Upandu m’Dziko Lachipolowe
UPANDU sivuto lamakono. Mbanda yoyamba inachitika zaka zikwi zambiri zapitazo pamene Kaini anapha mwambanda mchimwene wake Abele. Kugwirira chigololo ndi kugonana kwa ofanana ziŵalo zimatchulidwa m’Malemba Achihebri akale. (Genesis 4:8; 19:4, 5; 34:1-4) Anthu anali kufwambidwa m’zaka za zana loyamba za Nyengo Yathu ino, monga momwe fanizo la Msamariya wachifundo limasonyezera. (Luka 10:29-37) Koma pali kusiyana lerolino.
Kulingalira kwa anthu m’mizinda yambiri yaikulu ya dziko, kaya kukhale ku New York, London, Calcutta, kapena Bogotá, nkwakuti upandu ngwowanda koposa ndi wowopsa. Lipoti lochokera m’India Today lokhala ndi mutu wakuti “Kusalemekeza Mwambo Kosalamulirika” limati: “Chochitika chododometsa chowopseza kuswa chomangira cha makhalidwe abwino ndi mayanjano chomwe chimagwirizanitsa dziko pamodzi ndicho kuwonjezereka kwa chiwawa, kupanda ulemu, ndi kusalemekeza mwambo kosayeruzika.” M’kulimbana kwawo ndi upandu, ngakhale apolisi nthaŵi zina amayesedwa kupyola malire osungitsa lamulo nagwiritsira ntchito njira zaupandu iwo eni. Lipoti lapitalo lochokera ku India limati: “Imfa za m’ndende zikupitirizabe kupanga nkhani za panyuzi.” Ndipo zimenezo zirinso zowona m’maiko ena.
Chiwopsezo chakukhala mnkhole wa upandu chikuwoneka kukhala chikukulirakulirabe. Lipoti lochokera ku United States limanena kuti “limodzi mwa mabanja anayi Achimereka linakhudzidwapo ndi upandu wachiwawa kapena kuberedwa mu 1988.” Kuwonjezerapo, anthu tsopano akuchita maupandu achiwawa pa msinkhu wauchichepere. Magazini a ku Latin America otchedwa Visión akunena kuti “asanu ndi anayi mwa a sicarios [ambanda aganyu] khumi ngachichepere. [Iwo ndi] ‘ana’ m’lingaliro lamsinkhu ndi pansi pa chitetezo cha lamulo.” Ndiponso, kuchitidwa kwa maupandu achiwawa ndi achichepere liri vuto lapadziko lonse.
Baibulo linalosera pafupifupi zaka 2,000 zapitazo kuti: ‘Koma zindikira ichi, kuti masiku otsiriza zidzafika nthaŵi zowawitsa. Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, . . . osayera mtima, opanda chikondi chachibadwidwe, . . . osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino, achiŵembu, aliuma olimbirira, otukumuka mtima . . . Anthu oipa ndi onyenga, adzaipa chiipire, kusokeretsa ndi kusokeretsedwa.’—2 Timoteo 3:1-4, 13.
Chiyambire 1914, umboni ukuchuluka wakuti tikukhala m’masiku otsiriza ovutitsa amenewo. Pokhala litasakazidwa ndi nkhondo zadziko ziŵiri ndiponso ndi mikangano ina yaikulu, dziko lakhala losalamulirika, lachipolowe m’njira zambiri. Upandu ngwofala. Apandu atenga malo m’madera ambiri a m’mizinda, akumasintha njira ya moyo ya unyinji wa anthu omvera lamulo. Monga momwe nduna yotchuka ya ku United States inanenera kuti: “Pali zinthu zambiri zodetsa nkhaŵa tsopano, zinthu zomwe sitinkawopa. Nthaŵi zina timakhala amantha koposa chakuti nkukhala andende, pamene awo oyenera kuikidwa m’ndende ali omasuka.”
Monga chotulukapo, anthu lerolino akudzichinjiriza mwanjira zomwe zinali zosafunika zaka 20 kapena 30 zapitazo. Zitseko ziri ndi maloko aŵiri kapena atatu ndipo nzolimbitsidwa ndi zitsulo. Anthu m’madera ambiri amanyamula ndalama zochuluka zokhutiritsira wachifwamba kuti apeŵe kumenyedwa chifukwa chokhala opanda kanthu kopatsa mbalazo. Makwalala ambiri amakhala pafupifupi opanda anthu dzuŵa litaloŵa, oyendamo kaŵirikaŵiri ndi anthu osazoloŵerana ndi mkhalidwe wachitaganyacho okha, opusa osamvera, ndi awo omwe amakakamizidwa ndi mikhalidwe—ndiwo chandamali chokhweka cha olanda olusa omwe amayendayenda m’mizinda.
Kodi tingachitenji kuti tipeŵe kukhala minkhole ya upandu m’dziko ili lachipolowe ndi losalamulirika? Kodi tingalake motani?