkulu ‘akukhala pa madzi ambiri,’ kutanthauza “anthu, ndi makamu, ndi mitundu, ndi manenedwe.” (Chivumbulutso 17:1, 15) Komabe, iye sakukhala pa atumiki a Yehova, kuwasonkhezera ndi kuwalamulira mwachipembedzo. Mwachitsanzo, iwo amakana chiphunzitso chonyenga chachipembedzo chakuti moyo wa munthu sukhoza kufa. Iwo amadziŵa kuti munthu analengedwa “wamoyo,” kuti akufa “sadziŵa kanthu bi,” ndi kuti kudzakhala chiukiriro. (Genesis 2:7; Mlaliki 9:5, 10; Machitidwe 24:15) Chotero iwo samawopa kapena kulambira akufa. Kodi chiyamikiro cha ufulu wauzimu umenewo chimakupangitsani kukana mpatuko ndi kumamatira ku kulambira koyera kwa Yehova?​—Yohane 8:32.

Chiyamikiro kaamba ka chichilikizo cha tsiku ndi tsiku cha Yehova chiyenera kuwonjezera kutsimikiza mtima kwathu kwa kumtumikira mokhulupirika. Wamasalmo Davide analengeza kuti: “Wolemekezeka [Yehova, NW], tsiku ndi tsiku atisenzera katundu.” (Salmo 68:19) Pamalo ena wamasalmoyo anati: “Pakuti wandisiya atate wanga ndi amayi wanga, koma Yehova anditola.” (Salmo 27:10) Inde, munthu wotumikira Yehova mokhulupirika angasenzetse Mulungu mtolo wake wophiphiritsira, monga ngati nkhaŵa ndi ziyeso. Kodi mukusonyeza chiyamikiro kaamba ka chichilikizo chosalekeza cha Yehova mwakumtumikira mokhulupirika?​—Salmo 145:14.

Tamandani Yehova ndi Ufumu Wake

Chikhumbo cha kulemekeza Yehova chiyeneranso kutisonkhezera kumtumikira iye. Zolengedwa zakumwamba zimasonyezedwa kukhala zikulemekeza Mulungu ndi mawu akuti: “Muyenera inu, [Yehova, NW], ndi Mulungu wathu, kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphamvu; chifukwa mudalenga zonse, ndipo mwa chifuniro chanu zinakhala, nizinalengedwa.” (Chivumbulutso 4:11) Mfumu Davide anatamanda Mulungu mwakunena kuti: “Ukulu, ndi mphamvu, ndi ulemerero, ndi kulakika, ndi chifumu ndi zanu, Yehova . . . ufumu ndi wanu, Yehova . . . Zolemera ndi ulemu zifuma kwanu, ndipo muchita ufumu pa zonse . . . Motero tsono, Mulungu wathu, tikuyamikani ndi kulemekeza dzina lanu lokoma.” (1 Mbiri 29:10-13) Monga atumiki a Yehova, kodi sitimadzimva athayo kumlemekeza m’kalankhulidwe ndi kachitidwe poyembekezera kukwaniritsidwa kwa malonjezo ake?​—1 Akorinto 10:31.

Chikhumbo champhamvu chakulankhula za Ufumu wa Mulungu chimaperekanso chisonkhezero china chakutumikira Yehova. Cholinga chabwino chimenecho chinafotokozedwa bwino m’mawu a wamasalmo akuti: “Ntchito zanu zonse zidzakuyamikani, Yehova; ndi okondedwa anu adzakulemekezani. Adzanenera ulemerero wa ufumu wanu, adzalankhulira mphamvu yanu; kudziŵitsa ana a anthu zamphamvu zake, ndi ulemerero waukulu wa ufumu wake. Ufumu wanu ndiwo ufumu womka muyaya, ndi kuweruza kwanu kufikira mibadwo yonse yonse.” (Salmo 145:10-13) Kulengeza uthenga wa Ufumu ndintchito ya Akristu yofunika koposa imene ikuchitidwa m’tsiku lathu. (Mateyu 24:14; 28:19, 20) Kodi muli ndi chikhumbo champhamvu chakutamanda Yehova ndi kuuza ena ponena za Ufumu wake?

Kuyeretsedwa kwa dzina la Yehova ndi kulemekezedwa kwa ufumu wake kuyenera kukhala kofunika koposa kwa ife kotero kuti tiyenera kukhala ofunitsitsa kumtumikira mokhulupirika. Tingapempherere kuyeretsedwa kwa dzina la Yehova ndi kulemekezedwa kwa ufumu wake. (Mateyu 6:9) Tingachite mogwirizana ndi mapemphero athu mwakukhala ndi phande mokhazikika muuminisitala Wachikristu ndi kufalitsa chowonadi chonena za zinthu zofunika zimenezo.​—Ezekieli 36:23; 39:7.

Chimwemwe ndi Chikhutiro

Mwakutumikira Yehova mokhulupirika, timakhala ndi chikhutiro chakukondweretsa mtima wake ndi kutsimikizira Mdyerekezi kukhala wabodza. Ngakhale kuti monyenga Satana amanena kuti anthu amatumikira Mulungu chifukwa cha dyera, utumiki wathu wokhulupirika kwa Yehova, woperekedwa mwachikondi, umatsimikizira zonena za wotonzayo kukhala zabodza. (Yobu 1:8-12) Zimenezi zimatipatsa chifukwa chabwino chopitirizira kuchita zimene zanenedwa pa Miyambo 27:11 kuti: “Mwananga, khala wanzeru, nukondweretse mtima wanga; kuti ndimuyankhe yemwe anditonza.” Ndiponso, pamene titumikira Yehova mokhulupirika mosasamala kanthu za zonse zimene Satana amachita kuti atidodometse, mosakaikira kusunga umphumphu kwathu kudzalimbitsa okhulupirira anzathu.​—Afilipi 1:12-14.

Chimwemwe ndi chikhutiro chakukhala ndi phande m’kututa kwauzimu chiyenera kutifulumiza kutumikira Yehova mokhulupirika. Yesu anapeza chimwemwe m’kuthandiza anthu, makamaka mwauzimu. Lemba la Mateyu 9:35-38 limati: “Yesu anayendayenda m’mizinda yonse ndi m’midzi, namaphunzitsa m’masunagoge mwawo, nalalikira uthenga wabwino wa ufumuwo, nachiritsa nthenda iliyonse ndi zofooka zonse. Koma iye, powona makamuwo, anagwidwa m’mtima ndi chisoni chifukwa cha iwo, popeza anali okambululudwa ndi omwazikana, akunga nkhosa zopanda mbusa. Pomwepo ananena kwa ophunzira ake, Zotuta zichulukadi koma antchito ali oŵerengeka. Chifukwa chake pempherani Mwini zotuta kuti akokose antchito kukututa kwake.” Ngati ntchito yotutayo ipitiriza kwanthaŵi yaitali kuposa mmene tinayembekezerera, chimenecho chiyenera kutipatsa mwaŵi wowonjezereka wakupeza chimwemwe ndi chikhutiro m’kuthandiza ena mwauzimu. Imeneyinso ndinjira yosonyezera chikondi cha pamnansi chimene tiyenera kusonyeza.​—Mateyu 22:39.

Kodi Nchifukwa Ninji Mumatumikira Mulungu?

Tangokambitsirana zoŵerengeka za zifukwa zambiri zamphamvu zotumikirira Yehova mokhulupirika. Nkwabwino kulingalira mwapemphero zifukwa zathu zaumwini zotumikirira Mulungu, popeza kuti aliyense wa ife adzadziŵerengera mlandu kwa iye. (Aroma 14:12; Ahebri 4:13) Ndipo awo amene amaumirira kukhala ndi zolinga zadyera chabe sadzalandira chiyanjo chaumulungu.

Kodi nchiyani chimene chingayembekezeredwe ngati tili odera nkhaŵa kwambiri ndi kuyeretsedwa kwa dzina la Yehova ndi kupereka utumiki wopatulika kwa Mulungu ndi zolinga zopanda dyera? Eya, Yehova adzatidalitsa ife pamodzi ndi uminisitala wathu! (Miyambo 10:22) Tidzalandiranso moyo wamuyaya chifukwa tatumikira Yehova mokhulupirika.

[Chithunzi patsamba 9]

Zikwi zambiri zikutumikira Yehova ku Japan

[Chithunzi patsamba 10]

Kutumikira Yehova ku Côte d’Ivoire

[Mawu a Chithunzi patsamba 8]

SIX SERMONS, lolembedwa ndi George Storrs (1855)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena