Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 5/15 tsamba 10-15
  • Lingalirani Zitsanzo za Kuleza Mtima

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Lingalirani Zitsanzo za Kuleza Mtima
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Woleza Mtima Kaamba ka Dzina Lake
  • Kuleza Mtima Kaamba ka Anthu
  • Chitsanzo cha Kuleza Mtima cha Yesu
  • Zitsanzo Zina za Kuleza Mtima
  • Talingalirani Chitsanzo cha Paulo
  • Yehova Ndi Mulungu Woleza Mtima
    Nsanja ya Olonda—2001
  • ‘Valani Kuleza Mtima’
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Khalani Oleza Mtima pa Onse
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Kuleza Mtima
    Imbirani Yehova
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 5/15 tsamba 10-15

Lingalirani Zitsanzo za Kuleza Mtima

‘Mulungu . . . analekerera ndi [kuleza mtima kochuluka, “NW”] zotengera za mkwiyo zokonzekera chiwonongeko.’​—AROMA 9:22.

1. (a) Kodi Mawu ouziridwa a Mulungu amatipindulitsa motani? (b) Mogwirizana ndi chimenechi, kodi nchifukwa ninji mkhalidwe wa kuleza mtima ukulingaliridwa panopa?

YEHOVA Mulungu, Mlengi wathu, anatipatsa Mawu ake ouziridwa, Baibulo Lopatulika. Ilo liyenera kutumikira monga ‘nyali ya ku mapazi athu ndi kuunika kwa panjira pathu.’ (Salmo 119:105) Mawu a Mulungu amatithandizanso kukhala ‘okonzeka kuchita ntchito iriyonse yabwino.’ (2 Timoteo 3:16, 17) Njira imodzi imene limatikonzekeretsera ndiyo kutipatsa zitsanzo zabwino za kuleza mtima. Mkhalidwe umenewu uli chimodzi cha zipatso za mzimu wa Mulungu ndipo ngofunika koposa ku kupeza kwathu chivomerezo chake ndi kukhalira limodzi mogwirizana ndi anthu anzathu.​—Agalatiya 5:22, 23.

2. Kodi liwu Lachigiriki lomasuliridwa “kuleza mtima” limatanthauzanji, ndipo kodi ndani ali woyambirira m’kusonyeza mkhalidwe umenewu?

2 Liwu Lachigiriki lotembenuzidwa “kuleza mtima” m’lingaliro lenileni limatanthauza “mzimu wa kutalikitsa.” Kuleza mtima kwalongosoledwa kukhala “mkhalidwe wakudziletsa poyang’anizana ndi kuputidwa womwe sumabwezera mwamsanga kapena kupereka chilango mofulumira.” (Vine’s Expository Dictionary of Old and New Testament Words, lolembedwa ndi W. E. Vine, Volyumu 3, tsamba 12) Kukhala woleza mtima kumatanthauza kudziletsa ndi kukhala wolekereza. Ndipo kodi ndani yemwe ali woyambirira pakati pa awo omwe ali olekereza, kusonyeza kuleza mtima? Palibe wina woposa Yehova Mulungu. Chotero, pa Eksodo 34:6, tikuŵerenga kuti Yehova ali ‘Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wochuluka, ndi wachowonadi.’ Kwenikweni, Yehova akutchulidwa kukhala “wolekereza” nthaŵi zisanu ndi zitatu zowonjezereka m’Malemba.​—Numeri 14:18; Nehemiya 9:17; Salmo 86:15; 103:8; 145:8; Yoweli 2:13; Yona 4:2; Nahumu 1:3.

3. Kodi ndimikhalidwe iti imene imapangitsa kuleza mtima kwa Yehova?

3 Kukhala woleza mtima, kapena wolekereza, ndiko kumene tingayembekezere kwa Yehova Mulungu, popeza kuti iye ngopanda malire m’mphamvu ndi nzeru, wachiweruzo cholungama changwiro, ndipo ndiye munthu weniweni wa chikondi. (Deuteronomo 32:4; Yobu 12:13; Yesaya 40:26; 1 Yohane 4:8) Iye amailamulira mikhalidwe yake, akumailinganiza mwangwiro nthaŵi zonse. Kodi Mawu ake amavumbulanji ponena za chifukwa ndi mmene wasonyezera kuleza mtima kulinga kwa anthu opanda ungwiro?

Woleza Mtima Kaamba ka Dzina Lake

4. Kodi Mulungu wasonyeza kuleza mtima kulinga kwa ochimwa kaamba ka zifukwa zabwino ziti?

4 Kodi nchifukwa ninji Yehova ali woleza mtima? Kodi nchifukwa ninji samalanga ochimwa panthaŵi yomweyo? Sichifukwa chakuti alibe chikondwerero kapena changu kaamba ka chilungamo. Ayi, koma Yehova ali nzifukwa zabwino zokhalira wolekereza ndipo samalanga anthu mofulumira. Chifukwa china nchakuti dzina lake lidziŵikitsidwe. Chifukwa china nchakuti panafunikira nthaŵi kuti nkhani za uchifumu wa Mulungu ndi umphumphu wa anthu, zomwe zinadzutsidwa ndi kupanduka kwa m’Edene zithetsedwe. Komabe chifukwa china cha kuleza mtima kwa Mulungu nchakuti kumapatsa ochimwa mwaŵi wakuwongolera njira zawo.

5, 6. Kodi nchifukwa ninji Yehova anasonyeza kuleza mtima mchigwirizano ndi kupanduka kwa munthu?

5 Yehova anali woleza mtima pochita ndi anthu aŵiri oyambirira m’munda wa Edene. Pamene iwo anaswa lamulo lake loletsa kudya chipatso cha mtengo wakudziŵitsa zabwino ndi zoipa, iye akanawapha iwo ndi mngelo wochimwa yemwe ananyenga Hava panthaŵi yomweyo. Panalibe chikaikiro chirichonse kuti kulingalira kwa Yehova kwa chilungamo ndi chiweruzo cholungama kunalakwiridwa, kuti anakwiya ndi opanduka atatuwo. Iye akanakhala wolondola mwangwiro ngati akanaŵapha panthaŵi yomweyo. Mulungu anali atachenjeza mwamuna woyamba, Adamu kuti: ‘Koma mtengo wakudziŵitsa zabwino ndi zoipa usadye umenewo; chifukwa tsiku lomwe udzadya umenewo udzafa ndithu.’ (Genesis 2:17) Patsiku limene Adamu anachimwa, Mulungu anaitana olakwawo kuwazenga mlandu napereka chiweruzo cha imfa. Mwalamulo, Adamu ndi Hava anafa patsiku lomwelo. Komabe, Mlengi wathu woleza mtima anamulola Adamu kukhala ndi moyo kwa zaka 930.​—Genesis 5:5.

6 Mulungu anali ndi zifukwa zabwino zokhalira woleza mtima, kapena wolekereza, m’nkhaniyi. Ngati iye akanapha opandukawo panthaŵi yomweyo, ichi sichikanayankha chitonzo cha Mdyerekezi chakuti Yehova Mulungu sayenera kulambiridwa ndipo sangakhale ndi atumiki aumunthu omwe angasunge umphumphu wawo kwa iye mosasamala kanthu za mikhalidwe. Kuwonjezerapo, mafunso onga aŵa akanasiyidwa osayankhidwa: Kodi chinali cholakwa cha yani kuti Adamu ndi Hava anachimwa? Kodi poyambapo Yehova anawalenga ali ofooka mwamakhalidwe kwakuti sakanatha kuleŵa chiyeso ndiyeno nkuŵalanga chifukwa cholephera kuchita tero? Yankho la zonsezi nlowonekeratu kuchokera ku cholembedwa chopezeka m’bukhu la Yobu, mitu 1 ndi 2. Mwakulola fuko la anthu kuwonjezeka, Yehova anawalola anthu kukhala ndi mwaŵi wakutsimikizira zinenezo za Satana kukhala zabodza.

7. Kodi nchifukwa ninji Yehova sanamuphe Farao panthaŵi yomweyo?

7 Pamene Yehova anali pafupi kupulumutsa anthu ake, Aisrayeli, ku ukapolo Wachiigupto, iye anatsimikiziranso kukhala woleza mtima. Yehova akanakhoza kuwononga Farao ndi makamu ake ankhondo panthaŵi imodzi. Komabe, mmalo mochita zimenezi, Mulungu anaŵalekerera kwa kanthaŵi. Kaamba ka zifukwa zabwino zotani? Eya, m’kupita kwa nthaŵi, Farao anakhala wouma mutu m’kukana kwake kulola Aisrayeli kuchoka m’Igupto monga anthu aufulu a Yehova. Mwakutero iye anasonyeza kuti anali ‘chotengera cha mkwiyo’ choyenera chiwonongeko chifukwa chonyoza Yehova. (Aroma 9:14-24) Komabe, padali chifukwa chachikulu chimene Mulungu anakhalira woleza mtima m’nkhaniyi. Kupyolera mwa Mose, iye anamuuza Farao kuti: ‘Pakuti ndatambasula dzanja langa tsopano, kuti ndikupande iwe ndi anthu ako ndi mliri, ndi kuti uwonongeke pa dziko lapansi. Koma ndithu chifukwa chake ndakuimika kuti ndikuwonetse mphamvu yanga, ndi kuti alalikire dzina langa pa dziko lonse lapansi.’​—Eksodo 9:15, 16.

8. Kodi nchifukwa chabwino chotani chimene Mulungu sanaphere Aisrayeli opanduka m’chipululu?

8 Kuleza mtima kwa Yehova kunasonyezedwanso kaamba ka zifukwa zabwino pamene Aisrayeli anali m’chipululu. Iwo anayesa motani nanga kuleza mtima kwa Mulungu mwakulambira mwana wang’ombe wagolidi ndiponso mwakulephera kusonyeza chikhulupiriro pamene azondi khumi anabwerera ndi lipoti loipa! Mulungu sanawafafanize monga anthu ake popeza kuti dzina lake ndi mbiri yake yabwino zinaloŵetsedwamo. Inde, Yehova anasonyeza kuleza mtima kaamba ka dzina lake.​—Eksodo 32:10-14; Numeri 14:11-20.

Kuleza Mtima Kaamba ka Anthu

9. Kodi nchifukwa ninji Yehova anasonyeza kuleza mtima m’masiku a Nowa?

9 Yehova wakhala woleza mtima kwa anthu chiyambire pamene Adamu anachimwira mbadwa zake zonse, kuwachitira chisalungamo chachikulu mwakuchimwa. Kuleza mtima kwa Mulungu kunatheketsa kuti cholakwacho chiwongoleredwe nchakuti analola nthaŵi kaamba ka anthu olapa kukhala oyanjanitsidwa kwa iye. (Aroma 5:8-10) Yehova Mulungu anasonyezanso kuleza mtima kwa anthu m’tsiku la Nowa. Panthaŵiyo, ‘anaona Yehova kuti kuipa kwa anthu kunali kwakukulu pa dziko lapansi, ndiponso kuti ndingaliro zonse za maganizo a mitima yawo zinali zoipabe zokhazokha.’ (Genesis 6:5) Ngakhale kuti Mulungu akanatha kuseseratu fuko la anthu mwamsanga pamene anawona mkhalidwewu, iye analamula kuti akathetsa mkhalidwewo m’zaka 120. (Genesis 6:3) Kusonyezedwa kwa kuleza mtima kumeneku kunapatsa Nowa nthaŵi yakukhala ndi ana atatu, kuti akule ndi kukwatira, ndikuti banja limenelo limange chingalawa chopulumutsiramo miyoyo yawo ndi kupulumutsa zinyama. Mwanjirayi kunali kotheka kuti chifuno choyambirira cha Mulungu kaamba ka dziko lapansi chikwaniritsidwe.

10, 11. Kodi nchifukwa ninji Yehova anali woleza mtima motero ndi mtundu wa Israyeli?

10 Kumasulira kwina kwa kuleza mtima kumagwira ntchito makamaka m’zochita za Mulungu ndi anthu ake. Iko kuli “kupirira koleza mtima kwa cholakwa kapena kuputidwa, kophatikizapo kukana kutaya chiyembekezo cha chiwongolero cha unansi wosokonezedwawo.” (Insight on the Scriptures, Volyumu 2, tsamba 262; yofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.) Ichi chimasonya ku chifukwa chowonjezereka cha kuleza mtima kwa Mulungu kulinga kwa Aisrayeli. Iwo anafulatira Yehova mobwerezabwereza ndipo anakhala akapolo ku mitundu Yachikunja. Komabe, iye anasonyeza kuleza mtima mwakupulumutsa Aisrayeli ndikuwapatsa mwaŵi wakulapa.​—Oweruza 2:16-20.

11 Mafumu ambiri a Israyeli anatsogolera nzika zawo m’kulambira konyenga. Kodi Mulungu anachotsa mtunduwo panthaŵi yomweyo? Ayi, iye sanataye msanga chiyembekezo chakuwongolera unansi wosokonezedwawo. Mmalomwake, Yehova analekereza. Akumasonyeza kuleza mtima, Mulungu anaŵapatsa mwaŵi mobwerezabwereza wakuti alape. Timaŵerenga pa 2 Mbiri 36:15, 16 kuti: ‘Ndipo Yehova Mulungu wa makolo awo anatumiza kwa iwo ndi dzanja la mithenga yake, nalaŵirira mamawa kuituma, chifukwa anamvera chifundo anthu ake, ndi pokhala pake; koma ananyodola mithenga ya Mulungu, napeputsa mawu ake, naseka aneneri ake, mpaka ukali wa Mulungu unaukira anthu ake, mpaka panalibe cholanditsa.’

12. Kodi Malemba Achikristu Achigiriki akupereka umboni wotani wonena za chifukwa chimene Yehova aliri woleza mtima?

12 Malemba Achikristu Achigiriki amaperekanso umboni wakuti Yehova amasonyeza kuleza mtima kuti athandize anthu ake olakwa. Mwachitsanzo, mtumwi Paulo anafunsa Akristu ochimwa kuti: ‘Kapena upeputsa kodi kulemera kwa ubwino wake ndi chilekerero ndi chipiriro chake, wosadziŵa kuti ubwino wa Mulungu ukubwezera kuti ulape?’ (Aroma 2:4) Olingana nawo ali mawu a Petro akuti: [Yehova, NW] sazengereza nalo lonjezano, monga ena achiyesa chizengerezo; komatu aleza mtima kwa inu, wosafuna kuti ena awonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.’ (2 Petro 3:9) Moyenerera kwenikweni, tikuuzidwa ‘kukuyesa kulekerera kwa Ambuye wathu chipulumutso.’ (2 Petro 3:15) Chotero, tikuwona kuti Yehova ngoleza mtima, osati chifukwa cha malingaliro kapena kupepera, koma chifukwa chakuti dzina lake ndi zifuno zikuloŵetsedwamo ndipo iye ngwachifundo ndiponso wachikondi.

Chitsanzo cha Kuleza Mtima cha Yesu

13. Kodi ndiumboni Wamalemba wotani umene ulipo wakuti Yesu Kristu anali woleza mtima?

13 Chachiŵiri chokha kwa chitsanzo cha kuleza mtima chosonyezedwa ndi Mulungu ndichija cha Mwana wake, Mesiya, Yesu Kristu. Iye alidi chitsanzo chabwino koposa cha kudziletsa popanda kubwezera kofulumira mosasamala kanthu za kulakwiridwa.a Umboni wakuti Mesiya akakhala woleza mtima unaloseredwa ndi mneneri Yesaya m’mawu aŵa: ‘Iye anatsenderezedwa koma anadzichepetsa yekha osatsegula pakamwa pake; ngati nkhosa yotsogoleredwa kukaphedwa, ndi ngati mwana wa nkhosa amene ali du pamaso pa omsenga, motero sanatsegula pakamwa pake.’ (Yesaya 53:7) Yotsimikizira chowonadi chomwecho ndi ndemanga iyi ya Petro: ‘Pochitidwa chipongwe sanabwezera chipongwe, pakumva zowawa, sanaopsa, koma anapereka mlandu kwa iye woweruza kolungama.’ (1 Petro 2:23) Yesu ayenera kuti anayesedwa motani nanga pamene ophunzira ake ankatsutsana mobwerezabwereza ponena za amene anali wamkulu koposa! Komabe, iye anali woleza mtima motani nanga ndi wolekerera kwa iwo!​—Marko 9:34; Luka 9:46; 22:24.

14. Kodi chitsanzo cha Yesu cha kuleza mtima chiyenera kutifulumiza kuchita chiyani?

14 Tiyenera kutsanzira chitsanzo chimene Yesu anakhazikitsa cha kukhala woleza mtima. Paulo analemba kuti: ‘Tithamange mwachipiriro makaniwo adatiikira, ndi kupenyerera woyambira ndi womaliza wa chikhulupiriro chathu, Yesu, ameneyo, chifukwa cha chimwemwe choikidwacho pamaso pake, anapirira [mtengo wozunzirapo, NW] nanyoza manyazi, nakhala pa dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu. Pakuti talingalirani iye amene adapirira ndi ochimwa otsutsana naye kotere, kuti mungaleme ndi kukomoka m’moyo mwanu.’​—Ahebri 12:1-3.

15. Kodi timadziŵa motani kuti Yesu anali woleza mtima ndipo anapirira ziyeso mofunitsitsa?

15 Chenicheni chakuti Yesu anali woleza mtima ndipo anapirira ziyeso mofunitsitsa chingawonekere mwa mkhalidwe umene anasonyeza panthaŵi ya kugwidwa kwake. Pambuyo pomdzudzula Petro chifukwa chosolola lupanga kuti achinjirize Mbuye wake, Yesu anati: ‘Kapena uganiza kuti sindingathe kupemphera kwa Atate wanga, ndipo Iye adzanditumizira tsopano lino mabungwe a angelo oposa khumi ndi aŵiri? Koma pakutero malembo adzakwaniridwa bwanji, pakuti kuyenera chomwecho?’​—Mateyu 26:51-54; Yohane 18:10, 11.

Zitsanzo Zina za Kuleza Mtima

16. Kodi Malemba amasonyeza motani kuti Yosefe, mwana wa Yakobo anali woleza mtima?

16 Ngakhale anthu opanda ungwiro, ochimwa angasonyeze kuleza mtima. Malemba Achihebri ali ndi zitsanzo za kupirira koleza mtima kwa zolakwa za anthu opanda ungwiro. Mwachitsanzo, pali Yosefe, mwana wa Yakobo, kholo Lachihebri. Iye anapirira moleza mtima motani nanga chisalungamo chochitiridwa kwa iye ndi abale ake opeza ndi mkazi wa Potifara! (Genesis 37:18-28; 39:1-20) Yosefe sanalole ziyeso zimenezi kumpangitsa kukhala woipidwa. Izi zinawonekera pamene anauza abale ake kuti: “Musaphwetekwe mtima, musadzikwiyira inu nokha, kuti munandigulitsira ine kuno, pakuti Mulungu ananditumiza ine patsogolo panu kuti ndisunge moyo.” (Genesis 45:4, 5) Ha, ndichitsanzo chabwino chotani nanga cha kuleza mtima chimene Yosefe anakhazikitsa!

17, 18. Kodi tiri ndi umboni wotani wa kuleza mtima m’chochitika cha Davide?

17 Davide alinso chitsanzo china cha mtumiki wokhulupirika wa Yehova yemwe anapirira zolakwa moleza mtima, kusonyeza kuleza mtima. Akulondoledwa monga galu ndi Mfumu Sauli wansanjeyo, pazochitika ziŵiri Davide akanabwezera mwakumupha iye. (1 Samueli 24:1-22; 26:1-25) Koma Davide anayembekeza pa Mulungu, monga momwe kukuwonekera m’mawu ake kwa Abisai: ‘Yehova adzakantha [Sauli]; kapena tsiku la imfa yake lidzafika; kapena adzatsikira kunkhondo, nadzafako. Yehova andiletse ine kusamula dzanja langa pa wodzozedwa wa Yehova.’ (1 Samueli 26:10, 11) Inde, Davide anali nayo mphamvu yakuthetsa kusautsidwa kwake ndi Sauli. Mmalomwake, Davide anasankha kuleza mtima.

18 Lingaliraninso zimene zinachitika pamene Mfumu Davide ankhathaŵa mwana wake wachinyengo Abisalomu. Simeyi, Mbenjamini wa nyumba ya Sauli, anaponya Davide miyala namtukwana, nafuula: ‘Choka, choka, munthu wa mwazi iwe, woipa iwe.’ Abisai anafuna kuti Simeyi aphedwe, koma Davide anakana kubwezera. Mmalo mochita chimenechi, iye anasonyezanso mkhalidwe wa kuleza mtima.​—2 Samueli 16:5-13.

Talingalirani Chitsanzo cha Paulo

19, 20. Kodi mtumwi Paulo anadzisonyeza motani kukhala woleza mtima?

19 M’Malemba Achikristu Achigiriki, timapeza chitsanzo china chabwino cha kuleza mtima kwa munthu wopanda ungwiro​—mtumwi Paulo. Iye anasonyeza kupirira koleza mtima, kuleza mtima, mogwirizana ndi ponse paŵiri adani ake achipembedzo ndi anthu odzitcha Akristu. Inde, Paulo anasonyeza kuleza mtima ngakhale kuti ena mumpingo wa Korinto ananena kuti: ‘Akalatatu, ati, ndiwo olemera, ndi amphamvu; koma mawonekedwe a thupi lake ngofooka, ndi mawu ake ngachabe.’​—2 Akorinto 10:10; 11:5, 6, 22-33.

20 Chotero, Paulo anali ndi chifukwa chabwino chimene anauzira Akorinto kuti: ‘M’zonse tidzitsimikizira ife tokha monga atumiki a Mulungu, m’kupirira kwambiri, m’zisautso, m’zikakamizo, m’zopsinja, m’mikwingwirima, m’ndende, m’mapokoso, m’mavutitso, m’madikiro, m’masalo a chakudya; m’mayendedwe, m’chidziŵitso, m’chilekerero, m’kukoma mtima, mwa mzimu woyera, m’chikondi chosanyenga.’ (2 Akorinto 6:4-6) M’lingaliro lofananalo, mtumwiyo anakhoza kulembera wantchito mnzake Timoteo kuti: ‘Iwe watsatatsata chiphunzitso changa, mayendedwe, chitsimikizo mtima, chikhulupiriro, kuleza mtima, chikondi, chipiriro, mazunzo, kumva zowawa; . . . ndipo m’zonsezi Ambuye anandilanditsa.’ (2 Timoteo 3:10, 11) Ha, mtumwi Paulo anatikhazikitsira chitsanzo chabwino chotani nanga cha kuleza mtima!

21. Kodi nkhani yotsatira ingatithandize motani?

21 Momvekera bwino, Malemba ngodzaza ndi zitsanzo zabwino za kuleza mtima. Yehova ndi Mwana wake wokondedwa ndiwo zitsanzo zazikulu. Koma nkolimbikitsa chotani nanga kudziŵa kuti mkhalidwe umenewu wasonyezedwa ndi anthu opanda ungwiro, monga ngati Yosefe, Davide, ndi mtumwi Paulo! Nkhani yotsatira yakonzedwera kutithandiza kutsanzira zitsanzo zabwino zimenezo.

[Mawu a M’munsi]

a Kukhala woleza mtima sikumatanthauza kungovutika kwa nthaŵi yaitali. Ngati munthu wovutika kwa nthaŵi yaitali anakwiyitsidwa kapena kuipidwa chifukwa chakuti sakhoza kubwezera, iye sangakhale woleza mtima.

Kodi Mungayankhe Motani?

◻ Kodi kukhala woleza mtima kumatanthauzanji?

◻ Kodi Yehova wakhala woleza mtima makamaka kaamba ka zifukwa zotani?

◻ Kodi ndi m’njira zotani mmene Yesu anadzisonyezera kukhala woleza mtima?

◻ Kodi pali umboni Wamalemba wotani wakuti kuleza mtima kungasonyezedwe ndi anthu opanda ungwiro?

[Zithunzi patsamba 10]

Yosefe, Yesu, Davide, Paulo, ndi Yobu anali zitsanzo za kuleza mtima

[Chithunzi patsamba 13]

Yesu anasonyeza kuleza mtima kulinga kwa ophunzira ake

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena