Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w90 11/1 tsamba 10-15
  • Kawonedwe ka Mkristu ka Maulamuliro Aakulu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kawonedwe ka Mkristu ka Maulamuliro Aakulu
  • Nsanja ya Olonda​—1990
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuwazindikira Maulamuliro Aakulu
  • “Amakhala m’Malo Awo Aang’ono Mololedwa ndi Mulungu”
  • “Mulungu wa Nthawi Yino”
  • Olamulira Amaganizo Abwino
  • Lingaliro Lachikristu la Ulamuliro
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Mulungu ndi Kaisara
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Kulemekeza Ulamuliro N’chifukwa Chiyani Kuli Kofunika?
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Ntchito ya Maulamuliro Aakulu
    Nsanja ya Olonda​—1990
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda​—1990
w90 11/1 tsamba 10-15

Kawonedwe ka Mkristu ka Maulamuliro Aakulu

“Munthu aliyense akhale wogonjera ku maulamuliro aakulu, pakuti palibe ulamuliro wina kusiyapo wochokera kwa Mulungu; olamulira alipoŵa amakhala m’malo awo aang’ono mololedwa ndi Mulungu.”​—AROMA 13:1, “NW.”

1, 2. (a) Kodi nchifukwa ninji Paulo adali wandende m’Roma? (b) Kodi kuchitira apilu kwa Paulo kwa Kaisara kukudzutsa mafunso otani?

MTUMWI Paulo analemba mawu ali pamwambawo kwa Aroma pafupifupi 56 C.E. Zaka zoŵerengeka pambuyo pake, iye anadzipeza ali m’Roma monga wandende. Chifukwa ninji? Iye adaukiridwa ndi chipwirikiti cha anthu mu Yerusalemu ndikulanditsidwa ndi asilikali Achiroma. Pamene iye anatengedwera ku Kaisareya, anayang’anizana ndi zinenezo zonyenga, komabe anadzichinjiriza yekha pamaso pa bwanamkubwa Wachiroma, Felike. Felike anamsunga iye m’ndende kwa zaka ziŵiri, akumayembekezera kulandira chiphuphu. Pomalizira pake, Paulo anapempha bwanamkubwa wotsatira, Festo, kuti mlandu wake ukamvedwe ndi Kaisara.​—Machitidwe 21:27-32; 24:1–25:12.

2 Ichi chinali choyenera chake monga nzika ya Roma. Koma kodi kudali kolondola kwa Paulo kuchitira apilu kwa wolamulira maiko ambiri ameneyo pamene Yesu adasonyeza Satana kukhala “mkulu [weniweni] wa dziko lapansi” ndipo Paulo iyemwini anatcha Satana kukhala “mulungu wa nthawi yino ya pansi pano”? (Yohane 14:30; 2 Akorinto 4:4) Kapena kodi ulamuliro Wachiroma udali ndi ‘malo aang’ono’ amene adapangitsa Paulo kulingalira kuti kudali koyenera kutembenukira ku ulamulirowo kaamba ka kutetezera zoyenera zake? Kunena zowonadi, kodi mawu oyambirira a atumwiwo akuti, “Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu,” amavomereza Akristu kumvera olamulira aumunthu pamene kusamvera Mulungu sikukuloŵetsedwamo?​—Machitidwe 5:29.

3. Kodi Paulo akuvumbula lingaliro lolunjika lotani, ndipo kodi chikumbumtima chikuloŵetsedwamo motani?

3 Paulo akutithandiza kuyankha mafunso ameneŵa m’kalata yake kwa Aroma, m’mene akuvumbula lingaliro lolunjika kuloza ku maulamuliro a anthu. Pa Aroma 13:1-7, Paulo akumveketsa bwino lomwe mbali imene chikumbumtima cha Mkristu chiyenera kukhala nayo polinganiza chimvero chotheratu kwa Wolamulira Wamkulukulu, Yehova Mulungu, ndi chimvero chochepa ku “maulamuliro aakulu.”

Kuwazindikira Maulamuliro Aakulu

4. Kodi ndikuwongolera lingaliro kotani komwe kunachitidwa mu 1962, kukumadzutsa mafunso otani?

4 Kwa zaka zambiri, kufikira 1962, Mboni za Yehova zinkaganiza kuti maulamuliro aakuluwa adali Yehova Mulungu ndi Kristu Yesu. Komabe, mogwirizana ndi Miyambo 4:18, kuunika kunawonjezeka, ndipo lingaliro limeneli linawongoleredwa, kumene kungadzutse mafunso m’maganizo mwa anthu ena. Kodi tsopano talunjika ponena kuti maulamulirowa ndiwo mafumu, mapulezidenti, nduna zazikulu zaboma, ameya, oweruza, ndi ena amene ali ndi ulamuliro wandale m’dziko ndikuti tifunikira kugonjera pang’ono kwa iwo?

5. Kodi mawu apatsogolo ndi apambuyo a Aroma 13:1 amatithandiza motani kuzindikira maulamuliro aakulu, ndipo kodi ndimotani mmene matembenuzidwe osiyanasiyana a Baibulo amachilikizira chizindikiritso chimenechi?

5 Irenaeus, wolemba nkhani wa m’zaka za zana lachiŵiri C.E., anati anthu ena a m’tsiku lake, anati Paulo pa Aroma 13:1 ankalankhula “kusonya ku mphamvu zaungelo [kapena] za olamulira osawoneka.” Komabe, Irenaeus mwiniyo analingalira maulamuliro aakuluwo kukhala “maulamuliro a anthu enieni.” Mawu a Paulo apambuyo ndi patsogolo akusonyeza kuti Irenaeus adali wolunjika. M’mavesi othera a Aroma mutu 12, Paulo akulongosola mmene Akristu ayenera kukhalira pamaso pa “anthu onse,” kuchitira ngakhale ‘adani’ mwachikondi ndi molingalira. (Aroma 12:17-21) Momvekera, mawu akuti “anthu onse” akulozera kwa anthu okhala kunja kwa mpingo Wachikristu. Chotero “maulamuliro aakulu,” amene Paulo akupitiriza kuwalongosola, ayeneranso kukhala kunja kwa mpingo Wachikristu. Mogwirizana ndi ichi, onani mmene matembenuzidwe osiyanasiyana amamasulira mbali yoyamba ya Aroma 13:1: “Aliyense ayenera kumvera maulamuliro a boma” (Today’s English Version); “aliyense ayenera kudzigonjetsera ku maulamuliro olamulira” (New International Version); “aliyense afunikira kumvera maulamuliro a boma.”​—New Testament in Modern English ya Phillips.

6. Kodi ndimotani mmene mawu a Paulo okhudza kukhoma msonkho ndi kulipira amasonyezera kuti maulamuliro aakuluwa ayenera kukhala maulamuliro akudziko?

6 Paulo akupitiriza kunena kuti maulamuliro ameneŵa amafuna misonkho ndi kulipira. (Aroma 13:6, 7) Mpingo Wachikristu sumafuna misonkho kapena kulipira; osatinso Yehova kapena Yesu kapena ‘olamulira osawoneka’ ena onse. (2 Akorinto 9:7) Misonkho imakhomedwa ku maulamuliro akudziko okha. Momvana ndi ichi, mawu Achigiriki a “msonkho” ndi “kulipira” amene Paulo anawagwiritsira ntchito pa Aroma 13:7 amasonya mwachindunji ku ndalama zolipiridwa ku Boma.a

7, 8. (a) Kodi malemba osiyanasiyana amagwirizana motani ndi lingaliro lakuti Akristu ayenera kugonjera ku maulamuliro andale a dziko lino? (b) Kodi ndiliti lokha pamene Mkristu sadzagwirizana ndi malamulo a ‘olamulira’?

7 Kuwonjezerapo, chenjezo la Paulo la kukhala ogonjera ku maulamuliro aakulu nlogwirizana ndi lamulo la Yesu la kupereka kwa ‘Kaisara zake za Kaisara,’ pamene “Kaisara” akuimira ulamuliro wakudziko. (Mateyu 22:21) Zikugwirizananso ndi mawu a Paulo a pambuyo pake kwa Tito awa: ‘Uwakumbutse iwo agonje kwa akulu, ndi aulamuliro, akhale omvera, okonzeka pa ntchito iriyonse yabwino.’ (Tito 3:1) Chotero, pamene Akristu alamulidwa ndi maboma kukhalamo ndi phande m’ntchito za m’mudzi, iwo amagwirizana nawo moyenerera malinga ngati ntchitozo siziri m’loŵa mmalo wofuna kuti pakhale kupotoza kuti utumiki wosakhala wa m’Malemba uchitidwe kapena mwinamwake kuswa malamulo amakhalidwe abwino a Malemba, onga omwe akupezeka pa Yesaya 2:4.

8 Petro akutsimikiziranso kuti tiyenera kugonjera ku maulamuliro a dziko lino pamene akunena kuti: ‘Tadzigonjani kwa zoikika zonse za anthu, chifukwa cha Ambuye; ngakhale kwa mfumu, monga mutu wa onse kapena kwa akazembe, monga otumidwa ndi iye kukalanga ochita zoipa, koma kusimba ochita zabwino.’ (1 Petro 2:13, 14) Mogwirizana ndi ichi, Akristu akalabadiranso chenjezo ili la Paulo kwa Timoteo: ‘Ndidandaulira tsono, poyambayamba, kuti achitike mapembedzo, mapemphero, mapembedzero, mayamiko, chifukwa cha anthu onse; chifukwa cha mafumu ndi onse akuchita ulamuliro; kuti m’moyo mwathu tikakhale odikha mtima ndi achete.’b​—1 Timoteo 2:1, 2.

9. Kodi nchifukwa ninji kusonya maulamuliro a anthu kukhala “aakulu” sikumachotsera Yehova ulemerero?

9 Powatcha maulamuliro akudziko kukhala “aakulu,” kodi tikuchotsako pang’ono ulemu wofunikira kunka kwa Yehova? Ayi, chifukwa chakuti Yehova ngwamkulukulu kuposa ukulu wamba. Iye ndiye “Mfumu Ambuye,” “Wamkulukulu.” (Salmo 73:28, NW; Danieli 7:18, 22, 25, 27, NW; Chibvumbulutso 4:11; 6:10) Kugonjera kwathu koyenerera ku maulamuliro aumunthu sikuchotsa konse kulambira kwathu Wolamulira Wamkulukulu, Mfumu Ambuye Yehova. Nangano, kodi maulamuliro ameneŵa ngaakulu kumlingo wotani? Nkulinga kwa anthu anzawo okha ndiponso mkati mwa chigawo chawo cha ntchito. Iwo ali ndithayo la kulamulira ndi kuchinjiriza zitaganya za anthu, ndipo kaamba ka ichi iwo amapanga malamulo onena za mkhalidwe wa anthu.

“Amakhala m’Malo Awo Aang’ono Mololedwa ndi Mulungu”

10. (a) Kodi ndemanga ya Paulo yonena za ‘kukhazikitsa’ maulamuliro aakulu imatsimikiziranji ponena za ulamuliro wa Yehova mwini? (b) Kodi chomwe Yehova walola ponena za ‘kukhazikitsa’ olamulira ena nchiyani, ndipo motero kodi atumiki ake akuyesedwa motani?

10 Ukulu wa Yehova Mulungu pa maulamuliro akudziko ukuwonekera m’mfundo yakuti maulamuliro ameneŵa “amakhala m’malo awo aang’ono mololedwa ndi Mulungu.” (NW) Komabe, ndemanga imeneyi imadzutsa funso. Zaka zingapo Paulo atalemba mawu ameneŵa, wolamulira Wachiroma Nero anayambitsa mkupiti wa chizunzo chowopsa molimbana ndi Akristu. Kodi Mulungu mwaumwini anakhazika Nero pa malo akewo? Kutalitali! Sizikutanthauza kuti wolamulira aliyense payekha amasankhidwa ndi Mulungu ndikukhazikidwa m’malowo ‘mwa chisomo cha Mulungu.’ Mmalo mwake, Satana nthaŵi zina amapangitsa anthu ankhalwe kukhala pamalo a olamulira, ndipo Yehova amachilola chimenechi, limodzi ndi mayeso amene olamulira oterowo amabweretsa pa atumiki ake osunga umphumphu.​—Yerekezerani ndi Yobu 2:2-10.

11, 12. Kodi ndinkhani ziti zimene zinalembedwa zosonyeza kuti Yehova mwaumwini anayendetsa zinthu kuika kapena kuchotsa pamalo olamulira akudziko?

11 Komabe, Yehova mwaumwini walowereramo m’zochitika za olamulira kapena maboma ena kotero kuti atumikire zifuno zake zapamwamba. Mwachitsanzo, m’tsiku la Abrahamu, Akanani analoledwa kutsala m’dziko la Kanani. Komabe, pambuyo pake, Yehova anawazula napatsa dzikolo kwa mbewu ya Abrahamu. Paulendo wa m’chipululu wa Israyeli, Yehova sanalole kuti iwo akanthe Amoni, Moabu, ndi Phiri la Seiri. Koma adawalamuliradi kuti awononge maufumu a Sihoni ndi Ogi.​—Genesis 15:18-21; 24:37; Eksodo 34:11; Deuteronomo 2:4, 5, 9, 19, 24; 3:1, 2.

12 Israyeli atakhazikika m’Kanani, Yehova anapitiriza kukhala ndi chikondwerero chachindunji m’maulamuliro amene anayambukira anthu ake. Nthaŵi zina, pamene Israyeli anachimwa, Yehova anawalola kulamulidwa ndi ulamuliro wachikunja. Pamene analapa, iye anachotsa ulamuliro umenewo m’dzikomo. (Oweruza 2:11-23) Pomalizira pake, iye analola Yuda, limodzi ndi mitundu ina yambiri, kukhala pansi pa ulamuliro wa Babulo. (Yesaya 14:28–19:17; 23:1-12; 39:5-7) Israyeli atanka m’ndende m’Babulo, Yehova ananeneratu za kubuka ndi kugwa kwa maufumu adziko kumene kukayambukira anthu ake kuyambira nthaŵi ya Babulo mpaka m’tsiku lathu.​—Danieli, mitu 2, 7, 8, ndi 11.

13. (a) Mogwirizana ndi nyimbo ya Mose, kodi nchifukwa ninji Yehova anaikira anthu malire? (b) Kodi nchifukwa ninji Mulungu pambuyo pake anabwezeretsa Israyeli kudziko lake?

13 Mose anaimba motere ponena za Yehova: ‘Pamene Wam’mwambamwamba anagawira amitundu cholowa chawo, pamene anagawa ana a anthu, anaika malire a mitundu ya anthu, monga mwa kuwerenga kwawo kwa ana a Israyeli. Pakuti gawo la Yehova ndilo anthu ake; Yakobo ndiye muyeso wa cholowa chake.’ (Deuteronomo 32:8, 9; yerekezerani ndi Machitidwe 17:26.) Inde, kuti achite chifuniro chake, Mulungu anasankhiratu maulamuliro amene akakhalapo ndi ena amene akawonongedwa. Mwanjirayi, iye anagawira mbadwa za Abrahamu dziko monga cholowa ndipo pambuyo pake anawabwezeretsa ku dziko limenelo, kotero kuti pomalizira pake Mbewu yolonjezedwayo ikakhoza kubadwira m’menemo, monga mmene kunaloseredweradi.​—Danieli 9:25, 26; Mika 5:2.

14. Kwakukulukulu, kodi ndim’lingaliro lotani limene Yehova amaikira olamulira aumunthu m’malo awo aang’ono?

14 Komabe, m’zochitika zambiri, Yehova amakhazika olamulira m’malo awo aang’ono m’lingaliro lakuti amalola anthu kutenga malo a ulamuliro waung’onowo kwa wina ndi mnzake koma wochepa nthaŵi zonse kwa iye. Motero, pamene Yesu anaima pamaso pa Pontiyo Pilato, anauza wolamulira ameneyo kuti: ‘Simukadakhala nawo ulamuliro uliwonse pa ine, ngati sukadapatsidwa kwa inu kuchokera kumwamba.’ (Yohane 19:11) Ichi sichinatanthauze kuti Pilato mwiniyo anaikidwa m’malowo ndi Mulungu, koma chinatanthauza kuti kulamulira kwake kukhalapo ndi moyo kapena kufa kwa Yesu kudangokhalapo mwa kuloledwa ndi Mulungu.

“Mulungu wa Nthawi Yino”

15. Kodi Satana amachita ulamuliro m’dziko lino mwanjira yotani?

15 Komano, bwanji nanga za ndemanga ya m’Baibulo yakuti Satana ndiye mulungu, kapena wolamulira wa dziko lino? (Yohane 12:31; 2 Akorinto 4:4) Ndithudi, bwanji nanga za kudzitukumula kuja kwa Satana kulinga kwa Yesu pamene anawonetsa Yesu maufumu onse a dziko nati: “Ulamuliro wonse umenewu . . . unaperekedwa kwa ine; ndipo ndiupatsa kwa iye amene ndifuna.” (Luka 4:6) Yesu sanatsutse kudzitukumula kwa Satana. Ndipo mawu a Satana akugwirizana ndi mawu amene pambuyo pake Paulo anawalembera Aefeso akuti: ‘Kulimbana kwathu sitilimbana nawo mwazi ndi thupi, komatu nawo maukulu, ndi maulamuliro, ndi akuchita zolimbika a dziko lapansi a mdima uno, ndi a uzimu a choipa m’zakumwamba.’ (Aefeso 6:12) Kuwonjezera apa, bukhu la Chibvumbulutso limasonyeza Satana monga chinjoka chokalamba chimene chikupereka kwa chirombo chophiphiritsira dongosolo la ndale zadziko ‘mphamvu yake, ndi mpando wachifumu wake, ndi ulamuliro waukulu.’​—Chibvumbulutso 13:2.

16. (a) Kodi ulamuliro wa Satana ungawoneke motani kuti ngwokhala ndi polekezera? (b) Kodi Yehova amamulolelanji Satana kukhala ndi ulamuliro pakati pa anthu?

16 Komabe, onani kuti ndemanga ya Satana kwa Yesu yakuti, “Ulamuliro wonse umenewu . . . unaperekedwa kwa ine,” ikusonyeza kuti nayenso amachita ulamuliro kokha mwa kuloledwa. Kodi nchifukwa ninji Mulungu amapereka chilolezo chimenechi? Ntchito ya Satana monga wolamulira wa dziko inayamba kalelo m’Edeni pamene ananeneza Mulungu poyera za kunama ndikuchita ulamuliro Wake mosalungama. (Genesis 3:1-6) Adamu ndi Hava anatsatira Satana napandukira Yehova Mulungu. Panthaŵi imeneyo, ndi chiweruzo changwiro, Yehova akanakhoza kupha Satana ndi atsatiri ake aŵiri atsopanowo. (Genesis 2:16, 17) Koma mawu a Satana adalidi chitokoso kwa Yehova mwiniyo. Chotero m’nzeru zake Mulungu anamulola Satana kukhalapo kwa kanthaŵi kochepa, ndipo Adamu ndi Hava adaloledwa kubala ana asanamwalire. Mwanjirayi, Mulungu anapereka nthaŵi ndi mwaŵi kuti chinyengo cha chitokoso cha Satana chisonyezedwe poyera.​—Genesis 3:15-19.

17, 18. (a) Kodi tinganenerenji kuti Satana ndiye mulungu wa dziko lino? (b) Kodi ndimwanjira yotani mmene ziriri kuti “palibe ulamuliro” m’dziko lino “kusiyapo wochokera kwa Mulungu”?

17 Zochitika chiyambire nthaŵi ya Edeni zasonyeza kuti zinenezo za Satana zidali mabodza a mkunkhuniza. Mbadwa za Adamu sizinapeze mtendere konse ponse paŵiri mu ulamuliro wa Satana kapena wa anthu. (Mlaliki 8:9) Kumbali ina, zochita za Mulungu ndi anthu ake zasonyeza kupambana kwa ulamuliro waumulungu. (Yesaya 33:22) Koma popeza kuti mbadwa zambiri za Adamu sizimavomereza ufumu wa Yehova, m’kutero iwo mwadala kapena mosadziŵa amatumikira Satana monga mulungu wawo.​—Salmo 14:1; 1 Yohane 5:19.

18 Posachedwapa, nkhani zimene zinadzutsidwa m’Edeni zidzathetsedwa. Ufumu wa Mulungu udzalanda kulamulira kwa zochita zonse za anthu, ndipo Satana adzaikidwa kuphompho. (Yesaya 11:1-5; Chibvumbulutso 20:1-6) Komabe, pakali pano, mtundu winawake wa kakonzedwe, kapena mpangidwe, wafunikira kukonzedwera anthu kotero kuti pakhale moyo wadongosolo. Yehova ‘sali Mulungu wa chisokonezo koma wa mtendere.’ (1 Akorinto 14:33) Chotero, iye walola mipangidwe ya ulamuliro kukhalapo m’zitaganya zomwe zinapangidwa kunja kwa Edeni, ndipo waŵalola anthu kuchita ulamuliro m’kakonzedwe kameneka. Mwanjirayi nchifukwa chake kukunenedwa kuti “palibe ulamuliro wina kusiyapo wochokera kwa Mulungu.”

Olamulira Amaganizo Abwino

19. Kodi wolamulira aliyense waumunthu ali pansi pa kulamulira kwachindunji kwa Satana?

19 Chiyambire nthaŵi ya Edeni, Satana wakhala ndi ufulu waukulu pakati pa anthu, ndipo wagwiritsira ntchito ufulu umenewu kuyendetsa zinthu padziko lapansi, mogwirizana ndi kudzitukumula komwe anachita kwa Yesu. (Yobu 1:7; Mateyu 4:1-10) Komabe, zimenezi sizikutanthauza kuti wolamulira aliyense m’dziko lino amagonjera kotheratu ku ulamuliro wa Satana. Olamulira ena​—monga Nero m’zaka za zana loyamba ndi Adolf Hitler m’zana lathu​—asonyezadi mzimu wausatana. Koma ena sanatero. Sergio Paulo, kazembe wa ku Kupro, anali “munthu wanzeru” amene ‘anafunitsa kumva mawu a Mulungu.’ (Machitidwe 13:7) Galiyo, kazembe wa ku Akaya, anakana kukakamizidwa ndi Ayuda amene ananeneza Paulo. (Machitidwe 18:12-17) Olamulira ena ambiri molemekezeka achita ulamuliro wawo mwanzeru.​—Yerekezerani ndi Aroma 2:15.

20, 21. Kodi ndizochitika ziti za m’zaka za zana la 20 zimene zikusonyeza kuti olamulira aumunthu samachita chifuniro cha Satana nthaŵi zonse?

20 Bukhu la Chibvumbulutso linaneneratu kuti mkati mwa “tsiku la Ambuye,” loyambira mu 1914, Yehova akayendetsadi maulamuliro a anthu kulepheretsa zifuno za Satana. Chibvumbulutso chimafotokoza za chizunzo chachikulu, choyambitsidwa ndi Satana molimbana ndi Akristu odzozedwa, chimene chikamezedwa ndi “dziko.” (Chibvumbulutso 1:10; 12:16) Anthu a ‘m’dziko,’ chitaganya cha anthu chimene chiri padziko lapansi tsopano, akatetezera anthu a Yehova ku chizunzo cha Satana.

21 Kodi zimenezi zachitikadi? Inde. Mwachitsanzo, m’ma 1930 ndi m’ma 1940, Mboni za Yehova mu United States zidali pansi pa chipsinjo chachikulu, kuvutika ndi kuwukira kwa magulu ndi kugwidwa kosalungamitsika kobwerezabwereza. Iwo anapeza mpumulo pamene Khoti Lalikulu la U.S. linapereka malamulo angapo ozindikira ntchito yawo mwalamulo. M’malo enanso, maulamuliro athandiza anthu a Mulungu. Zaka 40 zapitazo mu Ireland, gulu la anthu a Roma Katolika linawukira Mboni ziŵiri mu mzinda wa Cork. Wapolisi wa kumaloko anathandiza Mbonizo, ndipo khoti la lamulo linapereka chilango kwa owukirawo. Chaka chathachi, mu Fiji, pa msonkhano wa nyakwawa zazikulu panaperekedwa lingaliro la kuletsa ntchito ya Mboni za Yehova. Nyakwawa mmodzi analankhula molimba mtima mokomera Mbonizo, ndipo lingalirolo linagonjetsedwa mosavuta.

22. Kodi ndimafunso otani amene adzafotokozedwa potsatira?

22 Ayi, maulamuliro akudziko samatumikira zofuna za Satana nthaŵi zonse. Akristu angagonjere ku maulamuliro aakulu popanda kugonjera kwa Satana iyemwini. Ndithudi, iwo adzakhala ogonjera kwa maulamuliro ameneŵa kwa utali umene Mulungu alola maulamulirowo kukhalapo. Komano, kodi kugonjera kumeneku kumatanthauzanji? Ndipo kodi Akristu angayembekezerenji kuchokera kwa maulamuliro aakulu ameneŵa? Mafunso ameneŵa adzafotokozedwa m’nkhani zophunzira zoyambira pa masamba 18 ndi 23 a magazini ano.

[Mawu a M’munsi]

a Mwachitsanzo, onani kugwiritsiridwa ntchito kwa liwu lakuti “msonkho” (phoʹros) pa Luka 20:22. Onaninso kugwiritsiridwa ntchito kwa liwu Lachigiriki lakuti teʹlos, limene panopa latembenuzidwa kukhala “kulipira,” pa Mateyu 17:25, (NW) pamene latembenuzidwa “misonkho ya katundu.”

b Nauni Yachigiriki yotembenuzidwa ‘akuchita ulamuliro,’ hy·pe·ro·kheʹ, njogwirizana ndi mneni wakuti hy·pe·reʹkho. Liwu lakuti “aakulu” m’mawu akuti “maulamuliro aakulu” lachokera ku mneni Wachigiriki ameneyu, chimene chikuwonjezera ku umboni wakuti maulamuliro aakuluwa ndiwo maulamuliro akudziko. Mamasuliridwe a Aroma 13:1 mu The New English Bible, akuti “Munthu aliyense agonjere ku maulamuliro aakulukulu,” ngosalunjika. Anthu ‘akuchita ulamuliro’ sali aakulukulu, chinkana kuti iwo angakhale aakulu kwa anthu ena.

Kodi Mungayankhe Motani?

◻ Kodi ndani omwe ali maulamuliro aakulu?

◻ Kodi tinganenerenji kuti “palibe ulamuliro kusiyapo wochokera kwa Mulungu”?

◻ Kodi nchifukwa ninji Yehova amalola dziko kukhala pansi pa ulamuliro wa Satana?

◻ Kodi ndimwanjira yotani mmene Mulungu amakhazikira olamulira aumunthu “m’malo awo aang’ono”?

[Chithunzi patsamba 13]

Roma atatenthedwa, Nero anasonyezadi mzimu wausatana

[Chithunzi patsamba 15]

Sergio Paulo, kazembe wa Kupro, anafuna kumva mawu a Mulungu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena