Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
◼ Pa Mateyu 10:21, kodi Yesu anali kutichenjeza kuti abale ambiri mumpingo adzaukira abale awo auzimu?
Ayi, imeneyo sindiyo mfundo ya chenjezo la Yesu, limene limati: ‘Ndipo mbale adzapereka mbale wake kuimfa, ndi atate mwana wake: ndipo ana adzatsutsa akuŵabala, nadzaŵafetsa iwo.’—Mateyu 10:21.
Mawu apatsogolo ndi apambuyo amasonyeza kuti Yesu ananena izi kwa atumwi 12 pamene anaŵatumiza paulendo wolalikira m’Israyeli. Zochuluka zomwe ananena zinali ndi tantahuzo lalikulu kwa atumwiwo. Mwachitsanzo, iye ananena kuti iwo anapatsidwa mphamvu yochiritsa mozizwitsa, kutulutsa ziŵanda, ndipo ngakhale kuukitsa akufa. (Mateyu 10:1, 8; 11:1) Mbiri yakale imatsimikizira kuti si Akristu onse analandira mphamvu zozizwitsa zoterozo, kutsimikizira kuti Yesu pano anali kulankhula kwa omvetsera odziŵika bwino—atumwi ake.
Komabe, zinthu zina zimene Yesu ananena zinaposa pa maulendo olalikira a atumwi. Iye anaŵauza kuti: ‘Chenjerani ndi anthu; . . . adzamuka nanu kwa akazembe ndi mafumu chifukwa cha ine, kukhala mboni ya kwa iwo, ndi kwa anthu akunja.’ (Mateyu 10:17, 18) Paulendowo, atumwi 12 amenewo mwachiwonekere anakumana ndi chitsutso, koma palibe umboni wakuti iwo anatengedwa “kwa akazembe ndi mafumu” kukachitira umboni kwa “anthu akunja.”a M’zaka zapambuyo pake, atumwiwo anawonekera pamaso pa olamulira, onga Mfumu Herode Agripa I ndi II, Sergio Paulo, Galiyo, ndipo ngakhale Wolamulira Nero. (Machitidwe 12:1, 2; 13:6, 7; 18:12; 25:8-12, 21; 26:1-3) Chotero mawu a Yesu anagwira ntchito pambuyo pake.
Uphungu wa Yesu unapitiriza ndi chenjezo lakuti: ‘Mbale adzapereka mbale wake kuimfa.’ Iye sanali kuloza kwa abale auzimu monga momwe sanali kulozera kwa atate auzimu kapena ana ndi mawu ake otsatira m’vesi 21 akuti: ‘Atate [adzapereka] mwana wake: ndipo ana adzatsutsa akuŵabala, nadzaŵafetsa iwo.’ Yesu anatanthauza kuti atumwi akakhoza kuyembekezera chidani kapena chitsutso kuchokera ngakhale kwa achibale.—Mateyu 10:35, 36.
Atumwiwo akafunikira chipiriro paulendo wolalikirawo. Yesu anapitirizabe kuti: ‘Adzada inu anthu onse chifukwa cha dzina langa; koma iye wakupirira kufikira chimaliziro, iyeyu adzapulumutsidwa.’—Mateyu 10:22.
Zinthu zina zimene Yesu anena pa chochitikacho ziri ndi tanthauzo kwa ife monga Mboni za Yehova lerolino. Ulaliki wathu umagogomezera Ufumu. Timachita uminisitala wathu kwaulere ndi kufunafuna anthu amene ali okondweretsedwa ndi uthengawo kapena amene ali ouyenerera. Kuchenjera nkoyenera. Otsutsa ngochuluka. Nthaŵi zina achibale, anansi, kapena ogwira nawo ntchito amadzetsa mavuto oopsa, makamaka kwa anthu owona mtima amene ayamba kulondola njira ya Chikristu chowona. Yesu anabwereza chenjezo lonena za chitsutso choterocho pamene anali kufotokoza ‘chizindikiro’ cha kukhalapo kwake. (Mateyu 24:3, 9, 10; Luka 21:16, 17) Iye anabwerezanso kufunikira kwathu kwa ‘kulimbika chilimbikire kufikira chimaliziro kuti tipulumuke.’ Inde, tifunikira kulimbika kufikira mapeto a moyo wathu kapena kufikira dongosolo iri la zinthu litha ndipo tingaloŵe m’dziko latsopano.—Mateyu 24:13.
[Mawu a M’munsi]
a Matembenuzidwe ena amamasulira mawuwo “osapembedza” (The Jerusalem Bible), “Akunja” (New International Version ndi matembenuzidwe a Moffatt ndi Lamsa), ndi “osakhulupirira” (The New English Bible).