Kusonkhana ndi Okonda Ufulu Woperekedwa ndi Mulungu
MBONI ZA YEHOVA nzapadera nthaŵi zonse m’njira zambiri. Izo zokha zimalankhula “chinenero choyera.” (Zekariya 3:9, NW) Ndizokhazo zimene ziri zogwirizana, zozindikiridwa ndi chikondi chofotokozedwa ndi Yesu Kristu. (Yohane 13:35) Ndipo izo zokha ndizo ziri ndi ufulu umene Yesu Kristu ananena kuti chowonadi chikaubweretsa, monga kwalembedwa pa Yohane 8:32 kuti: ‘Mudzazindikira chowonadi, ndipo chowonadi chidzakumasulani.’
Mawuwo amene Yesu Kristu, Mwana wa Mulungu, ananena kwa ophunzira ake, atsimikizira kukhala owona. Ndipo tsopano akuzindikiridwa koposa ndi kalelonse ndi Mboni za Yehova zonsezo zimene zinapezeka pa Misonkhano Yachigawo ya “Okonda Ufulu.” Programu yamsonkhano inamveketsa mwamphamvu kwa izo mbali zosiyanasiyana za ufulu wawo, mmene ziyenera kuugwiritsirira ntchito, thayo limene limadza ndi ufulu wawowo, ndi mmene zinaliri zodalitsidwa pokhala anthu omasuka.
Misonkhano yapanthaŵi yake ndi yothandiza imeneyi inayambira ku Chigawo Chadziko Chakumpoto pa June 7, 1991, mu Los Angeles, California, U.S.A. Programuyo inayamba pa 10:20 a.m. ndi kuseŵeredwa kwa nyimbo zamalimba, ndiyeno nyimbo ndi pemphero. Yotsegulira inali nkhani yamphamvu yozikidwa pa Yakobo 1:25. Malinga ndi The Jerusalem Bible, vesili limati: “Munthu amene amayang’ana mokhazikika palamulo langwiro la ufulu nakupanga chizoloŵezi chake—osati kumvetsera ndiyeno kuiŵala, koma mokangalika akumachita—adzakhala wokondwa m’zonse zimene achita.” Monga momwedi timayang’anira m’kalirole kuwona pamene tiyenera kudzikonza kuti tiwoneke bwino, momwemonso tifunikira kuumirira kuyang’anitsitsa m’lamulo langwiro la Mulungu la ufulu wakudziŵa m’mene tifunikira kusintha umunthu wathu. Ndipo tiyenera kuumirira kuyang’ana m’kalirole ameneyo.
Yotsatira inali nkhani ya tcheyamani, “Tikulandirani, Inu Nonse Okonda Ufulu.” Mboni za Yehova zimakonda ufulu, ndipo zimafuna kukhala zomasuka. Wokambayo anagwira mawu akatswiri a zamalamulo amene anasonyeza kuti sipangakhale ufulu popanda lamulo. Inde, Akristu sali omasuka kuchita mulimonse mmene amafunira koma ali omasuka kuchita chifuniro cha Yehova. Iwo amafuna kugwiritsira ntchito mokwanira ufulu wawo koma osati kuugwiritsira ntchito molakwa. Mboni za Yehova zasangalala ndi ufulu wowonjezereka makamaka chiyambire 1919. Wokambayo anasonyeza chigogomezero pa ufulu chopezeka m’mitu yamisonkhano ndi zofalitsidwa Zachikristu. Osonkhana onse akaphunzira zowonjezereka ponena za ufulu woperekedwa ndi Mulungu ndi mmene angaugwiritsirire ntchito.
Ndemanga zapanthaŵi yakezo zinatsatiridwa ndi kufunsidwa kwa okonda ufulu omwe anakondwa kupezekapo pamsonkhanopo. Misonkhano yoteroyo imakhala nthaŵi zachisangalalo, mongadi momwe mapwando atatu apachaka a Israyeli wakale analiri ndi chisangalalo chachikulu. Kufunsa kungapo kunawonetsa kuti misonkhano ndinthaŵi zachisangalalo zomangirira mwauzimu.
Ndiyeno panabwera nkhani yaikulu, “Chifuno ndi Kugwiritsiridwa Ntchito Kwa Ufulu Wathu Woperekedwa ndi Mulungu.” M’nkhaniyi osonkhanawo anaphunzira kuti Yehova yekha ndiye ali ndi ufulu wotheratu chifukwa chakuti ndiye Ulamuliro Womalizira ndipo ngwamphamvuyonse. Komabe, chifukwa cha dzina lake ndi ubwino wa zolengedwa zake, nthaŵi zina amaikira malire ufulu wake mwakusakwiya msanga ndi mwakudziletsa. Zolengedwa zake zaluntha zonse ziri ndi ufulu wocheperapo, popeza kuti ziyenera kugonjera kwa Yehova ndipo zimaikiridwa malire ndi malamulo ake achilengedwe ndi amakhalidwe. Yehova wazipatsa ufulu kuti zipeze chisangalalo koma makamaka kuti zimlemekeze ndi kumsangalatsa mwakumlambira. Chifukwa chakugwiritsira ntchito bwino ufulu wawo, Mboni za Yehova zakhala ndi mbiri yabwino padziko lonse ya kukhala zamakhalidwe abwino ndi zachangu muuminisitala wawo.
Lachisanu Masana
“Otanganitsidwa—m’Ntchito Zakufa Kapena Muutumiki wa Yehova?” unali mutu wogwira maganizo wa nkhani imene inatsegula chigawo cha masana Lachisanu. Ntchito zakufa zimaphatikizapo osati kokha zathupi komanso zina zimene ziri zakufa mwauzimu, zopanda pake, ndi zosaphula kanthu—monga ngati machitachita ongofuna kupeza ndalama. M’zimenezi, kudzisanthula mosamalitsa nkofunika kuwona ngati tikuika Ufumu patsogolo m’moyo wathu.
Nkhani yokhala ndi cholinga chofananacho inali yotsatira yakuti, “Kutsiriza Ntchito Yathu Monga Aminisitala a Mulungu.” Wokambayo anasonyeza kuti Akristu sayenera kudzikhutiritsa ndi utumiki wamba kapena kungofuna kukwaniritsa mlingo wa maola. Ayenera kufuna kukhala ogwira mtima m’mbali zonse za uminisitala wawo Wachikristu. Mfundozi zinamveketsedwa mwamphamvu mwa chitsanzo choperekedwa ndi mbali zakufunsa. Onse anafulumizidwa kutsiriza uminisitala wawo kumlingo wokwanira wothekera.
M’nkhani yakuti “Anthu Aufulu Koma Oŵerengeredwa Thayo,” wokambayo anagogomezera kuti ngakhale kuti anthu a Yehova amasamalira ufulu umene chowonadi chawabweretsera, ayenera kukumbukira kuti ufuluwo umadza ndi kuŵerengeredwa thayo. Ayenera kugwiritsira ntchito ufulu wawo, osati monga chodzikhululukira nacho cha mayendedwe oipa, koma kuchitamando cha Yehova. Monga Akristu, iwo ali oŵerengeredwa kwa “maulamuliro a akulu” ndipo ayeneranso kugwirizana ndi akulu mumpingo. (Aroma 13:1) Ndiponso, iwo ali oŵerengeredwa thayo m’mavalidwe awo, mapesedwe, ndi mayendedwe. Sayenera konse kuiŵala kuti ‘munthu aliyense wa ife adzadziŵerengera mlandu wake kwa Mulungu.’—Aroma 14:12; 1 Petro 2:16.
Ndiyeno panatsatira kukambitsirana za kufunika kwa Akristu kukhala “Opanda Mantha Pamene Mapeto a Dziko Lino Ayandikira.” Pamene kuli kwakuti anthu akuchita mantha ndi zimene zingabwere mtsogolo, Akristu ayenera kukhala opanda mantha kuchita uminisitala wawo. Kupanda mantha kuli chotulukapo cha kudalira Yehova, pakuti pamene munthu achuluka m’kuopa kusakondweretsa Mulungu, ndipamenenso amachepekera m’kuopa zolengedwa. Kuloŵeza malemba otonthoza kungalimbitse munthu kukhala wopanda mantha. Kuti akhale olimba mwauzimu ndi opanda mantha, atumiki a Mulungu amafunikiranso kugwiritsira ntchito bwino mwaŵi wonse wakuyanjana ndi okhulupirira anzawo. Aliyense ayeneranso kukumbukira mmene pemphero limathandizira kukhala wopanda mantha. Mwakukhala opanda mantha, Akristu adzasunga unansi wabwino ndi Yehova Mulungu.
Programu ya tsiku loyamba inatha ndi drama yopereka phunziro labwino yakuti Kumasulidwa Kukachirikiza Kulambira Kowona. Inasonyeza mmene banja lamakono linatengera phunziro kwa Ezara ndi gulu la anthu 7,000, omwe anadzimana kotero kuti abwerere ku Yerusalemu. Inatheketsa wosonkhana aliyense kusanthula zofunika zake zoyambirira ndi kuwona mmene angawonjezerere mwaŵi wake wautumiki. Dramayi inali ndi kenakake kwa akulu ndi achichepere omwe.
Loŵeruka M’maŵa
Pambuyo pa programu ya nyimbo zamalimba, nyimbo, pemphero, ndi kukambitsirana kwa lemba latsiku la Baibulo, programu ya pa Loŵeruka m’maŵa inali ndi nkhani yosiirana ya mutu wakuti “Ufulu Wokhala ndi Thayo m’Banja.” M’mbali yake yoyamba, “Mmene Atate Angatsanzirire Yehova,” atate anapatsidwa uphungu pa njira zosiyanasiyana zimene angatsanzirire Atate wathu wakumwamba. Timoteo woyamba 5:8 amati iwo ayenera kupezera banja osati zinthu zakuthupi zokha komanso zauzimu. Amatsanzira Yehova mwakukhala aphunzitsi abwino a banja lawo ndi mwakupereka chilango choyenera chachikondi pamene chifunika. Mfundozi zinasonyezedwa mwafanizo mwa mbali zakufunsa zingapo.
“Thayo Lochirikiza la Mkazi” inali mbali yotsatira ya nkhani yosiirana imeneyi. Inayamba ndi kugogomezera kuti mkazi ali ndi malo olemekezeka m’banja Lachikristu, mbali yakukhala wochirikiza. Kodi zimenezi zimafunanji kwa iye? Zimafuna kuti iye akhale wogonjera moyenerera, wosakakamiza konse mwamuna wake kuchita chinachake chofunidwa ndi iye yekha. Ayenera kusamalira bwino mathayo ake kwa mwamuna ndi ana ake, ndipo akhoza kupeza chikhutiritso chenicheni mwakusunga nyumba yake yaudongo ndi yaukhondo. Ndipo monga minisitala Wachikristu, iye angakhale ndi mipata yambiri yakutulukira muutumiki wakumunda. Kufunsa banja kunasonyeza nzeru ya uphungu Wamalemba woterowo.
Achichepere analandira mbali yawo m’nkhani yakuti “Ana Amene Amamvetsera ndi Kuphunzira.” Mwakuphunzitsa ana awo kumvetsera ndi kuphunzira, makolo amalemekeza Yehova ndi kusonyeza chikondi kwa abale awo auzimu ndi kwa ana awo enieniwo. Unansi wathithithi udzakhalapo pakati pa makolo ndi ana ngati akhala ndi nthaŵi yabwino pamodzi. Makolo ayenera kukhala okonzekera kuyankha mafunso a ana awo ndi kukulitsa chikhumbo chawo chakukhala ndi chidziŵitso. Kachiŵirinso, mbali za kufunsa zinasonyeza mmene ichi chingachitidwire.
Kenako panabwera uphungu wabwino wakuti “Khalani Waufulu Kutumikira Yehova.” Kodi ichi chimachitidwa motani? Mwakupeŵa kulondola ntchito zaudziko, maseŵera apamtima owononga nthaŵi, ndi zonulirapo zokondetsa zinthu zakuthupi. Yesu ndi mtumwi Paulo anapereka chitsanzo chabwino mwakukhala odzimana. Anthu a Yehova amafunikira kukhala ndi diso lakumodzi, losumikidwa pa zabwino za Ufumu. Ponena za kupeza zinthu zakuthupi, kuli kwanzeru kusunga ndalama tsopano ndi kugula mtsogolo mmalo mwakugula tsopano ndi kulipira mtsogolo. Achichepere ayenera kupeŵa kukhala ndi malingaliro omalota zisangalalo zakugonana ndi ntchito zaudziko. Mbali yakufunsa mpainiya wosakwatira inasonyeza madalitso amene amabwera pamene wina akhala womasuka kutumikira Yehova.
Programu ya m’maŵa pa Loŵeruka inatha ndi nkhani yakuti “Loŵani Muufulu mwa Kudzipatulira ndi Ubatizo.” Opita kuubatizo anakumbutsidwa kuti pamene kuli kwakuti chilengedwe chinaponyedwa muukapolo ndi chipanduko cha Adamu, Womasula wamphamvu, Yesu Kristu, anatsegula njira yoloŵa ufulu mwa nsembe yake. Wokambayo anasonyeza zimene zinaloŵetsedwamo m’kumasukira kuchita chifuniro cha Mulungu ndipo anagogomezera mathayo ndi madalitso a mtsogolo mwa opita kuubatizowo.
Loŵeruka Masana
Programu yamasana pa Loŵeruka inayamba ndi funso lokhudza moyo wonse lakuti “Kodi Ndiubwino wa Yani Umene Mumafunafuna?” Dziko limasonyeza mzimu wa Mdyerekezi wakudzifunira zokomera munthuwe. Komabe, Akristu ayenera kutsanzira mzimu wa Yesu Kristu wodzimana. Ha, nchitsanzo chabwino chotani nanga chimene iye anapereka! Anasiya ulemerero wakumwamba ndipo kenaka anapereka nsembe moyo wake waumunthu kaamba ka phindu lathu. Zitokoso zosonyeza kuti kaya ndiubwino wa yani umene timafunafuna zimabuka pamene pakhala kusamvana pakati pa Akristu m’nkhani zamalonda kapena zandalama, pamene pakhala kuwombana kwa maumunthu, ndi zina zotero. Zinthu zoterozo zimaika pachiyeso chikondi Chachikristu. Koma mwakufunafuna ubwino wa ena, munthu amakhaladi ndi chimwemwe chachikulu chakupatsa, ndipo adzapeza chivomerezo cha Yehova.
Ndiyeno panatsatira mutu wofanana kwambiri wakuti “Kuzindikira ndi Kugonjetsa Kufooka Kwauzimu.” Nkhaniyi inagogomezera kufunika kwakudziŵa zizindikiro za kufooka kwauzimu ndiyeno kuchitapo kanthu motsimikiza mtima m’kulimbana kwakugonjetsa Satana ndi misampha yake. Atumiki a Yehova ayenera kukulitsa chikondi chozama pa iye ndi udani pa chimene chiri choipa. Izi zimafuna kuti iwo amdziŵe Yehova mwa phunziro Labaibulo lokhazikika lokhala ndi cholinga, laumwini ndi labanja. Ayenera kupeŵa zosangulutsa zamtundu uliwonse zimene zimachirikiza chiwawa ndi chisembwere chakugonana. (Aefeso 5:3-5) Pemphero lanthaŵi zonse ndi kupezeka pamisonkhano mokhazikika zirinso zofunika m’kugonjetsa kufooka kwauzimu.
Mwinamwake imene anthu anakambitsirana kwambiri kuposa nkhani zonse zoperekedwa pamsonkhanowo inali ya mutu wakuti “Kodi Ukwati Ndiwo Mfungulo ya Chimwemwe?” Achichepere ambiri amaganiza choncho! Koma wokambayo anamveketsa bwino kuti pali zolengedwa zauzimu zokhulupirika zosaŵerengeka zimene ziri zachimwemwe ngakhale kuti sizokwatira, palinso Akristu odzipereka ambiri amene ali achimwemwe kwambiri ngakhale kuti sali muukwati. Ndiponso, okwatirana ambiri sali achimwemwe, monga momwe tikuwonera m’kukwera kwa zisudzulo. Wina angofunikira kulingalira pamadalitso ambiri amene Akristu odzipereka onse amasangalala nawo kotero kuti azindikire kuti ukwati, ngakhale kuti ungakhale dalitso, suli mfungulo ya chimwemwe.
Iyi inatsatiridwa ndi nkhani yosiirana yakuti “Ufulu Wachikristu m’Tsiku Lathu.” Wokamba woyamba analankhula pa “Mbali za Ufulu Wathu Wachikristu.” Izi zimaphatikizapo ufulu womasuka ku ziphunzitso zonyenga zachipembedzo monga Utatu, kusakhoza kufa kwa moyo wa munthu, ndi kuzunzika kwamuyaya. Kenako pali ufulu wakumasuka ku ukapolo wa uchimo. Ngakhale kuti Akristu ngopanda ungwiro, iwo ali omasuka ku zizoloŵezi zoipa monga kusuta, kutchova juga, uchidakwa, ndi kusadzisungira m’zakugonana. Palinso ufulu wakumasuka ku kupanda chiyembekezo, popeza kuti ali ndi chiyembekezo cha Paradaiso chimene chimawasonkhezera kuuzako ena ponena za icho.
Wokamba wotsatira anafunsa funso lakuti “Kodi Inu Monga Munthu Mumayamikira Ufulu Wotero?” Kuyamikira kumatanthauza kukonda, kusunga mosamalitsa. Kuti achite chimenecho, mtumiki wa Mulungu ayenera kuchenjera ndi chikhoterero chakufuna kupitirira malire a ufulu Wachikristu. Ufulu wadziko uli chinyengo, popeza kuti umagwetsera muukapolo wa uchimo ndi chivundi.
Wokamba womalizira m’nkhani yosiiranayo analankhula pa mutu wakuti “Okonda Ufulu Amachirimika.” Kuti achite chimenecho, Akristu ayenera kumamatira kwambiri kwa makolo awo akumwamba, Yehova ndi gulu lake longa mkazi wake. Anthu a Yehova sangadzilole kupambutsidwa ndi zonyengerera za mpatuko; iwo ayenera kukaniza awo amene amabweretsa malingaliro amakhalidwe oipa. Kuti achirimike muufulu waumulungu, Akristu ayenera kukhala ‘ndi moyo ndi mzimu.’—Agalatiya 5:25.
Nkhani yomalizira ya tsikulo inalidi yodzetsa chimwemwe. Mutu wake unali wakuti “Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako.” Yesu Kristu anali munthu wamkuluyo, popeza kuti iye anakhudza moyo wa anthu mwamphamvu kwambiri koposa magulu ankhondo onse amene anakhalako, magulu omenya nkhondo panyanja onse, nyumba zamalamulo zonse, ndi mafumu kuphatikiza pamodzi. Iye anali Mwana wa Mulungu, yemwe anakhalapo ndi moyo kumwamba asanabwere padziko lapansi. Yesu anatsanzira Atate wake wakumwamba bwino lomwe m’zimene ananena ndi kuphunzitsa ndi mmene anakhalira ndi moyo moti anakhoza kunena kuti: ‘Iye amene wandiwona ine wawona Atate.’ (Yohane 14:9) Ha, anasonyeza bwino chotani nanga Yesu kuti ‘Mulungu ndiye Chikondi’! (1 Yohane 4:8) Pambuyo pofotokoza zambiri ponena za mikhalidwe ya Yesu, wokambayo analongosola kuti mpambo wa nkhani zamutu wakuti “Moyo ndi Uminisitala za Yesu” unafalitsidwa mu Nsanja ya Olonda chiyambire mu April 1985. M’kuyankha mapempho ambiri, Sosaite tsopano inali kumasula bukhu latsopano lakuti The Greatest Man Who Ever Lived. Liri ndi mitu 133 ndipo linasindikizidwa m’mawonekedwe onse. Nkhani za mpambowo zinasindikizidwanso, ndipo zonse zinasonkhanitsidwa kupanga bukhu lamasamba 448. Zowonadi, tsiku la msonkhanoli linatha ndi chisangalalo chapadera!
Sande M’maŵa
Chigawo cha pa Sande m’maŵa chinayamba ndi nkhani yosiirana yakuti “Kutumikira Monga Asodzi a Anthu.” Nkhani yakuti “Kusodza Nsomba—Zenizeni ndi Zophiphiritsira” inayalira maziko nkhani zotsatirapo. Wokambayo anasonyeza kuti Yesu atachititsa kugwira nsomba kozizwitsa, anaitana asodziwo kukhala asodzi a anthu. Kwa nthaŵi yakutiyakuti, Yesu anaphunzitsa ophunzira ake kukhala asodzi a anthu, ndipo kuyambira pa Pentekoste wa 33 C.E., iwo anali achipambano m’kuthandiza makamu a amuna ndi akazi kukhala ophunzira.
Wokamba nkhani wotsatira anafotokoza fanizo la khoka lolembedwa pa Mateyu 13:47-50. Iye anasonyeza kuti khoka lophiphiritsira linaphatikizapo ponse paŵiri Akristu odzozedwa ndi Chikristu Chadziko, inde ndi chomalizirachi chifukwa cha ntchito yochitidwa yakutembenuza, kulemba, ndi kufalitsa Mabaibulo, ngakhale kuti zoyesayesa zimenezi zinakoka makamu aakulu a nsomba zosayenerera. Makamaka chiyambire 1919 pakhala ntchito yakulekanitsa, nsomba zosayenerera zikutaidwa, ndipo zabwinozo zikusonkhanitsidwira m’mipingo yonga zotengera imene yathandiza kutetezera ndi kusunga Akristu owona kaamba ka utumiki waumulungu.
Nkhani yachitatu, “Kusodza Anthu m’Madzi a Padziko Lonse,” inagogomezera thayo la Akristu onse odzipereka kukhala ndi phande m’kusodza kwapadziko lonse. Tsopano oposa pa 4,000,000 akukhala ndi phande m’ntchito imeneyi m’maiko oposa 200, ndipo m’zaka zaposachedwapa oposa pa 230,000 abatizidwa chaka chirichonse. Anthu a Yehova onse anasonkhezeredwa kukulitsa maluso awo akusodza, ndipo “asodzi” angapo achipambano kwenikweni anafunsidwa mafunso.
M’nkhani yotsatira, yamutu wakuti “Khalani Wogalamuka mu ‘Nthaŵi ya Mapeto,’” wokamba anandandalika zinthu zisanu ndi ziŵiri zothandiza anthu a Mulungu kukhala ogalamuka: kulimbana ndi zocheukitsa, kupemphera, kuchenjeza anthu za mapeto a dongosolo lino, kumamatira ku gulu la Yehova, kudzipenda kwa munthu wekha, kusinkhasinkha pamaulosi amene anakwaniritsidwa, ndi kukumbukira kuti chipulumutso chawo chiri pafupi kuposa pamene anakhala okhulupirira.
Programu ya m’maŵa inatha ndi kukambitsirana pa nkhani yakuti “Kodi Adzapulumuka Ndani ‘Nthaŵi ya Nsautso’?” Wokambayo anasonyeza mmene ulosi wa Yoweli unakwaniritsidwira kumlingo wakutiwakuti m’nthaŵi za atumwi, mmene ukupitirizira kukwaniritsidwa tsopano, ndi mmene udzakwaniritsidwira kotheratu mtsogolo pafupipa.
Sande Masana
Programu yamasana inayamba ndi nkhani yapoyera yakuti, “Kuchingamira Dziko Latsopano la Mulungu la Ufulu!” Nkhaniyi inapitiriza mutu wa msonkhanowo wa ufulu. Inasonyeza kuti Mawu a Mulungu amaneneratu za dziko latsopano m’mene mudzakhala ufulu womasuka ku chitsenderezo cha magulu a chipembedzo chonyenga, andale zadziko, azamalonda, ndi osankhana fuko. Mudzakhalanso ufulu womasuka ku uchimo ndi imfa. Thanzi langwiro lidzabwezeretsedwa kotero kuti anthu adzatha kukhala ndi moyo ku nthaŵi zonse m’chimwemwe padziko lapansi laparadaiso. Chifukwa chake, okonda chilungamo ali ndi chifukwa champhamvu chakuchingamira Mpangi wa dziko latsopano mwakufuula kuti: “Zikomo, Yehova, kaamba kakuti wadza ufulu wowona potsirizira pake!”
Nkhani yapoyera inatsatiridwa ndi chinachake chatsopano pa misonkhano yachigawo—kukambitsirana kwa phunziro la mlunguwo mu Nsanja ya Olonda. Ndiyeno msonkhanowo unafika kumapeto ndi nkhani yachisonkhezero ndi yolimbikitsa yakuti “Okonda Ufulu, Pitanibe Patsogolo.” Wokambayo mwachidule anamveketsa mfundo zazikulu za mutu wa msonkhano wa ufulu. Anagogomezera mmene anthu a Yehova aliri achimwemwe chifukwa cha ufulu, nandandalika njira zimene Akristu anapangira kupita patsogolo, ndi kuwasonkhezera kupitabe patsogolo mogwirizana kuti atute madalitso owonjezereka. Iye anamaliza ndi mawu akuti: “Pamene tikuchita zimenezi, Yehova apitirizetu kudalitsa aliyense wa tonsefe kotero kuti tipitebe patsogolo monga okonda ufulu.”
‘Pakuti cholengedwacho chagonjetsedwa kuutsiru, chosafuna mwini, koma chifukwa cha iye amene anachigonjetsa, ndi chiyembekezo kuti cholengedwa chomwe chidzamasulidwa ku ukapolo wa chivundi, ndi kuloŵa ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu.’—Aroma 8:20, 21.
[Zithunzi patsamba 25]
Nthumwi yachichepere pamsonkhano mu Prague, Chekosolovakiya
[Zithunzi patsamba 26]
1. Opita kuubatizo apita kumalo omizira mu Prague, Chekosolovakiya
2. Kubatizidwa monga mmodzi wa Mboni za Yehova mu Tallinn, Estonia
3. Zofalitsidwa zatsopano zinadzetsa chimwemwe kwa osonkhana mu Usolye-Sibirskoye, Siberia
4. Kumasulidwa kwa “New World Translation of the Holy Scriptures” m’zinenero za Chicheki ndi Chislovaki pamsonkhano mu Prague