Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 4/15 tsamba 14-20
  • Kodi Mudzatsanzira Chifundo cha Mulungu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mudzatsanzira Chifundo cha Mulungu?
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chiweruzo Cholungama Chaumulungu Chinachitidwa
  • Chiweruzo Cholungama Cholinganizidwa Ndi Chifundo
  • Kudera Nkhaŵa ndi Zotaika
  • Chikondwerero Chakumwamba​—Kukondwerera Chiyani?
  • Kutembenuka Mtima ndi Chifundo Zikugwira Ntchito
  • Yehova—Gwero la Chilungamo Chenicheni
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Tsanzirani Yehova—Chitani Chilungamo
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Chilungamo Posachedwapa Kaamba ka Mitundu Yonse
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Pamakhala Chisangalalo Munthu Wochimwa Akalapa
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 4/15 tsamba 14-20

Kodi Mudzatsanzira Chifundo cha Mulungu?

“Khalani akutsanza a Mulungu, monga ana okondedwa.”​—AEFESO 5:1.

1. Kodi nchifukwa ninji kutsanzira ena kuyenera kukhala kodetsa nkhaŵa kwa tonsefe?

KAYA kukhale kwabwino kapena koipa, anthu ambiri amatsanzira ena. Anthu amene amatizinga, ndi amene tingaŵatsanzire, angatiyambukire kwakukulu. Wolemba wouziridwa wa Miyambo 13:20 anachenjeza kuti: ‘Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru: koma mnzawo wa opusa adzapwetekedwa.’ Pamenepo, pali chifukwa chabwino chimene Mawu a Mulungu amanenera kuti: ‘Usatsanza chiri choipa komatu chimene chiri chokoma. Iye wakuchita chokoma achokera kwa Mulungu.’​—3 Yohane 11.

2. Kodi tiyenera kutsanzira yani, ndipo m’njira zotani?

2 Tiri ndi zitsanzo zabwino koposa za m’Baibulo za amuna ndi akazi omwe tingaŵatsanzire. (1 Akorinto 4:16; 11:1; Afilipi 3:17) Komabe, chitsanzo choyambirira chenicheni choti tichitsanzire ndi Mulungu. Pa Aefeso 4:31–5:2, pambuyo posonyeza zikhoterero ndi machitachita amene tiyenera kuŵapeŵa, mtumwi Paulo anafulumiza kuti tikhale ‘a mtima wachifundo, akukhululukirana nokha.’ Ichi chinatsogolera ku chenjezo lalikulu ili: ‘Chifukwa chake khalani akutsanza a Mulungu, monga ana okondedwa; ndipo yendani m’chikondi.’

3, 4. Kodi Mulungu anapereka kulongosola kotani kwa iye mwini, ndipo kodi nchifukwa ninji tiyenera kulingalira kukhala kwake Mulungu wolungama?

3 Kodi nziti zimene ziri njira ndi mikhalidwe ya Mulungu zimene tiyenera kuzitsanzira? Pali mbali zambiri za umunthu wake ndi zochita, monga momwe zingawonedwere m’njira imene iye anadzilongosolera yekha kwa Mose: ‘Yehova, Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wochuluka, ndi wachowonadi; wakusungira anthu osaŵerengeka chifundo, wakukhululukira mphulupulu ndi kulakwa ndi kuchimwa; koma wosamasula wopalamula; wakulangira ana ndi zidzukulu chifukwa cha mphulupulu ya atate awo.’​—Eksodo 34:6, 7.

4 Popeza kuti Yehova ali “wokonda chilungamo ndi chiweruzo cholungama,” tifunikira kudziŵadi ndi kutsanzira mbali imeneyi ya umunthu wake. (Salmo 33:5, NW; 37:28) Iye ali Mlengi, ndiponso Woweruza wamkulu ndi Wopereka Lamulo wa anthu, chotero amasonyeza chiweruzo cholungama kwa onse. (Yesaya 33:22) Izi zasonyezedwa bwino lomwe m’njira imene iye anafunira chiweruzo cholungama ndi kuchipangitsa kuchitidwa pakati pa anthu ake a Israyeli ndiponso pambuyo pake ku mpingo Wachikristu.

Chiweruzo Cholungama Chaumulungu Chinachitidwa

5, 6. Kodi chiweruzo cholungama chinasonyezedwa motani m’zochita za Mulungu ndi Israyeli?

5 Pamene ankasankha Israyeli monga anthu ake, Mulungu anafunsa kaya ngati iwo ‘akamvera mawu ake ndithu, ndi kusunga chipangano chake.’ Atasonkhana patsinde la Phiri la Sinai, iwo anayankha kuti: ‘Zonse adazilankhula Yehova tidzazichita.’ (Eksodo 19:3-8) Linali thayo lowopsa chotani nanga! Kupyolera mwa angelo, Mulungu anapatsa Aisrayeli malamulo okwanira 600, omwe iwo, monga anthu odzipereka kwa iye, anali ndi thayo lakuwasunga. Kodi bwanji ngati munthu wina sanatero? Katswiri wa Chilamulo cha Mulungu anafotokoza kuti: ‘Mawu adalankhulidwa ndi angelo adakhala okhazikika, ndipo cholakwira chirichonse ndi chosamvera chalandira mphotho yobwezera yolungama.’​—Ahebri 2:2.

6 Inde, Mwisrayeli amene sanamvere anayang’anizana ndi “mphotho yobwezera yolungama,” osati chiweruzo cholungama chopereŵera cha anthu, koma chiweruzo cholungama chochokera kwa Mlengi wathu. Mulungu anandandalitsa zilango zosiyanasiyana kaamba ka kuswa lamulo. Chilango chowopsa chinali ‘kusadzidwa,’ kapena kuphedwa. Icho chinagwira ntchito ku milandu yaikulu, yonga ngati kulambira mafano, kuchita chigololo, kugonana kwapachibale, kugonana ndi zinyama, kugonana kwa ofanana ziŵalo, kupereka ana nsembe, mbanda, ndi kugwiritsira ntchito molakwa mwazi. (Levitiko 17:14; 18:6-17, 21-29) Kuwonjezerapo, Mwisrayeli aliyense amene mwadala, mosalapa anaswa lamulo laumulungu lirilonse akanakhoza ‘kusadzidwa.’ (Numeri 4:15, 18; 15:30, 31) Pamene chiweruzo chaumulungu cholungama chimenechi chinachitidwa, ziyambukiro zikanazindikiridwa ndi mbadwa za wochita choipayo.

7. Kodi nziti zomwe zinali zotulukapo zina za kupereka chiweruzo cholungama kwa Mulungu pakati pa anthu akale?

7 Zilango zoterozo zinagogomezera kuwopsa kwakuswa lamulo laumulungu. Mwachitsanzo, ngati mwana anapezeka kuti nchidakwa ndiponso wosusuka, iye anabweretsedwa pamaso pa oweruza achikulire. Ngati iwo anapeza kuti anali wochita cholakwa mwadala, wosalapa, makolo ake anafunikira kukhala ndi phande m’kupereka chiweruzo cholungama. (Deuteronomo 21:18-21) Awo a ife omwe ndi makolo angazindikire kuti ichi sichinali chokhweka kuchichita. Komabe Mulungu anadziŵa kuti chinali chofunikira kotero kuti kuipa kusafalikire pakati pa alambiri owona. (Ezekieli 33:17-19) Izi zinakonzedwa ndi Uyo amene za iye tinganene kuti: ‘Njira zake zonse ndi chiweruzo; Mulungu wokhulupirika ndi wopanda chisalungamo; iye ndiye wolungama ndi wolunjika.’​—Deuteronomo 32:4.

8. Kodi chiweruzo cholungama chinazindikiritsa motani zochita za Mulungu ndi mpingo Wachikristu?

8 Pambuyo pa zaka mazana ambiri Mulungu anakana mtundu wa Israyeli ndikusankha mpingo Wachikristu. Koma Yehova sanasinthe. Iye anamamatirabe ku chiweruzo cholungama ndipo analongosoledwa kukhala “moto wonyeketsa.” (Ahebri 12:29; Luka 18:7, 8) Chotero iye anapitirizabe kukhala ndi makonzedwe operekera mantha aumulungu kumpingo wonse mwakuchotsa ochita zoipa. Akristu odzipereka omwe anakhala ochita zoipa osalapa anayenera kuchotsedwa.

9. Kodi kuchotsedwa nchiyani, ndipo kodi kumakwaniritsanji?

9 Kodi kuchotsedwa kumaloŵetsamonji? Tikupeza phunziro labwino m’njira imene vuto linasamaliridwira m’zaka za zana loyamba. Mkristu wa ku Korinto anachita chisembwere ndi mkazi wa atate ake ndipo sanalape, chotero Paulo analamula kuti achotsedwe mumpingo umenewo. Ichi chinayenera kuchitidwa kotero kuti atetezere chiyero cha anthu a Mulungu, popeza kuti ‘chotupitsa pang’ono chitupitsa mtanda wonse.’ Kumchotsa iye kukapangitsa kuti choipa chake chisanyazitse ponse paŵiri Mulungu ndi anthu Ake. Chilango chowopsa cha kuchotsedwa chingampangitse kuzindikira zinthu ndi kumpangitsa iye limodzi ndi mpingo kuwopa Mulungu.​—1 Akorinto 5:1-13; yerekezerani ndi Deuteronomo 17:2, 12, 13.

10. Kodi atumiki a Mulungu ayenera kuchita motani ngati munthu wina wachotsedwa?

10 Lamulo laumulungu nlakuti ngati wochita zoipa wachotsedwa, Akristu ayenera ‘kusayanjana naye . . . , kungakhale kukadya naye wotere, iyayi.’a Motero iye amasadzidwa kotheratu ku kuyanjana, kuphatikizapo kucheza ndi okhulupirika omwe amalemekeza ndipo akufuna kuyenda mogwirizana ndi lamulo la Mulungu. Ena angakhale achibale osakhala a m’banja limodzi, osati a banja limodzimodzilo. Chingakhale chovuta kwa achibale amenewo kugwiritsira ntchito chitsogozo chaumulungu chimenechi, monga momwe sizinaliri zokhweka kwa makolo Achihebri pansi pa Chilamulo cha Mose kukhala ndi phande m’kupha mwana woipa. Komabe, lamulo la Mulungu nlomvekera bwino; chifukwa chake tingakhale otsimikiza kuti kuchotsedwa nkolungama.​—1 Akorinto 5:1, 6-8, 11; Tito 3:10, 11; 2 Yohane 9-11; onani Nsanja ya Olonda ya March 15, 1982, masamba 26-31; April 15, 1988, masamba 28-31.

11. Kodi ndimotani mmene mbali zosiyanasiyana za umunthu wa Mulungu zingawonekere mogwirizana ndi kuchotsedwa?

11 Ngakhale ndi choncho, kumbukirani kuti Mulungu wathu sali kokha wolungama; alinso ‘wachifundo chochuluka, wokhululukira mphulupulu ndi kulakwa.’ (Numeri 14:18) Mawu ake amamveketsa bwino lomwe kuti munthu wochotsedwa angalape, kufuna chikhululukiro cha Mulungu. Pamenepo nchiyani? Oyang’anira okhala ndi luso angakumane naye kuti atsimikize mwapemphero ndi mosamalitsa ngati iye akuperekadi umboni wokhala wolapa pa choipa chomwe anachotsedwera. (Yerekezerani ndi Machitidwe 26:20.) Ngati nditero, iye angabwezeretsedwe mumpingo, monga momwe 2 Akorinto 2:6-11 akusonyezera kuti ndizo zinachitika kwa munthu wa ku Korintoyo. Komabe, anthu ena ochotsedwa akhala kunja kwa mpingo wa Mulungu kwa zaka zambiri, chotero kodi chinachake chingachitidwe kuwathandiza kupeza njira yobwererera?

Chiweruzo Cholungama Cholinganizidwa Ndi Chifundo

12, 13. Kodi nchifukwa ninji kutsanzira kwathu Mulungu kuyenera kuphatikizapo zoposa kungosonyeza chiweruzo chake cholungama?

12 Zomwe zafotokozedwazo zangokhudza kwakukulukulu mbali imodzi ya mikhalidwe ya Mulungu, monga momwe yatchulidwira pa Eksodo 34:6, 7. Komabe, mavesi amenewo amandandalitsa zambiri osati chiweruzo cholungama cha Mulungu chokha, ndipo awo amene akufuna kumtsanzira samasumika maganizo pa kusonyeza chiweruzo cholungama chokha. Ngati mukanafuna kupanga chitsanzo cha kachisi womangidwa ndi Solomo, kodi mukanaphunzira nsanamira imodzi yokha? (1 Mafumu 7:15-22) Ayi, popeza kuti iyo siikakupatsani chithunzi chokwanira cha mpangidwe ndi ntchito ya kachisiyo. Mofananamo, ngati tikufuna kutsanzira Mulungu, tifunikiranso kutengera njira zake zina ndi mikhalidwe, monga ngati kukhala kwake ‘wachifundo ndi wachisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wochuluka, ndi wachowonadi; wakusungira anthu osaŵerengeka chifundo, wakukhululukira mphulupulu ndi kulakwa ndi kuchimwa.’

13 Chifundo ndi kukhululukira ndiyo mikhalidwe yaikulu ya Mulungu, monga momwe tawonera m’njira imene anachitira ndi Israyeli. Mulungu wachiweruzo cholungama sanaleke kupereka chilango kaamba ka kulakwa kobwerezabwereza, komabe, iye anasonyeza chifundo chokwanira ndi kukhululukira. ‘Analangiza Mose njira zake, ndi ana a Israyeli machitidwe ake. Yehova ndiye wa nsoni zokoma ndi wachisomo, wosakwiya msanga, ndi wachifundo chochuluka. Sadzatsutsana nawo nthaŵi zonse; ndipo sadzasunga mkwiyo wake kosatha.’ (Salmo 103:7-9; 106:43-46) Inde, kulingalira zochita zake zakale m’zaka zoposa mazana ambiri zapitazo kumatsimikizira mawu amenewo kukhala owona.​—Salmo 86:15; 145:8, 9; Mika 7:18, 19.

14. Kodi Yesu anasonyeza motani kuti ankatsanzira chifundo cha Mulungu?

14 Popeza kuti Yesu Kristu ‘ali chinyezimiro cha ulemerero [wa Mulungu], ndi chizindikiro chenicheni cha chikhalidwe chake,’ tiyenera kumuyembekezera iye kusonyeza chifundo ndi kukhala wofunitsitsa kukhululukira mofananamo. (Ahebri 1:3) Iye anaterodi, monga mmene zochita zake ndi ena zimasonyezera. (Mateyu 20:30-34) Iye anagogomezeranso chifundo mwa mawu ake amene timaŵerenga m’Luka mutu 15. Mafanizo atatu amene ali mmenemo amatsimikizira kuti Yesu anatsanzira Yehova, ndipo amapereka maphunziro ofunika koposa kwa ife.

Kudera Nkhaŵa ndi Zotaika

15, 16. Kodi nchiyani chimene chinasonkhezera Yesu kupereka mafanizo m’Luka 15?

15 Mafanizo amenewo amatsimikizira chikondwerero chachifundo cha Mulungu mwa ochimwa, akumasonyeza chithunzi chogwirizana choti tichitsanzire. Talingalirani makhazikitsidwe a mafanizowo: ‘Koma amisonkho onse ndi anthu ochimwa analikumyandikira [Yesu] kudzamva iye. Ndipo Afarisi ndi alembi anadandaula nati, Uyu alandira anthu ochimwa, nadya nawo.’​—Luka 15:1, 2.

16 Anthu onse omwe analoŵetsedwamo anali Ayuda. Afarisiwo ndi alembiwo ankanyadira kumamatira kwawo ku Chilamulo cha Mose mosamalitsa, mtundu wa chilungamo chamwambo. Komabe, Mulungu sanavomerezane ndi kudzilungamitsa koteroko. (Luka 16:15) Mwachiwonekere, amisonkho otchulidwawo anali Ayuda omwe ankasonkhetsera msonkho Roma. Chifukwa chakuti ambiri anapempha ndalama zochuluka mopambanitsa kwa Ayuda anzawo, amisonkho anali kagulu konyozedwa. (Luka 19:2, 8) Iwo anaikidwa m’gulu limodzi ndi ‘ochimwa,’ amene anaphatikizapo anthu achisembwere, ngakhale achigololo. (Luka 5:27-32; Mateyu 21:32) Koma Yesu anaŵafunsa atsogoleri achipembedzo odandaulawo kuti:

17. Kodi fanizo loyamba la Yesu m’Luka 15 linali lotani?

17 ‘Munthu ndani wa inu ali nazo nkhosa makumi khumi, ndipo pakutaika imodzi ya izo, sasiya nanga m’chipululu zinazo makumi asanu ndi anayi mphambu zisanu ndi zinayi, nalondola yotaikayo kufikira aipeza? Ndipo pamene adaipeza, aisenza pa mapeŵa ake wokondwera. Ndipo pakufika kunyumba kwake amema abwenzi ake ndi anansi ake, nanena nawo, Kondwerani ndi ine, chifukwa ndinapeza nkhosa yanga yotaikayo. Ndinena kwa inu, kotero kudzakhala chimwemwe kumwamba chifukwa cha wochimwa mmodzi wotembenuka mtima, koposa anthu olungama makumi asanu ndi anayi mphambu asanu ndi anayi, amene alibe kusoŵa kutembenuka mtima.’ Atsogoleri achipembedzowo anamvetsetsa fanizolo, popeza kuti nkhosa ndi abusa anali ofala. Chifukwa chodera nkhaŵa, mbusayo anasiya nkhosa 99 kuti zidzidya padambo lozoloŵereka pamene iye ananka kukafuna yotaikayo. Akumaumirirabe kufikira ataipeza, iye ananyamula mwachikondi nkhosa yochititsidwa manthayo kubwerera ku gulu lankhosa.​—Luka 15:4-7.

18. Monga momwe kwagogomezeredwa m’fanizo lachiŵiri la Yesu m’Luka 15, kodi nchiyani chimene chinapangitsa chimwemwe?

18 Yesu anawonjezera fanizo lachiŵiri ili: ‘Kapena mkazi wanji ali nazo ndalama zasiliva khumi, ngati itaika imodzi, sayatsa nyali, nasesa m’nyumba yake, nafunafuna chisamalire kufikira akaipeza? Ndipo mmene aipeza amema abwenzi ake ndi anansi ake, nanena, Kondwerani ndi ine, chifukwa ndinapeza ndalama ndidatayayo. Chomwecho, ndinena kwa inu, kuli chimwemwe pamaso pa angelo a Mulungu chifukwa cha munthu wochimwa mmodzi amene atembenuka mtima.’ (Luka 15:8-10) Ndalama yasiliva inali yokwanira pafupifupi malipiro a tsiku limodzi a wantchito. Ndalama yasiliva ya mkaziyo ingakhale idali choloŵa cha banja, kapena ingakhale idapangidwa kukhala zokometsera. Pamene inataika, iye anafunafuna zolimba kuti aipeze ndalamayo, ndipo kenaka iye limodzi ndi mabwenzi ake aakazi anakondwera. Kodi ichi chikutiuzanji ponena za Mulungu?

Chikondwerero Chakumwamba​—Kukondwerera Chiyani?

19, 20. Kodi mafanizo aŵiri oyamba a Yesu m’Luka 15 anali kunena makamaka za yani, ndipo kodi ndi mfundo yaikulu yotani imene anapereka?

19 Mafanizo aŵiriwa anaperekedwa kuyankha kusulizidwa kwa Yesu, yemwe miyezi ingapo poyambirira anadzizindikiritsa kukhala ‘mbusa wabwino’ yemwe akapereka moyo wake kaamba ka nkhosa zake. (Yohane 10:11-15) Chikhalirechobe, mafanizowo kwakukulukulu sanali kulankhula za Yesu. Maphunziro omwe alembi ndi Afarisi anafunikira kuphunzira anazikidwa pa mkhalidwe ndi njira za Mulungu. Chotero, Yesu ananena kuti kumwamba kumakhala chimwemwe chifukwa cha wochimwa mmodzi amene atembenuka mtima. Anthu achipembedzo amenewo ananena kuti anatumikira Yehova, komabe sanamutsanzire. Kumbali ina, njira zachifundo za Yesu zinaimira chifuno cha Atate wake.​—Luka 18:10-14; Yohane 8:28, 29; 12:47-50; 14:7-11.

20 Ngati munthu mmodzi mwa anthu zana limodzi anachititsa chimwemwe, pamenepo ndalama imodzi mwa khumi inachititsa chimwemwe choposa. Ngakhale lerolino, timawona chisangalalo cha akazi ngati apeza ndalama! Panoponso, phunzirolo likusumika kumwamba, m’lingaliro lakuti “angelo a Mulungu” amakondwera ndi Yehova ‘chifukwa cha munthu mmodzi wochimwa amene atembenuka mtima.’ Onani liwu lomaliziralo, lakuti “atembenuka mtima.” Mafanizo ameneŵa anali kunenadi za ochimwa omwe atembenuka mtima. Ndipo mungawone kuti onse aŵiriwo anagogomezera kuyenera kwakukhala ndi chikondwerero chifukwa cha kutembenuka mtima kwawo.

21. Kodi ndiphunziro lotani limene tikuphunzira kuchokera ku mafanizo a Yesu m’Luka 15?

21 Atsogoleri achipembedzo osokeretsedwawo omwe anadzimva kukhala okhutira ndi kugonjera ku Chilamulo ananyalanyaza kukhala kwa Mulungu ‘wachifundo ndi chisomo, . . . kukhululukira mphulupulu ndi kulakwa ndi kuchimwa.’ (Eksodo 34:6, 7) Akanakhala kuti amatsanzira mbali imeneyi ya njira ndi umunthu wa Mulungu, iwo akanazindikira chifundo cha Yesu kulinga kwa ochimwa omwe anatembenuka mtima. Kodi bwanji za ife? Kodi tikulabadira phunzirolo ndikuligwiritsira ntchito? Eya, tamverani fanizo lachitatu la Yesu.

Kutembenuka Mtima ndi Chifundo Zikugwira Ntchito

22. Mwachidule, kodi Yesu anapereka fanizo lachitatu lotani m’Luka 15?

22 Kaŵirikaŵiri ilo latchedwa fanizo la mwana woloŵerera. Komabe, poliŵerenga mungawone chifukwa chimene ena amalilingalira kukhala fanizo la chikondi cha atate. Limasimba za mwana wamng’ono m’banja, yemwe anatenga choloŵa chake kwa atate wake. (Yerekezerani ndi Deuteronomo 21:17.) Mwana ameneyu akuchoka kunka kudziko lakutali, kumene akusakaza zinthu zake zonse mumkhalidwe wachitaiko, akumagwira ntchito yoŵeta nkhumba, ndipo wafikira pakulakalaka zakudya zankhumbazo. Pomalizira pake iye akuzindikira kulakwa kwake nagamulapo kubwerera kunyumba, kuti akangogwirira ntchito atate ake monga munthu waganyu. Pamene akuyandikira kunyumba, atate ake akukhala oyamba kukamchingamira, ngakhale kumchitira phwando. Mbale wake wamkulu, yemwe anatsala kunyumba kumagwira ntchito, akuipidwa ndi chifundo chosonyezedwacho. Koma tateyo akuti ayenera kukondwera chifukwa mwana yemwe anali wakufa wakhalanso ndi moyo tsopano.​—Luka 15:11-32.

23. Kodi tiyenera kuphunziranji m’fanizo la mwana woloŵerera?

23 Alembi ndi Afarisi ena angakhale analingalira kuti anayerekezeredwa ndi mwana wamkuluyo, mosiyana ndi ochimwa omwe anali ngati mwana wamng’onoyo. Komabe, kodi iwo anamvetsetsa mfundo yaikulu ya fanizolo, ndipo kodi ifeyo tikutero? Ilo likugogomezera mkhalidwe wofunika koposa wa Atate wathu wakumwamba wachifundo, kufunitsitsa kwake kukhululukira kozikidwa pa kutembenuka mtima kwa wochimwayo. Ilo liyenera kukhala linasonkhezera omvetsera kuvomereza mwachimwemwe ku kuomboledwa kwa ochimwa otembenuka mtima. Mmenemo ndi mmene Mulungu amawonera zinthu ndi mmene amachitirapo kanthu, ndipo awo omutsanzira amachita zofananazo.​—Yesaya 1:16, 17; 55:6, 7.

24, 25. Kodi ndinjira za Mulungu ziti zimene tiyenera kutsanzira?

24 Mwachiwonekere, chiweruzo cholungama chimazindikiritsa njira zonse za Mulungu, chotero awo amene akufuna kutsanzira Yehova amakonda ndi kulondola chiweruzo cholungama. Komabe, Mulungu wathu samasonkhezeredwa ndi chiweruzo cholungama chopanda maziko kapena cholimba. Chifundo chake ndi chikondi nzazikulu. Iye amasonyeza zimenezi mwakukhala wofunitsitsa kukhululukira kozikidwa pa kutembenuka mtima kowona. Pamenepo, nkoyenerera kuti Paulo anagwirizanitsa kukhululukira kwathu ndi kutsanzira Mulungu: ‘[Khalani] akukhululukirana nokha, monganso Mulungu mwa Kristu anakhululukira inu. Chifukwa chake khalani akutsanza a Mulungu, monga ana okondedwa.’​—Aefeso 4:32–5:2.

25 Kwanthaŵi yaitali Akristu owona akhala akuyesayesa kutsanza chiweruzo cholungama ndi chifundo ndi kufunitsitsa kukhululukira kwa Yehova. Pamene timdziŵa iye kwambiri, chimakhala chopepuka kumtsanzira m’mbali zimenezi. Komabe, kodi tingagwiritsire motani zimenezi kwa munthu yemwe moyenerera walandira chilango chachikulu chifukwa chakuti ankalondola njira ya tchimo? Tiyeni tiwone.

[Mawu a M’munsi]

a “Kuchotsedwa m’tchalitchi m’lingaliro lachisawawa kumatanthauza kachitidwe kadala m’kamene gulu limamana maudindo a umembala wake kwa awo omwe panthaŵi ina anali ndi kaimidwe kabwino. . . . Kuchotsedwa m’tchalitchi kunayambika m’nyengo Yachikristu kutanthauza kachitidwe kakuthamangitsa komwe chiungwe chachipembedzo chimamana ochimwawo misa, kulambira kwa mpingo, ndipo mothekera kwenikweni kuyanjana kwa mtundu uliwonse.”​—The International Standard Bible Encyclopedia.

Kodi Mwaphunziranji?

◻ Kodi chiweruzo cholungama cha Mulungu chinasonyezedwa motani mumpingo wa Israyeli ndi mpingo Wachikristu?

◻ Kodi nchifukwa ninji tiyenera kutsanzira chifundo cha Mulungu, kuwonjezera ku chiweruzo chake cholungama?

◻ Kodi nchiyani chomwe chinayambitsa mafanizo atatu a m’Luka mutu 15, ndipo kodi ndimaphunziro otani amene akutiphunzitsa?

[Chithunzi pamasamba 16, 17]

Chigwa cha er-Raha kutsogolo kwa Phiri la Sinai (kumanzere chakumbuyo)

[Mawu a Chithunzi]

Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.

[Mawu a Chithunzi patsamba 15]

Garo Nalbandian

[Mawu a Chithunzi patsamba 18]

Garo Nalbandian

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena