Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 5/1 tsamba 8-9
  • Kuwonekawoneka Komalizira, ndi Pentekoste wa 33 C.E.

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuwonekawoneka Komalizira, ndi Pentekoste wa 33 C.E.
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Nkhani Yofanana
  • Kuwonekera Komaliza, ndi Pentekoste wa 33 C.E.
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Anaonekera kwa Anthu Ambiri Mwambo wa Pentekosite Usanachitike
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Yesu Anabwerera Kumwamba
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • “Mudzakhala Mboni Zanga”
    ‘Kuchitira Umboni Mokwanira za Ufumu wa Mulungu’
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 5/1 tsamba 8-9

Moyo ndi Uminisitala za Yesu

Kuwonekawoneka Komalizira, ndi Pentekoste wa 33 C.E.

PANTHAŴI ina Yesu apanga makonzedwe akuti atumwi ake onse 11 akumane naye paphiri ku Galileya. Mwachiwonekere ophunzira ena auzidwa ponena za msonkhanowo, ndipo anthu oposa pa chiŵerengero cha 500 asonkhana. Ha, uwo ukhala msonkhano wokondweretsa chotani nanga pamene Yesu awonekera nayamba kuwaphunzitsa!

Zinthu zina zimene Yesu akufotokozera gulu lalikululo nzakuti Mulungu wampatsa mphamvu zonse kumwamba ndi padziko lapansi. ‘Chifukwa chake mukani,’ iye akulimbikitsa motero, ‘phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la mzimu woyera: ndi kuŵaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.’

Talingalirani chimenecho! Amuna, akazi, ndi ana onse alandira ntchito imodzimodziyi yakukhala ndi phande m’ntchito yopanga ophunzira. Otsutsa adzayesayesa kuletsa kulalikira kwawo ndi kuphunzitsa, koma Yesu akuŵatonthoza kuti: ‘Onani, ine ndiri pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthaŵi ya pansi pano.’ Yesu akhalabe pamodzi ndi atsatiri ake mwa mzimu woyera, kuwathandiza kukwaniritsa uminisitala wawo.

Yesu adzisonyeza wamoyo kwa ophunzira ake kwa nyengo ya masiku 40 pambuyo pa kuuka kwake. Mkati mwa kuwonekawoneka kumeneku, iye aŵalangiza ponena za Ufumu wa Mulungu, nagogomezera chimene mathayo awo ali monga ophunzira ake. Pachochitika china iye awonekera ngakhale kwa mbale wake wopeza Yakobo namkhutiritsa iyeyu yemwe anali wosakhulupirira panthaŵi ina kuti Iye ndithudi ndiye Kristu.

Pamene atumwi adakali ku Galileya, Yesu mwachiwonekere aŵalangiza kubwerera ku Yerusalemu. Pokumana nawo kumeneko, iye anawauza kuti: ‘Asachoke ku Yerusalemu, komatu alindire lonjezano la Atate, limene, anati, munalimva kwa ine; pakuti Yohane, anabatizadi ndi madzi; koma inu mudzabatizidwa ndi mzimu woyera, asanapite masiku ambiri.’

Pambuyo pake Yesu akumananso ndi atumwi ake naŵatsogolera kunja kwa mzinda nafika ku Betaniya, kum’mawa kwa therezi la Phiri la Azitona. Modabwitsa, mosasamala kanthu za zonse zimene iye wanena ponena za kupita kwake kumwamba kwaposachedwa, iwo akadakhulupirirabe kuti Ufumu wake udzakhazikitsidwa padziko lapansi. Chotero iwo afunsa kuti: ‘Ambuye, kodi nthaŵi ino mubwezera ufumu kwa Israyeli?’

Mmalo moyesayesa kuwongolera malingaliro awo olakwika, Yesu angoyankha kuti: ‘Sikuli kwa inu kudziŵa nthaŵi kapena nyengo, zimene Atate anaziika muulamuliro wake wa iye yekha.’ Ndiyeno, akumagogomezeranso ntchito imene iwo ayenera kuichita, iye akuti: ‘Mudzalandira mphamvu, mzimu woyera utadza pa inu: ndipo mudzakhala mboni zanga m’Yerusalemu, ndi m’Yudeya lonse, ndi m’Samariya, ndi kufikira malekezero ake a dziko.’

Pamene iwo adakali chipenyere, Yesu ayamba kunyamuka kupita kumwamba, ndiyeno mtambo umchotsa kumaso kwawo. Pambuyo povula thupi lake lanyama, iye akwera kumwamba monga munthu wauzimu. Pamene atumwi 11 amenewo apitirizabe kuyang’ana kumwamba, amuna aŵiri ovala zoyera awonekera kumbali kwawo. Angelo ameneŵa ovala matupi aumunthu afunsa kuti: ‘Amuna a ku Galileya, muimiranji ndi kuyang’ana kumwamba? Yesu amene walandiridwa kunka kumwamba kuchokera kwa inu, adzadza momwemo monga munamuwona alinkupita kumwamba.’

Njira imene Yesu wangosiira dziko lapansi njopanda dzoma lapoyera ndipo kokha ndi atsatiri ake okhulupirika akupenyerera. Chotero iye adzabwera m’njira imodzimodziyo​—yopanda dzoma lapoyera ndipo kokha ndi atsatiri ake okhulupirika akuzindikira kuti iye wabweranso ndipo wayamba kukhalapo kwake muulamuliro wa Ufumu.

Atumwiwo tsopano atsika kuchoka pa Phiri la Azitona, adutsa Chigwa cha Kedroni, naloŵanso m’Yerusalemu. Iwo akhala kumeneko momvera lamulo la Yesu. Masiku khumi pambuyo pake, pa Phwando Lachiyuda la Pentekoste wa 33 C.E., pamene pafupifupi ophunzira 120 asonkhana m’chipinda chapamwamba m’Yerusalemu, phokoso longa mkokomo wa mphepo yolimba lidzaza nyumba yonse. Malilime onga moto awonekera, ndipo limodzi likhala pa aliyense wa opezekapowo, ndiponso ophunzira onse ayamba kulankhula m’zinenero zosiyanasiyana. Uku ndikutsanulidwa kwa mzimu woyera umene Yesu adalonjeza! Mateyu 28:16-20; Luka 24:49-52; 1 Akorinto 15:5-7; Machitidwe 1:3-15; 2:1-4.

◆ Kodi nkwayani kumene Yesu apereka malangizo otsazikira ali paphiri ku Galileya, ndipo kodi malangizo ameneŵa ngotani?

◆ Kodi nchitonthozo chotani chimene Yesu apereka kwa ophunzira ake, ndipo kodi ndimotani mmene iye adzakhalira pamodzi nawo?

◆ Kodi nkuutali wotani pambuyo pa kuuka kwake kumene Yesu awonekera kwa ophunzira ake, ndipo kodi iye aŵaphunzitsanji?

◆ Kodi nkwa munthu uti, amene mwachiwonekere sanali wophunzira Yesu asanafe, kumene Yesu awonekera?

◆ Kodi ndimisonkhano iŵiri yomalizira iti imene Yesu akuchita ndi atumwi ake, ndipo kodi nchiyani chimene chichitika pa zochitikazi?

◆ Kodi ziridi motani kuti Yesu adzabweranso m’njira imodzimodziyo yonga imene wapitiramo?

◆ Kodi chichitika nchiyani pa Pentekoste wa 33 C.E.?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena