Kodi Mumatsatira Malangizo?
TATE wachikondi adzalangiza ana ake kotero kuti adzakhale achipambano ndi achimwemwe m’moyo pamene akula. Ndipo ana amene amakonda makolo awo ndi kuwalemekeza adzalandira malangizo oterowo chifukwa amadziŵa kuti adzawapindulitsa. Mofananamo, Atate wathu wachikondi wakumwamba, Yehova, amapereka kwa atumiki ake chitsogozo chimene chimawabweretsera chipambano ndi chisangalalo m’miyoyo yawo. Chifukwa chake, chiri chofunika kuti titsatire malangizo amene Mulungu amapereka kupyolera m’Mawu ake, Baibulo, ndi gulu lake lapadziko lapansi.
Mkati mwa Banja
Pali mbali zambiri mmene timapatsidwa malangizo. Mbali imodzi ndiyo m’banja. Ukwati ndi banja zinayambitsidwa ndi Mulungu. Baibulo limati Mulungu anakwatitsa anthu oyamba ndipo anaŵauza kuti abale ana. (Genesis 1:27, 28; 2:22-24) Mlengi wapereka malangizo kaamba ka ziŵalo zonse za banja ponena za mathayo awo osiyanasiyana. Mwachitsanzo, mwamuna ndi tate ndiye mutu wa banja, ichi chikutanthauza kuti ali ndi thayo lopereka malangizo, chakudya, zovala, pogona, chitetezo, ndi chilangizo. Iye amapanganso zosankha zofunika za banja. Monga mwamuna, iye ayenera kusonyeza kudera nkhaŵa kwa mkazi wake ndikumpatsa ulemu monga chotengera chochepa mphamvu. (Aefeso 5:22, 23; 1 Timoteo 5:8; 1 Petro 3:7) Mkazi ayenera kukhala wogonjera kwa mwamuna wake, kumpatsa ulemu waukulu, ndikukhala wothandiza ndi wothangatira wake. Ndipo Malemba amasonyeza kuti ana ayenera kukhala omvera makolo awo.—Genesis 2:18; Aefeso 6:1-3; 1 Petro 3:1, 2.
Kodi chimachitika nchiyani ngati malangizo ameneŵa anyalanyazidwa? Kusamvana ndi mikangano zimabuka pamene amuna sasonyeza kudera nkhaŵa akazi awo, ndiponso ngati akazi amasonyeza ulemu wochepa kaamba ka umutu wa mwamuna. Kwenikweni, zinthu zoterozo zapangitsa kusweka kwa maukwati ambiri. Kusamvera ndi kupanduka kwa ana kwabweretsa chisoni chachikulu kwa makolo ambiri. Kaŵirikaŵiri, makolo ayenera kupatsidwa liŵongo lalikulu chifukwa cholephera kulera ana awo mogwirizana ndi chilangizo choyenera, mwakutero kuwakwiyitsa iwo.—Aefeso 6:4.
Chinkana kuti ogwira ntchito ya mayanjano, akatswiri a maganizo, ndi ena apereka malingaliro osiyanasiyana onena za mmene tingachitire ndi mavuto a banja, palibe uphungu umene uli wokhutiritsa kuposa malangizo operekedwa m’Baibulo ndi Mlengi wa banja. Kutsatira malangizowa kumabweretsa chimwemwe ndi chikhutiritso chenicheni.—Salmo 19:7-9.
Mumpingo
Tiyenera kutsatira malangizo amene Mutu wa mpingo Wachikristu, Yesu Kristu, akupereka kupyolera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” ngalande yoikidwa ya gulu la Mulungu pano padziko lapansi. (Mateyu 24:45-47; Aefeso 5:23) Kuti mumpingo mukhale mtendere ndi umodzi, ziŵalo zake zonse ziyenera kuchita mogwirizana ndi chitsogozo choperekedwa. Mwachitsanzo, anthu amene amatsogolera kuphunzitsa mpingo ndi kuthandiza ena ayenera kumamatira ku zitsogozo zimene amalandira kuchokera ku gulu la Yehova. Ichi chidzathandizira kukhutiritsa kwa ntchito yawo. Malangizo ameneŵa angakhale pa mmene angakhalire ndi phande m’ntchito yolalikira, mmene angasamalire mavuto mumpingo, mmene angaperekere uphungu ndi chilimbikitso, mmene angatonthozere othodwetsedwa, ndi zina zotero. Palinso zitsogozo zonena za mmene angakonzekerere misonkhano yolangiza ndi yomangirira kwa onse oyanjana ndi mpingo Wachikristu.—Machitidwe 20:20; Aroma 12:6-8; Agalatiya 6:1; 1 Atesalonika 3:1-3.
Makamaka akulu mu mpingo, kapena oyang’anira, ayenera kukhazikitsa chitsanzo chabwino m’chimenechi. Bungwe Lolamulira limatumiza malangizo amene akulu ayenera kutsatira mosamalitsa ndi mokhulupirika. Iwo ayenera kuzoloŵeretsa ndi kugwiritsira ntchito malangizowo ku mikhalidwe yapamalopo. Tiyenera kukumbukira kuti amene akutsogoza mpingo Wachikristu ndi Yesu Kristu. Iye amazindikira mwangwiro zosoŵa za mipingo yonse padziko lonse, ndipo amapereka chilimbikitso ndi chithandizo chofunikira. Chotero, akulu sayenera kukaikakaika kugwiritsira ntchito chitsogozo chirichonse chimene amachilandira ku gulu lateokratiki la Mulungu. Ichi chidzatumikira monga chitsanzo chabwino kwa onse mumpingo ndipo chidzathandiza kuwagwirizanitsa pakati pawo ndi ubale wapadziko lonse Wachikristu.—Machitidwe 15:1-31; Ahebri 13:7; Chibvumbulutso 5:6.
Zotulukapo Zosangalatsa
Pamene m’misiri wanyumba akumanga nyumba yaikulu, iye amatsatira mosamalitsa malangizo a m’misiri wopanga mapulani kotero kuti nyumba imene akumangayo idzakhalitse. M’masiku achiwawa Chigumula chisanadze, Nowa anapatsidwa ntchito yomanga chingalawa. Iye anawuzidwa kamangidwe kake ndi anthu ndi zinyama zimene zikayenera kuloŵetsedwamo kuti zipulumuke Chigumula chomadzacho. Kodi Nowa anavomereza motani? Baibulo likuti: ‘Chotero anachita Nowa, monga mwa zonse anamlamulira iye Mulungu, momwemo anachita.’ Nowa yekha ndi awo amene anali naye m’chingalawa ndiwo anapulumuka Chigumula. (Genesis 6:5, 13-22; 7:23) Lerolino, tikukhala m’nthaŵi zimene ziri zofanana kwenikweni ndi masiku a Nowa, ndipo chifukwa cha chimenechi Mulungu adzasesa anthu onse oipa. Baibulo likutiuza masitepe amene tiyenera kutenga ngati tikufuna kukhala pakati pa opulumuka.—Mateyu 24:37-39; 2 Petro 3:5-7, 11.
Chotero, tiyeni tilandire moyamikira ndi kugwiritsira ntchito malangizo amene Yehova akupereka kupyolera m’Mawu ake olembedwa ndi gulu lake lapadziko lapansi. Kuchita tero kukatibweretsera chipambano ndi chisangalalo ndipo kudzapulumutsanso miyoyo yathu.