Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 2/1 tsamba 4-7
  • Kodi Nkuchitengeranji Mosamalitsa Chipembedzo?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Nkuchitengeranji Mosamalitsa Chipembedzo?
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chipembedzo Chofunikira Kuchitenga Mosamalitsa
  • “Zipatso” za Chipembedzo Chowona
  • Mapindu Amuyaya Ochokera m’Kulondola Chipembedzo Chowona
  • Kodi Mwapeza Chipembedzo Cholondola?
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Kodi Chipembedzo Chirichonse Chiri Chabwinodi?
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Kodi Ndingachidziwe Bwanji Chipembedzo Cholondola?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Kulondola Chipembedzo Choyera Kaamba ka Chipulumutso
    Nsanja ya Olonda—1991
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 2/1 tsamba 4-7

Kodi Nkuchitengeranji Mosamalitsa Chipembedzo?

“MUNTHU sangakhale ndi moyo ndi mkate wokha.” (Mateyu 4:4, The New English Bible) Mawu otchulidwa mobwerezabwerezaŵa amakhudza chosoŵa cha munthu chimene ambiri samachilingalira lerolino. Iwo amasonyeza kuti tiri ndi mbali yauzimu imene imafunikira kukhutiritsidwa. Chimenecho ndicho chifukwa chake uyo amene analankhula mawu amenewo, Yesu Kristu, ananenanso kuti: “Ngodalitsidwa awo amene amadziŵa kufunikira kwawo Mulungu.”​—Mateyu 5:3, NEB.

Chipembedzo chokha ndicho chingakwaniritse “kufunikira [kwathu] Mulungu.” Chipembedzo chokha ndicho chingayankhe mafunso ofunika ponena za chiyambi, chifuno, ndi tanthauzo la moyo. Ndipo nchipembedzo chokha chimene chingapereke tanthauzo lenileni ndi cholinga m’moyo wathu. Koma sichipembedzo chirichonse chimene chingachite zonsezi. Yesu anauza mkazi Wachisamariya kuti: ‘Olambira owona adzalambira Atate mumzimu ndi m’chowonadi.’ (Yohane 4:23) Kulambira ‘ndi chowonadi’ kumatanthauza zoposa kutsatira miyambo ndi madzoma olemekezedwa kwa nthaŵi yaitali. Izi kaŵirikaŵiri zimapereka kwa achilikizi ake ubwino wapakanthaŵi, ndikuwasiyabe ndi njala yauzimu.

Mwachitsanzo, Edwin O. Reischauer, yemwe kale anali kazembe wa U.S. ku Japan, ananena kuti: “Chishinto ndi Chibuda ziri kwenikweni miyambo ndi misonkhano osati zikhulupiriro zatanthauzo kwa anthu ambiri.” Kunena zowona, anthu ambiri a ku Japan ngokhutira kukhala ndi njira imeneyi. Koma kuyambika kwa “zipembedzo zatsopano” m’Japan kumasonyeza kusakhutira ndi chipembedzo chamwambo komakulakula.

“Zipembedzo zatsopanozo” zimasumika maganizo pa atsogoleri otchuka​—osati Mulungu. Ambiri a atsogoleri achipembedzo ameneŵa amati ngouziridwa mwaumulungu. Koma ziphunzitso zawo sizosiyana kwenikweni ndi msanganizo wa Chibuda, Chishinto, ndi zikhulupiriro zina​—kuphatikizapo mbali yaikulu ya nthanthi ya woziyambitsayo. Chisangalatso chawo kaŵirikaŵiri chimakhala m’malonjezo a moyo wabwinopo ndikudzinenera kwa mphamvu zachilendo kapena kuchiritsa. Koma kodi zipembedzo zoterozo zimapereka umboni wakuti zikuphunzitsa atsatiri ake kulambira ‘mumzimu ndi m’chowonadi’? Kutalitali. Choyamba, miyambo yachipembedzo imakhalapo kwa kanthaŵi kochepa kenaka nkuzimiririka. Mkhalidwe wawo wosakhalitsa umapereka chifukwa chochepa chakuzitengera mosamalitsa.

Chipembedzo Chofunikira Kuchitenga Mosamalitsa

Komabe, pali chipembedzo chimene chakhalapo kwa nthaŵi yaitali kuposa mtundu wina uliwonse wa kulambira. Icho nchipembedzo chophunzitsidwa m’Baibulo Lopatulika. Baibulo linayamba kulembedwa zaka mazana 35 apitawo, ndipo ‘nkhani’ zina zosungidwa m’mitu yake yakale ziri ndi madeti a zaka zoposa chikwi chimodzi kupyola pamene zinalembedwa.a Ilo liri ndi mbiri yakale kwambiri yopezeka ya chiyambi cha chipembedzo. Chimenecho chokha nchifukwa cholingalirira chipembedzo cha Baibulo mosamalitsa.

The Encyclopedia Americana ikunena motere ponena za Baibulo: “Kuunika kwake ‘kwapita m’dziko lonse.’ Ilo tsopano likulingaliridwa kukhala chuma cha miyambo ndi chipembedzo chimene ziphunzitso zake zosatha zimalonjeza kukhala zaphindu kwenikweni pamene chiyembekezo cha kutsungula kwa dziko chikuwonjezereka.” Koma ngati bukhu liridi chitsogozo chokhulupiririka chopezera chipembedzo chowona, kodi simungaliyembekezere kukhala lofalitsidwa koposa, kukhalapo kwa onse ofunafuna chowonadi?

Mmenemo ndimo mmene ziriri ndi Baibulo. Ilo latembenuzidwa m’zinenero 1,928, lathunthu kapena mbali zake, ndipo ndibukhu lofalitsidwa mofala m’mbiri. Kuwonjezerapo, ilo latsimikizira kukhala lolama m’mbiri yakale ndi sayansi. Sayansi ya zinthu zofukulidwa m’mabwinja ndi mbiri yakale zimachitira umboni kukwaniritsidwa kolongosoka kwa maulosi a Baibulo. Ilo nlopanda mitundu yonse ya kuchita maula ndi chinsinsi ndi kuwombeza. Zonsezi nzogwirizana ndi chonena cha Baibulo chakuti nlouziridwa mwaumulungu.b​—2 Timoteo 3:16.

“Zipatso” za Chipembedzo Chowona

Koma kodi sizowona kuti zipembedzo zambiri zimadzinenera kuti zimatsatira Baibulo? Ndipo kodi kutetana, chidani, ndi chinyengo sizimawonekera pakati pa anthu amene amati ndi Akristu? Inde, komatu ichi sindicho chifukwa chakusalingalirira Baibulo. Yesu Kristu iyemwini anasonyeza kuti anthu ambiri odzinenera kukhala Achikristu sadzavomerezedwa ndi Mulungu. (Onani Mateyu 7:13, 14, 21-23.) Pamenepo, kodi ndimotani mmene munthu angakhozere kuzindikira awo amene akuchita chipembedzo chowona chophunzitsidwa m’Baibulo? Yesu anayankha motere: ‘Mudzawazindikira ndi zipatso zawo. Kodi atchera mpesa paminga, kapena nkhuyu pamtula? Chomwecho mtengo wabwino uliwonse upatsa zipatso zokoma; koma mtengo wamphuchi upatsa zipatso zoipa. Inde chomwecho pa zipatso zawo mudzawazindikira iwo.’​—Mateyu 7:16, 17, 20.

Inde, chipembedzo chowona chiyenera kukhala mphamvu yosonkhezera kuchita zabwino, kutulutsa ziyambukiro zopindulitsa pakati pa alambiri. Mwachitsanzo, talingalirani za Akinori, mwamuna wa ku Japan, amene mwa mawu ake, “anakhala munthu weniweni wa mzimu wopikisana.” Iye anazifikira mwachipambano zonulirapo zake zakumaliza maphunziro pa yunivesite yapamwamba ndikupeza ntchito pakampani yotchuka. Iye sanachiwone chifukwa chophatikiziramo chipembedzo m’moyo wake. Iye analingalira kuti, ‘Chipembedzo ncha anthu ofooka omwe amafunikira ndodo yoyendera.’

Zonse zinkayenda bwino kufikira pamene tsiku lina, chifukwa cha chitsenderezo ndi kutopa, anadwala matenda owopsa. Khosi lake linapotoka, ndipo chibwano chake “chinazizira” kumbali ya phewa lake lakumanzere. “Mabwenzi” ambiri a pakampani pa Akinori anatsimikizira kukhala osapereka chitonthozo chenicheni m’nthaŵi ya nsautso yake. (Yerekezerani ndi Miyambo 17:17.) Choncho anakhala chidakwa nalingalira zodzipha.

Komabe, m’kupita kwa nthaŵi, mkazi wa Akinori anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Tsiku lina pokambitsirana, anamuuza lemba la Agalatiya 6:7, limene limati: ‘Chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta.’ Atakondweretsedwa ndi mawu ameneŵa, Akinori anagwirizana naye m’phunzirolo, ndipo zimene anaphunzira zinasintha lingaliro lake la tanthauzo la moyo. Pamene mkhalidwe wa Akinori unawala, matenda ake oyambitsidwa ndi chitsenderezo anayamba kutha! Mongadi momwe mwambi wa Baibulo umanenera kuti: “Mtima wabwino ndi moyo wa thupi.” (Miyambo 14:30) Inde, chipembedzo chowona chimabala zipatso zabwino!

Toshiro ndi mwamuna wina wa ku Japan amene anafikira pa kuzindikira mmene chipembedzo chowona chingakhalire mphamvu yakuchita zabwino. Ngakhale kuti anakhulupirira kuti chipembedzo chinali ndi phindu, iye sanachite kalikonse ponena za izo. Chikondwerero chake chinasumikidwa pa kukhala ndi nyumba yakeyake. Komabe, kufikira chonulirapo chimenecho sikunabweretse chikhutiro chimene ankachiyembekezera. Kuwonjezera apa, pamene iye ankaunguza pamalo ake antchito, anawona kuti machitachita a kusawona mtima anali ofala ndikuti zotulukapo zake zinali maunansi aumwini oipa. Toshiro anaipidwa ndi zomwe anaziona.

Tsiku lina mkazi wake anaitana mkulu wa mumpingo wa Mboni za Yehova wakumaloko kudzamchezera. Toshiro anazindikira nthaŵi yomweyo kuti mkuluyo anali wosiyana ndi mabwenzi ake. Chifukwa ninji? Mkuluyo anagwiritsira ntchito mowona mtima malamulo amakhalidwe abwino Abaibulo m’moyo wake. Atasangalatsidwa ndi zimenezi, Toshiro anavomereza pempho la kuphunzira Baibulo ndikuyamba kupanga chipembedzo cha Baibulo kukhala njira yake ya moyo.

Tikukuitanani nanunso kukhala wozoloŵerana ndi Mboni za Yehova. “Zipatso” zawo zimapereka umboni wakuti iwo akulambira ‘mumzimu ndi m’chowonadi.’ Iwo amagwira ntchito zolimba kupangitsa ziphunzitso za Baibulo kugwira ntchito m’miyoyo yawo. Ndipo pamene kuli kwakuti monga munthu payekha iwo sali angwiro, monga gulu iwo amasonyeza mmene chipembedzo chowona chiliri mphamvu yauzimu yopangitsa zabwino.

Zikwi zambiri za Mboni panthaŵi ina zinali zopanda chimwemwe ndi njira yawo ya moyo. Koma mwakugwiritsira ntchito malamulo amakhalidwe abwino a Baibulo, ambiri a iwo akhala okhoza kupanga masinthidwe ochititsa chidwi. Mwakukulitsa zimene Baibulo limazitcha ‘zipatso za mzimu,’ zotchedwa, mikhalidwe ya chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, ndi chiletso, iwo apeza mfungulo yopezera chimwemwe chaumwini.​—Agalatiya 5:22, 23.

Mapindu Amuyaya Ochokera m’Kulondola Chipembedzo Chowona

Komabe, chipembedzo chowona chiyenera kuchita zambiri kuposa kungosintha maumunthu kapena kuchepetsako mavuto aumwini. Mavuto apadziko lonse monga ngati kuipitsa, chiwopsezo cha nkhondo ya nyukliya, ndi kuwononga malo otizinga akuwopseza kuwononga planeti lathu lokongola. Mavuto azachuma amadodometsa chimwemwe ndi thanzi la anthu mamiliyoni ambiri. Palibe chipembedzo chomwe chingatengedwe mosamalitsa kusiyapo kokha ngati chimapereka chiyembekezo chothetsera mavuto apadziko lonse ameneŵa.

Chipembedzo cha Baibulo chimapereka chiyembekezo choterocho. Mulungu akulonjeza kubweretsa dziko latsopano lolungama pansi pa boma lakumwamba, kapena “ufumu.” (Mateyu 6:9, 10; 2 Petro 3:13; Chibvumbulutso 21:3, 4) Ufumu umenewu ndiwo mankhwala a matenda onse a anthu. Ndipo ponena za kukhalitsa kwa mapindu apadziko lonse lapansi amenewo, tikutsimikiziridwa motere m’Baibulo: ‘Ndipo dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake; koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthaŵi yonse.’ Inde, moyo wosatha wachimwemwe ndiwo chiyembekezo cha Mkristu wowona aliyense! (1 Yohane 2:17) Koma kokha awo amene amatenga chipembedzo chowona mosamalitsa ndiwo adzapindula ndi Ufumu ukudzawo. Chotero tikukufulumizani kuyamba kuphunzira Baibulo mosamalitsa.c (Yohane 17:3) Pamene mukuyamba kulola kuwala kwa Mawu a Mulungu kuwunikira moyo wanu, mudzakhala ndi chimwemwe chachikulu pamene ‘kufunikira [kwanu] Mulungu’ kukwaniritsidwa sitepe limodzi ndi limodzi. Ndithudi, mudzalandira madalitso osatha chifukwa chakuti munatenga chipembedzo​—chipembedzo chowona​—mosamalitsa.

[Mawu a M’munsi]

a Mwachitsanzo, onani Genesis 2:4; 5:1; 6:9.

b Kaamba ka chidziŵitso chowonjezereka, onani bukhu lakuti The Bible​—God’s Word or Man’s?, lopezeka kwa afalitsi a magazini ano.

c Mboni za Yehova zidzakhala zosangalala kukuthandizani m’nkhaniyi. Phunziro Labaibulo lapanyumba laulere lingalinganizidwe kaya mwakulembera ofalitsa magaziniŵa kapena kufikira mpingo wa Mboni za Yehova wam’mudzi mwanu.

[Chithunzi patsamba 5]

Kukhalapo kwa Baibulo m’zinenero zoposa 1,900 nkogwirizana ndi kunena kwake kwakuti nlouziridwa mwaumulungu

[Chithunzi patsamba 7]

Chipembedzo cha Baibulo chimapereka chiyembekezo cha mikhalidwe yamtendere pansi pa boma lakumwamba

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena