Chinenero Choyera Chigwirizanitsa Khamu Lalikulula Alambiri
CHINENERO choyera chopatsidwa ndi Mulungu ndicho mphamvu yogwirizanitsa Yachikristu. Umboni wa chimenecho unawonekera kwa onse amene anapezekapo pamsonkhano wa Mboni za Yehova wochitidwira Kumadzulo kwa Berlin kuyambira pa Lachiŵiri mpaka Lachisanu, July 24 mpaka 27, 1990, popeza kuti Mboni zochokera kumaiko osiyanasiyana 64 zinakapezekako.
Pamene Misonkhano Yachigawo ya “Kudzipereka Kwaumulungu” inachitidwa mu Poland mchilimwe cha 1989, nthumwi zikwi zambiri zinabwera kuchokera ku Russia ndi Chekoslovakiya, koma Kum’mawa kwa Jeremani kunachokera mazana oŵerengeka okha. Mkhalidwe wandale zadziko wasintha chotani nanga chiyambire pamenepo! Panthaŵiyi, nthumwi pafupifupi 30,000 zochokera Kum’mawa kwa Jeremani zinakomana ndi Mboni mu Olympia Stadium Kumadzulo kwa Berlin. Msonkhanowo unali wofanana ndi ina mazana ambiri yochitidwa m’mbali zina za dziko, mwachisawawa yoyambira pa Lachinayi mpaka Sande.
M’nkhani yake yotsegulira yamalonje pa Lachiŵiri, tcheyamani anafotokoza mbali imene misonkhano inachita chiyambire 1919 m’kuthandiza Mboni za Yehova kupanga kupita patsogolo m’kulankhula chinenero choyera. Msonkhanowu mofananamo ukathandiza onse opezekapo kuwongolera luso lawo lakulankhula chinenero choyera ndikukhala ndi moyo wogwirizana nacho. Iye anakumbutsa nthumwizo kuti mwakapesedwe kawo kenikeniko ndi makhalidwe, anthu a Yehova amasonyeza kupita patsogolo kumene akupanga m’kulankhula chinenero choyera.
“Chinenero Choyera cha Mitundu Yonse”
Moyenerera, nkhani yapadera ya msonkhanowo inali ndi mutu uli pamwambapa. Inazikidwa pa Zefaniya 3:9, (NW) pamene Mulungu analonjeza kuti: “Pakuti pamenepo ndidzapereka kwa amitundu kusinthira ku chinenero choyera, kuti iwo onse aitanire padzina la Yehova, kuti amtumikire mogwirizana.” Chinenero choyera chimaphatikizapo kumvetsetsa koyenera ndi chiyamikiro cha chowonadi chonena za Mulungu ndi zifuno zake. Yehova yekha ndiye angapereke zimenezi kupyolera mwa mzimu wake woyera. Kukonda chowonadi kuyenera kutisonkhezera kufuna kuphunzira chinenero choyera, chopanda chidetso chonse chamakhalidwe.
Ndiponso, kulankhula chinenero choyera sindiko kungogwiritsira ntchito mpambo wamawu wakutiwakuti. Mmalomwake, njira yathu ya moyo iyenera kugwirizana ndi zimene timazilankhula. Kwenikweni, kamvekedwe ka liwu lathu, mawonekedwe ankhope, ndi majesichala zirinso zofunika, popeza kuti zimasonyeza amene tiri mkati mwathu. Kuti tiyendere pamodzi ndi chinenero choyera chomafutukuka, tiyenera kukhala ndi programu ya kuphunzira yosalekeza ndi kupezeka pamisonkhano yonse yampingo mokhazikika.
Kuphunzira Chinenero Choyera
Monga momwe kunagogomezeredwa ndi nkhani ya pa Lachiŵiri masana, kuphunzira chinenero choyera kumatanthauza “Kupita Patsogolo Kuchokera ku Zoyamba Kunka ku Uchikulire.” Kukula nkofunika ngati titi tipitirizebe kumakula mwauzimu. Ichi chimatanthauza kutenga mwaŵi wa makonzedwe onse operekedwa kaamba ka kupita patsogolo kwauzimu ndi kugwiritsira ntchito malamulo amakhalidwe abwino a Baibulo tsiku ndi tsiku.
Kuti tikhale aluso m’chinenero choyera, tiyenera “Kuphunzitsidwa ndi Yehova,” mutu wa nkhani yosiirana ya pa Lachinayi mmawa. Mlankhuli woyamba anasonyeza mmene izi ‘Zinachitiridwa Chitsanzo ndi Yesu Kristu.’ Mfundo yakuti Yesu anaphunzitsidwa ndi Yehova inawoneka m’mawu ake ndi machitidwe. Chotero timafuna kutsanzira mmene iye anaphunzitsira. Ndipo monga momwe Yesu anagonjerera nthaŵi zonse ku chifuno cha Atate wake, nafenso tiyenera kutero.
Alankhuli atatu otsatira anasonyeza mmene Yehova amaphunzitsira kupyolera m’misonkhano yampingo ndi misonkhano yaikulu. Timapindula kuchokera ku misonkhano yonse isanu yampingo ndipo sitiyenera kunyalanyaza uliwonse wa iyo. Msonkhano uliwonse ngwofunika kaamba ka kupita patsogolo kwathu kwauzimu. Yehova amatiphunzitsanso pa maprogramu athu a msonkhano wadera, msonkhano wachigawo, ndi tsiku lamsonkhano wapadera. Kuti tipindule nayo yonseyi, tiyenera kutchera khutu mosamalitsa ndikugwiritsira ntchito zimene timaphunzira.
Nkhani yosiirana imeneyi inatsatiridwa ndi nkhani yakuti “Kudzimana Kaamba ka Phunziro Laumwini.” Kuti tilipezere nthaŵi, tiyenera kulabadira uphungu wa pa Aefeso 5:15, 16 wakuiwombola nthaŵi ku zinthu zosafunika kwambiri.
Chonulirapo chanzeru cha kuphunzira kwathu chinenero choyera ndicho kudzipereka ndi ubatizo. Chowonadi chimenechi chinagogomezeredwa m’nkhani yakuti “Ubatizo wa Awo Ophunzira Chinenero Choyera.” Chinenero chimenechi chikutsogoza ambiri ku kudzipereka ndi ubatizo. Komabe, munthu pambuyo pake ayenera kupitiriza kutsatira chitsanzo cha Yesu mwakulalikira mbiri yabwino mwachangu, akumavala umunthu watsopano, ndikulekana nalo dziko.
Chakudya Chauzimu Chotafuna
Osonkhana anakondwanso kulandira chakudya chauzimu chotafuna chozikidwa pa kukwaniritsidwa kwa zochitika zaulosi. Pa Lachinayi masana, nkhani ziŵiri zinazikidwa pamitu yotengedwa mu ulosi wa Ezekieli. Yoyamba, “Gareta la Yehova Lakumwamba Likuyenda,” inalongosola choyendera chakumwamba, chachikulu, chaulemerero ndi chochititsa mantha chikuthamanga paliŵiro lamphenzi. Chimachitira chithunzi gulu lakumwamba la Yehova, limene Mulungu akuliyendetsa mwakuti amalilamulira mwachikondi ndikuligwiritsira ntchito kuchita zifuniro zake. Ezekieli akuchitira chithunzi otsalira odzozedwa ndi mzimu, kwenikweni kuyambira 1919. Makamaka kuyambira 1935 ndipamene iwo agwirizana ndi ‘khamu lalikulu.’—Chibvumbulutso 7:9.
Nkhani yotsatira inali ndi mutu wakuti “Yenderani Limodzi ndi Gulu Lowoneka.” Palibe chikaikiro chakuti gulu lowoneka la Mulungu likuyendera pamodzi ndi gulu lakumwamba longa gareta. Monga momwe Ezekieli anachitira, atumiki a Yehova lerolino ayenera momvera kuchita ntchito yawo yaulosi mosasamala kanthu za mphwayi, kusekedwa, kapena ngakhale chitsutso. Kuyendera pamodzi kumatsogolera ku madalitso ambiri tsopano ndi moyo wosatha m’dziko latsopano lomayandikira mofulumira la Mulungu.
Pa Lachisanu mmawa, chakudya chauzimu chotafuna chinaperekedwa mwankhani zitatu zozikidwa pa Yesaya mutu 28. Yoyamba ya izi inasonyeza mwa mawu amphamvu kuti zidakwa zauzimu za Israyeli wakale ndi Yuda zinachitira chithunzi zidakwa zauzimu za Chikristu Chadziko. Ndipo monga momwe zakalezo zinakumanira ndi ziweruzo zoipitsitsa za Yehova, momwemonso zidzatero za Chikristu Chadziko.
Nkhani yotsatira, yokhala ndi mutu wakuti “Pobisalira Pawo—Bodza!,” inali ndi chenjezo lamphamvu lakuti: Mofanana ndimmene chikhulupiriro cha Yuda wakale mwa Igupto chinaliri pobisalira popanda pake, ndimmenenso chidzakhalira chigwirizano cha Chikristu Chadziko ndi maulamuliro andale am’tsiku lathu. Nkhani yachitatu pa Yesaya mutu 28, “Pitirizani Kuchenjeza za Ntchito Yachilendo ya Yehova,” inalunjikitsidwa kwa anthu a Mulungu. Chimene Yehova adzachita kwa Chikristu Chadziko moyenerera chikutchedwa chachilendo, popeza kuti chidzachidzera mochidabwitsa kotheratu. Lerolino, Yehova ali korona waulemerero kwa kagulu kakang’ono ka Akristu odzozedwa ndi kwa “nkhosa zina” zoposa mamiliyoni anayi. (Yohane 10:16) Mlankhuliyo anamaliza ndi mawu otentha maganizo akuti: “Lolani kuti changu chathu, chosankhapo chathu, ndi chikhulupiriro chithandizire ku chitamando chosatha cha Mulungu wathu, Yehova!”
Kulankhula Chinenero Choyera Kumatanthauza Kusonyeza Chikondi Chaubale
Pa Lachitatu masana, osonkhanawo anadziŵitsidwa mfundo yakuti kulankhula chinenero choyera kumatanthauzanso “Kulingalira Ana Amasiye ndi Akazi Amasiye m’Nsautso Yawo.” Anyamata opanda bambo angathandizidwe mwakuphunzitsidwa mwaumwini. Tingasonyeze kulingalira akazi amasiye mwamawu abwino olimbikitsa, mwakuwaphatikiza m’ntchito zathu Zachikristu ndi kukumana kwamayanjano, ndimwakuwapatsa thandizo la zinthu zakuthupi ngati ali oziyenerera ndi ozisowadi. Zofunsa zinasonyeza mmene zinthuzi zinkachitidwira.
Pa Lachinayi masana, nkhani inanso yogwira mtima inasonyeza “Mmene Akristu Amasamalirana.” Mboni za Yehova ziri ndi mbiri yabwino yakusamalirana, makamaka pamene pagwa masoka onga anamondwe ndi zivomezi, pamene pafunikira kulembera akuluakulu, kapena pamene pali zosoŵa zakumaloko. Koma pamene mavuto abuka chifukwa cha kupanda ungwiro kwaumunthu, tiyenera kugwiritsira ntchito malamulo amakhalidwe abwino oloŵetsedwamo mu uphungu wa Yesu pa Mateyu 5:23, 24 ndi 18:15-17. Makamaka m’malinganizidwe a bizinesi pakati pa abale ndipamene pali kufunika kwa kulemekezana ndi kuchita mosamala kotero kuti wolemba ntchito ndiponso wolembedwa ntchito sagwiritsira ntchito unansi wauzimu kudyera mnzake masuku pamutu.
Kulankhula Chinenero Choyera Kumatanthauza Kuyang’anira Mayendedwe Athu
Kufunika kwa kuyang’anira mayendedwe athu kunagogomezeredwa mobwerezabwereza. Chifukwa chake, mlankhuli woyamba pa Lachiŵiri masana anakamba pa mutu wakuti “Kumva ndi Kusunga Mawu a Mulungu.” Iye anasonyeza kuti panali zifukwa zazikulu ziŵiri zimene tinapitira kumisonkhano: kupeza chidziŵitso cholongosoka ndi kufulumizidwa kuchitapo kanthu pa chidziŵitsocho.
Nkhani yoyamba pa Lachitatu mmawa inapereka funso losanthula “Kristu ‘Anada Kusayeruzika’—Kodi Inu Mumatero?” Sikokwanira kukonda chilungamo. Tiyeneranso kuda kusayeruzika kotero kuti tikhale ndi chikumbumtima chabwino, kukhala ndi unansi wabwino ndi Yehova, kupeŵa kudzetsa chitonzo pa dzina lake, ndi kupeŵa kututa zipatso za kusayeruzika—chinyengo ndi imfa.
Yogwirizana kwambiri ndi mutu umenewo inali nkhani yotsatira, yamutu wakuti “Kanani Maloto Audziko, Londolani Zenizeni za Ufumu.” Satana, Hava, ndi angelo ochimwa onse analondola maloto amene anawawononga. Maloto audziko, okhala ndi maloto akondetsa zinthu zakuthupi kapena ochita ndi makhalidwe oipa, amatulukapo chinyengo ngakhale kuchita cholakwa chachikulu. Kuti tikanize maloto ameneŵa, tiyenera kulondola zenizeni za Ufumu kupyolera mwa phunziro, pemphero, kupezeka pamsonkhano, ndi uminisitala wapoyera.
Kuti tikhale ndi moyo woongoka Wachikristu, tiyenera kulabadiranso uphungu wopatsidwa pa Lachitatu masana m’nkhani yakuti “Akristu—Khalirani Moyo Ndalama Zimene Mupeza.” Kulephera kuchita ichi nkothekera kukhala ndi ziyambukiro zovulaza ponse paŵiri kuthupi ndi kuuzimu. Njira yanzeru ndiyo kuchepetsa zokhumba zadyera za munthuwe mwakusaloŵa m’ngongole zosafunikira ndi mwakulinganiza bajeti yabwino ndiyeno nkumamatira ku iyo. Tiyenera kukulitsa kudzipereka kwaumulungu panthaŵi zonse. Limodzi ndi kukwanira kwaumwini, iyi ndiyo njira yaphindu lalikulu.—1 Timoteo 6:6-7.
Kufunika kwa kuchenjera ndi mabwenzi athu kunagogomezeredwa m’nkhani ya pa Lachiŵiri yakuti “Kodi Mabwenzi Anu Ndiwo Mabwenzi a Yehova?” Mabwenzi athu ayenera kukhala Akristu omwe avala umunthu wonga wa Kristu ndipo ngachangu m’ntchito yolalikira. Mabwenzi akudziko sali mabwenzi a Mulungu, ndipo sitingamayanjane nawo popanda kudzivulaza tokha. Ngakhale mkati mwa mpingo, tiyenera kukhala osankha ngati mabwenzi athu ati akhale omangilira mowona.
Uphungu wapamwambawu wonena za mayendedwe unagogomezeredwa mowonekera bwino ndi drama yamakono. Iyo inali ndi mutu wakuti “Kulaka Machitachita Amachenjera a Mdyerekezi.”
Uphungu wa Chinenero Choyera ku Mabanja
Yofunikira kwambiri inali nkhani ya pa Lachitatu yakuti “Makolo—Senzani Mathayo Anu!” Makolo iwo eniwo ayenera kudziŵa chifuniro cha Mulungu ndikumachichita bwino koposa molingana ndi luso lawo. Iwo ayeneranso kuphunzitsa ana awo Mawu a Mulungu. Ndiponso, sikokwanira kungotengera ana ku misonkhano Yachikristu ndi muutumiki wakumunda. Iwo ayenera kuphunzitsidwa kukonda Yehova ndikuwona nzeru yothandiza ya kuchita zinthu zaumulungu.
Chotsatira panabwera nkhani yosiirana ya mutu wakuti “Banja m’Tsiku Lathu.” Mlankhuli woyamba anasonyeza kuti banja linachokera kwa Mulungu. Atate ayenera kukambirana bwino ponena za nkhani zauzimu. Amayi ayenera kukhala osamalira nyumba abwino, ndipo ana ayenera kusonyeza ulemu kwa Yehova mwakugwirizana ndi makolo awo.
Mlankhuli wotsatira anasonyeza kuti banja “Likuukiridwa ndi Adani.” Mavuto azandalama akuwonjezereka. Ziyeso zakuchita choipa zikuchuluka m’malo antchito, ndipo nkhani zoulutsidwa zikudzaza ndi chiwawa, chisembwere chakugonana, ndi zokopa za kukondetsa zinthu zakuthupi. Malangizo ayenera kuyamba mwamsanga, ndipo pafunikira khama lalikulu kuti tilake zisonkhezero zakudziko. Payenera kukhala kugwiritsira ntchito bwino ziwiya zateokratiki zoperekedwa ndi Watch Tower Society.
Nkhani yotsatira, yochita ndi ‘Kupulumuka Kuloŵa m’Dziko Latsopano’ kwa banja, inagogomezera mowonjezereka thayo lalikulu limene makolo ali nalo. Kuphunzitsa ana kuyenera kuchitidwa mofunitsitsa kwenikweni. Uphungu wabwino unaperekedwa ponena za maphunziro Abaibulo abanja ndi zimene ayenera kuziphunzira, zonsezo ndi cholinga chakufikira mitima ya ana. Ndikokha atatero pamene makolo ndi ana angayembekezere kupulumutsidwa kuloŵa m’dziko latsopano monga banja.
Yopereka uphungu wabwino ku mkhalidwe wabanja umene Mboni zambiri zirimo lerolino inali nkhani yakuti “Kupirira Mkati mwa Banja Logaŵanika.” Amene ali m’mikhalidwe yoteroyo analangizidwa kusataya chiyembekezo chakuti wosakhulupirirayo tsiku lina angakhale wokhulupirira. Therani nthaŵi ndi mnzanu wamuukwati wosakhulupirira ndipo tsimikizirani kuti mumafitsa zonse zofunikira kwa wamuukwati Wachikristu. Mungapeze thandizo kwa akulu kapena mwinamwake kuchokera kwa mabanja ena ogaŵanika.
Kulankhula Chinenero Choyera kwa Ena
Moyenerera kwambiri, chisamaliro chachikulu chinaperekedwa ku kugwiritsira ntchito mwaŵi wopezeka kuphunzitsa chinenero choyera kwa ena. Chifukwa chake, pa Lachitatu mmawa osonkhanawo anamva nkhani yakuti “Gwiritsirani Ntchito Nthaŵi Yanu Yofunika Mwanzeru.” Kuti tichite chimenecho tiyenera kukhazikitsa zofunika zoyambirira, mogwirizana ndi Mateyu 6:33, imene imati: ‘Koma muthange mwafuna Ufumu ndi chilungamo chake.’ Chimenecho chimaphatikizapo kupatula nthaŵi ya phunziro Labaibulo laumwini, kupezekapo pamisonkhano yonse, ndikukhala wokhazikika muuminisitala wakumunda. Ichi chimafunikiritsa kuti tiiwombole nthaŵi ku zinthu zosafunika kwambiri ngakhale kuti nzosangulutsa. Zofunsa zingapo zinasonyeza mmene ena ankachitira chimenechi.
Sitiyenera kuiŵala konse kuti ndife Mboni za Yehova. Pa Lachinayi masana, zitsanzo zingapo zinasonyeza mfundo yeniyeniyo pansi pa mutu wakuti “Pitirizani Kulankhula Chinenero Choyera pa Nyengo Iriyonse.” Zitsanzo zimenezi zinasonyeza mmene ichi chingachitidwire pochitira umboni m’khwalala, muumboni wamwamwaŵi, ndi mwakugwiritsira ntchito telefoni. Chikondi chopanda chinyengo kaamba ka Yehova Mulungu ndi mnansi wathu chidzatisonkhezera kulankhula chinenero choyera pa mpata uliwonse.
Yogwirizana kwambiri ndi mutu umenewu inali nkhani yotsatira, “Madalitso a Awo Osaleka.” Gulu la Mboni za Yehova lophunzitsa padziko lonse likuima mosemphana kotheratu ndi Chikristu Chadziko. Aliyense payekha, tiyenera kutsutsa zipsinjo zonse, zonga ngati chitsutso chalamulo, mphwaŵi yofalikira, ndi mavuto azachuma. Zitsanzo zozikidwa pa bukhu la Kukambitsirana za m’Malemba zinasonyeza mmene zipsinjo zimenezi zingalakidwire.
Yolimbikitsanso kulalikira kwachangu inali drama Yabaibulo yakuti Kuchita Chifuniro cha Mulungu ndi Changu. Inasonyeza mmene chinaliri changu cha Yehu kaamba ka dzina la Yehova ndimmene kuliri kofunika kwa ife kusonyeza kulimba mtima ndi changu chofananacho kaamba ka ntchito ya Mululngu.
Zotulutsidwa pa Msonkhano
Panali zotulutsidwa ziŵiri zapadera m’Chingelezi ndi m’Chijeremani pamsonkhanowo. Choyamba cha zofalitsidwa zimenezi chinamasulidwa m’chigwirizano ndi nkhani yamutu wakuti “Kupulumutsa Moyo Wanu ndi Mwazi—Motani?” Mlankhuliyo choyamba anakamba za maupandu ogwirizana ndi kuthiridwa mwazi. Iye anasonyeza kuti pali zinthu zina zambiri zogwiritsiridwa ntchito mmalo mwa mwazi kuloŵa m’malo mwazi wotaika. Mboni za Yehova zimakana mwazi osati chifukwa chakuti ngwosatetezereka koma chifukwa chakuti kuulandira kuli kupanda chiyero. Iwo amaukana, sichifukwa chakuti mwazi ungakhale woipitsidwa, koma chifukwa chakuti ngwopatulika kwa Mulungu. Mwazi umene ulidi wopatsa moyo ndimwazi wadipo wa Yesu Kristu. Pomaliza mlakhuliyo anasangalatsa omvetsera ake onse mwakutulutsa brosha yamasamba 32 yakuti How Can Blood Save Your Life?
Chotulutsidwa chachiŵiri chamtengo wapatali chinadza mogwirizana ndi nkhani yakuti “Funani Yehova, Anthu Inu.” Kwakukulukulu, anthu samamfunafuna Mulungu. Kukhalapo kwa zipembedzo zambiri zosiyanasiyana kumasonyeza mmene kufunafuna Mulungu kwa anthu kwakhalira kosokeretsedwa chifukwa cha kunyalanyaza kwawo Mawu a Mulungu. Monga momwe timawonera pa malipoti athu a Chikumbutso chaka ndi chaka, anthu mamiliyoni ambiri amafunikira kuthandizidwa kuti ayime ku mbali ya Yehova. Yesaya 55:6, 7 amasonyeza kuti Yehova alidi Mulungu wachikondi ndi wachifundo, wofuna ‘kukhululukira koposa.’ Monga Mboni zake, tapatsidwa chinenero choyera kotero kuti tingathandize ena kugwirizana nafe m’kutumikira Yehova mogwirizana.
Anthu a Yehova lerolino akuyang’anizana ndi chitokoso chifukwa cha kuyendayenda kwa anthu ochuluka. Monga chotulukapo, mitundu yonse ya zipembedzo ingakhale ikuneneredwa ndi anthu a m’gawo lathu. Kuti tikhoze kuthandiza Ahindu, Abuddha, Ashinto, ndi ena azipembedzo zina zambiri, Sosaite yapereka bukhu labwino lamasamba 384 lakuti Mankind’s Search for God. Ilo modalirika limapereka ziphunzitso zazikulu za zipembedzo zazikulu zakunja kwa Chikristu Chadziko. Komanso limafotokoza mbiri ya chipembedzo chonyenga mkati mwa Chikristu Chadziko. Pothandizidwa ndi bukhu limeneli, tingayambitse maphunziro Abaibulo ndi anthu onenera zipembedzo zosiyanasiyana.
Nkhani Yapoyera ndi Ndemanga Zomalizira
“Khalani Ogwirizana mwa Chinenero Choyera” ndiwo unali mutu wa nkhani yapoyera pa Lachisanu. Mlankhuli anasonyeza kuti ngakhale kuti zinenero zosiyanasiyana zokwanira zikwi zitatu tsopano zikukhala ngati zopinga ku chigwirizano, chinenero choyera chiri mphamvu yaikulu yogwirizanitsa. Icho chachinjiriza Mboni za Yehova motsutsana ndi zinyengo Zachibabulo, chawaphunzitsa kupatulika kwa moyo ndi mwazi, ndipo chawathandiza kukhalira moyo miyezo ya Baibulo imene imawapindulitsa mwauzimu ndi mwakuthupi. Onse amafunikira kukhala odera nkhaŵa za kuphunzira ndi kulankhula chinenero choyera, popeza kuti kokha anthu ochita motero ndiwo adzapulumuka Armagedo. Tiribe nthaŵi yozengereza kulabadira uphungu wa pa Zefaniya 2:1-3.
Pambuyo pa uphungu Wamalemba pa kufunika kwa ‘Kukhala Achangu m’Mapemphero,’ panadza ndemanga zomalizira zozikidwa pa mutu wakuti “Kuyenda Mogwirizana ndi Chinenero Choyera.” Chiŵerengero cha oyenda mogwirizana ndi chinenero choyera tsopano chikuwonjezekadi. Ndipo kuyamikira chinenero choyera kunasonyezedwa ndi omwe anapezeka pa misonkhano imeneyi mwa udongo wawo, ulemu, ndi kugwirizana m’malinganizidwe a zinthu. Zotulutsidwa zosindikizidwa chatsopanozo zidzathandiza Mboni za Yehova zonse kufalitsa chinenero choyera mogwira mtima koposa.
Mlankhuli womalizira wamsonkhanowo anawakumbutsa onse kufunika kwa chipiriro. Iye anasonyeza kuti monga chotulukapo cha msonkhano umenewu, onse ayenera kulimbitsidwa m’chitsimikizo chawo chamtima chakunkabe patsogolo. Iye kenaka anamaliza ndi mawu akuti: “Tiyeni tipitirizebe kuyenda mogwirizana ndi chinenero choyera choperekedwa ndi Mulungu kotero kuti tithe kulemekeza Atate wathu wachikondi wakumwamba, Yehova Mulungu, tsopano ndi kosatha!”
[Bokosi patsamba 26]
Chiŵerengero chapamwamba cha opezekapo pa msonkhano Kumadzulo kwa Berlin chinali 44,532, ndipo 1,018 anabatizidwa. Kunatengera opita kuubatizowo mphindi 19 kuti atuluke kunja kwa Olympia Stadium, ndipo mkati mwa nthaŵi yonseyi, panali kuwomba m’manja kopitirizabe. Panali pulatifomu yapadera kaamba ka nthumwi zolankhula Chingelezi. Anthu okwanira 6,000 a iwowa anamva programu yonse m’chinenero chawo. Pamsonkhanowu, panalinso anthu 4,500 ochokera ku Poland; mkati mwa maola aŵiri amasana, ziŵalo za Bungwe Lolamulira zinawapindulitsa mwakupereka nkhani zachidule.
[Zithunzi pamasamba 24, 25]
1. Olympia Stadium, Kumadzulo kwa Berlin
2. Programu yamsonkhano yosindikizidwa
3. Mabasi mazana aŵiri anabweretsa nthumwi kuchokera Kum’mawa Kwa Jeremani
4. Osonkhana a ku Poland anali achimwemwe kulandira zotulutsidwa zosindikizidwa
5. Zokometsera za maluŵa zinawalitsa malowo
6. A. D. Schroeder, mmodzi wa chiŵalo cha Bungwe Lolamulira pa programu Kumadzulo kwa Berlin