Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Nsautso pa Mtengo
ACHIFWAMBA aŵiri akutengedwa kukaphedwa limodzi ndi Yesu. Gululo linaima pamalo otchedwa Golgota, kapena Malo-a-bade, osati kutali ndi mzindawo.
Akaidiwo avulidwa zovala zawo. Kenaka akupatsidwa vinyo wosanganizidwa ndi mure. Mwachiwonekere wapangidwa ndi akazi a ku Yerusalemu, ndipo Aroma samakaniza kuti mankhwala oletsa kupweteka ameneŵa aperekedwe kwa anthu opita kukapachikidwa. Komabe, pamene Yesu walaŵa, akukana kumumwa. Chifukwa ninji? Mwachiwonekere akufuna kukhala ndi malingaliro ake onse pachiyeso chachikulu cha chikhulupiriro chake chimenechi.
Tsopano Yesu watambalalitsidwa pa mtengo manja ake ali pamwamba pa mutu wake. Asirikaliwo akukhomera misomali yaikulu m’manja mwake ndi m’mapazi. Iye akudzungunyuka ndi kupwetekako pamene misomaliyo ikuboola mnofu wake ndi minyewa. Pamene mtengowo waimikidwa, kupwetekako kukuwawitsa, popeza kuti kulemera kwa thupi kukung’amba zilonda zamisomalizo. Komabe, mmalo mowopseza, Yesu akuwapempherera asirikali Achiromawo nati: ‘Atate, muwakhululukire iwo, pakuti sadziŵa chimene achita.’
Pilato waika chizindikiro pamtengopo chomwe chiri ndi malemba akuti: ‘Yesu Mnazarayo, Mfumu ya Ayuda.’ Mwachiwonekere, iye walemba zimenezi osati kokha chifukwa chakuti amamulemekeza Yesu koma chifukwa chakuti waipidwa ndi ansembe Achiyuda omwe apempha chiweruzo cha imfa ya Yesu kuchokera kwa iye. Kuti chizindikirocho chiŵerengedwe ndi onse, Pilato wachilembetsa m’zinenero zitatu—m’Chihebri, m’Chilatini chalamulo, ndi m’Chigiriki chofala.
Ansembe aakulu, kuphatikizapo Kayafa ndi Anasi, akwiyitsidwa. Chilengezo chotsimikiza chimenechi chikuwononga ola lawo lachilakiko. Chotero iwo akutsutsa nati: “Musalembe, Mfumu ya Ayuda; koma kuti Iyeyu anati, Ndiri Mfumu ya Ayuda.” Akumasonyeza kuipidwa ndi kuti watumikira monga wopititsa patsogolo zolinga za ansembewo, Pilato akuyankha motsutsiratu kuti: ‘Chimene ndalemba, ndalemba.’
Ansembewo, limodzi ndi khamu lalikululo, akusonkhana tsopano pamalo opherawo, ndipo ansembewo akuyesayesa kukana umboni wa chizindikirocho. Iwo akubwereza umboni wonama womwe unaperekedwa koyambirirako pa kuzenga milandu kochitidwira ku Bwalo la Akulu. Chotero, nzosadabwitsa kuti odutsa m’njira akuyamba kulankhula monyoza, akumagwedeza mitu yawo mwamwano namati: ‘Nanga iwe, wopasula kachisi, ndi kummanganso masiku atatu, tadzipulumutsa wekha; ngati uli Mwana wa Mulungu, tsika pamtengopo.’
“Anapulumutsa ena, sangathe kudzipulumutsa yekha,” ansembe aakulu ndi mabwenzi awo achipembedzo akuloŵereramo tero. ‘Ndiye Mfumu ya Israyeli; atsike tsopano pamtengo wozunzirapowo, ndipo tidzamkhulupirira iye. Amakhulupirira Mulungu; Iye ampulumutse tsopano, ngati amfuna; pakuti anati, Ine ndine Mwana wa Mulungu.’
Potengeka ndi mzimuwu, asirikaliwonso akumseka Yesu. Iwo mwachipongwe akumpatsa vinyo wosasa, mwachiwonekere akumamuika pamwamba pa milomo yake youma. “Ngati Iwe ndiwe Mfumu ya Ayuda,” iwo anamtonza motero, “udzipulumutse wekha.” Ngakhale achifwambawo—amene anapachikidwa wina kulamanja kwa Yesu, ndi wina kulamanzere—akumseka. Tangolingalirani za chimenecho! Munthu wamkulu koposa yemwe anakhalapo, inde, uyo amene anathandizana ndi Yehova Mulungu m’kulenga zinthu zonse, akuvutika kotheratu ndi zitonzo zimenezi!
Asirikaliwo akutenga zovala za Yesu nazigawa mbali zinayi. Iwo akupanga maere kuti awone kuti zidzakhala za yani. Komabe, malaya amkati analibe msoko, ndiponso anali apamwamba. Chotero asirikaliwo ananena nati: ‘Tisang’ambe awa, koma tichite maere, awa akhale a yani.’ Chotero, mosadziŵa, iwo anakwaniritsa lemba limene linati: ‘Anagawana zovala zanga mwa iwo okha, ndipo pa malaya anga anachitira maere.’
M’kupita kwa nthaŵi, mmodzi wa achifwambawa wafikira pakuzindikira kuti Yesu ayenera kukhaladi mfumu. Chotero, akumadzudzula bwenzi lake, iye akuti: ‘Kodi suopa Mulungu, powona uli m’kulangika komweku? Ndipo ifetu kuyenera; pakuti tirikulandira zoyenera zimene tinazichita: koma munthu uyu sanachita kanthu kolakwa.’ Kenaka akulankhula ndi Yesu, akumapembedzera kuti: ‘Ndikumbukireni mmene muloŵa ufumu wanu.’
“Indetu ndinena ndi iwe lerolino,” (NW) Yesu akuyankha motero, “Udzakhala ndi ine m’Paradaiso.” (NW) Lonjezo limeneli lidzakwaniritsidwa pamene Yesu adzalamulira monga Mfumu kumwamba ndi kuukitsira wochita zoipa wolapayo ku moyo padziko lapansi la Paradaiso limene opulumuka Armagedo ndi mabwenzi awo adzakhala ndi mwaŵi wakulilima. Mateyu 27:33-44; Marko 15:22-32; Luka 23:27, 32-43; Yohane 19:17-24.
◆ Kodi nchifukwa ninji Yesu akukana kumwa vinyo wosanganizidwa ndi mure?
◆ Mwachiwonekere, kodi nchifukwa ninji chizindikiro chaikidwa pamtengo wa Yesu, ndipo ndi mkangano wowonjezereka wotani umene chikuyambitsa pakati pa Pilato ndi ansembe aakuluwo?
◆ Kodi ndimwano wowonjezereka wotani umene Yesu akulandira pamene ali pamtengopo, ndipo nchiyani chomwe mwachiwonekere chikuuyambitsa?
◆ Kodi ulosi wakwaniritsidwa motani m’zimene zikuchitidwa ku zovala za Yesu?
◆ Kodi ndikusintha kotani kumene mmodzi wa achifwambawo wakupanga, ndipo kodi Yesu adzakwaniritsa motani pempho lake?