Baibulo—Kodi Nlopatulikadi?
KODI ndi anthu angati lerolino amene amaliwona Baibulo kukhala lopatulika, Mawu a Mulungu? M’nyengo ino ya kukaikira, ambiri amalilingalira kukhala lachikale ndipo losayenerera, akumakaikira ngati liridi lopatulika. Ngakhale atsogoleri ena achipembedzo a Chikristu Chadziko amaphunzitsa kuti Baibulo nlodzazidwa ndi nthano ndi nthanthi. Amakaikira kuti ‘kaya kumasulira kwa Baibulo kwa mbiri yakale kungakhulupiriridwe ndi munthu waluntha.’—The Interpreter’s Dictionary of the Bible, Volyumu 2, tsamba 611.
Akatswiri otchuka akufesa mbewu za chikaikiro ponena za kuyenera kwa kulitcha Baibulo kukhala Mawu a Mulungu. Wina ananena kuti “ngati munthu akufuna kugwiritsira ntchito mtundu wa chinenero cha Mawu a Mulungu, mawu oyenerera kutchera Baibulo ngakuti ndi Mawu a Israyeli, Mawu a Akristu ena otchuka oyambirira.” (The Bible in the Modern World, lolembedwa ndi James Barr) Kodi mukulingalira motani? Kodi Baibulo ndi Mawu a Mulungu? Kodi nlopatulikadi?
Kodi Ndani Analemba Baibulo?
Kulembedwa kwa Genesis, bukhu loyamba la Baibulo, mwamwambo kumasonyedwa kwa Mose, Mhebri yemwe anakhala ndi moyo zaka 3,500 zapitazo. Mogwirizana ndi Baibulo lenilenilo, pafupifupi anthu 40 ochokera kumbali zosiyanasiyana za moyo anakhala ndi phande kulemba Malemba onse, kutulukapo kusonkhanitsidwa kwa mabuku 66, kapena zigawo za Baibulo. Komabe, amuna ameneŵa sanadzilingalire kukhala akonzi enieni a Baibulo. Wolemba wina anati: “Lemba liri lonse adaliuzira Mulungu.” (2 Timoteo 3:16) Wina analemba motere ponena za olemba Baibulo: “Anthu analankhula zochokera kwa Mulungu pamene anagwidwa ndi mzimu woyera.”—2 Petro 1:21, NW.
Ichi chimaika olembawo m’gulu la olembera, kapena alembi, olamuliridwa, kapena kutsogozedwa, ndi Mulungu. Mogwirizana ndi kunena kwa Baibulo, wolembayo kaŵirikaŵiri ankaloledwa kusankha mawu akeake polongosola chidziŵitso chopatsidwa ndi Mulungu. (Habakuku 2:2) Chimenecho ndicho chifukwa chake pali kalembedwe kosiyana m’Baibulo lonse. Koma kulembedwako nthaŵi zonse kunatsogozedwa ndi Mulungu.
Zowonadi, zonena za olembewo zakuti anauziridwa mwaumulungu mwa izo zokha siziri umboni wakuti Baibulo ndi uthenga waumulungu wochokera kwa Mlengi wonka kwa anthu. Komabe, kaya Wam’mwambamwambayo ndiye Mkonzi wa Baibulo kapena ayi kuyenera kuwonedwa bwino lomwe mwakulisanthula bukhulo mosamalitsa ndiponso mosapotozedwa maganizo. Kodi Baibulo limapereka umboni wokhala ndi mkonzi waumulungu? Kodi tinganenedi ndi chidaliro kuti Baibulo nlopatulika?