Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lfb phunziro 93 tsamba 216-tsamba 217 ndime 5
  • Yesu Anabwerera Kumwamba

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yesu Anabwerera Kumwamba
  • Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • Anaonekera kwa Anthu Ambiri Mwambo wa Pentekosite Usanachitike
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Kuwonekawoneka Komalizira, ndi Pentekoste wa 33 C.E.
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Kuwonekera Komaliza, ndi Pentekoste wa 33 C.E.
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Pa Phiri la Azitona
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
Onani Zambiri
Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
lfb phunziro 93 tsamba 216-tsamba 217 ndime 5
Yesu akukwera kupita kumwamba ndipo atumwi ake akumuyang’ana

MUTU 93

Yesu Anabwerera Kumwamba

Yesu ndi ophunzira ake anakumana ku Galileya. Kumeneko anawapatsa lamulo lofunika kwambiri lakuti: ‘Pitani mukaphunzitse anthu a m’mayiko onse kuti akhale ophunzira anga. Mukawaphunzitse zimene ndinakuphunzitsani ndipo mukawabatize.’ Kenako anawalonjeza kuti: ‘Ndikhala nanu limodzi.’

Yesu ataukitsidwa anakhala padzikoli masiku 40 ndipo anaonana ndi ophunzira ake ambiri ku Galileya ndi ku Yerusalemu. Anawaphunzitsa zinthu zambiri komanso anachita zodabwitsa. Kenako anakumana ndi atumwi ake komaliza paphiri la Maolivi. Anawauza kuti: ‘Musachoke ku Yerusalemu. Mudikire zimene Atate analonjeza.’

Atumwi akewo sanamvetse zimene Yesu ankatanthauza. Moti anamufunsa kuti: ‘Kodi tsopano mukhala Mfumu ya Aisiraeli?’ Koma iye anawayankha kuti: ‘Nthawi ya Mulungu yoti ndikhale Mfumu sinakwane. Mudzalandira mphamvu ya mzimu ndipo mudzakhala mboni zanga. Mudzaphunzitsa anthu ku Yerusalemu, ku Yudeya, ku Samariya mpaka kumalekezero a dziko.’

Kenako Yesu anayamba kukwera kumwamba ndipo anabisika m’mitambo. Atumwi akewo ankangoyang’anabe kumwamba koma Yesu anali atapita.

Ndiyeno atumwiwo anachoka paphiri la Maolivi n’kupita ku Yerusalemu. Nthawi zonse ankakumana m’chipinda cham’mwamba n’kumapemphera. Ankadikira kuti Yesu awapatse malangizo ena.

“Uthenga wabwino uwu wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni kwa anthu amitundu yonse, kenako mapeto adzafika.”​—Mateyu 24:14

Mafunso: Kodi Yesu anapereka lamulo liti kwa ophunzira ake? Kodi paphiri la Maolivi panachitika zotani?

Mateyu 28:16-20; Luka 24:49-53; Yohane 20:30, 31; Machitidwe 1:2-14; 1 Akorinto 15:3-6

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena