Khama Lichititsa Kupita Patsogolo
YOSIMBIDWA NDI JOSÉ MAGLOVSKY
Pamene wapolisi anagwira mkono wanga, ndinafunafuna atate. Komabe, mosadziŵa, iwo anali atatengeredwa kale ku polisi. Pamene ndinafika kumeneko, apolisi analanda zofalitsidwa zathu zonse, kuphatikizapo ma Baibulo athu, ndi kuwaunjika mulu umodzi pansi. Poona zimenezi, atate anafunsa kuti: “Kodi mukuika pansi ndi ma Baibulo omwe?” Mkulu wa apolisi anapepesa, ndiyeno anatola ma Baibulowo ndi kuwaika pa thebulo.
KODI tinafika motani ku polisiko? Kodi tinali kuchita chiyani? Kodi tinali m’dziko lokana Mulungu loyang’aniridwa ndi apolisi, kuti tinalandidwa ndi ma Baibulo omwe? Kuti ndiyankhe mafunso ameneŵa, ndidzakutengerani kumbuyo mu 1925, inenso ndisanabadwe.
M’chaka chimenecho atate, a Estefano Maglovsky, ndi amayi anga, a Juliana, anachoka m’dziko limene panthaŵiyo linali Yugoslavia ndi kusamukira ku Brazil, nakhala ku São Paulo. Ngakhale kuti Atate anali Mprotesitanti ndipo Amayi anali Mkatolika, chipembedzo sichinali chowagaŵanitsa. Kwenikweni, zaka khumi pambuyo pake kanthu kena kamene kanawagwirizanitsa mwachipembedzo kanachitika. Mwamuna mnzawo wa atate anawabweretsera kabuku ka zithunzi za maonekedwe okongola m’Chihangare kofotokoza mkhalidwe wa akufa. Iye anapatsidwa kabukuko monga mphatso, ndipo anapempha Atate kuti akaŵerenge ndi kumpatsa lingaliro lawo pa zimene kananena, makamaka pa nkhani ya “helo.” Atate anatha usiku wonse akumabwerezabwereza kuŵerenga kabukuko, ndipo tsiku lotsatira, pamene mwamuna mnzawoyo anafika kudzamva lingaliro lawo, Atatewo, ndi mtima wonse anati: “Ichi ndicho choonadi!”
Ziyambi Zazing’ono
Popeza kuti kabukuko kanali ka Mboni za Yehova, aŵiri onsewo anazifunafuna kuti adziŵe zambiri ponena za zikhulupiriro ndi ziphunzitso zawo. Pamene anazipeza, ziŵalo za banja lathu zingapo zinayamba kukambitsirana za Baibulo ndi Mboni. Chaka chimodzimodzicho, 1935, phunziro la Baibulo lokhazikika m’Chihangare linayambidwa, lokhala ndi avareji ya anthu asanu ndi atatu, ndipo kuyambira pamenepo tinali kukhala ndi maphunziro a Baibulo okhazikika panyumba pathu.
Patapita zaka ziŵiri za kuphunzira Baibulo, Atate anabatizidwa mu 1937 ndi kukhala Mboni ya Yehova yachangu, akumakhala ndi phande mu ntchito yolalikira ku nyumba ndi nyumba ndiponso kutumikira monga mtumiki woikidwa ndi wochititsa phunziro. Iwo anathandiza pa kupangidwa kwa mpingo woyamba mu São Paulo, m’chigawo cha Vila Mariana. Pambuyo pake mpingowo unasamutsidwira pakati pa mzinda ndipo unatchedwa Central Congregation. Zaka khumi pambuyo pake mpingo wachiŵiri unapangidwa, m’dera la Ypiranga, ndipo Atate anaikidwa kukhala mtumiki wa mpingo kumeneko. Mu 1954 mpingo wachitatu unapangidwa, m’chigawo cha Moinho Velho, kumene anatumikirakonso monga mtumiki wa mpingo.
Posapita nthaŵi pamene gulu limeneli linalimbitsidwa, iwo anayamba kuthandiza gulu lina lapafupi mu São Bernardo do Campo. Chifukwa cha dalitso la Yehova pa zoyesayesa za magulu aang’ono ameneŵa a Mboni m’zaka zonsezo, chiwonjezeko chake chakhala chachikulu, kwakuti mu 1994 m’mipingo 760 ya m’dera la São Paulo munali ofalitsa oposa 70,000. Mwachisoni, Atate anamwalira asanaone chiwonjezeko chimenechi. Iwo anamwalira mu 1958 pausinkhu wa zaka 57.
Kuyesayesa Kutsatira Chitsanzo cha Atate
Mkhalidwe wapadera wa atate, monga momwe zilili kwa Akristu ena okhwima maganizo, unali kuchereza kwawo alendo. (Onani 3 Yohane 1, 5-8.) Chotero, tinali ndi mwaŵi wa kulandira alendo onga ngati a Antonio Andrade ndi akazi awo ndi mwana wawo wamwamuna, amene anafika ku Brazil kuchokera ku United States ndi Mbale ndi Mlongo Yuille mu 1936. Ndiponso alendo ena apanyumba pathu anali omaliza maphunziro a Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower, Harry Black ndi Dillard Leathco, amene anali amishonale oyamba kutumizidwa ku Brazil mu 1945. Enanso ambiri anawatsatira. Abale ndi alongo ameneŵa anali magwero achilimbikitso osatha kwa aliyense m’banja lathu. Poyamikira zimenezi ndipo kaamba ka phindu la banja lathu, ndayesayesa kutsanzira chitsanzo cha atate cha mkhalidwe Wachikristu wa kuchereza alendo.
Ngakhale kuti ndinali ndi zaka zisanu ndi zinayi zokha pamene Atate anaphunzira choonadi mu 1935, monga mwana wamkulu, ndinayamba kutsagana nawo m’ntchito yawo ya teokrase. Tonsefe tinkapita nawo kumisonkhano ku Nyumba Yaufumu imene inali pa malikulu a Mboni ku São Paulo mu Eça de Queiroz Street, Number 141. Chifukwa cha kuphunzitsidwa ndi kulangizidwa ndi Atate, ndinakulitsa chikhumbo chachikulu cha kutumikira Yehova, ndipo mu 1940, ndinadzipatulira kwa Yehova, mwa kusonyeza zimenezi ndi kumizidwa m’madzi mu Tietê River, mtsinje umene tsopano waipitsidwa, umene umadutsa pakati pa São Paulo.
Posapita nthaŵi ndinazindikira tanthauzo la kukhala wofalitsa wokhazikika wa uthenga wabwino, kufesa ndi kuthirira uthenga wa choonadi kwa ena kuchita nawo maphunziro apanyumba a Baibulo. Tsopano, pamene ndikuona zikwizikwi za Mboni za Yehova zodzipatulira mu Brazil, ndimasangalala kwambiri podziŵa kuti ndinagwiritsiridwa ntchito ndi Iye kuthandiza ambiri a iwo kudziŵa choonadi kapena kukulitsa kuchiyamikira kwawo.
Pakati pa awo amene ndinathandiza panali Joaquim Melo, amene ndinampeza mu utumiki wa kukhomo ndi khomo. Ndinali kulankhula ndi amuna ena atatu amene anali kumvetsera koma osati mofunitsitsa. Ndiyeno ndinaona mnyamata wina amene anadzagwirizana nafe ndipo anali kumvetsera mosamalitsa. Poona chidwi chake, ndinatembenukira kwa iye ndipo, nditapereka umboni wabwino, ndinampempha kuti adzafike pa Phunziro Labuku Lampingo. Iye sanafike pa phunzirolo, koma anafika pa Sukulu Yautumiki Wateokratiki ndipo pambuyo pake anali kufika pa misonkhano nthaŵi zonse. Anapita patsogolo bwino kwambiri, anabatizidwa, ndipo kwa zaka zingapo anatumikira monga mtumiki woyendayenda, limodzi ndi mkazi wake.
Ndiyeno panali Arnaldo Orsi, amene ndinadziŵana naye ku ntchito. Nthaŵi zonse ndinkalalikira kwa wantchito mnzanga wina komano ndinaona kuti nthaŵi zonse mnyamata wina wandevu anali kumvetsera, chotero ndinayamba kulankhula naye. Iye anali wa m’banja Lachikatolika lamphamvu koma ankafunsa mafunso ambiri onena za nkhani zonga za kusuta fodya, kuonerera mafilimu aumaliseche, ndi kuchita maseŵero a nkhondo a judo. Ndinamsonyeza zimene Baibulo limanena, ndipo ndinachita chidwi pamene anandipempha tsiku lotsatira kuti ndikaonerere pamene akaphwanya kaliwo wake ndi laitala pamodzi ndi mtanda wake, akumawononga mafilimu ake azaumaliseche, ndi kumeta ndevu zake. Munthu wosinthidwa mu mphindi zoŵerengeka chabe! Analekanso maseŵero a judo napempha kuti ndizimchititsa phunziro la Baibulo tsiku lililonse. Mosasamala kanthu za chitsutso cha mkazi wake ndi atate wake, iye anapita patsogolo mwauzimu ndi thandizo la abale amene ankakhala pafupi naye. M’nthaŵi yaifupi, anabatizidwa ndipo lerolino akutumikira monga mkulu mumpingo. Nayenso mkazi wake ndi ana analandira choonadi.
Kukhala ndi Phande mu Utumiki wa Ufumu
Pamene ndinali ndi zaka 14, ndinayamba kugwira ntchito m’kampani yosatsa malonda, kumene ndinaphunzirako kulemba zikwangwani. Zimenezi zinali zothandizadi kwambiri, ndipo kwa zaka zingapo ndine ndekha mu São Paulo amene ndinali mbale amene anali kulemba zikwangwani zonyamula ndi za m’misewu zolengeza nkhani zapoyera ndi misonkhano ya Mboni za Yehova. Kwa zaka pafupifupi 30, ndinali ndi mwaŵi wa kutumikira monga woyang’anira Dipatimenti ya Zikwangwani ya msonkhano. Nthaŵi zonse ndinali kusunga masiku anga atchuthi kotero kuti ndikagwire ntchito pa misonkhano, ngakhale kugona mu holo ya msonkhano kuti zikwangwani zilembedweretu pasadakhale.
Ndinalinso ndi mwaŵi wa kugwira ntchito ndi galimoto lokhala ndi makina okuza mawu la Sosaite, chinthu chimene chinali chatsopano kwenikweni panthaŵiyo. Tinkaika zofalitsidwa zathu za Baibulo pathebulo, ndipo pamene galimoto lokhala ndi makina okuza mawu linaulutsa uthenga, tinkalankhula kwa anthu amene anatuluka m’nyumba zawo kudzaona zimene zinali kuchitika. Njira ina imene tinagwiritsira ntchito kudziŵikitsira uthenga wabwino wa Ufumu inali galamafoni ya m’manja, ndipo ndikali ndi malekodi ake ogwiritsiridwa ntchito pogaŵira zofalitsidwa za Sosaite. Motero mabuku ambiri ofotokoza Baibulo anagaŵiridwa.
M’masiku amenewo Tchalitchi cha Katolika chinali kuchita ligubo la mzera wautali la mwambo m’misewu ya São Paulo, kaŵirikaŵiri lokhala ndi amuna ena kutsogolo amene anali kulitsegulira njira. Pa Sande ina, ine ndi Atate tinali kugaŵira Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! pamsewu pamene mzera wautali wa ligubo la mwambo unaonekera. Mwachizoloŵezi chawo, Atate anali atavala chipeŵa chawo. Mmodzi wa amuna apatsogolo pa ligubolo anafuula kuti: “Vula chipeŵacho! Kodi suukuona kuti kukubwera ligubo?” Pamene anaona kuti Atatewo sanavule chipeŵa chawo, amuna ambiri anafika, namatikankhira kuzenera la sitolo ina ndi kupanga msokonezo. Zimenezi zinachititsa wapolisi wina kufika kudzaona zimene zinali kuchitika. Mmodzi wa amunawo anamgwira mkono, akumafuna kulankhula naye. “Chotsa dzanja lako pa yunifulomu yanga!” wapolisiyo analamula motero, akumapamantha dzanja la mwamunayo. Ndiyeno anafunsa zimene zinali kuchitika. Mwamunayo anafotokoza kuti Atate sanavule chipeŵa chawo kuchitira ulemu ligubolo, akumawonjezera kuti: “Ine ndine mtumwi wa Roma Katolika.” Yankho losayembekezereka linali lakuti: “Kodi wati ndiwe m’Roma eti? Uzibwerera ku Rome komweko! Kuno ndi ku Brazil.” Ndiyeno anatembenukira kwa ife, akumafunsa kuti: “Kodi ndani wayamba kufika pano?” Pamene Atate anayankha kuti ndi ife, wapolisiyo anathamangitsa amunawo ndi kutiuza kupitiriza ndi ntchito yathu. Iyeyo anaima pafupi nafe kufikira ligubo lonse linapyola—ndipo Atate sanavule chipeŵa chawo!
Zochitika zonga chimenechi zinali zakamodzikamodzi. Koma pamene zinachitika, kunali kolimbikitsa kudziŵa kuti panali anthu amene anafuna kuona chilungamo chikuchitidwa kwa anthu ochepa amene sanali kungomvera chinthu chilichonse cha Tchalitchi cha Katolika.
Panthaŵi ina, ndinapeza wachichepere wina amene anasonyeza chikondwerero nandipempha kudzabwereranso mlungu wotsatira. Nditabwerera anandilandira bwino kwambiri ndi kundipempha kuloŵa m’nyumba. Ndinadabwadi kupeza nditazingidwa ndi kagulu ka chiwawa ka achichepere konyodola ndi koyesayesa kundikwiyitsa! Mkalidwewo unaipa kwambiri, ndipo ndinalingalira kuti akayamba kundimenya. Ndinauza amene anandipempha kuloŵamoyo kuti ngati kalikonse kangandichitikire, iye ndiye amene adzakhala ndi mlandu ndi kuti banja langa linadziŵa kumene ndinali. Ndinawapempha kuti nditulukemo, ndipo anavomera. Komabe, ndisanachoke, ndinati ngati aliyense angafune kulankhula nane pa ndekha, ndidzakambitsirana naye. Pambuyo pake, ndinatulukira kuti kanali kagulu ka otengeka maganizo, mabwenzi a wansembe wina wakumaloko amene anawalimbikitsa kuchita msonkhano umenewu. Ndinali ndi chimwemwe kuwonjoka m’chiwembu chawocho.
Zoonadi, poyamba, kupita patsogolo kwa zinthu m’Brazil kunali kochedwa, kosaoneka bwino kwenikweni. Tinali kumayambiriro a ‘kuwoka,’ okhala ndi nthaŵi yochepa ya ‘kulimirira’ ndi ‘kututa’ zipatso za ntchito yathu. Nthaŵi zonse tinkakumbukira zimene mtumwi Paulo analemba: “Ndinawoka ine, anathirira Apolo; koma Mulungu anakulitsa. Chotero sali kanthu kapena wookayo, kapena wothirirayo; koma Mulungu amene akulitsa.” (1 Akorinto 3:6, 7) Omaliza maphunziro a Gileadi atafika mu 1945, tinaona kuti nthaŵi ya kukula kumeneko yoyembekezeredwa kwa nyengo yaitali inali itafika.
Kulimba Mtima Poyang’anizana ndi Chitsutso
Komabe, kukulako sikunali kudzachitika popanda chitsutso, makamaka Nkhondo Yadziko II itayambika ku Ulaya. Panali chizunzo chenicheni chifukwa chakuti anthu onse ndi akuluakulu ena a m’boma sanamvetsetse kaimidwe kathu kauchete. Panthaŵi ina, mu 1940, pamene tinali mu ntchito ya m’khwalala ndi zikwangwani pakati pa São Paulo, wapolisi wina anandifikira kumbuyo, nang’amba zikwangwanizo, ndi kundigwira mkono kumka nane ku polisi. Ndinafunafuna atate, koma sindinawaone. Sindinadziŵe kuti iwo ndi abale ndi alongo ena angapo, kuphatikizapo Mbale Yuille, amene anali kuyang’anira ntchitoyo mu Brazil, anali atatengeredwa kale ku polisi. Monga momwe ndatchulira m’ndime yoyambayo, ndinakakumananso ndi Atate kumeneko.
Popeza kuti ndinali mwana, sakananditsekera, choncho wapolisi ananditengera kunyumba nakandisiya kwa amayi. Nawonso alongo anamasulidwa usiku umodzimodziwo. Pambuyo pake apolisi anaganiza za kumasula abale onse, pafupifupi khumi a iwo, kusiyapo Mbale Yuille. Komabe, abalewo anaumirira kuti: “Kuli bwino kuti tonse amene tituluke kapena kusatuluka.” Apolisiwo sanalolere zimenezo, chotero onsewo anathera usikuwo pamodzi m’chipinda chozizira chokhala ndi pansi pa simenti. Onsewo anamasulidwa tsiku lotsatira popanda kuimbidwa mlandu. Abale anagwidwa kwa nthaŵi zingapo chifukwa cha kuchitira umboni ndi zikwangwani. Zikwangwanizo zinali kulengeza nkhani yapoyera ndiponso kabuku kakuti Fascism or Freedom, ndipo akuluakulu ena aboma anaona zimenezi kukhala zikutanthauza kuti tinali kuchirikiza Chifasizimu, zimene kaŵirikaŵiri zinachititsa kutiganizira molakwa.
Ntchito yankhondo youmiriza aliyense inadzetsanso mavuto kwa abale achichepere. Mu 1948, ndinali woyamba kumangidwa pankhani imeneyi mu Brazil. Akuluakulu aboma sanadziŵe zochita nane. Ndinasamutsidwira ku malo a asilikali ku Caçapava ndikupatsidwa ntchito yofesa ndi kusamalira ndiwo zamasamba m’dimba ndiponso kusesa chipinda chimene akulakulu anali kuseŵereramo. Ndinali ndi mipata yambiri ya kuchitira umboni kwa amunawo ndi kuwagaŵira zofalitsidwa. Ofesala wamkulu ndiye anali woyamba kulandira kope la buku la Sosaite la Children. Pambuyo pake, ndinapatsidwa kalasi loti ndiziphunzitsa zachipembedzo la asilikali pafupifupi 30 kapena 40 amene anali osakhoza kuchita maseŵero olimbitsa thupi ndipo anabindikiritsidwa m’chipinda. Potsirizira pake, nditakhala m’ndende pafupifupi miyezi khumi, ndinazengedwa mlandu ndi kumasulidwa. Ndimathokoza Yehova, amene anandipatsa nyonga yoyang’anizana ndi ziwopsezo, kusambulidwa, ndi kusekedwa zimene amuna ena anandichitira.
Mthandizi Wokhulupirika ndi Wodalirika
Pa June 2, 1951, ndinakwatira Barbara, ndipo kuyambira pamenepo iye wakhala bwenzi lodalirika ndi lokhulupirika pophunzitsa ana athu ndi kuwalera “m’maleredwe ndi chilangizo cha [Yehova, NW].” (Aefeso 6:4) Pa ana athu asanu, anayi akutumikira Yehova mwachisangalalo m’mathayo osiyanasiyana. Chiyembekezo chathu nchakuti, iwowo limodzi nafe tipitirizebe mwakhama kuyenda m’choonadi ndi kuchirikiza kupita patsogolo kwa gulu ndi ntchito imene ikuchitidwa. Ziŵalo za banja zimene zili m’chithunzithunzi cha m’nkhaniyi zonsezo ndi atumiki odzipatulira a Yehova kusiyapo wamng’ono kwambiriyo, khanda limene lili m’manja. Anayi ali akulu ndipo aŵiri ndi apainiya okhazikikanso, kusonyeza kuona kwa mawu a Miyambo 17:6: “Zidzukulu ndizo korona wa okalamba; ndipo ulemerero wa ana ndiwo atate awo.”
Tsopano, pa usinkhu wa zaka 68, thanzi langa silili labwino kwambiri. Mu 1991, ndinachitidwa opaleshoni yotsegula mitsempha itatu imene inatsekeka ndipo pambuyo pake ndinaikidwa mtsempha woikirira. Komabe, ndili ndi chimwemwe kukhala wokhoza kupitirizabe kutumikira monga woyang’anira wotsogoza mumpingo wa mu São Bernardo do Campo, potsatira mapazi a atate, amene anali pakati pa anthu oyamba kuyambitsa ntchitoyo kuno. Mbadwo wathu ulidi wapadera, wokhala ndi mwaŵi wa kukhala ndi phande mu ntchito imene sidzabwerezedwanso ya kulengeza kukhazikitsidwa kwa Ufumu wa Yehova Waumesiya. Chotero sitiyenera kuiŵala konse mawu a Paulo kwa Timoteo: “Koma iwe, . . . chita ntchito ya mlaliki wa uthenga wabwino, kwaniritsa utumiki wako.”—2 Timoteo 4:5.
[Chithunzi patsamba 23]
Makolo anga, a Estefano ndi a Juliana Maglovsky
[Chithunzi patsamba 26]
José ndi Barbara ndi ziŵalo za banja lawo la atumiki a Yehova odzipatulira