Tikulandirani ku Misonkhano Yachigawo ya “Okonda Ufulu!”
UFULU! Ha liwu limenelo limamveka mosangalatsa chotani nanga! Palibe amene amasangalala ndi kukhala muukapolo kapena mumsinga. Zaka zaposachedwapa zawona machitachita ambiri olinga ku ufulu wandale zadziko woyembekezeredwa kuposa zaka zina zirizonse zomwe tingazikumbukire.
Komabe, monga momwe ufulu wandale zadziko uliri wokhumbirika, pali ufulu umene uli wofunika koposa ndi wokhumbirika. Uli ufulu umene Yesu Kristu, Mwana wa Mulungu, analankhula za iwo pamene anauza ophunzira ake kuti: ‘Ngati mukhala inu m’mawu anga, muli akuphunzira anga ndithu; ndipo mudzazindikira chowonadi, ndipo chowonadi chidzakumasulani.’ (Yohane 8:31, 32) Uwu ndi ufulu ku zikhulupiriro zonyenga zachipembedzo, ufulu ku kuwopa anthu, ufulu ku ukapolo ku zomwerekera zauchimo, ndi zina zambiri.
Uli ufulu umenewu womwe ndi mutu wa Misonkhano Yachigawo ya “Okonda Ufulu” yodzachitidwa ndi Mboni za Yehova kuzungulira padziko lonse kuyambira chilimwe cha 1991. Chiyambire chaka cha 1919, chomwe chinazindikiritsidwa mwa kuchotsedwa kwa ziletso za boma pa awo otsogolera pakati pawo, anthu a Mulungu akhala akusangalala ndi ufulu wowonjezereka m’kulambira kwawo koyera.
Nkoyenerera kwenikweni kuti nkhani ya ufulu yakhala ikugogomezeredwa mkati mwa zakazi pamisonkhano yateokratiki, ndi mitu yonga ngati “Msonkhano Wateokratiki wa ‘Mtundu Waufulu’” ndi “Misonkhano Yachigawo ya ‘Ana Aufulu a Mulungu.’” Ufulu walongosoledwanso mokwanira m’mabuku onga ngati “The Truth Shall Make You Free” ndi Moyo Wosatha—Mu Ufulu wa Ana a Mulungu.
Ufulu wopatsidwa ndi Mulungu umene atumiki a Yehova ali nawo suli kokha kaamba ka ubwino wawo ndi chisangalalo. Monga momwe tikuŵerengera pa Agalatiya 5:13 kuti: ‘Pakuti adakuitanani inu, abale, mukhale mfulu; chokhacho musachite nawo ufulu wanu chothandizira thupi, komatu mwa chikondi chitiranani ukapolo.’ Msonkhano Wachigawo wa “Okonda Ufulu” udzatithandiza kuzindikira cholinga cha ufulu wathu, kutitheketsa kumamatira ku ufulu wathu wamtengo wapatali, ndikutisonyeza mmene tingaugwiritsire ntchito bwino koposa.
Msonkhanowo udzayamba Lachisanu m’mawa pa 10:20 ndi programu ya nyimbo imene idzatikonzekeretsa kaamba ka chakudya chauzimu chotsatirapo. Mutu wa tsiku loyamba ngwakuti “Kudziŵa Chowonadi Chomwe Chimatimasula,” wozikidwa pa Yohane 8:32. M’mawawo udzasonyeza ndemanga zamalonje za tcheyamani ndi nkhani yaikulu yakuti, “Cholinga ndi Ntchito ya Ufulu Wathu Wopatsidwa ndi Mulungu.” Nkhani imeneyi idzagogomezera kusiyana pakati pa ufulu wotheratu wa Yehova ndi ufulu wochepa umene Mulungu amatipatsa. Idzatilimbikitsanso kugwiritsira ntchito bwino koposa ufulu umene tiri nawo. Programu yamasana idzachita ndi mbali zosiyanasiyana za ufulu wathu ndi uminisitala wathu ndipo idzamaliza ndi drama yakuti, Omasulidwira Kupititsa Patsogolo Kulambira Kowona.
Mutu wa tsiku lachiŵiri ngwakuti “Kuchilimika mu Ufulu Wathu Wopatsidwa ndi Mulungu,” wozikidwa pa Agalatiya 5:1. Programu ya m’mawa idzasonyeza nkhani yosiirana yosonyeza mmene chiŵalo chirichonse cha banja chingasangalalire ndi ufulu wopatsidwa ndi Mulungu m’banja. Awo amene akonzekera kubatizidwa adzayamikira mwapadera ndemanga zokhudza mmene ufulu ungafikiridwe mwa kudzipereka ndi ubatizo. M’programu yamasana mudzaphatikizidwa kukambitsirana kosangalatsa kuti kaya ngati ukwati uli mfungulo ya chimwemwe kapena ayi. Padzakhalanso nkhani yosiirana yonena za mbali zosiyanasiyana za ufulu ndipo kenaka nkhani yomalizira imene ikusumika pa Nthumwi Yeniyeni ya Mulungu yobweretsa ufulu ndi moyo wosatha.
Tsiku la Sande liri ndi mutu wakuti “Kugwiritsira Ntchito Ufulu Wathu Mogwirizana ndi Mzimu wa Mulungu,” wozikidwa pa 2 Akorinto 3:17. Programuyo idzasonyeza nkhani yosiirana yosangalatsa koposa yonena za fanizo la Yesu lolembedwa pa Mateyu 13:47-50, kuvumbula mmene Mboni za Yehova zimatumikirira monga asodzi a anthu. Nkhani Yabaibulo yamasana njakuti “Kutamanda Dziko Latsopano la Ufulu la Mulungu!” Idzatsatiridwa ndi mbali yatsopano ya msonkhano wachigawo: chidule cha phunziro la Nsanja ya Olonda la mlunguwo. Ndipo programuyo idzatha ndi chenjezo Lamalemba kwa tonsefe kuti tipitirizebe kupita patsogolo m’kugwiritsira ntchito bwino ufulu wathu wopatsidwa ndi Mulungu m’mayendedwe athu ndi m’kuchitira umboni kwathu.
Tikuuza anthu onse okonda ufulu mawu a wamasalmo Davide kuti: “Talawani, ndipo onani kuti Yehova ndiye wabwino.” (Salmo 34:8) Pangani kuyesayesa kulikonse kothekera kuti mudzafikepo pamsonkhano umenewu. Tsimikizani mtima kupezekapo kuyambira pachigawo chotsegulira pa Lachisanu m’mawa mpaka nkhani yomalizira pa Sande masana. Ngati mubwera ndi chilakolako chauzimu chabwino, mukuzindikira mokwanira kusoŵa kwanu kwauzimu, mudzakhaladi achimwemwe! (Mateyu 5:3) Ndipo tiyeni tisanyalanyaze lamulo lamakhalidwe abwino ili, ‘Iye wakufesa mooloŵa manja, mooloŵa manjanso adzatuta.’ Ichi chimagwiranso ntchito ku kukonzekera kwakhama kumene timakupanga pasadakhale kuti tikapezekepo, mmene timamvetserera mwakhama ku programu pamene ikuperekedwa, ndi mmene timatengera motenthedwa maganizo mwaŵi wa utumiki wodzipereka mwaufulu uliwonse umene umatitsegukira mogwirizana ndi Msonkhano Wachigawo wa “Okonda Ufulu.”—2 Akorinto 9:6.