Ntchito ya Maulamuliro Aakulu
‘Pakuti ndiye mtumiki wa Mulungu, kuchitira iwo zabwino. Koma ngati uchita choipa, opatu.’—AROMA 13:4.
1, 2. Kodi ndimotani mmene anthu ambiri m’Chikristu Chadziko adziloŵetsera m’machitachita a kuukira?
ZAKA ziŵiri zapitazo msonkhano wa abishopu mu London unadzutsa nkhani yamkwiyo yolembedwa ndi mkonzi mu New York Post. Msonkhanowu unali Msonkhano wa pa Lambeth, umene abishopu aakulu oposa 500 a Angilikani anapezekako. Mkwiyowo unaputidwa ndi chigamulo choperekedwa pamsonkhanowo chofotokoza kuyanja anthu “omwe, pambuyo pa kulephera njira zina, amasankha kulimbana ndi zida kukhala njira yokha yopezera chilungamo.”
2 Post inanena kuti uku, kwenikweni, kunali kuvomereza uchigaŵenga. Komabe, abishopuwo ankangotsatira chikhoterero chomakulakula. Mkhalidwe wawo sunasiyane ndi wa wansembe Wachikatolika wa ku Ghana amene anayamikira nkhondo yachizembera kukhala njira yofulumira koposa, yotsimikizirika, ndiyachisungiko yomasulira Afirika; kapena bishopo Wachifirika wa Methodist amene anawinda “kuchita nkhondo yofuna chimasuko mpaka kumapeto kwenikweni”; kapena wa amishonale ambiri a Chikristu Chadziko mu Asia ndi Kum’mwera kwa Amereka amene anamenyana ndi oukira maboma okhazikitsidwa.
Akristu Owona ‘Samatsutsa Ulamuliro’
3, 4. (a) Kodi ndi malamulo amakhalidwe abwino otani amene akuswedwa ndi anthu odzitcha kukhala Akristu amene amachilikiza kuukira? (b) Kodi munthu wina anazindikira chiyani ponena za Mboni za Yehova?
3 M’zaka za zana loyamba, Yesu ananena motere za atsatiri ake: “Sakhala a dziko lapansi, monga Ine sindikhala wa dziko lapansi.” (Yohane 17:14) Munthu aliyense amene amadzitcha Mkristu amene amachilikiza kuukira ali kwakukulukulu mbali ya dziko. Iye sangakhale mtsatiri wa Yesu; salinso ‘wogonjera ku maulamuliro aakulu.’ (Aroma 13:1, NW) Iye angachite bwino kulabadira chenjezo la mtumwi Paulo lakuti “iye amene amatsutsana ndi ulamuliro watenga malo otsutsana ndi kakonzedwe ka Mulungu; awo amene atenga malo otsutsana nako adzalandira chilango kwa iwo eni.”—Aroma 13:2, NW.
4 Mosiyana ndi anthu ambiri m’Chikristu Chadziko, Mboni za Yehova sizitengako mbali m’chiwawa cha zida. Munthu wina wa ku Ulaya anazindikira kaimidweka. Iye akulemba motere: “Pamene ndinawona zimene chipembedzo ndi ndale zadziko zabala, ndinadzipereka ku kugwetsa dongosolo lamayanjano lokhazikitsidwa. Ndinagwirizana ndi kagulu ka zigaŵenga ndipo ndinaphunzitsidwa kugwiritsira ntchito zida zamitundu yonse; ndinakhalamo ndi phande m’kuba koukira ndi zida kwankhaninkhani. Moyo wanga unali pachiswe nthaŵi zambiri. Pamene nthaŵi inkapita, kunawonekeratu kuti tinkalephera nkhondoyo. Ndinakhwethemulidwa, wodzala ndi kupanda chiyembekezo m’moyo. Ndiyeno Mboni inagogoda pakhomo lathu. Iye anandiuza za Ufumu wa Mulungu. Ndikumaumirira kuti ndinali kutaya nthaŵi yanga, ndinapereka lingaliro lakuti mkazi wanga yekha amvetsere. Iye anamvetseradi, ndipo phunziro Labaibulo lapanyumba linayambitsidwa. Pomalizira pake, ndinavomereza kupezekapo paphunzirolo. Sindingathe kulongosola konse mpumulo umene ndinaupeza pamene ndinamvetsetsa mphamvu yosonkhezera anthu kuchita zoipa. Lonjezo lozizwitsa la Ufumu landipatsa chiyembekezo chochilikiza ndi chifuno m’moyo.”
5. Kodi nchifukwa ninji Akristu amakhala ogonjera mwamtendere ku maulamuliro aakulu, ndipo kodi izi zidzakhala motero kufikira liti?
5 Akristu ali oimira kapena athenga a Mulungu ndi a Kristu. (Yesaya 61:1, 2; 2 Akorinto 5:20; Aefeso 6:19, 20) Pokhala anthu otero, iwo amakhala auchete m’mikangano ya dziko lino. Ngakhale kuti madongosolo ena andale zadziko amawonekera kukhala ndi chipambano m’zachuma kuposa ena, ndipo ena amapereka ufulu wochuluka kwa anthu kuposa ena, Akristu samachilikiza kapena kukweza dongosolo limodzi pamwamba pa linzake. Iwo amadziŵa kuti madongosolo onse ngopanda ungwiro. Iko kali “kakonzedwe ka Mulungu” kuti iwo apitirizebe kukhalapo kufikira Ufumu wake utalanda ulamuliro. (Danieli 2:44) Chotero, Akristu amakhala ogonjera mwamtendere ku maulamuliro aakulu pamene akupititsa patsogolo ubwino wa onse mwakulalikira mbiri yabwino ya Ufumu.—Mateyu 24:14; 1 Petro 3:11, 12.
Kumvera Lamulo
6. Kodi nchifukwa ninji malamulo ambiri opangidwa ndi anthu ngabwino ngakhale kuti “dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo”?
6 Maboma a maiko amakhazikitsa dongosolo la malamulo, ndipo ambiri a malamulowa ngabwino. Kodi chimenechi chiyenera kutidabwitsa, polingalira kuti “dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo”? (1 Yohane 5:19) Ayi. Yehova anapatsa Adamu, tate woyambirira, chikumbumtima, ndipo lingaliro lachibadwa lamkatili la chabwino ndi choipa limawonekera m’njira zambiri m’malamulo a anthu. (Aroma 2:13-16) Hammurabi, wopanga lamulo wamakedzana Wachibabulo, analemba mawu oyamba ku mpambo wa malamulo ake motere: “Panthaŵi imeneyo [iwo] anandiloza kuti ndichilikize ubwino wa anthu, ineyo, Hammurabi, kalonga wopembedza, woopa mulungu, kupangitsa chilungamo kukhalamo m’dziko, kuwononga oipa ndi achabe, kotero kuti amphamvu asatsendereze ofooka.”
7. Ngati munthu wina aswa lamulo, kodi ndani yemwe ali ndi kuyenera kwa kupereka chilango, ndipo nchifukwa ninji?
7 Maboma ambiri anganene kuti cholinga cha malamulo awo nchofananacho: kuchilikiza ubwino wa nzika ndikukhalitsa dongosolo labwino m’chitaganya. Chotero, iwo amalanga ochita machitidwe osachilikiza mayanjano, monga ngati mbanda ndi kuba, naika malamulo oletsa, monga ngati malire a liŵiro loyendetsera ndi malamulo okhudza malo oimikapo magalimoto. Aliyense wakuswa mwadala malamulo awo amachita motsutsana ndi ulamulirowo ndipo “adzalandira chilango kwa iwo eni.” Chilango chochokera kwa yani? Osati kwenikweni kwa Mulungu. Liwu Lachigiriki limene panopa latembenuzidwa kukhala chilango lingasonye ku njira zakachitidwe zaboma mmalo mwa zilango zoperekedwa ndi Yehova. (Yerekezerani ndi 1 Akorinto 6:7.) Ngati munthu aliyense achita mosemphana ndi lamulo, ulamuliro waukulu uli ndi kuyenera kwakumpatsa chilango.
8. Kodi mpingo udzachita motani ngati chiŵalo chake chapalamula upandu waukulu?
8 Mboni za Yehova ziri ndi dzina labwino kaamba kosatsutsa maulamuliro a anthu. Zitachitika kuti munthu wina mumpingo waswa lamulo, mpingo sudzamthandiza iye kupeŵa chilango chalamulo. Ngati munthu aliyense waba, kupha, kufalitsa minyozo, kunama m’misonkho yake, kugwirira chigololo, kunyenga, kugwiritsira ntchito mankhwala oletsedwa ndi lamulo, kapena kutsutsa ulamuliro wolunjika mwanjira ina iriyonse, iye adzayang’anizana ndi chilango champhamvu mumpingo—ndipo sayenera kuganiza kuti akuzunzidwa pamene apatsidwa chilango ndi ulamuliro wakudziko.—1 Akorinto 5:12, 13; 1 Petro 2:13-17, 20.
Ochititsa Mantha
9. Kodi ndinjira yotani imene Akristu amatsatira moyenerera ngati awopsezedwa ndi anthu osaweruzika?
9 Paulo akupitiriza kufotokoza kwake maulamuliro aakulu, akumati: “Pakuti olamulira sachititsa mantha ntchito zabwino, koma zoipa. Kodi sufuna kuwopa ulamuliro? Chitabe zabwino, ndipo udzalandira kutama mmenemo.” (Aroma 13:3, NW) Sayenera kukhala Akristu okhulupirika amene ayenera kuwopa chilango chochokera ku ulamuliro koma ochita zoipa, awo amene amachita ‘ntchito zoipa,’ machitidwe aupandu. Pamene Mboni za Yehova zawopsezedwa ndi anthu osaweruzika oterowo, izo moyenerera zingavomereze chitetezo cha apolisi kapena asilikali kuchokera kwa ulamuliro.—Machitidwe 23:12-22.
10. Kodi Mboni za Yehova ‘zalandira chitamando’ motani kuchokera kwa olamulira?
10 Kwa Mkristu amene amasunga lamulo la ulamuliro waukulu, Paulo akuti: “Udzalandira kutama m’menemo.” Monga chitsanzo cha ichi, talingalirani makalata ena amene analandiridwa ndi Mboni za Yehova m’Brazil pambuyo pa misonkhano yawo yachigawo. Kuchokera kwa kansela wa dipatimenti ya zamaseŵera ya mzindawo kunabwera kalata yotere: “Chitamando chachikulu chiyenera kuperekedwa ku mkhalidwe wanu wa mtendere. Kuli kotonthoza m’dziko lovutitsidwa la lerolino kudziŵa kuti ambiri chotero akukhulupirirabe ndi kulambira Mulungu.” Kuchokera kwa dairekitala wa bwalo lamaseŵera la mzindawo kunabwera kalata iyi: “Mosasamala kanthu za chiŵerengero chachikulu cha opezekapo, palibe chochitika chomwe chinasimbidwa choipitsa chochitikacho, tikuyamikira gulu lamtenderelo.” Kuchokera ku ofesi ya meya kunabwera kalata iyi: “Tikufuna kugwiritsira ntchito mwaŵi umenewu kukuyamikirani chifukwa cha dongosolo lanu ndi kusunga mwambo kozizwitsa, ndipo tikufunirani chipambano m’zochita zanu zonse zamtsogolo.”
11. Kodi nchifukwa ninji kulalikidwa kwa mbiri yabwino sikunganenedwe mwanjira iriyonse kukhala ntchito yoipa?
11 Mawu akuti ‘kuchita zabwino’ amalozera ku machitidwe a chimvero kulinga ku malamulo a maulamuliro aakulu. Mogwirizanamo, ntchito yathu yolalikira, imene tinalamulidwa ndi Mulungu, osati munthu, siiri ntchito yoipa—mfundo imene maulamuliro andale zadziko ayenera kuidziŵa. Iyo iri utumiki wapoyera umene umakweza mkhalidwe wabwino wa anthu amene amavomereza. Chotero, tikuyembekezera kuti maulamuliro aakulu adzachinjiriza kuyenera kwathu kwa kulalikira kwa ena. Paulo anachita apilu kwa maulamuliro kotero kuti akhazikitse mwalamulo kulalikira kwa mbiri yabwino. (Machitidwe 16:35-40; 25:8-12; Afilipi 1:7) Posachedwapa, Mboni za Yehova zafuna ndikupeza kuzindikiridwa kwalamulo kofananako kwa ntchito yawo m’Jeremani wa Kum’mawa, Hungary, Poland, Romania, Benin, ndi Myanmar (Burma).
“Ndiye Mtumiki wa Mulungu”
12-14. Kodi maulamuliro aakulu achita motani monga mtumiki wa Mulungu (a) m’nthaŵi za Baibulo? (b) m’nthaŵi zamakono?
12 Polankhula za ulamuliro wakudziko, Paulo akupitiriza kunena kuti: ‘Pakuti ndiye mtumiki wa Mulungu, kuchitira iwe zabwino. Koma ngati uchita choipa, opatu, pakuti iye sagwira lupanga kwachabe; pakuti ndiye mtumiki wa Mulungu wakukwiyira ndi kubwezera chilango wochita zoipa.’—Aroma 13:4.
13 Nthaŵi zina maulamuliro a dziko atumikira monga mtumiki wa Mulungu m’njira zakutizakuti. Koresi anatero pamene analamula Ayuda kuchoka m’Babulo kubwerera kukamanga nyumba ya Mulungu. (Ezara 1:1-4; Yesaya 44:28) Aritasasta adali mtumiki wa Mulungu pamene adatumiza Ezara ndi chopereka chomangitsiranso nyumba imeneyo ndipo pambuyo pake pamene anatuma Nehemiya kukamanganso malinga a Yerusalemu. (Ezara 7:11-26; 8:25-30; Nehemiya 2:1-8) Ulamuliro waukulu Wachiroma unatumikira motero pamene unapulumutsa Paulo ku gulu la anthu oukira mu Yerusalemu, kum’chinjiriza pamene chombo chinamswekera, ndikupanga makonzedwe oti iye akhale ndi nyumba yakeyake m’Roma.—Machitidwe 21:31, 32; 28:7-10, 30, 31.
14 Mofananamo, maulamuliro akudziko atumikira monga mtumiki wa Mulungu m’nthaŵi zamakono. Mwachitsanzo, mu 1959, Khoti Lalikulu la ku Canada linalamula kuti m’modzi wa Mboni za Yehova amene anapatsidwa mlandu wa kufalitsa zinthu zokopa ena ndi zochititsa manyazi m’Quebec adali wopanda liŵongo—mwakutero kutsutsa kunyada ndi kudzikweza kwa yemwe panthaŵiyo adali nduna yaikulu ya Quebec, Maurice Duplessis.
15. Kodi ndi m’njira yachisawawa yotani mmene maulamuliro amachitira monga mtumiki wa Mulungu, ndipo kodi iko kumawapatsa kuyenera kotani?
15 Kuwonjezera apa, mwachisawawa, maboma adziko amatumikira monga mtumiki wa Mulungu mwakusungitsa bata kufikira pamene Ufumu wa Mulungu udzatenga thayo limenelo. Mogwirizana ndi Paulo, kufikira lerolino ulamuliro ‘ukugwira lupanga,’ kusonyeza kuyenera kwake kwa kupereka chilango. Kaŵirikaŵiri, ichi chimaphatikizapo kuikidwa m’ndende kapena kulipira faindi. M’maiko ena ichi chingaphatikizeponso chilango cha imfa.a Kumbali ina, maiko ambiri asankha kusapereka chilango cha imfa, ndipo kumeneko nkuyenera kwawonso.
16. (a) Popeza kuti ulamuliro ndiwo mtumiki wa Mulungu, kodi atumiki ena a Mulungu alingalira chiyani kukhala choyenera kuchichita? (b) Kodi ndintchito ya mtundu wanji imene Mkristu sangaivomere, ndipo nchifukwa ninji ayi?
16 Chenicheni chakuti maulamuliro aakulu ali mtumiki wa Mulungu chimalongosola chifukwa chake Danieli, Ahebri atatu, Nehemiya, ndi Moredekai anali okhoza kulandira maudindo aakulu m’maboma a Babulo ndi Perisiya. Motero iwo anatha kuchonderera kwa ulamuliro wa Boma kaamba ka ubwino wa anthu a Mulungu. (Nehemiya 1:11; Estere 10:3; Danieli 2:48, 49; 6:1, 2) Lerolino Akristu enanso amagwira ntchito m’boma. Koma popeza kuti iwo sali adziko, sagwirizana ndi zipani zandale zadziko, kufuna ntchito ya ndale zadziko, kapena kuvomereza maudindo opanga malamulo m’magulu a ndale zadziko.
Kufunika kwa Chikhulupiriro
17. Kodi ndimikhalidwe yotani imene ingapangitse ena omwe sali Akristu kutsutsana ndi ulamuliro?
17 Komabe, kodi bwanji ngati ulamuliro ulekerera ziphuphu kapena ngakhale kutsendereza? Kodi Akristu ayenera kuyesa kuuloŵa m’malo ulamulirowo ndi wina umene ukuwoneka kukhala wabwinoko? Eya, chisalungamo chaboma ndi ziphuphu sizinthu zatsopano. M’zaka za zana loyamba, Ufumu wa Roma udali ndi chisalungamo monga ngati ukapolo. Iwo unalekereranso nduna zokonda ziphuphu. Baibulo limasimba za osonkhetsa misonkho omwe ankanama, woweruza wosalungama, ndi kazembe wa boma amene anafunafuna ziphuphu.—Luka 3:12, 13; 18:2-5; Machitidwe 24:26, 27.
18, 19. (a) Kodi Akristu amachita motani ngati nduna zaboma zikulakwitsa zinthu kapena kutenga ziphuphu? (b) Kodi Akristu awongolera motani miyoyo ya anthu, monga momwe kwasonyezedwa ndi katswiri wa mbiri yakale ndi bokosi liri pansili?
18 Akristu akadayesa kuthetsa kuchita molakwa kumeneko panthaŵiyo, komatu iwo sanatero. Mwachitsanzo, Paulo sanalalikire za kutha kwa ukapolo, ndipo sadawawuze Akristu okhala ndi akapolo kumasula akapolo awo. M’malo mwake, iye analangiza akapolo ndi eni akapolo kusonyeza chifundo Chachikristu pamene ankachitirana zinthu. (1 Akorinto 7:20-24; Aefeso 6:1-9; Filemoni 10-16; onaninso 1 Petro 2:18.) Mofananamo, Akristu sanadziloŵetse m’machitachita akuukira. Iwo adali otanganitsidwa kwambiri kulalikira “mbiri yabwino ya mtendere.” (Machitidwe 10:36, NW) Mu 66 C.E., gulu lankhondo la Roma linazinga Yerusalemu ndipo kenaka nkuchoka. Mmalo mokhala ndi achilikizi opanduka a mzindawo, Akristu Achihebri ‘anathawira kumapiri’ pomvera chitsogozo cha Yesu.—Luka 21:20, 21.
19 Akristu oyambirira anakhala ndimoyo ndi zinthu monga mmene zinaliri ndipo anayesayesa kuwongolera miyoyo ya anthu mwakuwathandiza kutsatira malamulo amakhalidwe abwino a Baibulo. Katswiri wa mbiri yakale John Lord, m’bukhu lake lakuti The Old Roman World, analemba motere: “Zipambano zenizeni za Chikristu zinawonekera m’kusintha anthu amene anatsatira ziphunzitso zake kukhala abwino, mmalo mosintha ziungwe, kapena boma, kapena malamulo otchuka mofala.” Kodi Akristu lerolino ayenera kuchita mosiyana?
Pamene Boma Silingathandize
20, 21. (a) Kodi ndimotani mmene ulamuliro wakudziko wina unalephereratu kuchita monga mtumiki wa Mulungu? (b) Kodi Mboni za Yehova ziyenera kuchita motani pamene zikuzunzidwa mwachivomerezo cha Boma?
20 Mu September 1972, chizunzo chankhanza chinaulika motsutsana ndi Mboni za Yehova m’dziko lina la pakati pa Afirika. Anthu zikwi zambiri analandidwa katundu wawo nachitiridwa nkhalwe zina, kuphatikizapo kumenyedwa, kuzunzidwa, ndi kuphedwa. Kodi ulamuliro waukulu unakwaniritsa thayo lake la kuchinjiriza Mbonizo? Ayi! Mmalo mwake, iwo unalimbikitsa chiwawa, kukakamiza Akristu amtendere ameneŵa kuthaŵira kumaiko apafupi kaamba ka chisungiko.
21 Kodi Mboni za Yehova sizifunikira kuukira mokwiyira ozunza oterowo? Ayi. Akristu ayenera kupirira moleza mtima kupanda ulemu koteroko, akumachita modzichepetsa kutsanzira Yesu: “Pakumva zowawa, sanaopsa, koma anapereka mlandu kwa Iye woweruza molungama.” (1 Petro 2:23) Iwo amakumbukira kuti pamene Yesu anagwidwa m’munda wa Getsemane, iye anadzudzula wophunzira amene anamchinjiriza ndi lupanga, ndipo pambuyo pake anauza Pontiyo Pilato kuti: ‘Ufumu wanga suli wa dziko lino lapansi; ufumu wanga ukadakhala wa dziko lino lapansi, anyamata anga akadalimbika nkhondo, kuti ndisaperekedwe kwa Ayuda; koma tsopano ufumu wanga suli wochokera konkuno.’—Yohane 18:36; Mateyu 26:52; Luka 22:50, 51.
22. Kodi n’chitsanzo chabwino chotani chimene Mboni zina za mu Afirika zinakhazikitsa pamene zinavutika ndi chizunzo chowopsa?
22 Pokumbukira chitsanzo cha Yesu, Mboni za ku Afirika zimenezo zidalimba mtima kutsatira uphungu wa Paulo uwu: ‘Musabwezere munthu aliyense choipa chosinthana ndi choipa. Ganiziranitu zinthu za ulemu pamaso pa anthu onse. Ngati nkutheka, monga momwe mukhoza, khalani ndi mtendere ndi anthu onse. Musabwezere choipa, okondedwa, koma patukani pamkwiyo, pakuti kwalembedwa, kubwezera kuli kwanga, ine ndidzabwezera, ati Yehova.’ (Aroma 12:17-19; yerekezerani ndi Ahebri 10:32-34.) Abale athu a ku Afirikawa akhala chitsanzo chodzetsa nthumazi chotani nanga kwa tonsefe lerolino! Ngakhale pamene olamulira akana kuchita zinthu mwaulemu, Akristu owona samasiya malamulo amakhalidwe abwino a Baibulo.
23. Kodi ndimafunso otani amene atsala ofunikira kukambitsirana?
23 Komabe, kodi maulamuliro aakulu angayembekezerenji kwa Akristu? Ndipo kodi pali malire alionse ku malamulo amene iwo angawapange moyenerera? Izi tidzakambitsirana m’nkhani yotsatira.
[Mawu a M’munsi]
a Lamulo loperekedwa ndi Mulungu mu Israyeli wakale linaphatikizapo chilango cha imfa kaamba ka maupandu aakulu.—Eksodo 31:14; Levitiko 18:29; 20:2-6; Numeri 35:30.
Kodi Mungalongosole?
◻ Kodi ndi m’njira zina ziti zimene munthu ‘angatsutsirane ndi’ maulamuliro aakulu?
◻ Kodi nkati kamene kali “kakonzedwe ka Mulungu” ponena za ulamuliro waboma?
◻ Kodi maulamuliro ali “ochititsa mantha” m’njira yotani?
◻ Kodi maboma a anthu amatumikira motani monga “mtumiki wa Mulungu”?
[Bokosi patsamba 21]
Kalata Yochokera kwa Mkulu wa Apolisi
KALATA yokhala ndi mutu wakuti “Ntchito Yochitidwira Anthu Ambiri m’Boma la Minas Gerais” inafika ku ofesi yanthambi ya Watch Tower Society m’Brazil. Iyo inachokera kwa mkulu wa apolisi wa tauni ya Conquista. Kodi padali cholakwika chinachake? Talolani kalatayo ifotokoze. Iyo ikuti:
“Bwana Wokondedwa:
“Ndine wosangalala kudzidziŵikitsa ndekha kwa inu kupyolera m’kalatayi. Ndakhala mkulu wa apolisi m’tauni ya Conquista, Minas Gerais, kwa pafupifupi zaka zitatu. Pamene ndiri pantchito, nthaŵi zonse ndimayesayesa kukhala woona mtima, koma ndinkakhala ndi mavuto kusungitsa mtendere m’ndende. Ngakhale kuti akaidiwo ankaphunzitsidwa ntchito zina, iwo sankakhazikika.
“Miyezi ingapo yapitayo, Senhor O— anabwera m’tauni yathu nadzidziŵikitsa monga mmodzi wa Mboni za Yehova. Anayamba kulalikira Baibulo kwa akaidi ena, kuwaphunzitsa kuŵerenga ndi kulemba nawasonyeza maluso enieni a ukhondo ndi kuyanjana nawauzanso za Baibulo Lopatulika. Kugwira ntchito kwa mlalikiyu kunasonyeza kudzipereka, chikondi, ndi kudzikana. Mkhalidwe wa akaidiwo unasintha mofulumira nukhala wabwino, unadabwitsa ndi kuyamikiritsa openyerera.
“Polingalira zimene zinachitika m’ndende yathu, ndikufuna kudziŵitsa mwalamulo Watch Tower Bible and Tract Society za chiyamikiro chathu kaamba ka ntchito yabwino imene inachitidwa m’chitaganya chathu ndi mlaliki woyenerayo.”
Ponena za olamulira aboma, mtumwi Paulo anati: ‘Chita chabwino, ndipo udzalandira kutama m’menemo.’ (Aroma 13:3) Ichi chinakhaladi chowona m’nkhani yapamwambayo. Ha, ndiumboni wotani nanga wa mphamvu yochititsa kusintha ya Mawu a Mulungu kumene mbiri yabwino inakwaniritsa m’miyezi yoŵerengeka kumene dongosolo lopereka chilango chokhaulitsira linalephera kukwaniritsa kwa zaka zambiri!—Salmo 19:7-9.