Kulaka Upandu m’Dziko Lachipolowe
KODI mumawopa kutuluka panja usiku? Kodi mumafunikira maloko aŵiri kapena atatu ku zitseko ndi mazenera anu? Kodi galimoto lanu kapena njinga inayamba yabedwapo? Kodi mudaberedwapo wailesi m’galimoto lanu? Kodi mumachita mantha m’malo akutiakuti?
Ngati muyankha kuti inde ku lirilonse la mafunso ameneŵa, ndiko kuti mukuyesayesa kulaka upandu m’dziko lachipolowe. Kodi mungachitenji ponena za uwo? Kodi Baibulo lingakuthandizeni kuulaka?
Maganizo Aupandu ndi Chiweruzo Cholungama
M’dziko laupandu, muli mbali zitatu zazikulu izi: apandu, apolisi, ndi minkhole. Kodi chofunikira nchiyani kwa inuyo, mnkhole wothekera, kuti muthe kulaka upandu? Kodi mungasonkhezere iriyonse ya mbali zitatu zimenezi? Mwachitsanzo, kodi mungawasinthe apandu?
Eya, apandu ambiri apanga upandu kukhala ntchito yawo. Iwo ausankha monga njira ya moyo yosavuta. ‘Kodi nkugwiriranji ntchito ngati mungathe kukhalira moyo zinthu zomwe ena azipeza?’ ndiyo imawoneka kukhala nthanthi yawo. Achifwambawo amadziŵa kuti mnkhole wachikatikati udzapereka ndalama zake popanda kulimbana. Ndipo chiwopsezo chakugwidwa ndi kutumizidwa ku ndende pokhala chachikulu motero, upandu kwa iwo umapereka mphotho.
Kuwonjezerapo, kuzenga milandu m’makoti nkocholoŵanacholoŵana ndipo kumadya nthaŵi. M’maiko ambiri, muli makoti, oweruza, ndi ndende zochepa kwambiri. Milandu yaupandu imachulukitsitsa mosatha kuthedwa ndi dongosolo lozenga milandulo. Kuperekedwa kwa chiweruzo cholungama kumachedwa kwambiri chakuti mkhalidwe uli monga momwe Baibulo linaufotokozera zaka zikwi zitatu zapitazo kuti: ‘Popeza sambwezera choipa chake posachedwa atamtsutsa munthu, ana a anthu atsimikizadi mitima yawo kuchita zoipa.’ Monga momwe lamulo lamakhalidwe abwino Labaibulo limeneli limasonyezera, pali chiyembekezo chochepa chouthetsera mwa kuchepetsa chiŵerengero cha apandu kapena kuwasintha.—Mlaliki 8:11.
Bwanji ponena za mbali yachiŵiri, apolisi? Kodi pali chiyembekezo chirichonse chakuti apolisi adzautha mkhalidwewo? Iwo eniwo adzayankha kuti: Pokhala ndi malamulo amene kaŵirikaŵiri amayesedwa moyanja zoyenera za mpandu, pokhala ndi maloya osawona mtima omwe amakhotetsa lamulo mwaluso kuombola munthu waliŵongo, pokhala ndi zitaganya zozengereza kulipira ndalama zambiri kaamba ka ndende zowonjezereka ndi zazikulu, ndipo pokhala ndi antchito apolisi ochepa, chipambano chimene angachipange nchochepa kwenikweni motsutsana ndi mliri wa upandu.
Zimenezo zimasiya mbali yachitatu, minkhole yothekera: anthu wambafe. Kodi pali chirichonse chimene tingachite kudzithandiza tokha kulaka bwinopo mkhalidwe wosalamulirika umenewu?
Nzeru Yeniyeni ndi Kulingalira
Bukhu Labaibulo la Miyambo limati: ‘Sunga nzeru yeniyeni ndi kulingalira; ndipo mtima wako udzatengapo moyo, ndi khosi lako chisomo. Pompo udzayenda m’njira yako osawopa, osapunthwa phazi lako.’ Uphungu umenewu ungagwire ntchito m’mikhalidwe imene iri yokhoza kupanga wina kukhala mnkhole wa upandu. Kodi ndinjira zina zotani mmene nzeru yeniyeni ingatithandizire m’mbaliyi?—Miyambo 3:21-23.
Apandu amakhala ngati zilombo zakuthengo zolusa. Amafunafuna mnkhole wosavuta. Iwo samafuna kuika pachiswe kulimbanako ndi kugonjetsa kothekera ngati apeza mnkhole wosavuta wobwezera mofananamo. Chotero iwo amalondola okalamba, odwala, osokera, ndi awo amene angakhale osadziŵa za mkhalidwe wowopsa. Mbalazo zimasankha nthaŵi ndi malo zimene zimawayenerera bwino koposa kuti ziukire. Pano mpomwe minkhole yothekerayo ingagwiritsire ntchito nzeru yeniyeni.
Monga momwe Baibulo limawafotokozera, okonda zoipa kaŵirikaŵiri amachita ntchito zawo mumdima. (Aroma 13:12; Aefeso 5:11, 12) Nzowona kuti lerolino maupandu ambiri ochitidwa kwa anthu ndi katundu wawo amachitidwa usiku. (Yerekezerani ndi Yobu 24:14; 1 Atesalonika 5:2.) Chifukwa chake, pamene kuli kothekera munthu wanzeru adzapeŵa kukhala m’malo owopsa nthaŵi ya usiku. Mumzinda wodzala ndi upandu wa New York, cholembedwa cha apolisi cha tsiku ndi tsiku chimavumbula kuti anthu ambiri amafwambidwa dzuŵa litaloŵa ndipo makamaka pambuyo pa 10 koloko, kaŵirikaŵiri pamene akubwerera kunyumba zawo. Anthu olusawo amakhala m’makwalala opanda anthu akumafunafuna minkhole. Chotero, ngati inu mufunikira kupanga chosankha cha kuyembekeza basi kapena taxi kapena kuyenda kupyola malo owopsa, lezani mtima ndikuyembekeza. Apo phuluzi, chokumana nacho chikhoza kukhala chovulaza.
Mkristu wina anamenyedwa mowopsa ndi kulandidwa zinthu pamene mmalo moyembekeza basi pafupifupi teni koloko usiku, anayenda mtunda waufupi kusanade kwambiri. Munali anthu ena m’khwalalamo, koma mbala zitatu zidachera msampha opusa. Mmodzi anapereka chizindikiro kwa enawo pamene mnkhole wothekera anali kubwera m’khwalala. Popanda kunena mawu alionse, iwo anaukira mnkholeyo ndipo kenaka anamlanda zinthu. Kunatha mofulumira kwambiri chakuti ngakhale mnansi wapafupi adalibe nthaŵi yoloŵereramo. Mnkholeyo pambuyo pake anavomereza kuti: “Nthaŵi ina ndidzayembekeza basi.”
Tsinzina ntole wachichepere wotchedwa Wotsomphola Waluso m’bukhu la Dickens lakuti Oliver Twist, anali chitsanzo chabwino kwambiri cha opulupudza achichepere a m’makwalala amakono. Mosiyana ndi Wotsomphola Walusoyo, mbala ndi achifwamba alerolino, mosasamala kanthu za msinkhu, anganyamule mfuti kapena mpeni, ndipo adzaugwiritsira ntchito. Apaulendo osokera, alendo wamba, ndi ogula osakhazikika omasunzumira m’masitolo m’mzinda wapiringupiringu ndiwo minkhole yosavuta ya apandu osawona mtima otero. Iwo adzaba chirichonse chopezeka mofulumira kwambiri kuposa ndi mmene mungaphethirire diso! Kodi chimene chingapangitse mtima wa mbala kulakalaka nchiyani? Unyolo wagolidi kapena chokometsera chamtengo wapatali chovalidwa poyera. Kapena kamera yokoloŵekedwa m’khosi mwa wapaulendo. Kuli kofanana ndi kuvala chizindikiro chakuti, “Idzani mudzandibere!” Chotero, kuchenjera nkofunika. Bisani chokometsera chirichonse, ndipo nyamulani kamera m’mkhalidwe wosawonekera poyera, mwinamwake kubisa m’chola choguliramo zinthu. Imeneyi ndiyo nzeru yeniyeni.
Kukhala watcheru ndiyo njira ina yolakira upandu. Baibulo limati: ‘Wanzeru maso ake ali m’mutu wake, koma chitsiru chiyenda mumdima.’ (Mlaliki 2:14) Kugwiritsira ntchito chenjezo limeneli m’vuto la upandu kudzatsogolera wina kudziŵa anthu ongoyendayenda mokaikiritsa popanda chifuno chenicheni. Chenjerani ndi mbala zomwe zingabwere kumbuyo kwanu ndi kutsomphola chola chanu pamene mukuyenda mphepete mwa msewu. Popeza kuti zina zimakwera njinga ndi kutsomphola zinthu za anthu pamene zidutsa pafupi paliŵiro lalikulu, osayenda mphepete mwenimweni mwa msewu, makamaka ngati mwanyamula chola cha brifikesi kapena chakumanja cha mtundu uliwonse. Peŵani sitima za m’mzinda zomwe ziri pafupifupi zopanda anthu. Mumakhala osungika pamene muli ndi gulu la anthu m’malo owala bwino lomwe. Mbala sizimafuna kuwonedwa ndi kuzindikiridwa.
Kuba m’nyumba uli upandu wina wofala umene kaŵirikaŵiri ukhoza kupewedwa ngati anthu anali osamala kwambiri ndi upandu. Baibulo molondola linagwiritsira ntchito kuyerekezera uku: “Alowera pamazenera ngati mkhungu.” (Yoweli 2:9) Nzeru yeniyeni imalamulira kuti musamasiya zitseko kapena mazenera zosakhomedwa. Nthaŵi zonse zimakhala zowona kuti kuchinjiriza nkwabwino kwambiri kuposa kuchiritsa. Ndalama zowonjezereka zowonongedwera pa kutetezera nyumba yanu zilidi chinjirizo la kuberedwa ndi kuvulazidwa kwakuthupi.
Kodi Bwanji Ngati Mwafwambidwa?
Inde, kodi bwanji ngati, mosasamala kanthu za kudzichinjiriza konseko, mwakumana ndi wachifwamba? Yesani kukhazika mtima kapena musasonyeze mayendedwe amantha. Kumbukirani kuti mbalayo ingakhalenso yamantha ndipo ingaganizire molakwa kachitidwe kanu. Yesani kulankhula ndi kulingalira ndi munthuyo ngati iye angalole. (Inde, woukirayo angakhalenso wamkazi.) Nthaŵi zina achifwamba amakhala odekha podziŵa kuti akuukira Mkristu weniweni ndi wowona mtima. Mosasamala kanthu za kuchitapo kanthu kwawo, musayese kukana ngati akungofuna ndalama zanu zokha kapena katundu. Apatseni zirizonse zimene akuzifuna. Baibulo limaphunzitsa kuti moyo wa munthu ngwamtengo wapatali kuposa chirichonse chimene iye angakhale nacho.—Yerekezerani ndi Marko 8:36.
Mosakupangitsa kuwonekera kukhala kufufuza kosamalitsa, yesani kuzindikira mikhalidwe imene wachifwambayo angakhale nayo, kaya m’kavalidwe kapena mawonekedwe athupi. Kodi amatchula motani mawu? Maumboni ameneŵa angakhale othandiza pamene muchita lipoti upanduwo kwa apolisi, popeza kuti apandu ambiri amakhala ndi njira yawo yokhazikika yochitira zinthu ndipo chifukwa cha chimenecho angazindikiridwe mosavuta kwambiri.
Nanga bwanji ponena za kunyamula chida chodzichinjirizira? Ndithudi sikukakhala kwanzeru kwa Mkristu kunyamula zida. Ngati mbalayo ikalingalira kuti mufuna kutulutsa chida, iyo sidzazengereza kukupwetekani kapena kukuphani. Kuwonjezerapo, kodi mungatsatire motani lamulo lamakhalidwe abwino Labaibulo la ‘kukhala ndi mtendere ndi anthu onse’ ngati mwadzikonzekeretsa ndi chida kaamba ka kubwezera kwachiwawa?—Aroma 12:18.
Mosasamala kanthu za kudzichinjiriza komwe mungakupange, palibe chitsimikizo chakuti inu tsiku lina simudzakhala mnkhole. M’mizinda yodzala ndi upandu, zimachitika mutangokhala m’malo oipa panthaŵi yosayenera. Osati kale kwambiri m’New York, loya wina anachoka mu ofesi yake kupita kukagula kofi yakumwa. Pamene ankaloŵa m’sitolomo, achichepere ena anabwera chapafupi ndi galimoto naombela mfuti malowo. Loyayo anaphedwa ndi chipolopolo chomwe chinaloŵa m’mutu. Chifukwa cha ‘nthaŵi ndi zotigwera zamwadzidzidzi,’ iye anataya moyo wake. Kalanga, ndi tsoka lotani nanga! Kodi pali chiyembekezo chirichonse kaamba ka yankho lokhalitsa ku mliri wamakono wa upandu umene ukukweteza dziko?—Mlaliki 9:11, NW.
Pamene Upandu Udzatha
Pafupifupi zaka zikwi ziŵiri zapitazo, Yesu ananeneratu kuti kukadza mbadwo umene ukawona zochitika zowopsa kwambiri kuposa mbadwo wina uliwonse womwe unakhalako. Pokhala ndi wailesi yakanema ndi njira yolankhulana yamwamsanga, anthu mamiliyoni, ayi, zikwi za mamiliyoni, amachitira umboni nkhanza pa madongosolo a nyuzi zakumaloko pamene zikuchitidwadi. Dziko lonse lakhala ngati mudzi umodzi, ndipo nyuzi yadziko lonse yakhala ngati nyuzi ya pamudzipo yomveka mwamsanga. Monga chotulukapo, zochitika zenizeni zimafika panyumba tsiku ndi tsiku, ndipo monga momwe Yesu analosera, anthu ambiri “akukomoka ndi mantha, ndi kuyembekezera zinthu zirinkudza ku dziko lapansi.”—Luka 21:26.
Yesu anawoneratu zinthu zomwe zachitika chiyambire 1914, zochitika zimene zikakhala kalambula bwalo wa “mathedwe a nthawi ya pansi pano.” (Mateyu 24:3-14) Koma iye anatinso: ‘Pakuwona zinthu izi zirikuchitika, zindikirani kuti ufumu wa Mulungu uli pafupi.’ (Luka 21:31) Izi zikutanthauza kuti posachedwapa ulamuliro wolungama wa Mulungu udzayambukira dziko lapansi modabwitsa.—Mateyu 6:9, 10; Chibvumbulutso 21:1-4.
Muulamuliro umenewo, ofatsa okha, amtendere, ndi awo omvera Mulungu adzasangalala ndi mikhalidwe ya Paradaiso ya dziko lapansi. Kodi nchiyani chidzachitika kwa apandu ndi ochita zoipa? ‘Adzawamweta msanga monga udzu, ndipo adzafota monga msipu wauŵisi. Pakuti ochita zoipa adzadulidwa: koma iwo akuyembekeza Yehova, iwowa adzalandira dziko lapansi.’ Pansi pa boma lakumwamba lolungama limenelo, sipadzakhala chipolowe kapena upandu.—Salmo 37:2, 9.
Ngati mungakonde kudziŵa zambiri ponena za chiyembekezo chozikidwa pa Baibulo chimenechi cha boma ladziko lonse lokhalitsa ndi lamtendere, fikirani Mboni za Yehova za kwanuko kapena pa Nyumba Yaufumu yawo yakumaloko. Iwo adzakondwera kukuthandizani kulimvetsetsa Baibulo, kwaulere.
[Mawu Otsindika patsamba 6]
‘Ochita zoipa adzadulidwa: koma iwo akuyembekeza Yehova, iwowa adzalandira dziko lapansi’
[Zithunzi patsamba 7]
Tsinzina ntole Wotsomphola Waluso, wosimbidwa ndi Charles Dickens, anali katswiri wofanana ndi achifwamba amakono
[Mawu a Chithunzi]
Graphic Works of GEORGE CRUIKSHANK, by Richard A. Vogler, Dover Publications, Inc.