Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 2/1 tsamba 29
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Nkhani Yofanana
  • Labadirani Mawu Aulosi a Mulungu
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Tigwiritse Chikhulupiriro Chathu Chamtengo Wapatali!
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Chiyembekezo Chokhala ndi Chitsimikiziritso Chotsimikizirika
    Kusankha Njira Yabwino Koposa ya Moyo
  • Masomphenya a Ufumu wa Mulungu Asanduka Zenizeni
    Nsanja ya Olonda—2005
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 2/1 tsamba 29

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

◼ Kodi nchifukwa ninji kumasulira kwa 2 Petro 1:19 mu New World Translation of the Holy Scriptures kuli kosiyana ndi Mabaibulo ena?

Pogogomezera phindu la mawu ouziridwa a Mulungu, mtumwi Petro analemba kuti: “Monga chotulukapo tinatsimikiziridwa za mawu aulosi; ndipo mukuchita bwino powalabadira mofanana ndi nyali yowala mmalo a mdima, kufikira mbanda kucha nikauka nthanda, m’mitima mwanu.”​—2 Petro 1:19, NW.

Onani kuti mawu akuti “kufikira mbanda kucha nikauka nthanda” alekanitsidwa ndi makoma (zizindikiro zosonyeza kupuma pang’ono). Matembenuzidwe ambiri a Baibulo sapanga zimenezi.

Mwachitsanzo, Dr. James Moffatt amamasulira mbali yomalizira ya vesilo motere: “. . . iwala monga nyali m’malo amdima; kufikira Mbanda kucha nikauka nthanda m’mitima mwanu.” Kumasulira konga kumeneku kumatsogolera ku lingaliro lakuti kuuka kwa nthanda kumachitika m’mitima ya okhulupirira, monga ngati pamene akhala ndi kuunikiridwa kwauzimu.

Komabe, ngakhale kalelo m’tsiku la Mose, panali chisonyezero chakuti ‘nyenyezi yotuluka mwa Yakobo’ ikauka. (Numeri 24:17; yerekezerani ndi Salmo 89:34-37.) Yesu anadzizindikiritsa bwino lomwe kukhala “mbadwa ya Davide, nyenyezi yonyezimira ya nthanda.”​—Chibvumbulutso 22:16.

Chizindikiritso chimenechi cha “nthanda,” kapena “nyenyezi ya nthanda,” chikuyenerera mawu apambuyo ndi apatsogolo a lembalo a zimene mtumwi Petro ankafotokoza. Iye anali atangosonya ku masomphenya a kusandulika amene iye anawaona zaka 30 kuchiyambiyambi. (Mateyu 16:28–17:9) Masomphenya owala amenewo anasonya ku nthaŵi imene Yesu ‘akadza mu ufumu wake,’ kapena kulemekezedwa mu ulamuliro wa Ufumu. Chimene Petro anachiona chinagogomezera phindu la mawu a Mulungu; mofananamo, Akristu lerolino afunikira kulabadira mawu aulosi amenewo.

Pamene kuli kwakuti mitima ya anthu mwachisawawa inali​—ndipo idakali​—mumdima, zimenezo siziyenera kukhala tero kwa Akristu owona. Zimakhala ngati kuti ali ndi nyali yowala mmalo omwe akadakhala a mdima, mitima yawo. Petro anadziŵa kuti mwakulabadira mawu aulosi owunikira a Mulungu, Akristu akakhala ogalamuka ndi owunikiridwa ku mbanda kucha wa tsiku latsopano. Imeneyo ikakhala nthaŵi imene “nthanda,” kapena “nyenyezi yonyezimira ya nthanda,” ikayambadi kulamulira mu ulamuliro wa Ufumu.

Nzosangalatsa kuti E. W. Bullinger analemba za 2 Petro 1:19 motere: “Panopa, nkowonekeratu kuti payenera kukhala maburaketi, popeza kuti ndi ulosi umene uli kuunika kowalako, ndipo Kristu ndi kuwoneka Kwake ndizo nyenyezi ya Nthanda ndi kucha kwa Tsiku. Ndithudi, tanthauzo silingakhale lakuti tikuchenjezedwa kulabadira mawu aulosi kufikira Kristu atavumbulidwa m’mitima yathu! Ayi; koma tiyenera kulabadira m’mitima mwathu mawu aulosiwa, kufikira kukwaniritsidwa kutafika mwa kuwoneka kwa Kristu​—kuuka kwa Iye amene akutchedwa ‘Nyenyezi ya Nthanda.’”​—Figures of Speech Used in the Bible, 1898.

Mofananamo, matembenuzidwe ambiri a Baibulo amagwiritsira ntchito maburaketi pa 2 Petro 1:19.a New World Translation of the Holy Scriptures imasungabe dongosolo loyambirira la kalembedwe lopezeka m’Chigiriki choyambirira. Koma imagwiritsira ntchito makoma kuŵaika pawokha mawu akuti “kufikira mbanda kucha niuka nthanda” kuwapatula ku chilangizo cha kulabadira mawu ‘monga nyali yowala mmalo a mdima, m’mitima mwanu.’

[Mawu a M’munsi]

a Mwachitsanzo onani The Twentieth Century New Testament (kope la mu 1904), The Emphatic Diaglott (kope la mu 1942), Concordant Literal New Testament (1976).

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena