Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 12/1 tsamba 6-8
  • Kodi Chipembedzo Chirichonse Chiri Chabwinodi?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Chipembedzo Chirichonse Chiri Chabwinodi?
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kusiyana Kofunika Kwambiri
  • Kufunika kwa Kusankha
  • Mmene Mungasankhire Chipembedzo Cholondola
  • Chowonadi ndi Zipatso
  • Chipembedzo Chowona Chikulondoledwa Lerolino
  • Zipembedzo Zabodza Zimaphunzitsa Zinthu Zonama Zokhudza Mulungu
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Mapeto A Chipembedzo Chonyenga Ayandikira!
    Mapeto A Chipembedzo Chonyenga Ayandikira!
  • Chipembedzo Chanu Chiridi Nkanthu
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Kumasuka ku Chipembedzo Chonyenga
    Nsanja ya Olonda—1991
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 12/1 tsamba 6-8

Kodi Chipembedzo Chirichonse Chiri Chabwinodi?

“Mtsogolo mwa nthaŵi yathu ndimwangozi. Tikufunikira chipembedzo, koma sitipeza kwina kulikonse Mulungu wochiyenerera.”​—Lucian Blaga, wolemba ndakatulo ndi wanthanthi wa ku Romania

“Chipembedzo ndi atsogoleri ake akhala, ndipo mwina mwake adzakhalabe kwanthaŵi yaitali, pakati pa adani aakulu koposa a kupita patsogolo ndi ufulu.”​—Khristo Botev, wolemba ndakatulo wa ku Bulgaria

MAWU ogwidwa panopawa amasonyeza chothetsa nzeru chokhala ndi anthu ambiri owona mtima. Pansi pamtima amakumva kufunika kwa chipembedzo, koma Mulungu wachinsinsi amene atsogoleri achipembedzo amaphunzitsa sali Mulungu amene angamvetsetse ndi kumkonda. Ndiponso, iwo amazindikira kuti atsogoleri achipembedzo ndi zipembedzo zawo zachita zambiri kutsekereza kupita patsogolo ndi ufulu wa anthu. Inde, pamene kufunika kwa chipembedzo kukuzindikiridwa mowonjezereka, anthu owona mtima sangalandire chipembedzo chirichonse.

Kusiyana Kofunika Kwambiri

Chipembedzo chimachita mbali yofunika m’kakhalidwe ndi mbiri ya anthu. The New Encyclopædia Britannica imalankhula za chipembedzo “kukhala chinthu chenicheni m’zokumana nazo, mwambo, ndi mbiri ya anthu” ndipo ikuwonjezera kuti: “Maumboni a makhalidwe achipembedzo ndi kukhulupirika amawonekera m’mbali iriyonse ya moyo wa munthu.” Koma mbiri imasonyeza kuti palibe chirichonse cha zipembedzo zazikulu zapadziko chimene chakhala dalitso kwa anthu.

Nduna yaboma ya ku India Jawaharlal Nehru panthaŵi ina inathirira ndemanga yakuti: “Zochita za chomwe chimatchedwa chipembedzo, kapena pamlingo uliwonse chipembedzo cholinganizidwa, mu India ndi kwina kulikonse, zatidzaza ndi mantha.” Polingalira za nkhondo zomwe zamenyedwa ndi maupandu amene achitidwa m’dzina la chipembedzo, kodi ndithudi mungatsutsane naye?

M’zaka za zana la 18, wanthanthi wa ku Falansa Voltaire anasonyeza kusiyana kosangalatsa. Iye analemba kuti: “Mumanena kuti chipembedzo chapangitsa zinthu zoipa zosaŵerengeka. Koma muyenera kunena kuti malaulo, malaulo omwe akulamulira dziko lathu lachisoni. Malaulo ndiwo mdani woipitsitsa wa kulambira koyera kumene timafunikira kupereka kwa Wokhalako Wamkulukulu.” Voltaire analimbana ndi nkhanza yachipembedzo ya m’tsiku lake, koma anasungabe chikhulupiriro chake mwa Mulungu monga Mlengi wa chilengedwe chonse. Iye anawona kusiyana pakati pa chipembedzo chowona ndi chonyenga.

Kufunika kwa Kusankha

Sionse amene amavomerezana ndi Voltaire. Ena amanena kuti amawona ubwino m’zipembedzo zonse; chotero, samawona kufunika kwenikweni kwa kufunafuna chipembedzo chowona. Anthu oterowo ayenera kulabadira chenjezo loperekedwa ndi mneneri Yesaya, amene analemba kuti: “Tsoka kwa iwo amene ayesa zoipa zabwino, ndi zabwino zoipa; amene aika mdima m’malo mwa kuyera, ndi kuyera m’malo mwa mdima; amene aika zowawa m’malo mwa zotsekemera, ndi zotsekemera m’malo mwa zowawa!” (Yesaya 5:20) Chipembedzo chonyenga chabala zinthu zomwe ziri zoipa kwa anthu. Chapereka mdima wauzimu ndipo chaika kuwawa mkamwa mwa anthu owona mtima.

Chotero, chosankha sichiri pakati pakukhala wosakhulupirira kukhalako kwa Mulungu ndi kukhulupirira chipembedzo chirichonse. Siziri zokhweka motero. Pamene munthu wazindikira kufunika kwa Mulungu, munthuyo ayenera kufunafuna chipembedzo chowona. Monga momwe wofufuza Émile Poulat analembera bwino lomwe mu Le Grand Atlas des Religions (Atalasi Yaikulu Yazipembedzo) kuti: “Zinthu zimene [zipembedzo] zimaphunzitsa ndi kufuna nzosiyanasiyana kwambiri kwakuti nkosatheka kukhulupirira zonsezo.” Mogwirizana ndi zimenezi, Encyclopædia Universalis Yachifrench (Bukhu Lanazonse) imanena kuti: “Ngati chipembedzo chikhalapobe m’zaka za zana la 21, . . . munthu adzafunikira kusankha kaya ngati zinthu zopatulika zimene amapatsidwa ziri zowona kapena zabodza.”

Mmene Mungasankhire Chipembedzo Cholondola

Kodi nchiyani chimene chidzatitsogoza posankha chipembedzo cholondola? Encyclopædia Universalis njolondola pamene ikugogomezera kufunika kwa chowonadi. Chipembedzo chimene chimaphunzitsa mabodza sichingakhale chowona. Mneneri wamkulu koposa yemwe anakhalapo padziko lapansi ananena kuti: ‘Mulungu ndiye mzimu; ndipo omlambira iye ayenera kumlambira mumzimu ndi m’chowonadi.’​—Yohane 4:24.

Mneneri ameneyo anali Yesu Kristu, ndipo iye analengezanso kuti: “Chenjerani ndi aphunzitsi onyenga achipembedzo, amene amadza kwa inu atavala ngati nkhosa koma kwenikwenidi ali mimbulu yaumbombo. Mungawazindikire ndi zipatso zawo. . . . Mtengo uliwonse wabwino ubala zipatso zabwino, koma mtengo wamphuchi umabala zipatso zoipa.” (Mateyu 7:15-17, Phillips) Powona zipatso zoipa za zipembedzo “zazikulu” za m’dziko, ndipo ngakhale za mipatuko ndi timagulu timene tabuka, anthu ambiri owona mtima afikira pakuwona zonsezo kukhala ‘mitengo yamphuchi,’ mwachidule zosakhala bwino. Koma kodi ndimotani mmene angapezere chipembedzo chowona?

Mwachidziŵikire kukakhala kosatheka kuphunzira zikwizikwi za zipembedzo zonse za mkati ndi kunja kwa Chikristu Chadziko musanapange chosankha. Komabe, ngati tigwiritsira ntchito chowonadi ndi chipatso monga zoyesera​—monga momwe Yesu ananenera​—kuli kotheka kuzindikira chipembedzo chowona.

Chowonadi ndi Zipatso

Yesu anatchula chowonadi. Ponena za chimenechi, kodi ndigulu liti la okhulupirira amene amakana mabodza achipembedzo otengedwa ku miyambo yakale ndi nthanthi Zachigiriki zimene zimapezeka m’zipembedzo zambiri? Bodza limodzi loterolo ndilo chiphunzitso chakuti moyo wa munthu uli wosakhoza kufa.a Chiphunzitso chimenechi chabala chiphunzitso chonyoza Mulungu cha moto wahelo.

Yesu anatchulanso zipatso. Ponena za zimenezi, kodi mumadziŵa chipembedzo chimene chimatulutsa ubwenzi weniweni wamitundu yonse kumene zopinga za fuko, chinenero, ndi utundu zalakidwa ndi chikondi ndi kumvana? Kodi mumalidziŵa gulu lachipembedzo lapadziko lonse limene mamembala ake amalola kuzunzidwa m’malo molola andale zadziko kapena atsogoleri achipembedzo kuwasonkhezera kuda abale ndi alongo awo ndi kuwapha m’dzina la utundu kapena chipembedzo? Chipembedzo chimene chinakana mabodza achipembedzo oterowo ndipo chinabala zipatso zoterozo chikapereka umboni wamphamvu wakukhala chowona, kodi sichoncho?

Chipembedzo Chowona Chikulondoledwa Lerolino

Kodi chipembedzo choterocho chiripo? Inde, chiripo. Koma muyenera kuvomereza kuti sichiri chimodzi cha zipembedzo zazikulu za dziko. Kodi izi ziyenera kutidabwitsa? Ayi. Muulaliki wake wotchuka wa pa Phiri, Yesu ananena kuti: ‘Loŵani pa chipata chopapatiza; chifukwa chipata chiri chachikulu, ndi njira yakumuka nayo kukuonongeka iri yotakata; ndipo ali ambiri amene aloŵa pa icho. Pakuti chipata chiri chopapatiza, ndi ichepetsa njirayo yakumuka nayo kumoyo, ndipo akuchipeza chimenecho ali oŵerengeka.’​—Mateyu 7:13, 14.

Chotero kodi chipembedzo chowona chingapezeke kuti? Modzichepetsa ndi mowona mtima, tiyenera kunena kuti Mboni za Yehova zimapanga chitaganya chamitundu yonse choyenda ‘m’njira yochepetsa ndi yopapatiza’ imeneyi. Zowonadi, zipembedzo zazikulu monyoza zimatcha Mboni za Yehova kukhala kagulu kampatuko. Koma zimenezo ndizo zenizenizo zimene atsogoleri achipembedzo ampatuko a m’zaka za zana loyamba C.E. anatcha Akristu oyambirira.​—Machitidwe 24:1-14.

Kodi nchifukwa ninji Mboni za Yehova ziri ndichidaliro kuti ziri ndi chipembedzo chowona? Eya, izo zimapanga ubale wamitundu yonse umene umafika m’maiko oposa 200 ndi umene ukulaka kugaŵanikana kwa utundu, fuko, chinenero, ndi kaimidwe kamayanjano. Ndipo zimakana kukhulupirira ziphunzitso​—kaya zikhale zakale motani​—zimene zimasemphana ndi zomwe Baibulo limanena. Koma kodi izo zinafika motani pa mkhalidwe wokhumbirika umenewo? Ndipo kodi kulondola chipembedzo chowona kumaphatikizapo chiyani? Tidzakambitsirana funso limeneli ndi ena onena za chipembedzo m’nkhani ziŵiri zotsatirazi.

[Mawu a M’munsi]

a Kuti mupeze umboni wa chiyambi cha nthanthi cha chikhulupiriro chimenechi, onani bukhu la Mankind’s Search for God, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc., masamba 52-7.

[Chithunzi patsamba 7]

Nkhondo za Mtanda zinali mbali ya zipatso zoipa za chipembedzo chonyenga

[Mawu a Chithunzi]

Bibliothèque Nationale, Paris

[Chithunzi patsamba 8]

Chipembedzo chowona chimabala zipatso zabwino

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena