Yehova Anadalitsa Kutsimikiza Mtima Kwanga
MONGA MOMWE YASIMBIDWIRA NDI RICHARD WUTTKE
“Iwe udzamwalira mkati mwa miyezi itatu!” “Kodi ukutanthauzanji?” “Chimenechi nchimene dokotala amene unapitako ku Assis wandiuza,” m’chimwene wanga William anayankha motero.
KOMA ndinafuna kukhala ndi moyo, sindinafune kumwalira. Kwa nthaŵi yoyamba, ndinapemphera kwa Mulungu kaamba ka thandizo. Mwachimwemwe, zaka 46 pambuyo pake, ndinganene kuti ngakhale kuti dokotalayo sananene limene linali vuto langa, kupima kwake kudali kolakwika. Komabe, chiwopsyezocho chinandipangitsa kulingalira za chifuno cha moyo wanga ndi kufunika kwa kutumikira Mlengi wathu.
Banja Lathu Liri pa Ulendo
Pamene ndinabadwa pa November 11, 1921, makolo anga ankakhala mu Grosen, tauni yaing’ono kum’mawa kwa Jeremani. Iwo anabadwira mu Russia kwa makolo ochokera ku Jeremani. Komano, pamene kusinthika kwa Bolshevik mu 1917 kunayambitsa ulamuliro wa Communism, iwo limodzi ndi anthu ena ochokera ku Jeremani anathamangitsidwa m’dzikolo ndipo anataikiridwa katundu wawo yense. Pambuyo paulendo wautali wapasitima yoyenda mofulumira, makolo anga ndi ana awo aang’ono anafika kumalire a Jeremani. Komabe, iwo anakanizidwa kuloŵa m’dzikolo ndipo anafunikira kubwerera ku Russia. Kumeneko anakanizidwa kuloŵanso, chotero anafunikira kubwereranso ku Jeremani. Pambuyo pa miyezi yambiri ya kuvutika, iwo pomalizira pake analoledwa kuloŵa m’dzikolo.
Pamene ndidali ndi zaka khumi, atate anga anamwalira. Zaka ziŵiri pambuyo pake, mu 1933, Hitler anakhala wolamulira, ndipo ndinakakamizika kugwirizana ndi gulu lotchedwa Nazi Youth. Mkati mwa ulamuliro wa Hitler, panali mavuto kwa Ajeremani obadwira ku maiko ena, ndipo chinali chowonekeratu kuti Jeremani anali kukonzekera nkhondo ina. Chotero tinalingalira zosamukira ku Brazil, polimbikitsidwa ndi ena omwe adasamukira kale kumeneko. Tinafika mu Santos, Brazil, mu May 1936.
Pambuyo pogwira ntchito pamunda wa khofi kwa miyezi yoŵerengeka, tinagula pulazi yaing’ono m’chigawo chachonde pafupi ndi Maracaí m’boma la São Paulo. Pamene tinkamanga nyumba yathu, tinali okhoza kukhala m’nyumba ya minisitala wa Lutheran. Iye anatilimbikitsa kuti tidzipita ku tchalitchi chake koma pamene iye, ndipo pambuyo pake mloŵa m’malo wake, anayamba kulankhula za ndale zadziko m’maulaliki ake, tinachoka m’tchalitchicho.
Nthaŵi Yoyamba Kumva Chowonadi cha Baibulo
Panali pafupifupi pa nyengo imeneyi pamene m’chimwene wanga anandiuza za kupima kogwetsa ulesi kwa dokotala uja. Choncho ndinapita ku São Paulo kuti ndikamve lingaliro lachiŵiri. Pamene ndidali konko, banja lomwe ndinkakhala nalo linalandira mlendo, bwenzi lawo, Otto Erbert. Iye anali m’modzi wa Mboni za Yehova, ndipo anayamba kuchitira umboni kwa ife. Komabe, banjalo silinayamikire chimene ankanena, ndipo mmodzi ndi mmodzi iwo anachoka m’chipindacho, akumandisiya ine ndi mlendo wawoyo.
Otto analankhula nane kwa pafupifupi maola aŵiri pankhani za moto wa helo; kusafa kwa moyo; Mulungu wowona, Yehova; Ufumu wake; ndi chiyembekezo chakukhala ndi moyo kosatha padziko lapansi la paradaiso. Munali mtsogolo mowala chotani nanga mmene iye anasonyeza! Zinali zosiyana chotani nanga ndi zimene ndinaphunzira m’Tchalitchi cha Lutheran! Pomalizira pake, Otto anafunsa kuti: “Kodi umakhulupirira ziphunzitso zonyenga za Chikristu Chadziko kapena Baibulo?”
“Baibulo,” ndinayankha motero.
“Pamenepo uyenera kuliphunzira!” iye anafulumiza tero, akumawonjezera kuti: “Ngati ungakonde kumva zambiri ponena za ilo, ubwere kudzandiwona.” Popeza kuti ndinakonda zimene ndinamva, makamaka ponena za kukhala ndimoyo kosatha padziko lapansi, ndinapita kukamuwona tsiku lotsatira. Kukambirana kwachiŵiriku kunandikhutiritsa kuti ndinapeza ‘chowonadi chimene chimamasula anthu.’ (Yohane 8:32) Ndinachokako ndi kabukhu kakuti, Health and Life, ndi chiitano chopita ku phunziro Labaibulo lophunziridwa m’Chijeremani.
Kukwaniritsa Chikhumbo Changa Chakuya
Panthaŵiyi, ndinkalandira thandizo lamankhwala loyenera ndipo ndinali wokhoza kubwerera kunyumba. Ndinapita ndi Otto Erbert limodzi nane patchuthi. Amayi anga anali achimwemwe kwambiri kuti ndinkaphunzira Baibulo, bukhu lomwe nthaŵi zonse linali pagome pathu koma silinkaŵerengedwa. Otto atabwerera ku São Paulo, ndinkaphunzira Baibulo ndi banja langa pafupifupi usiku uliwonse, mothekera monga mmene ndinathera. Ndinali wachimwemwe pamene amayi anga, m’chimwene wanga Robert, ndi mlongo wanga Olga onsewo analandira uthenga wa chowonadi. Nthaŵi zonse nyumba yathu inali malo apakati a machitachita amayanjano, koma pambuyo pa miyezi iŵiri ya kuchitira umboni kwathu, anthu analeka kubwera. Mmodzi wa awo amene ankakonda kubwera kwathu anati: “Ngati mupitiriza ndi ichi, mudzachita misala!”
Komabe, chikhumbo changa cha kutumikira Yehova chinapitirizabe kukula. Ndinagula mabuku ambiri, ndipo ndinkawaŵerenga usiku wonse. Koma mabuku onse anali m’Chijeremani, ndipo ndinazindikira kuti ngati ndinati ndiphunzitse ena, ndinafunikira kuphunzira Chipwitikizi. Chotero, mu 1945, ndinasamukira ku São Paulo kukaphunzira Chipwitikizi. Ndinkakhala ndi Otto Erbert, amene pambuyo pake anakwatira mlongo wanga Olga.
Pamodzi ndi anthu ena 50, ndinayamba kupezeka pamisonkhano m’Nyumba Yaufumu imodzi yokhayo ya São Paulo. Mpingo umodzi umenewo wakula tsopano kukhala mipingo yoposa 510 mu São Paulo yaikuluyo, yokhala ndi ofalitsa Aufumu oposa 50,000. Pa January 6, 1946, ndinabatizidwa m’kuchitira chithunzi kudzipereka kwanga kuchita chifuniro cha Mulungu. Chaka chimodzimodzicho ndinapezeka pa Msonkhano Wateokratiki wa “Kondwerani Amitundu” mu São Paulo, msonkhano wanga woyamba waukulu. Chidali chosangalatsa chotani nanga kuwona anthu 1,700 akupezekapo pa Sande! Pamsonkhano umenewu ndinakumana ndi Otto Estelmann, amene anandilimbikitsa, nati: “Richard, udakali wachichepere; wathanzi labwino; choncho khala mpainiya.”
Ndidali ntalingalirapo za uminisitala wa nthaŵi zonse, koma tsopano ndinatero mosamalitsa kwenikweni. Anthu ena aŵiri ndi ineyo, tinadziikira miyezi isanu ndi umodzi kutsogolo pamene tidzayamba. Pamene nthaŵiyo inafika, ndinaŵafunsa kuti: “Kodi mwakonzekera kupita?” Palibe amene anali wokonzekera. Chotero ndinaŵawuza kuti ndidzayamba. “Udzakhala ndi mavuto,” iwo anachenjeza motero. Koma ndinamamatira ku chosankha changa. Pa May 24, 1947, ndinalandira gawo langa monga mpainiya wokhazikika.
Makomo Atsopano a Utumiki Atseguka
Gawo langa linali lalikulu kwabasi, kuphatikizapo magawo okhala anthu ndi abizinesi a São Paulo. Ndinagawira mabuku ndi timabuku mazana ambiri mwezi uliwonse. M’mawa wina ndinaloŵa m’chipinda chachikulu mmene amuna angapo ankagwira ntchito. Ndinapita kwa mwamuna woyamba ndi kumgaŵira bukhu la “The Truth Shall Make You Free.”
“Kodi uli ndi mabuku angati m’chola chako?” iye anafunsa motero.
“Pafupifupi 20,” ndinayankha motero. Iye anatenga onsewo napatsa mwamuna aliyense yemwe analipo. Iyo inali nyumba yosonkhanira mumzinda!
Komabe, chimwemwe changa chachikulu chinali m’kutsogoza maphunziro Abaibulo apanyumba. M’zaka zinayi, chiyamikiro chinke kwa Yehova, anthu 38 mwa awo amene ndinaphunzira nawo anabatizidwa. Anthu angapo anatenga uminisitala wa nthaŵi zonse. Pakati pawo panali Afonso Grigalhunas, yemwe anatumikira kwa zaka zoposa khumi monga mpainiya wothandiza, kufikira imfa yake mu 1988—ndipo anachita zimenezo ngakhale kuti anali ndi mwendo woumba. Ndiyeno panali banja la Ciuffa. Francisco, mwana wamwamuna, anatumikira kwa zaka zambiri monga woyang’anira woyendayenda, ndipo mlongo wake, Ângela, adakali mpainiya.
Mu 1951 ndinaitanidwa kukhala woyang’anira woyendayenda. Gawo langa linaphatikizapo madera aakulu a maboma a Rio Grande do Sul ndi Santa Catarina. Anthu zikwi zambiri ochokera ku Yuropu ankakhala kumeneko kum’mwera kwa Brazil. Maulendo ambiri anapangidwa kwa anthu okhala kutali ndi magulu, popeza kuti kunali mipingo yochepa panthaŵiyo. Padali mitsinje yambiri koma maulalo ochepa, ichi chinatanthauza kuoloka yaing’onoyo sutukesi yanga iri kumsana ndipo typewriter yanga ndi chola ziri m’manja. Misewu inali yosalimidwa ndipo inali yamajidumajidu. Kuti ndichinjirize zovala zanga ku fumbi, ndinkavala mkanjo wopepuka. Ichi chinapangitsa ena kuganiza kuti ndinali wansembe wawo watsopano, ndipo anayesa kumpsopsona dzanja langa.
Kuchinjiriza Zabwino Zaufumu
Pamene ndinayesera kukumbukira mavutowo, ndinatsatira lamulo lamakhalidwe abwino ili: Ngati anthu ena amakhala kutali ndi mizinda, kuyenda m’tinjira timeneti ndi kuoloka mitsinjeyi, kodi ine ndingalekerenji kuchita chofananacho, makamaka popeza ndiri ndi uthenga wofunika woterowo umene ndiyenera kuwubweretsa?
Kaŵirikaŵiri mavuto osiyanasiyana ankabuka m’matauni aang’onowo. Mwachitsanzo, nthaŵi ina tinapanga makonzedwe a kukhala ndi msonkhano m’sukulu yakumaloko yapafupi ndi paki. Kumbali ina ya pakiyo kunali bawa yaing’ono ndi tchalitchi cha Katolika. Pamene mphunzitsiyo sanabwere kudzatsegula sukuluyo, ndinasankhapo zopereka nkhaniyo m’mapakimo. Mwamsanga itayambika nkhaniyo, amuna asanu ndi mmodzi anatuluka m’bawamo ndikuyamba kufuula ndi kulozaloza. Tinadzadziŵa pambuyo pake kuti analipiridwa ndi wansembe kuti achite izi.
Ndinayamba kulankhula mofuula, ndikumalankhula mwachindunji kwa iwo. Iwo analeka, ndipo mmodzi wa iwo anati: “Iye akulankhula za Mulungu. Kodi wansembe anganenerenji kuti iye ngwa Mdyerekezi?” Pamene wansembeyo anawona kuti amunawo sakatha kuthetsa msonkhanowo, iye anakwera galimoto yake ya jeep ndikumayendetsa mozungulira pakiyo, akumafuula kuti: “Aliyense amene ndi Mkatolika sayenera kupezeka pa msonkhano umenewu!” Palibe amene anachoka, ndipo msonkhanowo unamalizidwa mwachimwemwe.
Mu Mirante do Paranapanema, São Paulo, ndinachezera mkulu wa apolisi kufotokoza mtundu wa ntchito yathu ndikupempha chilolezo cha kugwiritsira ntchito holo kaamba ka nkhani yapoyera. Iye anakonza kuti tikagwiritsire ntchito holo ya kalabu. Tinamuuza kuti tinkakonzekeranso mahandibilu olengezera nkhaniyo. “Kodi ndi mbali iti ya tauni imene mukufuna kuwagaŵira iwo?” iye anafunsa motero. Titamuuza, iye anapempha kuti ena agaŵiridwe kumbali ina ya tauni. Pa Sande iye anabwera ku nkhaniyo, limodzi ndi apolisi ena aŵiri, monga momwe iye ananenera, “kudzasungitsa bata.”
“Kodi ukufuna kuti ndikuitane kubwera kudzapereka nkhani yako?” iye anafunsa motero.
“Ndingakondedi chimenecho,” ndinayankha tero, “koma ndiloleni ndilongosole mmene timawaitanira alankhuli athu.” Pambuyo pondiitana, iye anakhala pansi papulatifomupo kuti amvetsere. Ndikhulupirireni anthuni, linali gulu lotchera khutu mwabata zedi. Tinalibe mavuto kumeneko, kodi nkukhalirakonji ndi apolisi aŵiri pakhomo ndi mkulu wawo ali khale papulatifomu!
Mu March 1956 ndinaikidwa kukhala woyang’anira wachigawo ndi kutumikira misonkhano mu Brazil monse. Mitunda yoyenda inali yaitali. Kamodzi chinatenga masiku atatu kuchoka pa malo a msonkhano amodzi kumka ku ena. Kumbali yakumpoto ya dzikolo, nthaŵi zina tinkayendera pa station wagon. Izi zinalibe mazenera, motero zinali ndi ziboo zolowetsa mpweya wabwino, ili linali lingaliro labwino, popeza kuti okweramowo anaphatikizapo nkhuku ndi nkhumba!
Gileadi Ilimbikitsa Kutsimikiza Mtima Kwanga
Chinali chosangalatsa chotani nanga kupezekapo pa Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower mu 1958! Kalasi lathu linamaliza maphunziro panthaŵi ya msonkhano wa pa Yankee Stadium ndi Polo Grounds chilimwe chimenecho, kumene anthu 253,922 ochokera m’maiko 123 osiyanasiyana anapezekapo pa nkhani yapoyera. Anali namtindi wotani nanga! Kenaka ndinabwerera ku Brazil, wotsimikiza mtima kuposa ndi kale lonse kupitirizabe kulengeza Ufumu wa Yehova.
Mu 1962 ndinakwatira Ruth Honemann, yemwe anatumikira kale zaka zoposa zisanu ndi chimodzi monga m’mishonale mu Brazil. Chiyambire ukwati wathu ndapitirizabe kusangalala ndi mwaŵi wowonjezereka wa utumiki, kuchititsa maphunziro m’Sukulu Yautumiki Waufumu ndi Sukulu Yautumiki Waupainiya, limodzinso ndi kutenga chitsogozo m’kukonzekera misonkhano yamtundu ndi ya mitundu yonse ndi kumanga Holo Yosonkhaniramo yoyamba mu São Paulo.
Pakali pano tikusangalala ndi mwaŵi waukulu koposa wa ntchito zathu zateokratiki monga ziŵalo za banja la Beteli la ku Brazil. Kuyang’ana m’mbuyo ku zaka zoposa 40 za utumiki wa nthaŵi zonse, zaka 35 za izo monga woyang’anira woyendayenda, ndinganene kuti zakhala zodzala ndi ntchito zachimwemwe ndi zopatsa mphotho. (Miyambo 10:22) Ndaphunzira zambiri m’gulu la Yehova, kuphatikizapo kufunika kwa kusonyeza kudera nkhaŵa ena, kukhala bwenzi osati bwana, ndikusakhala wotanganitsidwa kwambiri kuchita kulephera kusamalira zosoŵa za ena. Pomaliza, ndingakonde kuuza makamaka achichepere, monga momwe Mbale Estelmann anandiuzira zaka zambiri zapitazo kuti: ‘Ndinu achichepere; ndinu athanzi labwino; choncho khalani mpainiya!’
[Chithunzi patsamba 29]
Nyumba yathu yapanthaŵi ino, Beteli ya Brazil